Miyambo kapena Maprinsipulo a Baibulo—Nchiti Chimatsogolera Moyo Wanu?
MWAMUNA wa Chijapani pocheza ku dziko lina la ku Asia anayang’ana ndi kudabwitsika kosakhulupiririka. Womuchereza wake, kugwiritsira ntchito timitengo take todyera, ananyamula nthuli ya nyama kuchoka pa mbale yoperekera chakudya, anasankha nthuli yabwino, ndipo kenaka anaika iyo mu mbale ya mpunga ya mlendo wake! Kubwerera ku mudzi ku Japani, ichi chikanawonedwa kukhala makhalidwe oipa. Palibe wina aliyense akanagwiritsira ntchito timitengo take todyera kutenga chakudya kuchokera mu mbale yomwe aliyense angatengemo kokha ngati timitengoto tinatembenuzidwa choyamba kotero kuti mbali imene anaika mkamwa mwake isakhudze chakudya. Koma mcherezi wake kwenikweni anali kungofuna kokha kumlemekeza iye, osati kumukhumudwitsa. Chomwe chinali chosalingalirika mu Japani chinali chisonyezero chaulemu mu dziko lina!
Ha ndi motani mmene miyambo imasiyanirana! Ha ndi motani mmene miyambo yambiri simatsatira dongosolo la chikhalidwe! Ndipo kodi ndani amene anganene miyambo imene iri yabwino koposa? Komabe, miyambo ina imakhala yozikidwa pa matsenga kapena ziphunzitso zonyenga. Kwa awo amene chikumbumtima chawo chaphunzitsidwa ndi Baibulo, miyambo yoteroyo mwachiwonekere iri yoyenera kupewedwa. Kodi nchiyani chimene chingamuthandize wina amene akukhumba kukondweretsa Mulungu kusankha kuti ndi miyambo iti imene ayenera kulondola ndipo kumlingo wotani? Kutsatira maprinsipulo a Baibulo kungathandize, popeza kuti Mkristu amalivomereza Baibulo kukhala monga njira yake ya kaimidwe mosasamala kanthu kuti ndi kuti kumene iye amakhala. .
Kugwiritsira Ntchito Maprinsipulo a Baibulo
Kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yaikulu mkugwira ntchito pa mtima wa munthu wodzichepetsa ndi kubweretsa moyo wake mokulira mchigwirizano ndi njira ya Mulungu kwachitiridwa chitsanzo mokhazikika. Mtumwi Paulo ananena kuti Akristu a ku Tesalonika analandira Mawu a Mulungu “monga momwe ali ndithu mawu a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.” (1 Atesalonika 2:13) Mawu amenewa ali amphamvu kotero kuti, monga mmene 1 Akorinto 6:9-11 imalozela, anapangitsa ambiri mu Korinto wakale, wodziwika kaamba ka makhalidwe ake oipa, kusiya njira zawo zakale za umbala, dama, kuledzera, ndi kugonana kwa aziwalo zofanana. Kodi Mawu a Mulungu akugwiranso ntchito pa inu? Kodi maprinsipulo ake amalamulira moyo wanu ku mlingo wokulira, kukutheketsani inu kuzindikira chomwe mungachite pamene mukumanizana mwachindunji ndi miyambo ya kumaloko?
Nthawi zina chimakhala cha chiwonekere kuti mwambo uli mwachindunji wotsutsana ndi maprinsipulo a Baibulo. Mu njira zimenezo wina wodziwa makhalidwe a Yehova ndi wokhumba kumukondweretsa iye adzapewa miyambo yoteroyo. Mwachitsanzo, mwambo ungakhale uja wakutentha lubani pa maliro ndi cholinga chofuna kupereka mtendere kwa wofedwa kapena kwa “moyo wake wochoka” kapena kumupatsa iye kuperekezedwa kwabwino ndi kupanga “moyo wake” kukondwera. Kapena ungakhale wakuti nyumba, maseti a TV, magalimoto, ndi zina zotero, zimatenthedwa ndi cholinga chofuna kumupatsa iye chikondwerero m’dziko la mizimu. Komabe, Mkristu amene amakhulupirira mawu a Baibulo onena kuti akufa “sadziwa kanthubi” amadziwa kuti machitachita amenewa ali ozikidwa pa zikhulupiriro zonyenga ndipo chotero ayenera kupewa izo.—Mlaliki 9:5, 10; Masalmo 146:4
Komabe, pamene miyambo siiri mwachindunji yoipitsa maprinsipulo a Baibulo koma imangokupanga iko kukhala kovuta kutumikira Yehova Mulungu mokwanira, kuli kovuta kudula malire ndi kusonyeza kuti maprinsipulo a Baibulo amatsogolera moyo wanu. Kulingalira kwapamwamba kwa maphunziro ndi kupita patsogolo kwa zinthu za kuthupi, kugonjera makolo kwa moyo wonse, ndi kusankhira kwa makolo kwa mnzanu wa mu ukwati iri pakati pa miyambo yofala kwambiri yomwe ingakhudze unansi wa wina ndi Yehova. Kodi ndi motani mmene maprinsipulo a Baibulo angagwiritsiridwe ntchito mu mikhalidwe monga ngati imeneyi?
[Chithunzi patsamba 3]
Kutentha zifaniziro pa maliro