Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 220
  • “Gawo Loti Likhale Chopereka Chanu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Gawo Loti Likhale Chopereka Chanu”
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Chopereka”
  • “Malo Onse Oti Aperekedwe”
  • “Malo a Mtsogoleri”
  • “Chopereka Chopatulika”
  • “Malo Otsala”
  • “Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • “Kachisi” ndi “Kalonga” Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Mapeto Akufikira”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 220

BOKOSI 21A

‘Gawo Loti Likhale Chopereka Chanu’

EZEKIELI 48:8

Tiyeni tiyendere limodzi ndi Ezekieli pamene akuonetsetsa malo amene Yehova anawapatula. Malo amenewa ali ndi mbali 5. Kodi mbali zake ndi ziti? Nanga ali ndi ntchito yotani?

Mapu a malo amene Yehova anawapatula otchedwa ‘chopereka.’ Pakati pa mapu amenewa pali malo ofanana mbali zonse okwana mikono 25,000 (makilomita 13) kuchokera kumpoto kukafika kummwera komanso mikono 25,000 kuchokera kummawa kukafika kumadzulo. Kachigawo kameneka kakutchedwa ‘malo onse oti aperekedwe’ ndipo agawidwa m’mbali zitatu, zomwe ndi chigawo chakumtunda, chigawo chapakati pomwe pali kachisi ndi chigawo cha mmunsi pomwe pali mzinda wotchedwa ‘Yehova ali Kumeneko.’

“Chopereka”

Malo amenewa anali oti azigwiritsidwa ntchito ndi oyang’anira ndipo akudziwikanso kuti “chopereka chopatulika.”

EZEK. 48:8

“Malo Onse Oti Aperekedwe”

Malo amenewa anaikidwa padera kuti akhale a ansembe, Alevi komanso a mzinda. Anthu onse ochokera m’mafuko onse 12 ankalowa m’malo amenewa kudzalambira Yehova komanso kudzathandiza pa ntchito zosiyanasiyana.

EZEK. 48:20

“Malo a Mtsogoleri”

“Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli.” “Akhale a mtsogoleri wa anthu.”

EZEK. 45:7, 8; 48:21, 22

“Chopereka Chopatulika”

Malo amenewa akutchulidwanso kuti “gawo loyera.” Mbali ya kumtunda inali ya “Alevi.” Anali “malo opatulika.” Mbali yapakati inali “chopereka chopatulika cha ansembe.” Anali “oti adzamangepo nyumba zawo komanso adzakhala malo opatulika omangapo kachisi.”

EZEK. 45:1-5; 48:9-14

“Malo Otsala”

“Malo amenewa adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli” ndipo adzakhala “malo a mzinda oti munthu aliyense angagwiritse ntchito. Malo amenewa akhale oti anthu azimangako nyumba komanso kudyetserako ziweto.”

EZEK. 45:6; 48:15-19

Bwererani ku mutu 21, ndime 3

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena