Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 74 tsamba 176-tsamba 177 ndime 4
  • Yesu Anakhala Mesiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anakhala Mesiya
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yohane Abatiza Yesu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankabatizidwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Anali Kalambula Bwalo wa Mesiya
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yohane Anakonza Njira
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 74 tsamba 176-tsamba 177 ndime 4
Yesu atabatizidwa ndi Yohane, mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unadzamutera

MUTU 74

Yesu Anakhala Mesiya

Yohane ankalalikira kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera.’ Yesu ali ndi zaka 30 anapita kumtsinje wa Yorodano kumene Yohane ankabatiza anthu. Pa nthawiyi Yesu ankachokera ku Galileya. Iye ankafuna kuti Yohane amubatize koma Yohaneyo anati: ‘Ayi, ine si woyenera kubatiza inu. Inuyo ndi amene mukuyenera kundibatiza ine.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Yehova akufuna kuti undibatize.’ Choncho anapita mumtsinje wa Yorodano ndipo Yohane anabatiza Yesu pomuviika thupi lonse m’madzi.

Yesu atavuuka m’madzimo anayamba kupemphera. Ndiyeno kumwamba kunatseguka ndipo mzimu wa Mulungu wooneka ngati nkhunda unatsika n’kudzamutera. Kenako Yehova analankhula ali kumwamba kuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”

Mzimu wa Mulungu utafika pa Yesu, Yesuyo anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Tsopano anali wokonzeka kuyamba kugwira ntchito imene Mulungu anamutuma.

Yesu atangobatizidwa anapita m’chipululu ndipo anakhalamo masiku 40. Atachoka m’chipululumo anapita kukaona Yohane. Yohane ataona Yesu akubwera poteropo anati: ‘Uyu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.’ Apa Yohane ankafuna kuti anthu adziwe kuti Yesu ndi Mesiya. Koma kodi ukudziwa zimene zinachitika pamene Yesu anali kuchipululu? Tiona m’mutu wotsatira.

“Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.’”​—Maliko 1:11

Mafunso: N’chifukwa chiyani Yesu anabatizidwa? N’chifukwa chiyani Yohane ananena kuti Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu?

Mateyu 3:13-17; Maliko 1:9-11; Luka 3:21-23; Yohane 1:29-34; Yesaya 42:1; Aheberi 10:7-9

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena