NYIMBO 119
Tikhale Ndi Chikhulupiriro Cholimba
Losindikizidwa
1. Kale Mulungu ankalankhula
Kudzera mwa aneneri.
Pano kudzera mwa Mwana wake
Akuti: ‘Lapanitu.’
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni
M’pamene tingadzapulumuke.
2. Timamvera lamulo la Yesu
Loti tizilalikira.
Tilengezabe molimba mtima,
Anthu amve uthenga.
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni
M’pamene tingadzapulumuke.
3. Talimbitsa chikhulupiriro
Sitidzabwerera m’mbuyo.
Tikudziwa kuti M’lungu wathu
Adzatipulumutsa.
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni
M’pamene tingadzapulumuke.
(Onaninso Aroma 10:10; Aef 3:12; Aheb. 11:6; 1 Yoh. 5:4.)