Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 9
  • Kukhala Achifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala Achifundo
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Chisoni Chimalimbikitsa Munthu Kukhala Wokoma Mtima ndi Wachifundo
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Muzisonyeza Kuti Mumawaganizira
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muzimvera Ena Chisoni
    Galamukani!—2020
  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 9

ULENDO WOBWEREZA

Yesu ndi ophunzira ake atsika ngalawa ndipo akupita kumtunda komwe kuli anthu omwe akuwadikira.

Maliko 6:30-34

PHUNZIRO 9

Kukhala Achifundo

Mfundo yaikulu: “Muzisangalala ndi anthu amene akusangalala ndipo muzilira ndi anthu amene akulira.”​—Aroma 12:15.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu ndi ophunzira ake atsika ngalawa ndipo akupita kumtunda komwe kuli anthu omwe akuwadikira.

VIDIYO: Yesu Anachitira Chifundo Gulu la Anthu

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Maliko 6:30-34. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. N’chifukwa chiyani Yesu ndi atumwi ake anaganiza zopita “kwaokhaokha”?

  2. N’chiyani chinachititsa Yesu kuti alalikire gulu la anthulo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Chifundo chimatilimbikitsa kuti tizithandiza anthu, osati kungofuna kuwalalikira kokha.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzimvetsera mwatcheru. Muzimupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Musamamudule mawu kapena kunyalanyaza zomwe akunena. Mukamamvetsera anthu mwatcheru, adzaona kuti mumalemekeza maganizo awo.

4. Muzimuganizira. Potengera zomwe mwaona pocheza naye, dzifunseni kuti:

  1. ‘N’chifukwa chiyani akufunikira kumva choonadi?’

  2. ‘Kodi kuphunzira Baibulo kungamuthandize bwanji pa moyo wake komanso kuti akhale ndi tsogolo labwino?’

5. Muzikambirana naye zinthu zomwe zingamuthandize. Pasanapite nthawi yaitali, musonyezeni mmene phunziro la Baibulo lingamuthandizire pa zochitika za tsiku ndi tsiku komanso kupeza mayankho a mafunso ake.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma 10:13, 14; Afil. 2:3, 4; 1 Pet. 3:8

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena