NYIMBO 35
“Muzitha Kusankha Zinthu Zimene Ndi Zofunikadi Kwambiri”
Losindikizidwa
1. Kuzindikira kumatithandiza
Kusankha mwanzeru.
Timadziwa zomwe n’zofunika
Kuti tizizichita.
(KOLASI)
Tizidana ndi zoipa
Kuti M’lungu
Azisangalala.
Tizipeza madalitso
Tikamasankha zofunika.
2. Palibe chofunika kuposa
Kulengeza uthenga,
Kufufuza a njala ya choonadi
N’kuwaphunzitsa.
(KOLASI)
Tizidana ndi zoipa
Kuti M’lungu
Azisangalala.
Tizipeza madalitso
Tikamasankha zofunika.
3. Tikamachita zofunika
Tidzakhala okhutira.
Mtendere wa Mulungu
Udzateteza mitima yathu.
(KOLASI)
Tizidana ndi zoipa
Kuti M’lungu
Azisangalala.
Tizipeza madalitso
Tikamasankha zofunika.
(Onaninso Sal. 97:10; Yoh. 21:15-17; Afil. 4:7.)