Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 206
  • Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu!
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtsinjewo Ukubweretsa Madalitso
  • Madzi Opatsa Moyo
  • Mitengo ya Zipatso Komanso Yochiritsa
  • “Kulikonse Kumene Mtsinjewo Ukupita, Chilichonse Chidzakhala ndi Moyo”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Madalitso a Yehova pa “Dziko” Lathu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Mitsinje ya Madalitso Ochokera kwa Yehova
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 206

BOKOSI 19B

Mtsinje Waung’ono Unakhala Waukulu!

Ezekieli anaona kamtsinje kakang’ono kakuchokera m’nyumba yopatulika ya Yehova ndipo mozizwitsa unakhala mtsinje waukulu utangodutsa kamtunda kochepa. M’mbali mwa mtsinjewo, Ezekieli anaona mitengo ikuluikulu imene imabereka zipatso zokoma komanso kuchiritsa anthu. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

Mtsinje ukuchokera m’nyumba ya Yehova ndipo ukukhala mtsinje waukulu. Zizindikiro zosonyeza kuzama kwa mtsinje. Mikono 1,000: kulekeza m’mapazi. Mikono 2,000: kulekeza m’maondo. Mikono 3,000: kulekeza m’chiuno. Mikono 4,000: pozama kwambiri posatheka kuwoloka ndi mapazi.

Mtsinjewo Ukubweretsa Madalitso

KALE: Ayuda omwe anali ku ukapolo atabwerera kudziko lakwawo analandira madalitso ochuluka pamene anathandiza nawo kubwezeretsa kulambira koyera pakachisi

MASIKU ANO: Mu 1919 kulambira koyera kunabwezeretsedwa ndipo zinatsegula mwayi wa madalitso ankhaninkhani kwa atumiki okhulupirika a Mulungu

M’TSOGOLO: Pambuyo pa Aramagedo, Yehova adzatidalitsa mwakuthupi komanso mwauzimu

Madzi Opatsa Moyo

KALE: Yehova anadalitsa kwambiri anthu ake omvera ngakhale pamene chiwerengero chawo chinkawonjezeka ndipo anawathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu

MASIKU ANO: M’Paradaiso wauzimu amene akukulirakulira anthu ambiri akulandira madalitso auzimu kuchokera kwa Yehova ndipo zawathandiza kuti akhale amoyo mwauzimu

M’TSOGOLO: Anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo komanso anthu mamiliyoni ambirimbiri amene adzaukitsidwe, adzasangalala ndi madalitso ochokera kwa Yehova ndipo madalitsowo adzakhala okwanira kwa aliyense

Mitengo ya Zipatso Komanso Yochiritsa

KALE: Mwauzimu Yehova anadyetsa anthu ake okhulupirika m’dziko lobwezeretsedwa. Iye anawachiritsanso matenda auzimu amene anadwala kwa nthawi yaitali

MASIKU ANO: Mfundo zambiri za choonadi cha m’Baibulo zikuthandiza anthu a Mulungu kuti akhalebe okhulupirika kwa iye komanso kuti azipewa machimo akuluakulu ndimaganizo oipa a anthu am’dzikoli

M’TSOGOLO: Khristu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse omvera kuti akhale angwiro ndipo adzasangalala ndi moyo wathanzi komanso wangwiro kwamuyaya

Bwererani ku mutu 19, ndime 4-21

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena