BOKOSI 9E
“Nthawi Yobwezeretsa Zinthu Zonse”
MACHITIDWE 3:21
Pamene mtumwi Petulo ananena za “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse,” ankalosera za nthawi yapadera imene inayamba pamene Khristu anakhala pampando wachifumu mpaka kumapeto kwa Ulamuliro wake wa Zaka 1,000.
1914—Yesu Khristu wakhala pampando wachifumu kumwamba. Anthu a Mulungu anabwezeretsedwa mwauzimu kuyambira mu 1919
Masiku Otsiriza
ARAMAGEDO—Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu unayamba, ndipo “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inaphatikizapo madalitso amene anthu okhulupirika padziko lapansi analandira
Ulamuliro wa Zaka 1,000
KUTHA KWA ULAMULIRO WA KHRISTU WA ZAKA 1,000—Yesu wamaliza ntchito yonse yobwezeretsa zinthu ndipo akupereka Ufumu kwa Atate ake
Paradaiso Wamuyaya
ULAMULIRO WA YESU UDZACHITITSA KUTI . . .
dzina la Mulungu lilemekezedwe
anthu asadzadwalenso
achikulire adzakhalenso anyamata
amene anafa adzauke
anthu okhulupirika adzakhale angwiro
dziko lapansi lidzakhale Paradaiso