Kukhala Moyandikira ku Gulu la Yehova
Monga yalongosoledwa ndi John Barr
NDINALI paulendo womalizira wakuchezera kunyumba chaka chimodzi kumbuyoko June wapita, kuuluka kuchokera ku Glasgow kupita ku Aberdeen. Ndege yathu inakwera pamwamba pa dziko lobiriwira la ku Scotland ndi pamwamba pa mtsinje wa Clyde, maganizo anga anabwerera mu chaka cha 1906 ndi mudzi waung’ono umenewo wa Bishopton, wokhazikitsidwa kufupi ndi kum’mwera kwa mtsinje wo.
Mwawona, chimenecho chinali chaka ndi malo pamene agogo anga akazi, Emily Jewell, anayamba kuwerenga mabukhu a “Charles T. Russell,” The Divine Plan of the Ages. Mwamsanga maso ake anatsegulidwa ku chowonadi chakuti Baibulo siliphunzitsa nthanthi ya moto wa mu helo. Mwamsanga ana ake aakazi achikulire Bessie ndi Emily (womalizirayo kenaka anakhala mayi wanga) nawonso ayamba kuwona kuunika kwa chowonadi komawala kupyola mu nkhungu ya ziphunzitso zonyenga zophunzitsidwa ndi United Free Church of Scotland. Mu 1908 agogo anga anabatizidwa mu chisonyezero cha kudzipereka kwawo kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo ana ake a akazi anabatizidwa mwamsanga pambuyo pake.
Atate anga anali mlembi wa gawo mu tchalitchi chimodzimodzicho cha United Free Church mu Bishopton. Iwo nthawi zonse anachipeza icho chovuta kulandira chiphunzitso cha Utatu, chotero minisitala wa tchalitchi anadzipereka kulalikira uthenga wapadera kaamba ka phindu lake tsiku la Sande limodzi. Chimenecho iye anachichita! Pamene anamvetsera ku kulongosola koyeserako, atate anga tsopano anatsimikiziridwa kuti chiphunzitso cha Utatu chinali chabodza. Iwo anachisiya tchalitchicho ndipo anabatizidwa mu 1912 mu chisonyezero cha kudzipereka kwawo kwa Yehova. Mwamsanga pambuyo pake makolo anga anasamukira ku Aberdeen ndi ana awo awiri, Louie ndi James, ndipo ine ndinabadwira kumeneko mu 1913.
Malingaliro anga ponena za zaka zoyambirira zimenezo ndi ponena za kuyesayesa kwa makolo anga kulera ana atatu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova” anabwerera kwa iye pamene ndegeyo inayamba kufika pamwamba pa mapiri, mitsinje, ndi zigwa zomwe ndinazidziwa kuyambira ku ubwana. (Aefeso 6:4) Pam’mawa wokongola wowala dzuwa bwino umenewu, ndinadzimva wachiyamikiro chotani nanga kulinga kwa Yehova kaamba ka chiphunzitso cha makolo choterocho! Ndinadziwa kuti icho chinaperekako kulinga ku kukhala kwanga nthawi zonse moyandikira ku gulu la Yehova.
Phindu la Kuphunzitsa Koyambirira
Banja lathu nthawi zonse linali logwirizana mwachimwemwe. Ngati Atate ndi Amayi anali ndi kawonedwe kena kosiyana, iwo nthawi zonse anayesera kusasonyeza icho pamaso pa anafe. Ichi chinapanga mwa ife osati kokha ulemu kaamba ka makolo komanso kaamba ka malo otizinga a mtendere weniweni ndi chisungiko mkati mwa nyumba yathu.
Ena a malingaliro anga akale amazikidwa pa mayanjano omwe tinali kupanga m’nyumba mwathu madzulo. Tinapereka zosangulutsa zathu zathu, kumachita zinthu monga ngati kuyimba limodzi ndi zoyimbira zathu ndi kusewera limodzi masewera monga ngati Monopoly. Ndiponso, mosasamala kathu kuti ndi wotanganitsidwa chotani mmene Atate analiri, iwo sanalephere kuwononga nthawi yawo ndi ife tsiku lirilonse, kuwerenga mofuula kuchokera mu Baibulo ndi zofalitsidwa za Watch Tower, ndiponso kuchokera mu mabukhu ena ponse paŵiri a mtundu wopepuka ndi wosamalitsa. Izi zonse zinatumikira kuika banja lathu pamodzi pamene tinali kukula.
Tinali banja lokha la “m’chowonadi” kumbali imeneyo ya kumpoto kwa Scotland mu zaka zoyambirira zimenezo. Monga chotulukapo chake, nyumba yathu inadziŵika bwino kwambiri kwa oimira oyendayenda ambiri a Watch Tower Society (oyenda pa ulendo wa chipembedzo monga mmene ankatchedŵera nthawiyo), monga ngati Albert Lloyd, Herbert Senior, ndi Fred Scott. Ena a amenewa anabwera ngakhale kuchokera ku malikulu a Sosaite mu Brooklyn, New York, kuphatikizapo W. E. Van Amburgh ndi A. H. Macmillan. Maulendo amenewa anali mbiri zazikulu mu zaka zanga zoyambirira.
Kufikira ku tsiku lino ndimadzimva kukhala woyamikira kaamba ka mzimu wa kuchereza wosonyezedwa ndi makolo anga. Ichi chinalemeretsa moyo wathu wa banja, ndipo ngakhale kuti ndinali wachichepere, ndinayamba kufutukuka mu chiyamikiro changa kaamba ka chiyanjo chonse cha abale. Ha, ndi mokulira chotani nanga mmene makolo anga anachitira kulinga ku kukulitsa chomangilira champhumphu pakati pa ana awo ndi chiyanjano cha abale a dziko lonse!
Kuchita ndi Vuto Laumwini
Pamene ndinalowa mu zaka zanga za pakati pa 13 ndi 19, mowonjezereka ndinakhala mnyamata wa manyazi ndi wodzibweza. Pamene ndinali kukula, ndinachipezanso icho kukhala chovuta kwambiri kukumana ndi anthu ndi kukambitsirana nawo. Manyazi amenewa anapereka vuto lalikulu m’njira zanga makamaka pamene chinabwera ku kutsimikizira chikhulupiriro changa mwa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.
Mwamsanga pambuyo pa Nkhondo ya Dziko I, agogo anga akazi ndi mayi anga anakhala Mboni zoyamba mu Aberdeen kutenga mbali mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Anafe tinagawana mu kugawira timatrakiti, koma tsopano kwa ine kulankhula ndi anthu pa nyumba zawo—nkulekeraji, popeza chimenecho chinali chinachake chosiyana kotheratu! Chimenecho chinalidi chitokoso chenicheni. Koma pomalizira ndinachikumaniza icho. Sindidzaiwala nkomwe masana a Sande limenelo mu November 1927 pamene ndinauza atate anga kuti ndidzatsagana nawo mu utumiki wa ku khomo ndi khomo. Imeneyo inali nthawi yanga yoyamba kuwona misozi mu masaya a atate wanga—misozi ya chimwemwe!
Ngozi ya Banja Inandiyambukira
Mtendere wabata wa moyo wa banja lathu unathetsedwa madzulo amodzi a June 25, 1929, pamene ndinali ndi zaka 16. Pambuyo pa tsiku mu utumiki, mayi wanga ndi mlongo wanga anali kuthamangira kunyumba kukakonzekera chakudya cha madzulo cha Atate. Mwadzidzidzi, njinga yamoto yothamanga kwambiri inawagunda Amayi, kuwakankhira iwo kumbali kwa khwalala kwa chifupifupi mikono 40 (37 m). Mabala awo a m’mutu anali owopsya kotero kuti sanayembekezeredwe kukhala ndi moyo. Koma chiyamikiro ku chisamaliro chachikondi, cha miyezi yambiri cha mlongo wanga Louie, iwo anapulumuka. M’kupita kwanthawi, amayi anali okhoza kutsogoza moyo wachibadwa kufikira imfa yawo mu 1952.
Chokumana nacho chovulaza chimenecho chinachita chinachake chofunika kwambiri kwa ine—chinandipangitsa ine kuyang’ana mosamalitsa pa moyo wanga ndi mmene ndinali kuchita ndi iwo. Chirimwe chimenecho ndinayamba kuphunzira Baibulo mozama kuposa ndi kale lonse—ndinachipanga chowonadi kukhala changa. Apa panali posinthira papakulu kwa ine, ndipo ndinapereka moyo wanga ku utumiki wa Yehova. Komabe, chinali kufikira pambuyo pa zaka zina zochulukira kuti ndinali ndi mwawi wa kusonyezera kudzipereka kwanga mwa ubatizo wa m’madzi.
Kulowa mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse
Pamene ndinasiya sukulu mu 1932, ndinayamba maphunziro a umakaniki ndi uinjiniya wa magetsi. Mu Britain masiku amenewo, panalibe kulimbikitsa kumene kulipo lerolino kwa achichepere kulowa mu ntchito yolalikira ya nthawi zonse monga apainiya. Komabe, pamene zaka zinapita, ndinadziwa kumene ndinayenera kuwonongera mphamvu zanga—mu utumiki wa nthawi zonse.
Ndimakumbukira mowala chinachake chimene tinaphunzira kumayambiriro kwa 1938 chomwe chinagogomezera kwa ine mapindu akukhala moyandikira ku gulu la Yehova ndipo mwaumwini ndinagwiritsira ntchito malangizo amenewo. Inali kope ya magazini ya Nsanja ya Olonda yonena za Yona yomwe inalongosola zokumana nazo zimene iye anapyolamo pamene anali kuthawa kuchoka ku gawo lake lautumiki. Ndinatenga phunziroli ku mtima kupanga maganizo anga kuti sindiyenera kukana thayo langa lomwe lingabwere kwa ine kupyolera mu gulu la Yehova. Ndinazindikira zochepa panthawiyo kuti ndi mathayo a teokratiki otani amene anali kutsogolo kwanga kuyesa chigamulo changa.
Ndinapemphera kaamba ka chitsogozo, ndipo yankho linabwera kupyolera mu kalata yodzidzimutsa yochokera ku malikulu a Sosaite mu London, kundifunsa ine kulingalira za kukhala m’modzi wa chiwalo cha banja la Beteli. Mofunitsitsa ndinatenga mawiwo kupyola chitseko chachikulu chotsogolera ku mwawi wokulira wa utumiki. Chotero, mu April 1939 ndinadzipeza ine mwini ndikugwira ntchito limodzi ndi Harold King, amene pambuyo pake anatumikira monga mishonale mu China ndipo, chifukwa cha ntchito yake yolalikira, anawononga zaka zambiri mu ndende ya chikomyunizimu. Tinagwira ntchito yosonkhanitsa makina okopera malemba ndiponso makina osewerera mawu ogwiritsidwa ntchito kusewerera pa makomo a anthu uthenga wojambulidwa.
Harold ndi ine tinalingalira mitundu yonse yosiyana ya anthu amene akamvetsera ku uthenga wa Ufumu kupyolera mu makina amene tinali kupanga. Mu njira imeneyi sitinataye chiyang’aniro chamapeto a zotulukapo za ntchito yathu. Kuyambira pamenepo, mu mathayo osiyanasiyana amene ndinalandira pa Beteli, ndinakalamira kusunga kayang’anidwe kameneka. Chimenecho chapangitsa ntchito yanga kukhaladi yachimwemwe ndipo nthawi zonse yatanthauzo m’chigwirizano ndi ntchito yolalikira Ufumu.
Mwawi wa Utumiki
Mwamsanga pambuyo pa kufika ku Beteli ya ku London, ndinasankhidwa monga mtumiki wa kampani (tsopano wotchedwa woyang’anira womatsogolera) wa mpingo wokhala ndi oposa 200. Kumbuyoku, ndinali woyang’anira wa mpingo wa ofalitsa khumi okha! Kenaka ndinaikidwa woyang’anira wa Dipartimenti ya Mawu kaamba ka msonkhano wozizwitsa wadziko lonse wopangidwa kunja mu Leicester mu 1941. Kufikira ku nthawi imeneyi ndinali ndi chizolowezi chochepera cha za mawu.
Pambuyo pake ndinagawiridwa ntchito ya woyang’anira woyendayenda monga mtumiki wa abale, tsopano wotchedwa woyang’anira wadera. Munali kokha atumiki asanu ndi m’modzi oterowo mu Britain pamene ntchitoyo inayambidwa mu January 1943. Thayo langa linayenera kutha kokha kwa mwezi umodzi, koma inathera mu kuchezera kwanga mipingo koposa zaka zitatu. Mkati mwa zaka zovuta zimenezo za Nkhondo ya Dziko II, ndinali woyang’anira wa misonkhano itatu yaikulu—chinachake chimene ndinali ndisanachichitepo ndi kale lonse.
Ntchito yoyendayenda mu masiku amenewo inali yosiyana ndi mmene iliri lerolino. Nthawi zonse tinali kuyendayenda, ndipo kuyendayenda mu Britain mkati mwa zaka za nkhondo zimenezo chinali china chake chovuta kwambiri. Panthaŵi yoposa imodzi, ndinayenera kupita pa njinga ku mbali ya ulendo wanga pakati pa mipingo. M’malo mochezera mpingo umodzi pa mlungu, monga mmene amachitira woyang’anira woyendayenda lerolino, ngati mipingo inali yaing’ono, tinali kuchezera isanu ndi umodzi ya iyo mkati mwa mlungu umodzi!
Pano pali imene inali ndandanda ya tsiku limodzi: Kudzuka pa 5:30 a. m. ; pambuyo pakufisula, kuyenda ku mpingo wotsatira kotero kuti ndikafufuze zolembera za mpingo pofika ora lachisanu ndi chitatu la tsiku. Masana kaŵirikaŵiri anali kuwonongedwera mu utumiki wa m’munda, ichi chinatsatiridwa m’madzulo ndi kukumana kwa ora limodzi ndi atumiki a mpingo ndipo kenaka kupereka nkhani ku mpingo. Kamodzikamodzi ndinali kugona isanakwane 11, kapena mochedwerapo ngati ndinalemberatu ripoti la mpingo latsikulo madzulo omwewo. Lolemba lirilonse linaikidwa pambali kaamba ka kumaliza maripoti a mlungu, phunziro laumwini, ndi ntchito ina iriyonse yokonzekera kaamba ka mlungu wotsatira.
“Ndandanda yotanganitsidwa kwambiri ya mlungu,” kodi mukutero? Inde, iyo inali, koma, ha, chinali chopatsa mphoto chotani nanga kudzimva kuti tinali kulimbikitsa abale mkati mwa zaka za nkhondo zimenezo pamene kunalibe kuyanjana kwathithithi kwakaŵirikaŵiri ndi gulu! Mu lingaliro lenileni, tinali ndi chikwaniritso cha kudzimva kuti tinali kuthandiza mipingo “kukhala yolimba mu chikhulupiriro.”—Machitidwe 16:5.
Kubwerera ku Utumiki wa pa Beteli
Ndinafunsidwa kubwerera ku utumiki wa pa Beteli mu April 1946. Ndinali wachimwemwe kuchita tero, koma ndinadzimva kuti moyo wanga unali utalemeretsedwa mwauzimu monga chotulukapo cha zaka zitatu ndi theka zimenezo mu ntchito yoyendayenda. Gulu linatanthauza zochuluka kwa ine tsopano, ndipo ndinadzimva ngati kuti ndinali kuchita chimene chinalongosoledwa pa Masalmo 48:12, 13: “Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge; . . . yesetsani zinyumba zake.” Kukhala nditayenda kwambiri mozungulira pakati pa anthu a Mulungu kunapangitsa chikondi changa kukula kaamba ka “gulu lonse la abale.”—l Petro 2: 17, NW.
Kutsatira kubwerera kwanga ku Beteli, ndinapatsidwa mwayi wa kusamalira kaamba ka kusindikiza kokulira komwe kunali kuchitidwa pa malo athu osindikizira mu London ndipo kenaka ndinalowetsedwa mu ntchito yojambula mawu kuchoka pa pepala la pulasitiki kuwaika pa lata lomwe amagwiritsira ntchito pa makina ; osindikizira. Kenaka, mu September 1977 ndinali ndi mwawi wapadera koposa womwe unaperekedwa kwa ine wakukhala chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, lokhazikitsidwa mu Brooklyn, New York, U. S. A.
Ndiyenera kuvomereza kuti nthawi zina ndinadzimva ngati ‘ndinayenera kuthawa’ kuchokera ku ena a mathayo ovuta kwambiri opatsidwa kwa ine. Koma kenaka ndinakumbukira Yona ndi cholakwa chimene anapanga, ndipo ndinabwereza kwa inemwini lonjezo labwino kwambiri lopezeka pa Masalmo 55:22: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakugwiriziza. Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Ndimowona chotani nanga mmene ndapezera mawuwa kukhala!
Yehova safunsa aliyense wa ife kuchita chinachake chimene akudziwa kuti sitingathe kuchisamalira. Komabe, kuli kokha mu mphamvu yake kuti tiri okhoza kuchita chimene iye watifunsa kuchita. Ndipo chinthu china—ngati inu mowonadi mumakonda abale anu ogwira ntchito limodzi ndi inu, iwo adzakuchirikizani ndi kukusamalirani, kugwira limodzi nanu “ndi mtima umodzi” ndi cholinga chofuna kukuthandizani kunyamula gawo lanu la ntchito logawiridwa.—Zefaniya 3:9.
Maunansi Apadera
Ndithudi, pamakhala nthawi zonse abale ena Achikristu kwa amene mumadzimva kumangika kwapadera. M’modzi wa amenewa anali Alfred Pryce Hughes, amene anamwalira mu 1978. Mbiri ya moyo wake inawoneka m’kope la April 1, 1963, la Nsanja ya Olonda ya chingelezi. Kwa zaka zambiri anatumikira monga mtumiki wa nthambi, ndipo pambuyo pake monga chiwalo cha Komiti ya Nthambi. Iye anakondedwa mokulira ndi abale m’munda wa Chibritishi chifukwa cha ulemu wake wokulira ku gulu la Yehova ndi kukhulupirika kwake ku ilo ndi chikondi chake kaamba ka abale onse. Chinthu china chinali chikondi chake kaamba ka utumiki wa m’munda. Ichi sichinazilale nkomwe m’moyo wake wonse, mosasamala kanthu kuti ndi thayo lotani limene iye anayenera kulisamalira. Kugwira ntchito limodzi ndi abale okhulupirika monga Pryce kunatanthau za zochuluka kwa ine, kulimbikitsa kulimbamtima kwanga kukhala moyandikira ku gulu la Yehova ndi kukhala wokangalika mu utumiki.
Pa October 29, 1960, ndinalowa mu unansi wapadera mopambana ndi mpainiya wachangu kwa nthawi yaitali ndi mishonale wa kalasi 11 la wa Gilieadi, amene panthawiyo anali kutumikira mu Ireland. Pa tsiku limenelo Mildred Willett ndi ine tinakwatirana, ndipo kuyambira nthawi imeneyo iye wakhala mchirikizi wokhulupirika kwa ine mu utumiki wa pa Beteli.
Mayi ake a Mildred asanamwalire mu 1965, anachenjeza mwana wake “kusachitira nsanje Yehova.” Mildred nthawi zonse amakumbukira mawu a mayi wake, ndipo ichi chamuthandiza kuchinjiriza kusakhala wosakhutiritsidwa pamene kaŵirikaŵiri ndinayenera kugwira ntchito nthawi yowonjezera. Ichi mokulira chandithandiza ine kusamalira kaamba ka ntchito ina yowonjezereka mwachimwemwe yomwe ingabwera mu njira yanga. Tonsefe tasangalala makamaka ndi kugawana mu zokumana nazo zopatsa mphoto za mu utumiki.
Banja limodzi lachichepere lomwe tinaphunzira nalo Baibulo, mwachitsanzo, linapanga kupita patsogolo kofulumira kufika ku nsonga ya kudzipereka ndi ubatizo ndipo mokhazikika kugawana mu utumiki. Tinali achimwemwe koposa! Kenaka, mwadzidzidzi, mopanda chifukwa chenicheni, iwo analeka kuyanjana. Mildred ndi ine tinagawana kukhumudwitsidwaku, ndipo tinapitiriza kudabwa kuti ndi pati pamene tinalakwa mkuwaphunzitsa kwathu iwo. Mokhazikika tinapemphera kwa Yehova kuti atsegule mitima yawo kutsimikizira chikondi chawo kaamba ka chowonadi. Kodi mungalingalire chimwemwe chomwe tinali nacho pamene tinalandira kalata yochokera kwa awiri amenewa chifupifupi zaka khumi pambuyo pake kutiuza ife kuti anali kuyanjananso mokangalika ndipo kuti nyumba yawo inali malo apakati a Phunziro la Bukhu?
Mwamunayo Will analemba: “Ndikufuna kukuyamikirani inu kaamba ka thandizo lonselo ndi kulingalira kwachikondi kumene munatipatsa ife. . . Kugwa kwanga kunali chifukwa cha kulakwa kwanga, chiyamikiro changa cha mtima sichinali cholondola . . . Tapeza chimwemwe chachikulu kubwereranso mu gulu la Yehova . . . Ndikukulemberani usiku uno ndi chikumbumtima chosangalatsa, lolani kuti Yehova apitirizebe kukudalitsani inu nonse awiri mu utumiki wanu kwa iye.”
, Mu kalata ina, mayi anatilembera ife ponena za mnyamata wake Mike: “Ndiri wosangalala kwambiri kuti angelo anamukhazika iye pafupi ndi inu.” Kodi nchiyani chimene iye anatanthauza? Chabwino, Mike anakhala akubwera ku misonkhano limodzi ndi mayi wake ndi mbale wake wamng’ono, koma sanali wokondweretsedwa kwemkweni mu chowonadi. Mildred anamuwona mnyamatayo atakhala yekha ndipo anacheza ndi iye. Kenaka tonse awiri tinamuitana iye ndi mbale wake kubwera ku Beteli ya ku London ndi kuwona ntchito imene tinkachita.
Pambuyo pake, Mike anabwera, ndipo zimene anawona zinawunikira chikondwerero chake mokwanira kupitiriza kukhala ndi phunziro la Baibulo. Chotulukapo chake? Iye tsopano ali mkulu mu mpingo, ndipo mkazi wake ndi anyamata awiri ali okangalika mu utumiki. Nthawi ina yapita mkazi wa Mike analemba: “[Mike]mobwerezabwereza amatchula zokumana ndi inu awiri. . . Anali wokhudzidwa chotani nanga ndi chikondi chanu ndi chikondwerero mwa iye.”
Pamene mkazi wanga ndi ine talandira zisonyezero za chiyamikiro kuchokera kwa wina wake wonga Will kapena Mike amene tinali ndi mwawi wa kuwathandiza, mitima yathu imasefukira ndi chiyamikiro kwa Yehova! Ndi mphatso za mtengo wapatali chotani nanga mmene “makalata a chiyamikiro” amoyo amenewa aliri—mbali yachimwemwe yonseyo yolandiridwa kuchokera mu kukhala moyandikira ku gulu la Yehova.—2 Akorinto 3:1-3.
Kutumikira pa Malikulu a Dziko Lonse
“Mtundu mwa iwo wokha.” Mmenemo ndi mmene mkonzi wa nyuzipepala ya Brooklyn Heights analongosolera banja lalikulu la Mboni zoposa 3, 500 zokhala ku malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York, ndi ku Watchtower Farms, yokhala chifupifupi mamailosi zana (160 km) ku mtunda kwa New York. Zowonadi, odzozedwa a Yehova alidi mtundu wauzimu m’maso mwa Yehova! Lerolino, makamu ochokera ku mitundu yambiri yachikunja akubwera ndi kunena kwa a mtundu umenewu: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zekariya 8:23; 1 Petro 2:9.
Kodi mungayamikire, nanga, ndi chosangalatsa chotani mmene chinaliri kwa mkazi wanga ndi ine kukhala mbali yokhazikika ya banja la Beteli lalikulu limeneli? Ndinganene mopanda kukaikira kulikonse kuti zaka zapita zisanu ndi zitatu za moyo wanga zakhala zowonekera koposa mu chokumana nacho changa chonse chateokratiki. Pano mumamva kugunda mtima kwa gulu lowoneka ndi maso la Yehova; pano chakudya chauzimu chimakonzekeretsedwa ndipo kenaka kutumizidwa kungodya zinayi za dziko; pano mumawona mzimu wa Yehova ukugwira ntchito kutsogoza ndi kuwongolera zosankha zofunika zomwe ziyenera kuchitidwa; ndipo pano mumamva chitsimikiziro cha dalitso la Yehova kuposa kwina kulikonse pa ntchito ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Zokumana nazo zonsezi zaposachedwa ndi zitsimikiziro zandipatsa ine chikhumbo chowonjezereka champhamvu cha kukhala moyandikira koposa kwa anthu a Yehova.
Ndakamba kokha mbali yochepa ya zokumana nazo zanga za m’moyo. Komabe, zingakuthandizeni inu kumvetsetsa nchifukwa ninji, pamene ndege yanga pomalizira inagunda pansi pa Bwalo la Ndege la Aberdeen m’dzuwa lowala bwino la mwezi wa June umenewo, ndinadzimva woyamikira koposa kwa Yehova kuti ndinali ndidakali mbali ya gulu laubale wa dziko lonse wa chikondi. Ndawononga nthawi yanga yakuuluka kubwereramo mu zaka zanga za mu chowonadi, ndipo ichi chandikumbutsa ine kachiwirinso kuti ndi chopindulitsa chotani nanga mmene chiriri kwa ife kwanthawi ndi nthawi kuwerengera madalitso athu ochuluka amene ali pa dzanja la Yehova.—Masalmo 40:5.
Mlongo wanga Louie, anali pamenepo kundilandira ine—adakali wokhulupirika, wachangu, ndi wokhulupirika pambuyo pa zaka 60 za kudzipereka ku utumiki wa Yehova. Ndiyamikira Yehova kaamba ka dalitso lowonjezereka limenelo, popeza kodi mtumwi Paulo sananene kuti kuli kukhulupirika kumene Yehova amayang’ana mwa “athenga ake” onse? (1 Akorinto 4:2) Ndichilimbikitso chotani nanga chimene chiwalo chimodzi chabanja chingapereke kwa wina mwakukhala wokhulupirika!
Mose kamodzi anapemphera kuti: “Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” (Masalmo 90: 12) Pamene Mildred ndi ine tikukula, timayamikira nthawi zonse kufunika kwakuyedzamira pa nzeru ya Yehova kotero kuti tigwiritsire moyo wathu m’njira imene imasonyeza chikondi chathu kaamba ka iye ndi abale athu. Yehova mwachikondi amatisonyeza ife njirayo ngati tikukhala moyandikira ku gulu lake.
[Chithunzi patsamba 28]
John Barr (kumanzere kutsogolo) chifupifupi chaka cha 1930 ndi mlongo wake, mbale wake, ndi makolo ake
[Chithunzi patsamba 31]
John Barr, lerolino, ndi mkazi wake Mildred