Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 47
  • Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 47
Phunziro 47. Wophunzira Baibulo akuona mnzake akubatizidwa pamsonkhano ndipo akuganizira zoti nayenso abatizidwe.

PHUNZIRO 47

Kodi Mwakonzeka Kubatizidwa?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Pofika pano mwaphunzira zambiri zokhudza Yehova kuchokera m’Baibulo. Sitikukayikira kuti zomwe mwakhala mukuphunzira zakuthandizani kusintha zinthu zina pa moyo wanu. Komabe n’kutheka kuti pali zinthu zina zimene zikukulepheretsani kuti mudzipereke kwa Yehova komanso kubatizidwa. M’phunziroli tikambirana zinthu zina zimene zimalepheretsa anthu kubatizidwa komanso zomwe inuyo mungachite kuti zimenezi zisakulepheretseni kubatizidwa.

1. Kodi muyenera kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe?

Kuti mubatizidwe, muyenera ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti muyenera kudziwa yankho la funso lililonse limene anthu angafunse lokhudza Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale Akhristu amene anabatizidwa kalekale, amapitirizabe kuphunzira zinthu zina. (Akolose 1:9, 10) Komabe, kuti mubatizidwe mufunika kuyamba kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Akulu amumpingo adzakuthandizani kudziwa ngati mwadziwa zinthu zokwanira zokhudza Baibulo.

2. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene muyenera kuchita kuti mubatizidwe?

Kuti mubatizidwe muyenera ‘kulapa ndi kutembenuka.’ (Werengani Machitidwe 3:19.) Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kudzimvera chisoni chifukwa cha machimo amene munachita komanso kupempha Yehova kuti akukhululukireni. Muyeneranso kuyesetsa kupewa kuchita zimene Mulungu amaziona kuti ndi zoipa n’kumachita zimene iye amafuna. Kuwonjezera pamenepa, muyeneranso kumachita nawo misonkhano yampingo ndiponso kulalikira monga wofalitsa wosabatizidwa.

3. N’chifukwa chiyani simuyenera kulola kuti mantha akulepheretseni kubatizidwa?

Anthu ena amaopa kubatizidwa chifukwa amaona kuti akhoza kulephera kukwaniritsa zimene anamulonjeza Yehova. N’zoona kuti nthawi zina mukhoza kulakwitsadi zinthu. Koma dziwani kuti ngakhale amuna ndi akazi okhulupirika amene amatchulidwa m’Baibulo nawonso ankalakwitsa zinazake. Yehova sayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu mosalakwitsa kanthu. (Werengani Salimo 103:13, 14.) Yehova amasangalala mukamayesetsa kuchita zabwino. Iye ndi wokonzeka kukuthandizani. Ndipotu Yehova amatitsimikizira kuti ‘palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi chake.’​—Werengani Aroma 8:38, 39.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mmene kumudziwa bwino Yehova komanso kulola kuti akuthandizeni kungakuthandizireni kuti muthane ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kubatizidwa.

Zithunzi: Mtsikana akuchita khama polimbana ndi zinthu zimene zingamulepheretse kubatizidwa. Zithunzizi zabwerezedwa m’phunziroli.

4. Yesetsani kumudziwa bwino Yehova

Mtsikana akuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova.

Kodi mukuyenera kudziwa zinthu zochuluka bwanji zokhudza Yehova kuti mubatizidwe? Kuti muzikonda Yehova ndiponso kuchita zinthu zomusangalatsa muyenera kumudziwa bwino. Onerani VIDIYO kuti muone mmene anzanu ena padziko lonse achitira zimenezi. Kenako mukambirane funso lotsatirali.

VIDIYO: Zimene Munthu Angachite Kuti Abatizidwe (3:56)

  • N’chiyani chimene chinathandiza anthu omwe ali muvidiyoyi kuti abatizidwe?

Werengani Aroma 12:2, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mukukayikira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zoona kapena ngati zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa zilidi zolondola?

  • Ngati ndi choncho, muchitapo chiyani?

5. N’zotheka kuthana ndi zinthu zimene zingakulepheretseni kubatizidwa

Mtsikana akuika Baibulo m’chikwama chake ndipo mayi ake akumukalipira.

Aliyense amakumana ndi mavuto akasankha kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

VIDIYO: Anathana Ndi Zinthu Zomwe Zikanamulepheretsa Kubatizidwa (5:22)

  • Kodi Narangerel anathana ndi zinthu ziti zomwe zikanamulepheretsa kutumikira Yehova?

  • Kodi kukonda Yehova kunamuthandiza bwanji kuti athane ndi zinthu zomwe zikanamulepheretsa kubatizidwa?

Werengani Miyambo 29:25 ndi 2 Timoteyo 1:7, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani timalimba mtima n’kuthana ndi zinthu zomwe zikanatilepheretsa kutumikira Yehova?

6. Musamakayikire kuti Yehova akuthandizani

Mtsikana akulalikira mayi wachikulire. Ali limodzi ndi munthu yemwe amamuphunzitsa Baibulo.

Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kuti muzichita zomusangalatsa. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso awa.

VIDIYO: Yehova Mulungu Adzakuthandizani (2:50)

  • Muvidiyoyi, n’chiyani chimene chinkalepheretsa wophunzira uja kuti abatizidwe?

  • Kodi anaphunzira mfundo iti yomwe inamuthandiza kuti asamakayikire kuti Yehova amuthandiza?

Werengani Yesaya 41:10, 13, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti mungakwanitse zonse zimene munalonjeza pamene munkadzipereka kwa Yehova?

7. Pitirizani kuyamikira Yehova chifukwa cha chikondi chimene anakusonyezani

Mtsikana akupemphera.

Mukamaganizira kwambiri chikondi chimene Yehova anakusonyezani m’pamene mumamuyamikira kwambiri ndipo zimenezi zingakuchititseni kuti muzimutumikira kwa moyo wanu wonse. Werengani Salimo 40:5, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova wakuchitirani zimene mumaziyamikira kwambiri?

Mneneri Yeremiya ankakonda Yehova ndi Mawu ake komanso ankayamikira kwambiri mwayi wodziwika ndi dzina la Yehova. Iye ananena kuti: “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.” (Yeremiya 15:16) Yankhani mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani kukhala wa Mboni za Yehova ndi mwayi wapadera?

  • Kodi inuyo mukufuna kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova?

  • Kodi pali chilichonse chimene chikukulepheretsani kubatizidwa?

  • Kodi mungatani kuti mukwaniritse cholinga chanu choti mubatizidwe?

Mtsikana akubatizidwa.

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikuopa kuti ndikabatizidwa ndikhoza kulephera kukwaniritsa zonse zomwe ndingalonjeze.”

  • Kodi inunso mukuona choncho?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova angakuthandizeni kuthana ndi vuto lililonse lomwe lingakulepheretseni kuti mubatizidwe.

Kubwereza

  • Kodi mufunika kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe?

  • Kodi mukufunikira kusintha zinthu ziti pa moyo wanu kuti mubatizidwe?

  • N’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kubatizidwa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani chifukwa chake kukonda Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu abatizidwe.

“Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?” (Nsanja ya Olonda, March 2020)

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite ngati pali zinazake zimene zikukulepheretsani kubatizidwa.

“Chikundiletsa Kubatizidwa N’chiyani?” (Nsanja ya Olonda, March 2019)

Onani zimene munthu wina anachita kuti athane ndi zinthu zimene zinkamulepheretsa kubatizidwa.

‘N’chifukwa Chiyani Mukuzengereza Kubatizidwa?’ (1:10)

Poyamba munthu wina, dzina lake Ataa, ankazengereza kubatizidwa. Onani chimene chinamuthandiza kutsimikizira kuti akufunikira kubatizidwa.

Ndine Woyenereradi Kulandira Madalitso Onsewa? (7:21)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena