Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 11
  • Kuphunzitsa M’njira Yosavuta

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzitsa M’njira Yosavuta
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Mmene Mungaphunzitsire ndi Buku la “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale”
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Konzekerani Bwino Pokaphunzitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 11

KUPHUNZITSA ANTHU

Yesu akuphunzitsa anthu kufupi ndi madzi. Mbalame zikuuluka mumlengalenga ndipo chapafupi pali maluwa.

Mat. 6:25-27

PHUNZIRO 11

Kuphunzitsa M’njira Yosavuta

Mfundo yaikulu: ‘Muzilankhula zomveka.’​—1 Akor. 14:9.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu akuphunzitsa anthu kufupi ndi madzi. Mbalame zikuuluka mumlengalenga ndipo chapafupi pali maluwa.

VIDIYO: Yesu Anasonyeza Mmene Atate Amatikondera

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Mateyu 6:25-27. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Yesu anasonyeza bwanji mmene Yehova amatikondera?

  2. Ngakhale kuti Yesu ankadziwa zambiri zokhudza mbalame, koma kodi anangosankha kutchula mfundo iti? N’chifukwa chiyani imeneyi inali njira yabwino yophunzitsira?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tikamaphunzitsa m’njira yosavuta kumva, tidzathandiza anthu kukumbukira zomwe tawaphunzitsa ndipo zidzawafika pa mtima.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Musamalankhule kwambiri. M’malo mofotokoza chilichonse chomwe mukudziwa pa nkhaniyo, gwiritsani ntchito mfundo zomwe zili m’mutu womwe mukuphunzirawo. Mukafunsa funso, muzimudikira moleza mtima kuti ayankhe. Ngati sakudziwa yankho kapena ngati wayankha zosemphana ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa, funsani mafunso owonjezera omuthandiza kuganizira nkhaniyo. Wophunzirayo akangomvetsa mfundo yaikulu, pitani pa mfundo ina.

4. Muzithandiza wophunzira kugwirizanitsa mfundo zatsopano ndi zomwe akudziwa kale. Mwachitsanzo, musanayambe kukambirana nkhani ya kuuka kwa akufa, bwerezani mwachidule zomwe munaphunzira kale zokhudza mmene akufa alili.

5. Muzigwiritsa ntchito mafanizo mwanzeru. Musananene fanizo, dzifunseni kuti:

  1. ‘Kodi fanizoli ndi losavuta kumva?’

  2. ‘Kodi angamvetse mfundo ya mufanizoli mosavuta?’

  3. ‘Kodi lingamuthandize kukumbukira mfundo yaikulu, osati fanizo lokhalo?’

ONANINSO MALEMBA AWA

Mat. 11:25; Yoh. 16:12; 1 Akor. 2:1

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena