NYIMBO 125
“Osangalala Ndi Anthu Achifundo”
Losindikizidwa
1. Yehova ndi wachifundo,
Amasonyeza chifundo.
Iye ndi wokoma mtima.
Amatisamaliradi.
Amamvanso mapemphero
Ochokera kwa olapa.
Amadziwa ndife fumbi,
Amatikomera mtima.
2. Tikachimwa n’kupemphera,
M’lungu amakhululuka.
Yesu anatiphunzitsa
Mmene tingapempherere,
Muzitikhululukira,
Takhululukira ena.
Tisasungenso zifukwa.
Tidzapezadi mtendere.
3. Tikapatsa ena mphatso
Tizisonyeza chifundo.
Tisamafune kutchuka
Koma kungowathandiza.
M’lungu yemwe amaona
Adzatibwezera ndithu.
Anthu onse achifundo
Mulungu amawakonda.
(Onaninso Mat. 6:2-4, 12-14.)