NYIMBO 103
Abusa Ndi Mphatso
Losindikizidwa
1. Yehova watipatsa mphatso,
Abusa mu mpingo.
Mwachitsanzo chawo chabwino
Amatiphunzitsa.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa akulu
Omwe timadalira.
Amadera nkhawa tonsefe
Ndiye tiziwakonda.
2. Abusawa ndi achikondi,
Amaleza mtima.
Tikapunthwa amathandiza
Kutitu tichire.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa akulu
Omwe timadalira.
Amadera nkhawa tonsefe
Ndiye tiziwakonda.
3. Amatipatsa malangizo,
Tisasocheretu.
Tizisangalatsa Mulungu
Pomutumikira.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa akulu
Omwe timadalira.
Amadera nkhawa tonsefe
Ndiye tiziwakonda.
(Onaninso Yes. 32:1, 2; Yer. 3:15; Yoh. 21:15-17; Mac. 20:28.)