GAWO 4
“Ndi Mphamvu Zanga Zonse, Ndidzateteza Dzina Langa Loyera”—Satana Analephera Kuthetsa Kulambira Koyera
MFUNDO YAIKULU: Yehova adzateteza anthu ake pa chisautso chachikulu
Yehova amakonda anthu, komabe tikuyenera kuyankha mlandu kwa iye chifukwa cha zochita zathu. Koma kodi amamva bwanji akaona anthu amene amati amamulambira akuchita zinthu zoipa? Kodi adzadziwa bwanji anthu oyenera kuwapulumutsa pa chisautso chachikulu? Nanga n’chifukwa chiyani Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, adzaphe anthu mamiliyoni ambirimbiri?