Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 101 tsamba 234-tsamba 235 ndime 4
  • Paulo Anatumizidwa ku Roma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paulo Anatumizidwa ku Roma
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • “Palibe Amene Ataye Moyo Wake”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Lengezani Ufumu wa Yehova Molimba Mtima!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Anachitira Umboni Mokwanira”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 101 tsamba 234-tsamba 235 ndime 4
Ngalawa inasweka pafupi ndi chilumba cha Melita ndipo Paulo ndi anthu ena akusambira kapena kugwiritsa ntchito zidutswa za ngalawa zomwe zinkayandama kuti apulumuke

MUTU 101

Paulo Anatumizidwa ku Roma

Ulendo wachitatu wa Paulo unakathera ku Yerusalemu. Atafika kumeneko anamangidwa. Ndiyeno usiku anaona masomphenya. Yesu anamuuza kuti: ‘Udzapita ku Roma ndipo ukalalikira kumeneko.’ Paulo anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku Kaisareya komwe anakakhala m’ndende zaka ziwiri. Pa nthawi imene mlandu wake unkazengedwa ndi bwanamkubwa wina dzina lake Fesito, Paulo ananena kuti: ‘Ndikupempha kuti mlandu wangawu ukaweruzidwe kwa Kaisara.’ Ndiyeno Fesito anati: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Popita ku Romako Paulo anatengedwa pa sitima yapamadzi ndipo abale awiri, Luka ndi Arisitako anapita nawo.

Ali panyanja kunachitika chimphepo choopsa kwa masiku ambiri. Aliyense ankaganiza kuti palibe amene apulumuke. Koma Paulo ananena kuti: ‘Anthu inu, mngelo wandiuza m’maloto kuti: “Usaope Paulo. Ukafika ku Roma ndipo aliyense musitimayi saafa.” Choncho musachite mantha. Palibe amene afe.’

Chimphepocho chinawomba kwa masiku 14. Kenako anayamba kuona chilumba cha Melita. Koma sitimayo inatitimira mumchenga ndipo inayamba kusweka chifukwa cha mafunde. Ngakhale zinali choncho, anthu onse 276 amene anali mmenemo anakafika kumtunda. Ena anasambira pomwe ena anagwiritsa ntchito zidutswa za sitimayo zomwe zinkayandama. Atafika, anthu apachilumbapo anawalandira bwino n’kuwayatsira moto kuti awothe.

Patapita miyezi itatu, asilikali anatenga Paulo pa sitima ina n’kupita naye ku Roma. Atafika, abale anabwera kudzamuona. Paulo atawaona anathokoza Yehova ndipo analimba mtima. Ngakhale kuti anali mkaidi, ankaloledwa kukhala m’nyumba ina ya lendi ndipo ankalonderedwa ndi msilikali. Iye anakhala kumeneko zaka ziwiri. Anthu akabwera kudzamuona, ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso za Yesu. Komanso iye analemba makalata opita kumipingo ya ku Asia Minor ndi ku Yudeya. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito Paulo kuti uthenga wabwino ufike kwa anthu a mitundu ina.

“Tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta.”​—2 Akorinto 6:4

Mafunso: N’chifukwa chiyani Fesito anatumiza Paulo ku Roma? Kodi n’chiyani chinachitika pamene Paulo ankapita ku Roma?

Machitidwe 21:30; 23:11; 25:8-12; 27:1-44; 28:1-31; Aroma 15:25, 26

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena