NYIMBO 127
Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
Losindikizidwa
1. Ndipereke chani kwa inu M’lungu
Pokuthokozani chifukwa cha moyo?
Mawu anuwa amandiunikira.
Ndithandizeni kuti ndidzifufuze.
(VESI LOKOMETSERA)
Ndalonjeza kutumikira inu
Mofunitsitsa ndi moyo wanga wonse.
Ndinasankha ndekha kutumikira.
Ndikufuna n’kusangalatseni.
M’lungu n’thandizeni kudzifufuza
Kuti ndizichita chifuniro chanu.
Mumafunatu ndizikhulupirika.
Ndikufuna ndizikusangalatsani.
(Onaninso Sal. 18:25; 116:12; Miy. 11:20.)