Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/1 tsamba 8-13
  • Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero za Okalamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero za Okalamba
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupereka Ulemu kwa Akazi Amasiye
  • Monga Akulu Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero Zawo
  • Monga Munthu Payekha Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero Zawo
  • Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mulungu Amasamalira Okalamba
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kukwaniritsa Zosowa za Okalamba Athu—Chitokoso cha Mkristu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/1 tsamba 8-13

Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero za Okalamba

Mukumayang’anitsitsa Osati mokondwera ndi Zinthu zanu zokha, Komanso mokondwera Ndi zija za ena.”​—AFILIPI 2:4, NW.

1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene bungwe lolamulira la mu zana loyamba linasonyezera chikondwerero mu ntchito za okalamba? (b) odi ndi chitsimikizo chotani chimene chiripo kuti ntchito yolalikira sinali kunyalanyazidwa?

MWAMSANGA pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E. “chinabuka chidandaulo [mu mpingo wa Chikristu] kumbali ya Ayuda olankhula Chigriki kudandaula pa Ayuda olankhula Chihebri, popeza amasiye awo anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku [cha chakudya cha osowa].” Mosakaikira ambiri a amasiye amenewa anali okalamba ndipo osakhoza kudzitumikira iwo eni. Pa chochitika chirichonse, atumwi iwo eni analowereramo, akulankhula: “Chifukwa chake, abale, yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchitoyi.”​—Machitidwe 6: 1-3.

2 Akristu oyambirira anawona kusamalira zosowa monga “ntchito yofunika.” Zaka zingapo pambuyo pake wophunzira Yakobo analemba: “Mapembedzedwe ena ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi atate ndiwo: Kucheza ndi ana a masiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” (Yakobo 1:27) Kodi ichi chikatanthauza kuti, mwakutero, ntchito yolalikira yofunika kwambiri iyenera kunyalanyazidwa? Ayi, popeza mbiriyo mu Machitidwe imanena kuti pambuyo pa kulinganiza bwino ntchito yosamalira akazi amasiye, “ndipo mawu a Mulungu anakula, ndipo chiwerengero cha akuphunzira chidachulukatu mu Yerusalemu.”​—Machitidwe 6:7.

3. Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chikuperekedwa pa Afilipi 2:4, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri mwapadera choyenerera lerolino?

3 Lerolino tikuyang’anizana ndi “nthawi zowawitsa zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1) Kusamalira kaamba ka zosowa za moyo wa banja ndi ntchito ya kuthupi kungatisiye ife ndi mphamvu yochepera—​kapena chikhumbo—​cha kudera nkhawa ife eni ndi zosowa za okalamba. Moyenerera, ndiyeno, Afilipi 2:4 akutifulumiza ife “kuyang’anitsitsa, osati mokondwera ndi zinthu [zathu] zokha, komanso mokondwera ndi zija za ena.” Kodi ndimotani mmene ichi chingachitidwire molinganizika, m’njira yokhoza kugwirirapo ntchito?

Kupereka Ulemu kwa Akazi Amasiye

4. (a) Nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene mpingo wa m’zana loyamba “unachitira ulemu” akazi amasiye? (b) Kodi zopereka zoterozo zinali zoyenerera nthawi zonse?

4 Mu 1 Timoteo mutu 5, Paulo akusonyeza ndimotani mmene Akristu oyambirira anasamalirira akazi amasiye okalamba m’mpingo. Iye anafulumiza Timoteo: “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.” (Versi 3) Akazi amasiye okalamba anapatulidwa monga oyenera kulandira ulemu mu mtundu wa thandizo la ndalama lokhazikika. Oterowo anachotsedwapo pa mtundu uliwonse wachirikizo lowoneka ndi maso ndipo ‘akanayika kokha chiyembekezo chawo mwa Mulungu ndi kupitiriza mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.’ (Versi 5) Kodi ndimotani mmene mapemphero awo kaamba ka chakudya amayankhidwira? Kupyolera mu mpingo. Mu mkhalidwe wolinganizika, akazi amasiye oyenerera anapatsidwa mkhalidwe wa moyo woyenerera. Komabe, ngati mkazi wamasiye anali ndi njira yopezera ndalama, kapena achibale okhoza kumuchirikiza iye, zoperekedwa zoterozo sizinali zoyenera.​—Maversi 4, 16.

5. (a) Kodi ndimotani mmene akazi amasiye ena ‘anatsatira zokondweretsa thupi’? (b) Kodi mpingo unali ndi thayo lakuchirikiza oterowo?

5 “Koma iye [mkazi wamasiye] wakutsata zomkondweretsa” anachenjeza Paulo, “[adafa mwauzimu] pokhala ali ndi moyo.” (Versi 6) Paulo sakulongosola ndimotani mmene ena analiri, monga mmene Kingdom, Interlinear imasonyezera icho, “kukonda zokondweretsa thupi.” Ena angakhale akumenyana nkhondo ndi “zilakolako zawo zadama” (Versi 11) Komabe, malinga ndi Liddell & Scott’s Greek-English Lexicon, “kukhala wokonda zokondweretsa thupi” kungakhale kunaphatikizanso ‘kukhala mokhweka kapena mu zosangulutsa zopambanitsa kapena kumwerekera.’ Mwinamwake, mwakutero, ena anafuna mpingo kuwalemeretsa iwo, kuwapatsa ndalama zowonjezereka zopanda ntchito, moyo wakudzimwerekeretsa wosadziletsa. Mu nkhani iriyonse, Paulo anasonyeza kuti oterowo sanali oyenerera kulandira chirikizo la mpingo.

6, 7, ndi mawu a m’munsi. (a) Kodi nchiyani chomwe chinali “ndandanda”? (b) Kodi nchifukwa ninji awo amene anali asanafikitse zaka 60 sanayeneretsedwe kaamba ka kulandira chirikizo? (c) Kodi ndimotani mmene Paulo anathandizira akazi amasiye achichepere kuchokera ku kulandira “chiweruzo” chachikulu?

6 Paulo kenaka anati: “Lolani wamasiye aikidwe pa ndandanda [ya awo olandira chirikizo la ndalama] yemwe wafikira zaka zosachepera makumi asanu ndi limodzi.” Mu tsiku la Paulo mkazi wa zaka zoposa 60 anali kuwonedwa mwachiwonekere monga wosakhoza kudzichirikiza iyemwini ndipo mosakaikira kukwatiwanso.a “Kumbali ina,” Paulo anati,“muwakane akazi amasiye ang’ono [kaamba ka kulembetsa], pakuti pamene ayamba kumuchitira Kristu chipongwe afuna kukwatiwa; pokhala nacho chitsutso popeza adataya chikhulupiriro chawo choyamba.”—Maversi 9, 11, 12.

7 Kukanakhala kuti “ndandandayo” inali yotseguka kwa akazi amasiye achichepere, ena mwamsanga akanalengeza chikhumbo chakukhala osakwatiwa. M’kupita kwa nthawi, ngakhale kuli tero, akanakhala ndi vuto m’kuletsa “zikhumbo zawo zakugonana” ndi kufuna kukwatiwanso, ‘pokhala nacho chitsutso popeza anataya chikhulupiriro chawo choyamba’ chakukhala osakwatiwa. (Yerekezani ndi Mlaliki5:2-6. ) Paulo anapewetsa mavuto amenewo, mowonjezereka akumanena, “chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang’ono nabale ana.”​—Versi 14.

8. (a) Kodi ndimotani mmene malangizo a Paulo anachinjirizira mpingo? (b) Kodi akazi amasiye osowa kapena amuna okalamba anasamaliridwanso?

8 Mtumwiyo anaikanso malire kukulembetsa kwa awo okhala ndi zolembera zokhalitsa za ntchito yabwino Yachikristu. (Versi 10) Mpingo chotero sunali “malo abwino” kwa aulesi kapena aumbombo. (2 Atesalonika 3: 10, 11) Koma bwanji ponena za amuna okalamba kapena akazi amasiye ang’ono? Ngati oterowo anali ndi zosowa, mpingo mosakaikira ukanasamalira iwo pamaziko amunthu aliyense payekha​—Yerekezani ndi 1 Yohane 3: 17, 18.

9. (a) Kodi ndi chifukwa ninji makonzedwe kaamba ka chisamaliro cha okalamba lerolino angasiyane ndi awo amene anapangidwa mu zana loyamba? (b) Kodi nchiyani chimene kukambitsirana kwa Paulo kwa akazi amasiye mu 1 Timoteo mutu 5 kumatithandizira ife kuyamikira lerolino?

9 Makonzedwe oterowo mwachiwonekere anali oyenerera kaamba ka zosowa za mipingo ya zana—loyamba. Koma monga mmene The Expositor’s Bible Commentary imawonera: “Lerolino, ndi ndalama zosungidwa kaamba ka thandizo pa nthawi za tsoka, chisungiko cha mayanjano, ndi mwawi wa ntchito, mkhalidwe uli wosiyana kotheratu.” Monga chotulukapo cha kusintha kwa kawonedwe ka chitaganya ndi chuma, kawirikawiri sichiri choyenerera kaamba ka mipingo lerolino kusunga ndandanda ya zoperekedwa kwa okalamba. Mosasamala kanthu za chimenecho, mawu a Paulo kwa Timoteo angatithandize ife kuyamikira: (1) Mavuto a okalamba ali chodetsa nkhawa ku mpingo wonse​—makamaka kwa akulu. (2) Chisamaliro cha okalamba chiyenera kulinganizidwa bwino. (3) Chisamaliro choterocho chiri ndi malire kwa awo omwe alidi osowa.

Monga Akulu Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero Zawo

10. Kodi ndimotani mmene akulu lerolino angatengere chitsogozo mkusonyeza chikondwerero mwaokalamba?

10 Kodi ndimotani mmene oyang’anira lerolino amatengera chitsogozo mkusonyeza chikondwerero mwa achikulire? Kwa nthawi ndi nthawi iwo angasonyeze zosowa za okalamba pa zikalata za misonkhano yawo. Pamene thandizo lachindunji likufunika, iwo angakonze kaamba ka kulipereka iro. Iwo sangapereke mwaumwini chisamalirocho, monga mmene kuliri kuti kawirikawiri amapezeka ambiri ofunitsitsa​—-kuphatikizapo achichepere​—mu mpingo omwe angathandize. Komabe, iwo moyandikira angayang’anire chisamaliro choterocho mwina mwake mwakupatsa mbale kugwirizanitsa chisamaliro choperekedwa kwa munthu.

11. Kodi ndimotani mmene akulu angadzizoloweretse iwo eni ndi zosowa za okalamba?

11 Solomo anapereka uphungu: “Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji.” (Miyambo 27:23) Oyang’anira chotero mwaumwini angachezere okalamba kotero kuti agamulepo bwino koposa ndimotani mmene “angagawirire. . . molingana ndi zosowa zawo.” (Aroma 12:13) Woyang’anira woyendayenda akuchiika icho mu njira iyi: “Okalamba ena ali odzidalira koposa, ndipo kungowafunsa kokha kuti nchiyani chimene chifunikira kuchitidwa sichiri chabwino. Chiri chabwino koposa kuzindikira chimene chifunikira kuchitidwa ndi kupitiriza ndi ntchitoyo!” Mu Japan oyang’anira ena anapeza kuti mlongo wa zaka 80 anafunikira chisamaliro chachikulu. Iwo akusimba: “Tsopano timachiwona ku icho kuti winawake walankhula naye kawiri pa tsiku, mmawa ndi mmadzulo mwakumuchezera kapena mwa lamya.”​—Yerekezani ndi Mateyu 25:36.

12. (a) Kodi ndimotani mmene akulu angawonere ku icho kuti okalamba akupeza mapindu a misonkhano ya mpingo? (b) Kodi ndi kugwiritsira ntchito kwabwino kotani kumene kungapangidwe ndi matepu otulutsidwa ndi Sosaite?

12 Oyang’anira alinso odera nkhawa kuti okalamba apeze phindu la misonkhano ya mpingo. (Ahebri 10:24, 25) Kodi ena amafunikira choyenderamo? Kodi ena ali kokha osakhoza “kumvetsera ndi kupeza nsonga ya” misonkhano chifukwa cha kusamvetsetsa? (Mateyu 15:10) Mwinamwake chingakhale chanzeru kwambiri kuika zothandizira kumvetsera kaamba ka iwo. Mofananamo unyinji wa mipingo lerolino imakhala ndi misonkhano yawo itatengedwa pa lamya kotero kuti opunduka angamvetsere ali kunyumba kwawo. Ena anakopa misonkhano pa tepu kaamba ka awo amene akudwala kwambiri kuti nawonso apezekepo​—nthaŵi zina kugula matepu reko rda kaamba ka iwo. Kulankhula za matepu, mkulu mu Germany anawona: “Ndakhala nditayendera okalamba ochulukirapo amene amangokhala kokha patsogolo pa wailesi yakanema ndi kuyang’ana pa maprogramu omwe sangalongosoledwe kukhala omangirira mwauzimu.” Bwanji osawalimbikitsa iwo mmalo mwake kumvetsera kumatepu otulutsidwa ndi Sosaite, monga aja okhala ndi nyimbo za Ufumu ndi kuwerenga kwa Baibulo?

13. Kodi ndimotani mmene okalamba angathandizidwire kukhalabe okangalika monga olengeza a Ufumu?

13 Ziwalo zina zakale za mpingo zakhala zosakhazikika kapena alaliki osakangalika. Msinkhu, ngakhale kuli tero, sumaletsa kwenikweni wina kulalikira “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14) Ena angavomereze ku chiyitano chokhweka kugwira nanu ntchito mu utumiki wa m’munda. Mwinamwake mungadzutsenso chikondi chawo kaamba ka kulalikira mwakugawana nawo zokumana nazo za mu utumiki wa m’munda. Ngati kukwera masitepe liri vuto konzani kaamba ka iwo kugwira ntchito mu malo amene ali ndi chikwepe kapena malo okhala amene alibe masitepe. Ofalitsa ena amatenganso okalamba kumaphunziro awo a Baibulo​—kapena kutsogoza phunzirolo mnyumba ya wokalambayo.

14. ndi bokosi. (a) Kodi nchiyani chimene akulu angachite ngati mbale kapena mlongo wokalamba ali m’chipsyinjo cha kusowa ndalama? (b) Kodi ndimotani mmene mipingo ina yakwaniritsira ku zosowa za ofalitsa okalamba?

14‘Ndalama zichinjiriza.’ (Mlaliki 7:12) Koma nthawi zambiri pamene mbale wokalamba kapena mlongo ali m’chipsyinjo chachikulu cha kusowa ndalama ndipo alibe anansi ofuna kumuthandiza. Aliyense payekha mu mpingo, ngakhale kuli tero, amakhala wachimwemwe kuthandiza pamene adziwitsidwa za kusowako. (Yakobo 2:15-17) Akulu nawonso angayang’ane mu mautumiki a boma kapena mautumiki amayanjano, malamulo a kusunga ndalama kaamba ka kugwiritsira ntchito pa nthawi za tsoka, ndalama zolandira pamene munthu waleka ntchito, ndi zina zotero, zomwe zingakhaleko. M’maiko ena, ngakhale kuli tero, mautumiki oterowo amakhala ovuta kuwapeza ndipo sipangakhale njira ina yosiyana koma kutsatira njira yopezeka pa 1 Timoteo mutu 5 ndi kukonza kaamba ka mpingo wonse kupereka thandizo. (Onani Olinganmdwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 122-3. )

Ofalitsa mu Nigeria mokhazikika anathandiza mpainiya wokhazikika wa zaka 82 ndi mkazi wake ndi mphatso zakuthupi. Pamene boma linandandalitsa kaamba ka kugwetsa .nyumba imene anali kukhalamo, mpingo unawaitana iwo kukhala mu chipinda cholumikizidwa ku Nyumba ya Ufumu kufikira malo ena ogona atakonzedwa.

Mu Brazil mpingo unaitana namwino kusamalira kaamba ka okalamba awiri. Pa nthawi imodzimodziyo, mlongo anagawiridwa kukonza nyumba, kukonza chakudya chawo, ndi kusamalira kaamba ka zosowa zina zakuthupi. Mwezi uliwonse mpingo umaika pambali ndalama kaamba ka kugwiritsira ntchito kwawo.

15. (a) Kodi kuli malire alionse pa thandizo limene mpingo ungapereke? (b) Kodi ndimotani mmene uphunguwa pa Luka 11:34 ungakhalire woyenerera kaamba ka oterowo omwe angakhale ofunsira mopambanitsa?

15 Mofanana ndi mzana loyamba, zoperekedwa zoterozo ziri zoyenera kaamba ka awo omwe mowonadi azifuna izo. Oyang’anira sali pansi pa thayo kufikira zifunsiro zopitirira muyezo kapena kusamalira kaamba ka zikakamizo zosayenerera kaamba ka chisamaliro. Okalamba, nawonso, ayenera kukhala ndi ‘diso labwino.​’—Luka 11:34, NW.

Monga Munthu Payekha Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero Zawo

16, 17. (a) Kodi nchifukwa ninji chiri chofunika kaamba ka ena pambali pa akulu kutenga chikondwerero mwa Okalamba? (b) Kodi ndimotani mmene ofalitsa otanganitsidwa ‘angadzipezere nthawi’kaamba ka okalamba?

16 Nthawi ina kumbuyoku mlongo wokalamba anagonekedwa m’chipatala. Adokotala anapeza kuti vuto lake linali kuperewera kwa chakudya. “Ngati ambiri mu mpingo anatenga chikondwerero chaumwini mwa iye,” analemba motero mkulu, “mwinamwake ichi sichikanachitika.” Inde, akulu sali okha amene ayenera kutenga chikondwerero mwa iwo. Paulo anati: “Tiri ziwalo wina ndi mzake.”​—Aefeso 4:25.

17 Mosakaikira ena a inu muli kale otopetsedwa ndi mathayo aumwini. Koma ‘kumayang’anitsitsa osati mokondwera ndi zinthu zanu zokha.’ (Afilipi 2:4) Ndi kulinganizidwa koyenera kwaumwini, inu kaŵirikaŵiri mungadzipezere nthawi’ (Aefeso 5:16) Mwachitsanzo, kodi mungachezere okalamba pambuyo pautumiki wa m’munda? Masiku a mkati mwa mlungu ali mwapadera masiku akusungulumwa kwa ena. Achichepere apakati pa zaka 13 ndi 19 nawonso, angadzilowetse m’kuchezera okalamba ndi kugwira ntchito kaamba ka iwo. Anapemphera motero mlongo m’modzi amene anathandizidwa ndi wachichepere: “Zikomo Yehova kaamba ka mbale wachichepere John. Iye ali munthu wabwino chotani nanga.”

18. (a) Kodi ndimotani mmene kukambitsirana ndi okalamba kungakhalire kovuta nthawi zina? (b) Kodi ndimotani mmene wina angapangire kuchezera kapena kukambitsirana ndi munthu wokalamba kukhala komangirira?

18 Pa misonkhano, kodi mumangopatsa okalamba kokha moni wamwambo? Mutangoyerekeza, sichingakhale chopepuka kulankhulana ndi wina amene samva kwambiri kapena ali ndi vuto mkudzilongosola iyemwini. Ndipo popeza kulephera kwa umoyo wabwino kumatenga mbali yaikulu, okalamba ambiri samakhala ndi mkhalidwe wachimwemwe kwenikweni. Mosasamala kanthu za chimenecho, “ofatsa mtima apambana odzikuza mtima.” (Mlaliki 7:8) Ndi kuyesetsa kochepera, “kusinthana kwa kulimbikitsana” kwenikweni kungayambike. (Aroma 1:12) Yesani kupereka chokumana nacho cha mu utumiki wa m’munda. Gawanani nsonga imene mwawerenga mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Kapena chabwino koposa, mvetserani. (Yerekezani ndi Yobu 32:7. ) Okalamba amakhala ndi zambiri zofuna kugawana ngati muwalola iwo. Anavomereza mkulu mmodzi: “Kuchezera mbale wokalamba kunandithandiza ine kwambiri.”

19. (a) Kudera nkhawa kaamba ka okalamba kumafutukulidwa kwa ndani? (b) Kodi ndi ziti zomwe ziri njira zina mu zimene tingatsimikizire kukhala athandizo kwa mabanja amene akusamalira makolo okalamba?

19 Kodi kudera nkhaŵa kwanu kaamba ka okalamba sikuyenera kufutukiranso kwa mabanja amene akusamalira iwo? Banja limodzi limene linali kuyang’anira makolo okalamba linasimba: “Mmalo mwakutilimbikitsa ife, ena mu mpingo akhala osuliza. Mlongo m’modzi ananena: ‘Ngati upitiriza kuphonya misonkhano, udzadwala mwauzimu Koma iye sanali wofunitsitsa kuchita chirichonse kutithandiza ife kufika ku misonkhano yambiri.” Okhala ndi kukhwethemula kofananako ali malonjezo osatsimikizirika onga ngati, Ngati mudzafuna thandizo, ndidziwitseni. Awa kaŵirikaŵiri amafanana ndi kunena kuti, “Mukapfunde ndi kukhuta.” (Yakobo 2:16) Chiri chabwino koposa chotani nanga kulola kudera nkhawa kwanu kusinthira ku ntchito! Likusimba banja limodzi: “Mabwenzi athu akhala ozizwitsa ndi ochirikiza! Ena angasamalire amayi kwa masiku angapo kwa kanthaŵi kotero kuti tingakhale ndi kupuma kwa kanthaŵi. Ena amatenga iwo pa maphunziro a Baibulo. Ndipo chikutilimbikitsadi ife kwenikweni pamene ena akufunsa ponena zaumoyo wawo.”

20, 21. Kodi nchiyani chomwe okalamba angachite kuthandiza awo amene akuwasamalira iwo?

20 Mokulira okalamba athu akusamalidwa bwino kwambiri. Komabe, kodi nchiyani chimene mboni zokalamba izo zeni zingachite kotero kuti ntchito yokulira ikuchitidwa ndi Ahebri 13:17. ) Gwirizanani ndi makonzedwe a akulu kaamba ka chisamaliro chanu. Sonyezani kuthokoza ndi chiyamikiro kaamba ka ntchito zonse zachifundo zomwe zikuchitidwa, ndi kupewa kulamulira koposa kapena kukhala wosuliza mopambanitsa. Ndipo ngakhale kuti kuwawa ndi kupweteka kwa ukalamba kuli kwenikweni, yesani kusonyeza mkhalidwe wachimwemwe, weniweni.​—Miyambo 15:13.

21 ‘Abalewo ali ozizwitsa. Sindikudziwa kuti nchiyani chomwe ndingachite popanda iwo,’ okalamba ambiri anamvedwa akumanena tero, Mosasamala kanthu za chimenecho, thayo loyambirira la kusamalira okalamba liri pa ana awo. Kodi nchiyani chimene ichi chimaphatikizapo, ndipo ndimotani mmene chitokoso chimenechi chingakumanizidwire?

Mawu a M’munsi

a Levitiko 27:1-7 imalozera ku kuwomboledwa kwa aliyense payekha ‘kopatsidwa’ (mwa chowinda) ku kachisi monga wogwira ntchito. Mtengo wa chiwombolo unasiyanasiyana molingana ndi msinkhu. Pa msinkhu wa 60 mtengo umenewo unatsika kotheratu mwachiwonekere chifukwa munthu wa msinkhu umenewo analingaliridwa kukhala wosakhoza kugwira ntchito monga wachichepere. The Encyclopcedia Judaica mowonjezera ikunena kuti: “Malinga ndi Talmud, ukalamba . . . umayamba pa 60.”

Kodi Mumakumbukira?

◻ Kodi ndi zopereka zotani zimene zinapangidwa mu zana loyamba kaamba ka akazi amasiye okalamba?

◻ Kodi ndimotani mmene oyang’anira angalinganizire chisamaliro cha okalamba mu mpingo?

◻ Kodi ndimotani mmene munthu aliyense payekha mu mpingo angasonyezere chikondwerero mwa abale ndi alongo okalamba?

◻ Kodi ndi chiyani chimene okalamba angachite kuthandiza awo amene akuwasamalira iwo?

[Bokisi pa tsamba 11]

Kuthandiza Okalamba​—Zimene Ena Akuchita

Mpingo mu Brazil umapeza njira yabwino yakusamalira kaamba ka zosowa za kuthupi za mbale yemwe anakhala. pafupi ndi Nyumba ya Ufumu yawo: Gulu la phunziro la bukhu lomwe linagawiridwa kuyeretsa holo linayeretsanso nyumba yake.

Mpingo wina kumeneko unapeza njira yaifupi yakusungira mbale wopunduka kukhala wokangalika mu Sukulu ya Utumiki ya Teokratiki. Pamene nthaŵiyake ya kupereka nkhani yafika, mbale amagawiridwa kutenga ofalitsa awiri kapena atatu ndi lye kukachezera mbaleyo. Msonkhano wachidule umatsegulidwa ndi pemphero, ndipo mbaleyo amapereka nkhani yake. Uphungu woyenerera umaperekedwa. Ndi chilimbikitso chotani nanga mmene kuchezera kumeneko kumatsimikizira kukhala!

Oyang’anira oyendayenda apereka zitsanzo zabwino mkutenga chitsogozo. Mu mpingo umodzi mbale mmodzi wokalamba yemwe anali wotsekerezedwa kukhala pa mpando wa anthu osatha kuyenda anali waukali ndipo monga chotulukapo chake samayenderedwa kawirikawiri. Woyang’anira woyendayenda, ngakhale kuli tero, anakonza kukampatsa mbaleyo kuwona kwapadera kwa nkhani yakei yazithuzmthunzi. Mbale wachikulireyo anafulumizidwa ku mlsozi ndi zimene lye anawona. Akutero woyang’anira: “Ndinadzimva kukhala wofupidwa mokulira kuwona ndimotani mmene chisamaliro chochepa ndi chikondi chingabweretsere zotulukapozoterozo”

Akulu ena mu Nigeria anapanga ulendo waubusa kwa mbale wokalamba nai kupeza kuti iye anali kudwala kwadzawoneni. lye mwamsanga anatengedwa ku chipatala. Mbale wokalambayo anapezeka akufunikira chisamaliro chamankhwala chokulira koma anali wosakhoza kulipira kaamba ka iwo. Pamene mpingo unadziwitsidwa za kusowa kwake, ofalitsa anabwera ndi ndalama zokwanira kusamalira kaamba ka zowonongedwa zake. Akulu awiri anasinthana kumuyendetsa iye kunyumba ndi kuchipatala ngakhale kuti ichi chinafunikfra kutenga nthawi ina kuchoka ku ntchito. Iwo anali ndi chimwemwe, ngakhale kuli tero, chakuwona mbaleyo akuchira kumatenda ake ndikuyamba upainiya wothandizira kufikira imfa yake zaka zina zinayi pambuyopake.

Mu Philippines mlongo wokalamba analibe banja. Mpingo unapanga makonzedwe kaamba ka kumusamalira mkati mwa zaka zitatu zakudwala kwake. Iwo anamupatsa iye malo ang’ono a kukhalapo, kumugulira iye zakudya tsiku lirilonse, ndikusamalira kaamba ka ukhondo wake.

[Chithunzi patsamba 10

Onse angakhale ndi mbali m’lemekeza okalamba athu mu mpingo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena