PHUNZIRO 02
Baibulo Limatithandiza Kuti Tikhale Ndi Chiyembekezo
Anthu padziko lonse amakumana ndi mavuto amene amawachititsa kuti azikhumudwa, azida nkhawa komanso azimva kupweteka. Kodi inunso munakumanapo ndi vuto limene linakuchititsani kumva chonchi? Mwina panopa mukudwala kapena munthu amene munkamukonda anamwalira. Mwina mukudzifunsa kuti, ‘Koma zinthu zidzakhalanso bwino?’ Baibulo limayankha mogwira mtima funso limeneli.
1. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?
Baibulo limafotokoza chifukwa chake padzikoli pali mavuto ochuluka chonchi, komanso limatiuza uthenga wabwino wakuti posachedwapa mavuto onsewa atha. Zimene Baibulo limalonjeza zingatithandize kukhala ndi “tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino.” (Werengani Yeremiya 29:11, 12.) Malonjezo amenewa amatithandiza kuti tizitha kupirira mavuto, tiziona zinthu moyenera ndiponso amatitsimikizira kuti tidzakhala osangalala mpaka kalekale.
2. Kodi Baibulo limafotokoza kuti m’tsogolomu mudzachitika zotani?
Baibulo limanena kuti m’tsogolomu “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.” (Werengani Chivumbulutso 21:4.) Mavuto amene tikukumana nawo masiku ano monga umphawi, kupanda chilungamo, matenda komanso imfa sadzakhalaponso. Baibulo limalonjeza kuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.
3. Kodi inuyo mungatani kuti muzikhulupirira kuti zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi?
Anthu ambiri amafuna zinthu zabwino zitachitika, koma sakhulupirira ndi mtima wonse kuti zidzachitikadi. Koma zimene Baibulo limalonjeza zidzachitika ndithu. Tingakhulupirire kwambiri zimene Baibulo limanena ngati tikuyesetsa ‘kufufuza Malemba mosamala.’ (Machitidwe 17:11) Mukamaphunzira Baibulo, mudziwa zimene limanena zokhudza zimene zidzachitike m’tsogolo. Ndiye zili ndi inu kuzikhulupirira kapena ayi.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani zinthu zina zimene Baibulo limalonjeza kuti zidzachitika m’tsogolo ndipo onani mmene chiyembekezo chotchulidwa m’Baibulo chikuthandizira anthu masiku ano.
4. Baibulo limatilonjeza moyo wosatha komanso wopanda mavuto
Taonani malonjezo otsatirawa amene amapezeka m’Baibulo. Kodi ndi malonjezo ati amene akusangalatsani kwambiri? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?
Werengani malemba amene ali pa lonjezo lililonse, kenako yankhani mafunso awa:
Kodi malemba amenewa akukupangitsani kuyembekezera zinthu zabwino? Nanga angathandizenso anthu a m’banja lanu ndi anzanu kuyembekezera zinthu zabwino?
Yerekezerani kuti muli m’dziko lomwe
PALIBE ALIYENSE AMENE . . . |
ALIYENSE ALI NDI MWAYI . . . |
---|---|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
|
5. Zimene Baibulo likulonjeza zingakuthandizeni panopa
Anthu ambiri amakhumudwa kapenanso kukwiya akaona mavuto amene ali m’dzikoli. Anthu ena amayesetsa kumenyera ufulu kuti zinthu zisinthe. Onani mmene malonjezo a m’Baibulo akuti zinthu zidzasintha akuthandizira anthu masiku ano. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zinkamupweteka kwambiri Rafika?
Ngakhale kuti zinthu zopanda chilungamozo sizinathe, kodi Baibulo linamuthandiza bwanji?
Zimene Baibulo limatilonjeza zimatithandiza kuti tiziyembekezera kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino ndipo timasiya kukhumudwa n’kumapirira mavuto athu bwinobwino. Werengani Miyambo 17:22 ndi Aroma 12:12, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuganiza kuti uthenga wa chiyembekezo wopezeka m’Baibulo ungakuthandizeni pa moyo wanu masiku ano? N’chifukwa chiyani mukutero?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Zimene Baibulo limalonjeza ndi zabwino kwambiri, koma sizingatheke.”
N’chifukwa chiyani muyenera kufufuza umboni wakuti zimene Baibulo limalonjeza zidzachitikadi?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo ndipo limatilonjeza kuti tidzasangalala m’tsogolo. Zimenezi zimatithandiza kuti tipirire mavuto athu panopa.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani anthu akufunika kudziwa zimene Mulungu akutilonjeza?
Kodi Baibulo limati m’tsogolo mudzachitika zotani?
Kodi kuyembekezera kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino kungatithandize bwanji masiku ano?
ONANI ZINANSO
Onani mmene kuyembekezera zinthu zabwino kungakuthandizireni mukakhala pa mavuto.
“Kodi Chiyembekezo Mungachipeze Kuti?” (Galamukani!, May 8, 2004)
Onani mmene kuyembekezera zinthu zabwino za m’tsogolo kungathandizire anthu amene akudwala.
“Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?” (Nkhani yapawebusaiti)
Mukamaonera nyimboyi, muziganizira mmene inuyo ndi banja lanu mudzasangalalire ndi moyo m’Paradaiso amene Baibulo linalonjeza.
Onani mmene munthu wina yemwe ankamenyera ufulu wa anthu ndi zinyama anasinthira moyo wake atangophunzira zimene Baibulo limalonjeza zokhudza m’tsogolo.
“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2013)