Kumaliza Maphunziro kwa Kalasi ya 83 ya Gileadi Zowonadi Nthaŵi ya Chochitika cha Phwando
“YAMIKANI Yehova pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosatha.” (Masalmo 136:1) Kumeneko kunali kudzimva kochokera mu mtima kwa anthu 4,391 omwe anapezekapo pa maseŵera a kumaliza maphunziro kwa kalasi ya 83 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower chirimwe chino. Nkhani, zokumana nazo, ndi chitsanzo cha Baibulo zoperekedwa mkati mwa maseŵerawo zinapangitsa onse kuchoka osangalatsidwa. Kumaliza maphunziroko kunachitika pa September 6, 1987, pa Holo ya Msonkhano yokongola ya Jersey City, yomwe kumbuyoko inkadziŵika monga Stanley Theater.
Pambuyo pa nyimbo yotsegulira, ndi pemphero ndi John Booth wa Bungwe Lolamulira, tcheyamani, Albert Schroeder, chiwalo china cha Bungwe Lolamulira, analandira onse ku chochitika cha phwando chimenechi. Ophunzira 24 anabwera kuchokera ku maiko asanu, ndipo iwo tsopano anali kutumizidwa ku maiko osiyanasiyana asanu ndi atatu. Mbale Schroeder anawunikira chidaliro chimene anthu a Yehova ali nacho chifukwa cha chikhulupiriro chawo chozikidwa pa zinthu zotsimikizirika. Iwo amadziŵa, mwachitsanzo, kuti Yehova ali Wolamulira wa Chilengedwe chonse ndipo kuti Mawu ake, Baibulo Loyera, liri chowonadi chotheratu. Ichi chiri chosiyana kotheratu ndi nthanthi za anthu zozikidwa pa zosatsimikizirika ndi ziyerekezo.
Mlankhuli woyamba anali Martin Poetzinger, yemwenso ali chiwalo cha Bungwe Lolamulira, yemwe anatha zaka zisanu ndi zinayi m’misasa ya chibalo ya Nazi. Mutu wake unali wakuti “Ndi Mwandani Mmene Mukhulupirira?” wozikidwa pa Miyambo 3:5, 6. Iye anagogomezera kwa ophunzirawo kufunika kwa kukhulupirira kotheratu mwa Yehova ndi gulu lake lowoneka ndi maso, limodzinso ndi kudzitsimikizira mwaumwini kukhala wodalirika. Kuphunzitsidwa kwa ophunzirawo pa Gileadi kunali kokha maziko; tsopano iwo anayenera kumanga pa iwo kutsatira uphungu wa Paulo pa Aefeso 5:15, 16. ‘Musangoima chiriri,’ anafulumiza tero mlankhuliyo. ‘Mudzakhala ndi mavuto anu mu gawo lanu la umishonale monga ngati chinenero, nyengo, chakudya, ndi zina zotero; koma mwa kukhulupirira Yehova, mungathetse mavuto onsewo. Chikondi kaamba ka anthu chiri mfungulo yanu ku chipambano. Chilimbikitso chirichonse chiri chochokera kwa Mulungu; kukhumudwitsa kulikonse kuli kochokera kwa Satana.’
Mlankhuli wotsatira anali Eldor Timm, chiwalo cha Komiti ya Fakitare, yemwe anazika ndemanga zake pa 2 Akorinto 13:5: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro.” Ophunzirawo athana nawo mayeso olemba, iye anatero, koma iwo adzapitiriza kuyang’anizana ndi mayeso ena m’magawo awo a umishonale. Mmene akayang’anizirana ndi mayeso amenewo chikatsimikizira chipambano chawo monga amishonale. Iwo ayenera kukhala ogalamuka motsutsana ndi chidaliro chopambanitsa mwa kulabadira uphungu wakuti: “Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:12) Iwo adzapitiriza kupanga ziwongolero ngati apitiriza kukhala ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo.
Chiwalo cha Service Department Committee, Joel Adams, anatsatirapo. Iye analankhula pa mutu wakuti: “Lingalirani Monga Yesu, Sonyezani Chikondwerero Chaumwini mwa Ena.” Chinali chitsanzo chabwino chotani nanga chimene Yesu anakhazikitsa m’nkhaniyi! Chitsanzo chake cha kupanda dyera ndi kudzichepetsa chinawunikiridwa kaamba ka ife pa Afilipi 2:3-5. Ngati ena ali chiyeso kwa ife chifukwa cha zophophonya zawo kapena kusowa luso, lolani ife tipite m’njira yathu kukasonyeza chifundo kwa iwo. Mkati mwa Sukulu ya Gileadi, ambiri anasonyeza chikondwerero mwa ophunzira; tsopano chinali kwa iwo kuchita chofananacho kulinga kwa ena. Amishonale achipambano kwambiri ali awo amene amasonyeza chikondwerero m’miyambo, chilankhulo, zosowa, ndi zina zotero za ena.
Kenaka, ophunzirawo analimbikitsidwa ndi mmodzi amene anakhala m’mishonale kwa zaka zambiri, Lloyd Barry, yemwenso ali chiwalo cha Bungwe Lolamulira. Iye analankhula pa mutu wakuti “Imbani kwa Yehova,” wozikidwa pa Masalmo 96:1. Anthu a Yehova amasangalala ndi kuimba. Kuimba kumayendera limodzi ndi chimwemwe, ndipo chotero iye analimbikitsa ophunzirawo kusataya chimwemwe chawo cha kubweretsa ena m’chowonadi. ‘Ngati mukafunikira kuphunzira chinenero chatsopano,’ iye anafulumiza kuti, ‘ikani mtima wanu mu icho kuyambira pa chiyambi. Mdyerekezi adzayesera kukukhumudwitsani, kukupangitsani inu kukhumba kunyumba, kupangitsa kusagwirizana m’mathayo anu. Musamulole iye ngakhale mpang’ono pomwe!’ Mbale Barry analozera ku “mphunzitsi wamkulu wa amishonale,” Edwin Skinner, yemwe wakhala mu gawo lake lachilendo mu India kwa zaka 60, ndipo amene tsopano pa msinkhu wa zaka 93 akuchitabe ntchito ya tsiku lathunthu. Mogwirizana ndi Mbale Skinner, mfungulo ku chipambano monga m’mishonale imaphatikizapo mawu anayi: “Kudzichepetsa iri mfungulo yaikulu!”
Kutsatira ndemanga zimenezi, tcheyamani anaŵerenga unyinji wa matelegramu oyamikira ophunzirawo ndi kupereka malonje kwa iwo. Mauthengawo analandiridwa kuchokera ku Bolivia, Canada, Ecuador, Honduras, Spain, Sweden, ndi Trinidad.
Jack Redford, mmodzi wa alangizi a pa Sukulu ya Gileadi, analankhula pa mutu wakuti “Pitirizanibe Kukhala Bwenzi la Yehova.” Iye anayamba mwakudziŵitsa kuti pali maphunziro a zamalonda ambiri amene amapereka maphunziro pa kupeza chipambano mu bizinesi mwa kupeza mabwenzi ndi kusonkhezera anthu. Ophunzirawo, monga amishonale a mtsogolo, aphunzitsidwanso mmene angapezere mabwenzi ndi kusonkhezera anthu, komabe, osati kaamba ka phindu la dyera, koma chifukwa chakuti anthu oterowo angakhale mabwenzi a Mulungu. ‘Wanu uli moyo wa kudzipereka kwaumwini,’ anatero mlankhuliyo. ‘Munalandira kwaulere, patsani kwaulere. Palibe chikhutiritso kapena chimwemwe chochulukira koposa kupambana m’kuthandiza anthu kukhala mabwenzi a Mulungu. Ubwenzi ndi Mulungu uli ulemu waukulu koposa umene cholengedwa chirichonse chingakhale nawo. Yakobo 2:23 amatiuza kuti Abrahamu anakhala bwenzi la Yehova chifukwa cha kusonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu. Iye anapita kudziko lachilendo ndipo sanayang’ane m’mbuyo; ndiponso inu amishonale simuyenera kuyang’ana m’mbuyo, koma, m’malomwake, yang’anani kutsogolo ku madalitso m’dziko latsopano la Mulungu.’
Ulysses Glass, mlangizi wa pa Gileadi ndi registrar wa sukuluyo, tsopano analankhula pa mutu wakuti “Phunziro Lomalizira.” Iye anadziŵitsa kuti ophunzirawo anaphunzira mmene malamulo a Yehova aliri ofika kutali ndi achindunji. Mwanjira ya chitsanzo, iye analozera ku tsatanetsatane wochuluka wogwirizana ndi nsembe zoperekedwa pa Tsiku la Chitetezero ndi nyama zambiri zomwe zinaphatikizidwamo. (Levitiko, mutu 16) Iye anayamikira ophunzirawo kaamba ka chiyamikiro chawo chosonyezedwa chochokera mu mtima ndipo ananena kuti Masalmo 145:7 amalongosola bwino khalidwe lawo lamaganizo: “Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu.” M’mawu ake omalizira, iye anagwiranso mawu Miyambo 3:5-7, akumagogomezera kufunika kwawo kwa ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse.’
Mbale F. W. Franz, prezidenti wa zaka 94 za kubadwa wa Sukulu ya Gileadi ndiponso prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, anapereka nkhani yomalizira ya m’mawamo. Mu iyo iye anafotokoza mbiri yakale ya Sosaite kuyambira pa nthaŵi ya prezidenti woyamba, C. T. Russell, kufikira pa kukhazikitsidwa kwa Sukulu ya Gileadi. Kupereka kwake kwamphamvu ndi kotenthedwa maganizo kunayamikiridwa mokulira ndi onse. Pambuyo pa nkhani yake, ophunzira 24 analandira zipepala zawo zosonyeza kumaliza maphunziro limodzinso ndi mphatso zina, ndipo kenaka mmodzi wa ophunzirawo anaŵerenga kalata yabwino yosonyeza chiyamikiro cha ophunzirawo kaamba ka thandizo lonse limene analandira kuchokera kwa Bungwe Lolamulira ndiponso kuchokera ku banja la Beteli.
Pambuyo pa kupuma kwa chifupifupi maora aŵiri, Phil Wilcox, chiwalo cha Komiti ya Watchtower Farms, anatsogoza phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda ya posachedwapa mu limene mafunso ophunziridwa anayankhidwa ndi ophunzirawo. Chimenecho chinatsatiridwa ndi programu ya ophunzirawo mu imene iwo anachitira chitsanzo zokumana nazo zimene anasangalala nazo pamene anali kuchitira umboni mkati mwa Lachitatu masana mu Mzinda wa New York. Iyi inali mbali ya maphunziro awo a pa Gileadi. Iwo mowonekeranso anachitira chitsanzo mavuto osiyanasiyana amene angayembekeze kukumana nawo pamene afika ku magawo awo achilendo.
Monga mapeto oyenerera ku programu yonse, ophunzirawo anapereka chitsanzo cha Baibulo atavala zovala za pa chitsanzo m’mbali ziŵiri, kuwunikira kuwopsya kwa nthaŵi zimene tirimo. Chitsanzocho chinachita ichi mwa kuyerekeza masiku athu ndi nyengo za chiweruzo chapita. Pa 4:15 p.m., ndi kuimbidwa kwa nyimbo ya “Kuwonjezeka kwa Teokratiki” ndi pemphero ndi chiwalo cha Bungwe Lolamulira Milton Henschel, programu yosangalatsa koposayo inafika ku mapeto ake.
[Chithunzi patsamba 23]
Kalasi Lomaliza Maphunziro la 83 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
Mu ndandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuchokera kutsogolo kupita kumbuyo ndipo maina andandalikidwa kuchokera ku lamanzere kupita kulamanja mu mzera uliwonse. (1) Melin, D.; Goode, M.; Ramos, M.; Chow, N.; Hermanson, A.; Dagostini, D. (2) David, E.; DiPaolo, A.; Neiman, D.; Shephard, J.; Foster, M.; Ramos, R. (3) Foster, W.; Melin, D.; Fristad, D.; Fristad, R.; White L.; Dagostini, F. (4) Neiman, D.; Ness, S.; Shephard, D.; Goode, J.; White, K.; Hermanson, L.