MUTU 100
Paulo ndi Timoteyo
Timoteyo anali m’bale wachinyamata mumpingo wa ku Lusitara. Bambo ake anali Mgiriki ndipo mayi ake anali Myuda. Timoteyo anaphunzira Mawu a Mulungu kuyambira ali wakhanda ndipo amene ankamuphunzitsa ndi mayi ake, a Yunike ndi agogo ake, a Loisi.
Paulo atafika ku Lusitara pa ulendo wake wachiwiri, anazindikira kuti Timoteyo amakonda kwambiri abale ndipo ali ndi mtima wofuna kuwathandiza. Choncho Paulo anapempha Timoteyo kuti aziyenda naye. Paulo anaphunzitsa Timoteyo kulalikira komanso kuphunzitsa uthenga wabwino mwaluso.
Mzimu woyera unkathandiza Paulo ndi Timoteyo kulikonse kumene ankapita. Tsiku lina usiku, Paulo anaona m’masomphenya munthu akumuuza kuti apite ku Makedoniya kukawathandiza. Choncho Paulo, Timoteyo, Sila ndi anthu ena anapita kukalalikira ku Makedoniya ndipo anakhazikitsa mipingo.
Atafika mumzinda wa Tesalonika, anthu ambiri anakhala Akhristu. Koma Ayuda ena ankachitira nsanje Paulo ndi anzakewo. Iwo anakopa gulu la anthu n’kutenga Paulo ndi anzakewo kupita nawo kwa olamulira a mzinda. Anthuwo ankafuula kuti: ‘Anthu awa ndi adani a boma la Roma!’ Apa moyo wa Paulo ndi Timoteyo unali pa ngozi choncho kutangoda iwo anathawira ku Bereya.
Anthu a ku Bereya anali ofunitsitsa kumvetsera uthenga wabwino ndipo Agiriki ndi Ayuda omwe, anakhala okhulupirira. Koma Ayuda amene anachokera ku Tesalonika atabwera anayambitsa chipolowe, ndiye Paulo anachoka kupita ku Atene. Timoteyo ndi Sila anatsala ku Bereya komweko kuti azilimbikitsa abale. Patapita nthawi, Paulo anatumiza Timoteyo ku Tesalonika kuti akalimbikitse abale kumeneko, omwe ankazunzidwa kwambiri. Kenako anamutumizanso kumipingo ina kuti akalimbikitse abale ndi alongo.
Paulo anauza Timoteyo kuti: ‘Amene akufuna kutumikira Yehova adzazunzidwa.’ Timoteyo anazunzidwa ndiponso kutsekeredwa m’ndende chifukwa chotumikira Mulungu. Iye ankaona kuti umenewu unali mwayi wake wosonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova.
Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: ‘Ndakutumizirani Timoteyo kuti adzakuphunzitseni zoyenera kuchita potumikira Mulungu komanso polalikira.’ Paulo anachita zimenezi chifukwa chakuti Timoteyo anali wodalirika. Paulo ndi Timoteyo ankagwirizana kwambiri ndipo anatumikira Mulungu limodzi kwa zaka zambiri.
“Ndilibe wina amene ali ndi mtima ngati wake, amene angasamaliredi moona mtima zosowa zanu. Anthu ena onse akungoganizira zofuna zawo zokha, osati za Yesu Khristu.”—Afilipi 2:20, 21