Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 11/15 tsamba 3-4
  • Kodi Chipembedzo Chakhutiritsa Zosowa Zathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chipembedzo Chakhutiritsa Zosowa Zathu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chipembedzo Chirichonse Chiri Chabwinodi?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
    Mapeto A Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!
  • Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Zipembedzo Zimalakwitsa Pati?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 11/15 tsamba 3-4

Kodi Chipembedzo Chakhutiritsa Zosowa Zathu?

MARIA anali virigo wa Roma Katolika kwa zaka 21. Iye anakula m’malo a chipembedzo kwambiri. Nkulekelanji, popeza monga mwana, ankauka usiku kupemphera kaamba ka ena! Kenaka, ngakhale kuli tero, umphaŵi, mavuto, ndi kusoweka kwa chilungamo komwe kunalipo mosasamala kanthu za zikwi za zaka za chisonkhezero cha chipembedzo zinampanga iye kudabwa: ‘Kodi chipembedzo chakhutiritsadi zosowa zathu?’

Zipembedzo zambiri zimapititsa patsogolo malingaliro ndi maprinsipulo a makhalidwe abwino. Koma chipembedzo kaŵirikaŵiri chimawonedwa monga choyambitsa mavuto, kuwonjezera ku mavuto athu, m’malo mwa kukhutiritsa zosowa zathu. Mwachitsanzo, lingalirani ndemanga izi zopangidwa ndi owonerera a chiwonetsero cha chipembedzo: “Chifukwa cha mkati kwenikweni kaamba ka kusaka kwankhalwe kuli chipembedzo.” (National Review) “Chisonkhezero chachikulu kwambiri cha nkhondo sichirinso umbombo koma chipembedzo.” (Toronto Star) “Kuphulika kwa Mabomba ‘konse kunachitidwa ndi Akristu obatizidwa.’”​—The Tampa Tribune.

Kodi nchodabwitsa kuti anthu ena amakana kudzinenera kwa chipembedzo kuti icho chiri chokhutiritsa cha zosowa zathu? Iwo awona zipatso zake. Mwachitsanzo, “chinali chiShinto, chipembedzo chachibadwa cha ku Japan, chomwe sichinapereke kokha chichirikizo chake cha mtima wonse ku makina a nkhondo komanso chinapereka chikhulupiriro chake,” inatero The Christian Century. Ndi zipembedzo zingati zomwe zachita chimenecho​—‘kupereka chichikirizo cha mtima wonse ku makina a nkhondo’! Lingalirani za kupha kwaunyinji ndi zotulukapo zosonkhezeredwa ndi a Budha ndi a Hindu mu Sri Lanka, kupha ndi nsautso zokhudza Akatolika ndi a Protestanti mu Ireland​—nkulekelanji, ndandandayo ikuwoneka yosatha! “A Hindu, a Silamu, a Sikhs ndi magulu ampatuko ena akhala akukhetsa mwazi wa wina ndi mnzake kwa zaka mazana mu India,” inalira U.S.News & World Report.

Ena sangawone chipembedzo monga chisonkhezero choipa, koma iwo mowonadi samawona icho monga mphamvu yolimba kaamba ka chabwino. National Catholic Reporter ananena ponena za “kulephera kwa matchalitchi a mwambo kwa kufikira mokhutiritsa zofuna ndi zosowa za anthu.” Ndipo magazini ya Liberty inanena kuti chitaganya chikuwona kuti chikuwoneka atsogoleri a chipembedzo monga “wodalitsa-wokhutiritsa-wopembedza” wotulutsidwa kokha pa zochitika za mapwando. Iyo ikuwonjezera kuti: “M’malingaliro a anthu ambiri iye ali mtumiki wa malo apamwamba.” Kodi inu mwawona chipembedzo m’njira yotero​—osati choyenera kutivulaza komanso chosayenerera kutichitira ife zabwino zambiri?

Chipembedzo lerolino chiri mokulira monga mmene chinaliri pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi. Iye ananena kuti atsogoleri a chipembedzo a m’tsiku lake analemekeza Mulungu ndi milomo yawo. Zotulukapo za machitachita awo zinali zakuti iwo anawonjezera ku zolemetsa za anthu m’malo mwa kukhutiritsa zosowa zawo. “Iwo anapanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenzetsa pa mapewa a anthu,” iye anatero. (Mateyu 23:4) Lerolino, chipembedzo chimalonjeza zambiri koma chikuwona kupereka zochepa. Chotero kodi pali chifukwa cha kukhulupirira kuti chipembedzo chingakhutiritse zosowa zathu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena