NYIMBO 1
Makhalidwe a Yehova
Losindikizidwa
1. Yehova M’lungu ndinu wamphamvu.
Mumapereka moyo ndi kuwala.
Chilengedwe chimalengezadi
Zamphamvu zanu zazikulu.
2. Mumaweruza mwachilungamo.
Mwatiphunzitsa malamulo anu.
Timapezanso nzeru zakuya
Tikawerenga mawu anu.
3. Ndinu wabwino mumatikonda.
Mumatipatsa mphatso zabwinodi.
Tilalikire za dzina lanu
Mosangalala nthawi zonse.
(Onaninso Sal. 36:9; 145:6-13; Mlal. 3:14; Yak. 1:17.)