Mfunso Ochokera kwa Owerenga
◼ Kodi chiri choyenera kulankhula za “dziko latsopano” likudzalo?
Funso limeneli moyenerera lingafunsidwe, popeza liwu la Chigriki
kaŵirikaŵiri lotanthauzidwa “dziko,”ko’smos, moyenerera limatanthauza mtundu wa anthu, ndipo Mulungu sadzapanga mtundu watsopano wa fuko la anthu. Mkuwonjezerapo, mu Baibulo sitipeza mawu akuti kainos’ ko’smos (mchenicheni, “dziko latsopano“).
Koma kugwiritsira ntchito kwa Baibulo kwa ko’smos kumalola kaamba ka Akristu kulankhula za “dziko latsopano“ pamene akulozera ku Paradaiso alinkudzayo wobwezeretsedwa padziko lapansi. The New International Dictionary of New Testament Theology ikulongosola: ‘Nauni yakuti kosmos poyambirira inatanthauza kumangirira, koma makamaka limatanthauza dongosolo.’ Bukhu lotanthauzira mawu limenelo likuwonjezera kuti liwulo liri ndi tanthauzo. lachindunji, monga ngati “kukongoletsa ndi kukometsera” “kukonzanso kwa moyo mu banja la munthu,” ndi “nzika za dziko lapansi, umunthu.”
Mu Malemba Achikristu a Chigriki, liwu lakuti ko’smos kawirikawiri limagwiritsidwa ntchito mu lingaliro la banja lonse la mtundu wa anthu. Ife chotero timaWerenga kuti “onse anachimwa [kunena kuti, onse a mbadwa zopanda ungwiro za Adamu] naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:19, 23) .Kumbali ina, “Mulungu anakonda dziko lapansi [ko’smos] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha kuti yense wakukhulupirira . . . akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) inde, nsembe ya Kristu iripo kwa aliyense mu banja la mtundu wa anthu yemwe amasonyeza chikhulupiriro.
Ngati kumeneko kunali kugwiritsira ntchito kokha kwa Baibulo kwa ko’smos, kungakhale kolakwa kulankhula ponena za “dziko la tsopano” likudzalo. Chifukwa ninji? Chifukwa ena a mtundu wa anthu adzapulumuka chisautso chachikulu chikudzacho. Amenewa kenaka adzakhala ndi mwawi wakukhala mu Paradaiso wobwezeretsedwanso. Chotero Mulungu sadzalenganso fuko latsopano la mtundu wa anthu, mtundu wa anthu watsopano, dziko latsopano la anthu. Komabe, Baibulo silimagwiritsira ntchito ko’smos kokha kutanthauza mtundu wonse wa anthu.
Mwachitsanzo, nthawi zina liwu la Chigriki limasonyeza anthu onse omwe ali opatulidwa kuchokera kwa Mulungu. Ahebri 11:7 amanena kuti “ndi chikhulupiriro Nowa . . . anatsutsa dziko lapansi [ko’smos]“ lye mwachiwonekere sanatsutse munthu aliyense womalizira, onse a mtundu wa anthu; Nowa ndi asanu ndi awiri a banja lake anapulumuka Chigumula. Mofananamo, Yesu anapemphera: “Ine ndiwapempherera iwo, sindipempherera dziko lapansi [ko’smos], koma iwo amene mwandipatsa ine . . . dziko lapansi lidana nawo, chifukwa sali a dziko lapansi, monga ine sindiri wa dziko lapansi.”—Yohane 17:9, 14; yerekezani ndi 2 Petro 2:5; 3:6.
Lolani ife, ngakhale kuli tero, tilunjikitse chidwi pa lingaliro lina mulimene Baibulo limagwiritsira ntchito ko’smos. Ichi chiri kusonyeza kachitidwe kantchito, dongosolo, kapena mbali zonse za moyo wa munthua Timakumana ndi kugwiritsira ntchito koteroko mu ndemanga ya Yesu: “Pakuti munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse [ko’smos] nataya moyo wake?” (Mateyu 16:2b) Mwa chiwonekere, Yesu sanali kulozera ku ‘kupeza kwa munthu kwa dziko lonse la mtundu wa anthu,’ osatinso kwa ‘dziko lonse la anthu opatulidwa kuchokera kwa Mulungu.’ Sunali umunthu umene munthu wokonda zakuthupi angapeze, koma unali chimene anthu ali nacho, kuchita, kapena kukonza. Ichi chinali chowonanso ponena za kawonedwe ka mtumwi Paulo ponena za ‘kudera nkhawa kaamba ka zinthu za mdziko’ kwa munthu wokwatira. Mofananamo, Mkristu sayenera ‘kukhala monga akuchita nalo dziko lapansi.’ -1 Akorinto 7:31-33.
Mu lingaliro limeneli, koʹsmos liri ndi tanthauzo lofanana ku liwu la Chigriki lakuti aion’, lomwe lingagwiritsidwe ntchito monga “dongosolo lakachitidwe ka zinthu“ kapena “mbadwo.” (Onaninso Aid to Bible Understanding, masamba 1671-4. ) Timapeza mu mbali zina kuti mawu awiri amenewo angathe kusinthidwa. Lingalirani zitsanzo ziwiri izi za kufanana kwa pakati pa koʹsmos ndi ai·onʹ: (1) Paulo analemba kuti awo amene anakanidwa ndi Dema, yemwe “anakonda dongosolo lakachitidwe ka zinthu liripoli [ai·onʹ]“ Koma mtumwi Yohane anadzudzula motsutsana ndi ‘kukonda dziko [ko’smos],’ kuchokera ku limene kumachokera “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo.” (2 Timoteo 4:10; 1 Yohane2:15-17) (2) Yohane 12:31 amalankhula ponena za “mkulu wa dziko iri lapansi [ko’smos]“ amene akuzindikiritsidwa pa 2 Akorinto 4:4 monga “mulungu wa dongosolo iri la zinthu [ai·onʹ]“
Mofananamo, koʹsmos, kapena “dziko lapansi,“ lingagwiritsidwe ntchito mchigwirizano ndi mtundu wonse wa anthu limodzinso ndi makhazikitsidwe a ntchito a mbali ya mtundu wa anthu. Kaamba ka chifukwa ichi, moyenerera ndipo ndi kulondola kofanana tingalankhule za kubwera kwa “dongosolo latsopano la kachitidwe ka zinthu“ kapena za “dziko latsopano.” Iri lidzakhala makhazikitsidwe antchito atsopano, dongosolo ladziko, kapena mbali ya moyo wa anthu. Ambiri amene adzakhala mu Paradaiso wa padziko lapansi wobwezeretsedwanso adzakhala atakhalapo kale m’dongosolo lakale la kachitidwe ka zinthu. Koma iwo adzakhala atapulumuka iro kapena adzakhala ataukitsidwa. Chotero iwo adzakhala anthu amodzimodziwo. Kulibeko, ngakhale kuli tero, dziko la mtundu wa anthu opatulidwa kuchokera kwa Mulungu ndipo ndi makonzedwe atsopano, kapena dongosolo, lozikidwa pa chipambano cha chifuno chovumbulutsidwa cha Mulungu, chakuti Paradaiso wobwezeretsedwa adzakhala dziko latsopano.
[Mawu a M’munsi]
a Bukhu lotanthauzira mawu logwidwa mawu pamwambapo limaloza kuti ngakhale mu nthawi zakale, mu Chigriki chosazikidwa pa Baibulo “kosmos linali liwu lenileni kaamba ka dongosolo la dziko, dongosolo la kachitidwe ka zinthu ka dziko.”
[Chithunzi patsamba 31]
Mtundu wa anthu olungama udzabwezeretsa Paradaiso mu dziko latsopano