Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 12/15 tsamba 8-9
  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Yesu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Yesu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yesu Kwenikweni Ndani?
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Mwana wa Munthu Ndi Ndani?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Anakhalabe Wokhulupirika Panthawi Yovuta
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 12/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali Yesu?

PAMENE chingalawa chonyamula Yesu ndi ophunzira ake chinafika pa Betsaida, anthu akubweretsa munthu wakhungu kwa iye ndi kumupempha kuti agwire munthuyo ndi kumchiritsa. Yesu akutsogolera munthuyo ndi dzanja lake kunja kwa mudzi ndipo, pambuyo pakuthira malovu m’maso mwake, iye akufunsa kuti: “Uwona kanthu kodi?”

“Ndiwona anthu,” munthuyo akuyankha, “pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.” Akuika dzanja lake pamaso pa munthuyo, Yesu abwezeretsa kuwona kwake kotero kuti iye akukhoza kuwona mowonekera bwino. Yesu kenaka akutumiza munthuyo kumudzi ndi malangizo akuti asalowe mu mzinda.

Yesu tsopano akuchokapo ndi ophunzira ake kaamba ka mudzi wa ku Kaisareya wa Filipi, chakumapeto kwa kumpoto kwa Palesitina. Iwo ali malo okwera okwanira chifupifupi makilomita 48 ku malo okongola a Kaisareya wa Filipi, chifupifupi mamita 345 pa mtunda wa nyanja. Ulendowo utenga mwinamwake masiku angapo.

M’njira, Yesu apatuka yekha ndi kupemphera. Kokha miyezi isanu ndi inayi kapena khumi yatsala imfa yake isanadze, ndipo ali wodera nkhaŵa ponena za ophunzira ake. Ambiri aleka kale kumtsatira iye. Ena ake mwachiwonekere ali osokonezeka ndi ogwiritsidwa mwala chifukwa chakuti anakana kuyesayesa kwa anthu kwa kumpanga iye mfumu ndiponso chifukwa chakuti iye sanakhoze, pamene anavutitsidwa ndi adani ake, kupereka chizindikiro kuchokera kumwamba kutsimikizira kukhala kwake Mfumu. Kodi nchiyani chimene atumwi akakhulupirira ponena za chizindikiritso chake? Pamene anabwera kumalo kumene iye anali kupempherera, Yesu akufunsa kuti: “Anthu anena kuti ndine yani?”

“Ena ati Yohane Mbatizi,” iwo akuyankha, “koma ena Eliya, ndipo enanso Yeremiya kapena m’modzi wa aneneri.” Inde, iwo aganizira kuti Yesu ali m’modzi wa amuna amenewa owukitsidwa kuchokera kwa akufa!

“Koma inu mutani kuti ine ndine yani?” Yesu akufunsa.

Petro mwamsanga akuyankha kuti: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”

Pambuyo pa kulongosola kuvomereza kwa kuyankha kwa Petro, Yesu akunena kuti: “Ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pathanthwe iri ndidzakhazika mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.” Pano Yesu akulengeza choyamba kuti iye adzamanga mpingo ndikuti ngakhale imfa sidzasunga ziwalo zake mu ukapolo pambuyo pa ntchito yawo yokhulupirika pa dziko lapansi. Kenaka akuuza Petro kuti: “Ndidzakupatsa mfungulo za ufumu wakumwamba.”

Yesu chotero akuvumbula kuti Petro adzalandira mathayo apadera. Ayi, Petro sanapatsidwe malo oyamba pakati pa atumwi, kapena kuti iye wapangidwa kukhala maziko a mpingo. Yesu iyemwini ndiye Mwala wapangondya pa umene mpingo wake udzamangidwa. Koma Petro adzapatsidwa mfungulo zitatu za kutsegulira, monga mmene kunaliri, mwaŵi kaamba ka gulu la anthu kuloŵa mu ufumu wakumwamba.

Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yoyamba pa Pentekoste wa 33 C.E. pamene iye anasonyeza Ayuda olapa chimene akafunikira kuchita kuti apulumutsidwe. Iye anagwiritsira ntchito yachiŵiri mwamsanga pambuyo pake pamene iye anatsegulira a Samariya okhulupirira kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Kenaka, mu 36 C.E. iye anagwiritsira ntchito mfungulo yachitatu mwa kutsegulira kwa Akunja osadulidwa, Koneliyo ndi mabwenzi ake, mwaŵi wofananawo.

Yesu akupitiriza kukambitsirana kwake ndi ophunzira ake. Iye akuwakhumudwitsa mwa kuwauza za kuvutika ndi imfa zimene iye adzayang’anizana nazo posachedwa mu Yerusalemu. Pambuyo pa kulephera kumvetsetsa kuti Yesu adzaukitsidwa ku moyo wakumwamba, Petro akumtenga Yesu pambali. “Dzichitireni chifundo, Ambuye,” iye akutero. “Sichidzatero kwa inu ayi.” Akupotoloka, Yesu ayankha kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe! Ndiwe chondikhumudwitsa ine, chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.”

Mwachiwonekere, ena pambali pa atumwi akuyenda pamodzi ndi Yesu, chotero iye akuwaitana iwo kuti alongosole kuti sichidzakhala chopepuka kukhala omtsatira. “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga,” iye akutero, “adzikane yekha natenge [mtengo wake wozunzirapo NW] nanditsate ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha ine ndi mbiri yabwino adzaupeza.”

Inde, atsatiri a Yesu afunikira kukhala olimbika ndi kudzikana kwaumwini ngati ati atsimikizire chipulumutso chawo, monga mmene iye akulongosolera kuti: “Pakuti aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha ine ndi mawu anga, Mwana wamunthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wa Atate ake, ndi wa angelo oyera.” Marko 8:22-38; Mateyu 16:13-28; Luka 9:18-27.

◆ Nchifukwa ninji Yesu ali wodera nkhaŵa ponena za ophunzira ake?

◆ Kodi ndi kawonedwe kotani kulinga ku chizindikiritso cha Yesu kamene anthu ali nako?

◆ Kodi ndi mfungulo zotani zimene zinaperekedwa kwa Petro, ndipo zinagwiritsiridwa ntchito motani?

◆ Kodi ndi kuwongolera kotani kumene Petro analandira, ndipo nchifukwa ninji?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena