Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 4/1 tsamba 15-20
  • Chisungiko cha Dziko Lonse Pansi pa “Kalonga wa Mtendere”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chisungiko cha Dziko Lonse Pansi pa “Kalonga wa Mtendere”
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Waphungu” ndi “Tate Wosatha”
  • Boma la Ufumu la “Kalonga wa Mtendere”
  • Chiwembu cha Makono Chidzaphwanyidwa
  • Kuima Mopanda Mantha Kaamba ka Ulamuliro Wadziko Lonse wa Yehova
  • Kubadwa kwa Mwana Kwakukulu Koposa kwa Padziko Lapansi Kutsogolera ku Chisungiko cha Dziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Nliti Pamene Mtendere Wokhalitsa Udzabweradi?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 4/1 tsamba 15-20

Chisungiko cha Dziko Lonse Pansi pa “Kalonga wa Mtendere”

“Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”​—yesaya 9:7.

1, 2. (a) Kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kudzakhala nthawi ya chiyani, ndipo ndi liti pamene kubadwaku kunachitika? (b) Kodi nchiyani chimene charter ya Mitundu Yogwirizana inagawira ku gululo, koma kodi nchiyani chimene pangano la Ufumu linapereka kwa Yesu Kristu? (c) Kodi timadziwa motani kuti Yehova mosakaikira adzamamatira kupangano la Ufumu?

MONGA mmene kubadwa kwa Yesu, mwana wangwiro, inali nthawi yachimwemwe chapadera, choteronso kubadwa kwa Ufumu wolonjezedwa kalewo idzakhala nthawi yachimwemwe chokulira. (Masalmo 96:10-12) Malinga ndi zenizeni za mbiri ya makono, ufumu umenewo unaikidwa pa mapewa a Yesu wolemekezedwa mu 1914. Kukhalapo kwa gulu la Mitundu Yogwirizana lerolino sikumabisa chenicheni chimenecho. Palibe mtsogoleri aliyense wa ziwalo 159 za UN amene ali wanyumba ya Davide. Angakhale kuli tero, charter ya chiwembu chadziko lonse chimenecho chimapereka kwa iwo ntchito ya kufikira mtendere wa dziko lonse ndi chisungiko kaamba ka mtundu wa anthu.

2 Koma pangano la Yehova kaamba ka Ufumu silinachotsedwe. Pa Yesaya 9:7 mawu akuti “mpando wachifumu wa Davide” amatsimikizira pangano limene Mulungu anapangana ndi Davide kaamba ka ufumu wosatha. Kuwonjezerapo, Yehova walumbira ku mapeto ake achipambano. Chakuti Yehova adzamamatira ku pangano limeneli chamveketsedwa bwino pa Masalmo 89:3, 4, 35, 36: “Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga, ndinalumbirira Davide mtumiki wanga; ndidzakhazika mbewu yako ku nthawi zonse, ‘ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwo mibadwo.’ Ndinalumbira kamodzi m’chiyero changa; sichidzanamizira Davide; mbewu yake idzakhala ku nthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.” Pangano limenelo, limodzinso ndi mutu wakuti “Kalonga wa Mtendere,” limapereka kwa Yesu Kristu thayo lakubweretsa chisungiko chadziko lonse.

3. Kodi ndi chifukwa ninji nthawi kaamba ka “Kalonga wa Mtendere” yakuyamba kulamulira kwache siiri nthawi kaamba ka mtendere kaamba ka kumwamba kapena dziko lapansi?

3 Komabe, nthawi kaamba ka Yehova Mulungu yakukhazikitsa boma lake pa mapewa a Kalonga wake wovekedwa Ufumu siinayenera kukhala chaka cha mtendere kaya kumwamba kapena padziko lapansi. Malinga ndi Chivumbulutso mutu 12, kubadwa kwa Ufumu wake kudzatsatiridwa ndi nkhondo kumwamba. Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake zinamenyana motsutsana ndi boma lokhazikitsidwa chatsopano, ndi Mfumu yokhazikitsidwa chatsopano limodzi ndi angelo ake oyera anamenyana motsutsana ndi mphamvu za uchiwanda zimenezo. Chotulukapo chake chinali chakuti Satana ndi ziwanda zake zinatulutsidwa kumwamba ndi kuponyedwa pansi padziko lathu. Mofananamo, mfuu inayimba: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.” (Chivumbulutso 12: 12) Kuyambira pamene Mdyerekezi anaponyedwa pansi, dziko lathu lapansi lakhala mwachisoni malo achiwawa ndi nkhondo yosayerekezeka. Ndimotani nanga mmene mtundu wa anthu ukufunira ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere,” popeza iwo udzatulukamo mu chisungiko chadziko lonse!

4. Nchifukwa ninji dzina lakuti “Mulungu Wamphamvu” siliyenera kusokonezedwa ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

4 Malinga ndi Yesaya 9:6, maina ena mkuwonjezera ku “Kalonga wa Mtendere,” anayenera kuwonjezeredwa ku dzina la ulemerero la Yesu Kristu. Limodzi lamaina amenewa linayenera kukhala “Mulungu Wamphamvu.” Iye sanayenera kutchedwa Mulungu wamphamvuyonse, ngati kuti iye anali chiwalo chofanana cha milungu yautatu. Ngakhale pa tsiku lake la kuukitsidwa, iye anachilola icho kudziwika kuti iye anali wochepera kwa Yehova. Iye anawonekera kwa Mariya wa Magadala ndi kumutumiza iye kukadziwitsa ophunzira ake odera nkhawa ndi kuti iye anali kubwerera kwa Atate wawo ndi kwa Atate wake ndi kwa Mulungu wawo ndi Mulungu wake. (Yohane 20:17) Kufikira kutsiku lino, iye akupitirizabe kutsogolera chilengedwe chonse mkulambiridwa kwa “Mulungu wa milungu,” Yehova. (Danieli 11:36) Aha, inde, Yesu Kristu ali ndi Mulungu ndikuti Mulungu sali Yesu iye mwini koma kuti ali Atate wakumwamba Yehova. Ndi mokulira chotani nanga mmene “Kalonga wa Mtendere” akutumikira monga mtsogoleri wa mtendere wosatha wa dziko lonse ndi chisungiko!

5. Nchifukwa ninji Yesu Kristu ali amene ali woyeneretsedwa kwambiri kutsogolera zolengedwa zonse za nzeru mkulambira Mulungu wowona ndi wamoyo, Yehova?

5 Kwa nthawi zonse, Mwana wa Mulungu waulemerero adzapitiriza kutsogolera zolengedwa zonse zanzeru mkulambiridwa kwa ameneyu ndi Mulungu yekha wamoyo wowona, Yehova. Mwana wokwezedwa wa Mulungu mwachiwonekere ali woyeneretsedwa kaamba ka ichi. Pa zolengedwa zonse za kumwamba ndi padziko lapansi, Mwana wa Mulungu waulemerero ali amene wamudziwa Yehova kwa nthawi yaitali ndipo mwathithithi kwambiri. Pa 1 Akorinto 2:11 mtumwi Paulo akuti: “Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye?” Chotero ichi chiri mnkhani ya Yesu Kristu. Angakhale kuti iye anagwiritsidwa ntchito ndi Yehova Mulungu mkulenga munthu, chinali chinthu china kaamba ka iye kukhala munthu iye mwiniyo, kukhala wozunguliridwa ndi mikhalidwe yonse ya padziko lapansi ndi kukhala ndi chokumana nacho cha maganizo a munthu. Chotero kwalembedwa kuti “ngakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo” monga munthu pano padziko lapansi. (Ahebri 5:8) Iyedi anatsimikizira kukhala woyenerera kukhala mwa chisungiko wopatsidwa ‘ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi’ ndi kukhala ndi dzina lakuti “Mulungu Wamphamvu”​—Mateyu 28:18; yerekezani ndi Afilipi 2:5-11.

“Waphungu” ndi “Tate Wosatha”

6. Kodi ndimotani mmene Yesu wakhala ali kutumikirira monga “Waphungu,” ndipo kodi ndimotani mmene “khamu lalikulu” lapindulira kuchokera ku uphungu wake wozizwitsa?

6 Kaamba ka zifukwa zotsimikizirika zimenezi, Kalonga wa Mulungu wakumwamba mothekera ali wokhoza kutumikira mtundu wa anthu monga “Waphungu.” (Yesaya 9:6) Uphungu wake uli wanzeru nthawi zonse, wangwiro, ndi wopanda cholakwa. Monga Mgwirizanitsi pakati pa Yehova Mulungu ndi awo amene atengedwa mu chipangano chatsopano, iye wakhala akutumikiradi monga waphungu kwa zaka mazana 19 apitawo. Tsopano, kuyambira 1935, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lakhala likutenga uphungu wake ndipo likupeza malangizo abwino kwambiri ndi chitsogozo. (Chivumbulutso 7:9-17; Yohane 10:16) Monga mtumwi kaamba ka ntchito iyi yopereka uphungu, “nthawi ino yamapeto a dongosolo iri la zinthu” wadzutsa “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” wolonjezedwa ndi kumukhazikitsa iye pamwamba pa zinthu zake zonse za padziko lapansi kapena zikondwerero zake za Ufumu. (Mateyu 24:3, 45-47; Luka 12:42-44) “Khamu lalikulu” tsopano likulandira uphungu wa uzimu womwe ulidi wodabwitsa ndi woyenerera chifukwa uli wozikidwa pa Mawu ovumbulutsidwa a Mulungu.

7. Nchifukwa ninji Satana Mdyerekezi sali mulungu wamphamvu kwa anthu a Yehova?

7 Monga chotulukapo chawo cha kuvomereza ku uphungu umenewo, Satana Mdyerekezi, “mulungu wadongosolo iri la zinthu,” salinso mulungu wamphamvu kwa ife monga anthu a Yehova. (2 Akorinto 4:4) Ife momvera tatuluka mu Babulo Wamkulu, dziko lachipembedzo chonyenga, ndipo sitigawanakonso mu machimo ake oipa. Tatenga kaimidwe kathu kosagwedezeka pambali pa amene pa mapewa pake Yehova Mulungu wakhazikitsa boma lake.

8. (a) Kodi nchifukwa ninji dzina lakuti “Tate Wosatha” liri losangalatsa kwambiri mwapadera kwa “khamu lalikuhr? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa awo amene akulola Satana Mdyerekezi kukhala tate wawo wauzimu?

8 Dzina lakuti “Tate Wosatha” liri lokondeka. “Khamu lalikulu” la “nkhosa zina” mwapadera limayamikira liwu limeneli. Utate wa Satana Mdyerekezi sunasangalatse iwo. Iwo amanjenjemera ndi mantha pamene akumbukira atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda omwe anatsutsana ndi Yesu ndipo kwa amene anati: “Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, pakuti mwa iye munalibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. (Yohane 8:44) “Khamu lalikulu” latuluka pakati pa ana auzimu amenewo a Satana Mdyerekezi, amene utate wake pakati pa anthu ochimwa sudzakhala kunthawi yosatha. Awo amene amamlola iye kukhala Utate wawo wauzimu adzatha limodzi naye. Chiwonongeko chosatha, chophiphiritsidwa ndi “moto wosatha” wa pa Mateyu 25:41, ukudikira Mdyerekezi ndi anthu onse amene sathawa kuchokera ku utate wake.​—Mateyu 25:41-46.

9. Kodi ndimotani mmene “khamu lalikulu” likulawira utate wa “Tate Wosatha”?

9 Kumbali ina, “khamu lalikulu” likulawa utate wa “Tate Wosatha.”a Motani? Mwakumvetsera ku mawu ake ndi kukhala “nkhosa zina” zake ndi mwakuyanjana ndi otsalira aIsrayeli wauzimu. Unansi wabanja umenewu umawonetsa mtendere. Kulemba pansi pa kuuziridwa, mtumwi Paulo analozera kwa Yehova pa Aroma 16:20 monga “Mulungu amene apereka mtendere.” Ndi moyenerera chotani, nanga, kuti Mwana wake wobadwa yekha ayenera kutchedwa “Kalonga wa Mtendere”! Mwakubwezeretsa mtendere ku dziko lonse, “Kalonga wa Mtendere” mosakaikira adzamamatira ku dzina lake lapamwamba lalikulu.

Boma la Ufumu la “Kalonga wa Mtendere”

10, 11. Pambuyo pa kulosera kubadwa kwa mwana kwakukulu koposa ndi kale lonse, kodi nchiyani chimene Yesaya anapitiriza kunena, ndipo kodi nchiyani chimene mawu ake amatanthauza?

10 Pamene Yesaya ananeneratu kubadwa kwakukulu kwa mwana​—inde, kumeneko kwa Mwana wa Mulungu yemwe anapatsidwa ulemu ndi dzina lakuti “Kalonga wa Mtendere”​—mneneriyo anatsogozedwa ndi mzimu wa Yehova kunena kuti: “Za kuenjezeka kwa ulamuliro wake ndi za mtendere sizidzatha. . .changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”​—Yesaya 9:7.

11 Mkunena kuti “za kuenjezeka kwa ulamuliro wake,” ulosiwo unasonyeza kuti gawo la “Kalonga wa Mtendere” silidzakhala lalifupi kusakupatira dziko lonse la padziko lapansi. Sipadzakhala malire padziko omwe adzatsendereza ulamuliro wake. Ulamuliro wake udzakwaniritsa dziko lonse. Mkuwonjezerapo, mu Paradaiso wapadziko lapansi amene akudza, sikudzakhala kutha kwa mtendere. Sipadzakhalanso kusamvana kuli konse. Mtendere udzafutukulidwa ku dziko lonse lapansi ndipo udzakhalapo nthawi zonse. (Masalmo 72:7) Mtendere mnkhaniyi umatanthauza zochulukira kuposa kupanda chiwawa ndi nkhondo. Umaphatikiza chiweruzo ndi chilungamo, popeza Yesaya ananena kuti ulamuliro wake udzachirikizidwa ndi “chiweruziro ndi chilungamo, kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse.” Kudzakhala madalitso ambiri kaamba ka mtundu wa anthu. Ndipo changu chosatopa cha Yehova Mulungu chidzakwaniritsa izi m’nthawi yathu.

12. Kodi ndimotani mmene boma limene liri pa mapewa a “Kalonga wa Mtendere” likuimiridwira kuzungulira dziko lonse lapansi?

12 Angakhale tsopano boma limeneli pa mapewa a “Kalonga wa Mtendere” likuimiridwa kuzungulira padziko lonse lapansi. Kulandira kwa boma lake lakumwamba la ufumu kukufutukulika mwamsanga. Otsalira a ophunzira a Yesu Kristu auzimu asonkhanitsidwa kotheratu kuchokera pakati pa mitundu. Mkuwonjezerapo, “khamu lalikulu” likusonkhanitsidwa kuchokera ku maiko osiyanasiyana oposa 200. Tsopano pali mboni za Yehova 3, 229, 022, ndipo ntchito yosangalatsa yosonkhanitsa sinathebe. “Khamu lalikulu” limeneli limalemekeza boma limene liri pa mapewa a “Kalonga wa Mtendere.” Ziwalo zake ziri zoyamikira kwambiri kukhala nzika. za boma limenelo ndi kukhala akalonga kuzun ngulira padziko lonse lapansi, mchigwir&ano ndi “atumiki mmalo mwa Kristu,” otsalira odzozedwa.​—2 Akorinto 5:20.

Chiwembu cha Makono Chidzaphwanyidwa

13. (a) Kodi nchiyani chimene athenga a Ufumu akukalamira kuchita pakati pa iwo eni? (b) Kodi ndimotani mmene Mulungu amawonera Mitundu Yogwirizana?

13 Athenga a Ufumuwo amasunganso mtendere pakati pawo. Iwo ‘mofunitsitsa amasamalira kusunga umodzi wa mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.’[ (Aefeso 4:3) Iwo amapanga ichi mosasamala kanthu za phokoso lomwe tsopano likuzungulira padziko lonse lapansi Udani wautundu mkati ndi kunja kwa Mitundu Yogwirizana mchenicheni waima motsutsana ndi boma la “Kalonga wa Mtendere.” Monga mmene Mulungu amawonera icho, Mitundu Yogwirizana iri chiwembu chonyansa chadziko lottse. Nchifukwa ninji? Chifukwa chimadzilalikira icho chokha kukhala chikupeza zolinga zimene Mulungu anakhazikitsa kokha pa “Kalonga wa Mtendere” wake kuzipeza. Ndipo chimayitanira pa anthu a mitundu yonse kuchirikiza icho mkukhazikitsa chisungiko chadziko lonse mwa zoyesayesa za munthu. Icho chinalalikira 1986 kukhala “Chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse.” Icho chotero chikuzitsimikizira icho chokha kukhala chiwembu motsutsana ndi “Kalonga wa Mtendere” ndi pangano la Yehova ndi iye kaamba ka Ufumu wosatha.

14. Kodi ndimotani mmene mneneri Yesaya anachenjezera awo amene amatsutsana ndi Yehova ndi pangano lake la Ufumu?

14 Kaamba ka chifukwa chonga ichi, mneneri Yesaya anachenjeza Mfumu Ahazi ndi nzika zake nthawi imeneyo kusafuna mtendere ndi chisungiko mwakulowa mchigwirizano ndi Mphamvu ya Dziko ya Asuri. Chenjezolo likupezeka pa Yesaya 8:9, 10. Kulemba mwandakatulo, mneneriyo anachenjeza awo onse amene amatsutsana ndi Yehova ndi pangano lake la Ufumu: “Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka. Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mawu, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.”

15. Kodi nchiyani chimene chidzapangika kwa chiwembu chotsutsana ndi pangano la Ufumu lerolino, monga mmene kwasonyezedwera ndi chiwembu cha masiku a Mfumu Ahazi?

15 Chotero lolani mitundu pansi pa kalonga wadziko iri, Satana Mdyerekezi, kuchita chiwembu ndi pangano la Ufumu ndi ulamuliro wa Mlowa Mmalo ndi Mfumu. Chiwembucho chidzathyokathyoka ku zidutswa. Monga mmene chinaliri chiwembu cha m’masiku a Mfumu Ahazi. Mfumu Rezini ya Aramu ndi Mfumu Peka ya Israyeli sanawope magulu ankhondo a Yehova, koma anapanga chiwembu motsutsana ndi pangano lake la Ufumu. Chabwino, chiwembu chawo chinathyoledwa muzidutswa. Mofananamo, Mfumu Ahazi ya Yuda sinawope Yehova koma inalowa mu chiwembu ndi mphamvu ya dziko ya Asuri. Ichi sichinamuthandize kwenikweni Ahazi ndi kumubweretsera mtendere ndi chisungiko. Chinabweretsa nsautso ndi ukapolo. Choipitsitsa cha zonse, chinapangitsa Ahazi kusakhala mchiyanjo ndi Yehova.

16. Kodi ndimotani mmene Yehova anathyolera chiwembu cha Asuri motsutsana ndi pangano la Ufumu, ndipo kodi nchiyani chimene ichi chinalosera mtsiku lathu?

16 Pambuyo pa imfa ya Ahazi ndipo m’masiku a mwana wake Hezekiya, Yehova wamakamu anathyolathyola chiwembu cha Asuri motsutsana ndi pangano la Ufumu. Mfumu ya Suri inakakamizidwa kubwerera kuchokera ku dziko la Yuda pambuyo pa kuphedwa kwa ankhondo ake 185, 000 ndi mngelo wa Yehova. Mdaniyo sanalase ngakhale mubvi umodzi pa mzinda wa Yerusalemu. (Yesaya 37:33-36) Chigonjetso chofananacho cha chiwembu cha dziko lonse cha mtsiku lathu motsutsana ndi pangano la Ufumu la Yehova ndi “Kalonga wa Mtendere” chiri chotsimikizirika, popeza Mulungu ali ndi Kalonga Imanueli ndi onse amene amalemekeza iye!

Kuima Mopanda Mantha Kaamba ka Ulamuliro Wadziko Lonse wa Yehova

17. (a) Kodi nchiyani chimene ndale za dziko posachedwapa zidzachita kwa Babulo Wamkulu, ndipo kodi nchiyani chimene anthu a Yehova adzafuna ndi kulandira? (b) Pambuyo pa kuchotsa Babulo Wamkulu, kodi nchiyani chimene olamulira opanda umulungu tsopano adzachita, kumufulumiza Yehova kuchita kachitidwe kotani?

17 Ziwalo za ndale za dziko posachedwapa zidzalunjikitsa zoyesayesa zawo osati motsutsana ndi Chipembedzo cha Dziko koma ndi Babulo Wamkulu yense. Dziko lonse lachipembedzo chonyenga, kumuchotsa iye. Panthawi imeneyo, chitetezero cha umulungu cha anthu a Yehova chidzayenera kugwira ntchito ku muyezo wapadera. Kufulumizidwa ndi chipambano chosangalatsa pa Babulo Wamkulu, atsogoleri opanda umulunguwo mwaukali adzaukila awo amene ali kumbali ya Ufumu ndi Yesu Kristu. Kenaka Yehova adzagwiritsira ntchito “Kalonga wa Mtendere” kumenya “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Yesu Kristu adzatsimikizira kukhala womenya nkhondo wosalakidwa amene boma lake silidzachepetsedwa. Iye adzatsimikizira kukhala “Mulungu Wamphamvu” pansi pa chipambano cha Mulungu wampha mvuyonse, Yehova. “Mulungu Wamphamvu” ameneyu adzamaliza ntchito yake yowalitsidwa ndi chipambano pa Armagedo yomwe idzafuula popanda kutha ku nthawi zonka muyaya. Onse alemekeze chimpambano chosayerekezeka chimenecho!

18. Mkayang’anidwe ka chiwembu chamakono motsutsana ndi pangano la Ufumu, kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova zatsimikizira kuchita, ndipo ndi chotulukapo chotani?

18 Chotero, ndiyeno, pitani patsogolo ku kuwonekera kwa dziko lonse lapansi komwe sikunachitikepo ndi kale lonse, inu, mboni zonse za Yehova, ndi chidaliro chotheratu mwa Mulungu wanu ndi Mfumu yake yolamulira, “Kalonga wa Mtendere”! Sonyezani kupanda mantha kowonekera kwa chiwembu chadziko lonse chomwe chiripochi. Ndi kulalikira kwanu kuli konse uthenga wa Ufumu ndi chipambano chake chikudza pa chiwembu chadziko lonse pa Armagedo, khalani inu nonse zizindikiro ndi zozizwitsa ku ulemerero wa Yehova. Pamene Mdyerekezi atembenuza olamulira adziko motsutsana ndi ife, kumbukirani, chipambano chidzakhala ndi awo amene adzaima owona ndi kukhulupirika kaamba ka Ufumu wa Imanueli, “Kalonga wa Mtendere,” popeza “Mulungu Ali Nafe”! (Mateyu 1:23; yerekezani ndi Yesaya 8:10. ) Ndipo lolani angelo onse akumwamba ndi mtundu wonse wa anthu osunga umphumphu padziko lapansi unene “Amen” ku kuyeretsedwa kwa ulamuliro wa Yehova pazolengedwa zake zonse kumwamba ndi padziko lapansi, ndi chisungiko chomwe sichidzatha!

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka kukambitairana kwatsatanetsatane kwa ntchito ya Yesu Kristu monga “Tate Wosatha,” wonani mutu 20 wa bukhu la Worldwide Security Under the “Prince of Peace,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc

Mafunso Mwachidule

◻ Kodi ndimotani mmene dzina la “Mulungu Wamphamvu” limagwirira ntchito kwa Yesu Kristu?

◻ Ndimotani mmene Yesu wakhalira ali kutumikira monga “Waphungu”?

◻ Ndi utate wandani umene tiyenera kufuna, ndipo ndi wandani umene tiyenera kukana?

◻ Kodi nchiyani mchenicheni chimene chiri Mitundu Yogwirizana?

◻ Kodi nchiyani chimene chidzachitika ku chiwembu cha masiku ano motsutsana ndi pangano la Ufumu ndi Mlowa Mmalo wake, Kalonga wa Mtendere”?

[Chithunzi patsamba 16 17]

Dziko lonse lapansi lidzagwirizana mkulambira kwa mtendere kwa Wolamulira wa Dziko Lonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena