Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 12/15 tsamba 10-15
  • Yembekeza Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yembekeza Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mwamsanga Kwenikweni Pa​—Chiyembekezo!
  • Chiyembekezo Chinakhalabe Chamoyo
  • Nthaŵi ya Chiyembekezo Tsopano
  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mbewu ya Njoka—Yavumbulidwa Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 12/15 tsamba 10-15

Yembekeza Yehova

“Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.”​—MASALMO 37:34.

1, 2. Ndi kuti kumene mtundu wa anthu ukuwoneka kukhala ukuimirira, ndipo ndimotani mmene Mitundu Yogwirizana ikulowetsedweramo?

MWALUNTHA, banja la munthu lafikira ku mlingo wake wofika patali kwenikweni wa kakulidwe. Chifukwa cha kuyesayesa kwake, ilo potsirizira pake lafikira pa mbadwo wa nyukliya. Mphamvu za atomiki zikuwoneka kukhala zokhoza kupereka mphamvu zokulira ndipo chotero kutsegula zinthu zazikulu kuzungulira dziko lonse. Mophiphiritsira, ilo lakonzanso njira kaamba ka kuvulaza kwakukulu kwa mtundu wa anthu.

2 Kodi nchiyani chimene chikuima m’njira ya kudziwononga okha kwa banja la munthu mu chipiyoyo cha nyukliya? Icho chingawonekere kukhala Chigwirizano cha Mitundu, chimene chimadzitukumula kaamba ka kukhala ndi ziwalo za mitundu 159 zokhala ndi mtundu uliwonse wa maboma. Mwa ndale za dziko, maboma amenewa samavomerezana lina ndi linzake, lirilonse likumakhulupirira kuti kapangidwe kake ka kulamulira kali kokulira, inde, kabwino koposa. Chotero, mkati mwake, UN liri bungwe losamvana. Kunyada kwa ufuko ndi chikhumbo kaamba ka kudziimira pa lokha kumafalikira. Ndiponso, chiŵerengero chachikulu cha mitundu chakana chikhulupiriro mwa Mulungu, ndi kukhala okana Mulungu.

3. Kodi ndimotani mmene kawonedwe ka Chikristu cha dziko ka Mulungu kamasiyanirana kuchokera ku kamene Mulungu iyemwini ali nako?

3 Dzina lakuti Chikristu cha Dziko limagwirabe ntchito ku mitundu imene simafuna kudziwikitsidwa monga yopanda umulungu koma yodzinenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu m’chigwirizano ndi “Mulungu Atate” mu utatu wogwirizana ndi Yesu ndi umunthu wa “mzukwa woyera,” kapena mzimu woyera. Ziwalo za Utatu zimalengezedwa kukhala zofanana. Komabe atate wa Yesu anauza mneneri Yesaya kulemba mawu awa achizindikiritso: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Kunena kuti Yehova, kapena Yahweh (The Jerusalem Bible), kwapanga cholembedwa cha m’mbiri yakale chosakhoza kuyerekezedwa kaamba ka iye.

4. Mitundu Yogwirizana ikucheutsa mtundu wa anthu kuchokera ku chiyani?

4 Popanda chilemekezo chirichonse ku iyo, Mitundu Yogwirizana yapatuka kuchoka ku kupereka ulemu woyenera ndi chizindikiritso ku dzina la Mulungu. Iyo siimalimbikitsa mtundu wa anthu, womwe tsopano ukuyang’anizana ndi kusowa chochita kwake koipa, kukhala ndi chiyembekezo mwa wokhala ndi dzina limenelo. Komabe, Ameneyo akudziŵikitsidwa bwino lomwe monga “Mulungu wa chiyembekezo,” powona kuti iye wakhazikitsa maziko a chiyembekezo chokha chenicheni chimene mtundu wa anthu ungakhale nacho tsopano. (Aroma 15:13, King James Version) Chiyembekezo chimene iye amapereka chalimbikitsa ndi kupatsa mphamvu amuna ndi akazi ambiri.

Mwamsanga Kwenikweni Pa​—Chiyembekezo!

5. Kodi ndi liti pamene maziko a chiyembekezo anakhazikitsidwa?

5 Maziko a kukhala ndi chiyembekezo chimenecho anakhazikitsidwa poyambirirapo m’mbiri ya banja la munthu. Inde, chinakhazikitsidwa mwamsanga makolo athu oyambirira asanatulutsidwe kuchoka m’mudzi wa munda wawo wa Edeni mu Middle East. Mawu olembedwa mu chinenero cha Chihebri ponena za munda umenewo, kapena paradaiso, sali kokha mbiri, osatinso nthano ya anthu omwe anapatuka kuchoka pa kulambira Mlengi wawo.​—Genesis 2:7–3:24.

6. Kodi ndimotani mmene mtundu wa anthu unadzafunikira chiyembekezo?

6 Koposa zaka 4,000 pambuyo pake, mtumwi Wachikristu Paulo anawuziridwa kulemba kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Mu zina za zolembedwa zake, iye anazindikiritsa mwamuna wopatsidwa mlanduyo: “Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.” (1 Akorinto 15:22) Sing’anga wotchedwa Luka, m’mutu wachitatu wa Uthenga wake, anazindikiritsa mzera wa mbadwo wa Yesu kubwerera kwa Adamu, amene, asanachotsedwe mu Edeni, anamva uthenga wa Yehova wa chiyembekezo.​—Luka 3:23-38.

7. Kodi ndi chinthu cholimbikitsa chotani chimene Mulungu anachita pamene Adamu anali adakali wamoyo?

7 Mwachibadwa, inu mungafune kudziwa za mkati mwa uthengawo. Koma musanauŵerenge, dziŵani chenicheni chakuti kwa nthaŵi yaitali Yehova wakhala wopereka chiyembekezo. Pachiyambi Adamu anali mwana wa mwamuna wa Mulungu wa dziko lapansi, ndipo Mulungu anamulola iye kubala ana. Ngati munawoneratu masomphenya a mkhalidwe wina, inu mungafune kulimbikitsa kapena kupereka chiyembekezo kwa mbadwa zanu. Mulungu anachita chinachake chofananako. Pambuyo pa kumva kwa Adamu mawu a Mulungu a kulengezedwa kwa kukanidwa kwa iye mwaumwini, iye anamva mawu a chiyembekezo kaamba ka mbadwa zake.

8. Kodi ndimotani mmene Genesis 3:15 amaperekera maziko kaamba ka chiyembekezo?

8 Kodi ndi ati omwe anali mawu amenewo kuchokera kwa Mulungu wopatsa chiyembekezo ameneyu? Kwa “njoka” imene inaphatikizidwa mu uchimo wa Adamu, Mulungu anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake [mbadwa]. Ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalikira chitende chake.” (Genesis 3:14, 15) Inu mungadabwe mmene mawu amenewo anganenedwere kukhala odzutsa chiyembekezo. Choyamba, tikuphunzira kuti “chinjoka” chikafunikira kulaliridwa mutu wake.

9. Kodi ndani anali “chinjoka” cholozeredwako pa Genesis 3:14, 15?

9 Mu Chivumbulutso 12:9 chalembedwa kuti: “Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Inde, “chinjoka” chomwe chinaphatikizidwa mu Edeni sichinali china choposa cholengedwa chauzimu choipa chodziŵika monga Satana Mdyerekezi. Osati kokha kuti chinjoka chophiphiritsira chimenecho chinadzakhala ndi angelo m’mwamba, icho chakhalanso ndi “mbewu” pansi pano pa dziko lapansi, “mbewu” imene m’nthaŵi yoyenera idzaphwanyidwa kuchotsedwa pa kukhalapo pamodzi ndi iye.

10. Kodi ndimotani mmene Yesu anatsimikizirira chizindikiritso cha “njoka”?

10 Kutsimikizira kuzindikiritsa kumeneku kwa Mdyerekezi monga “chinjoka” chomwe chinali kumbuyo kwa kugwa kwa makolo athu oyambirira, Yesu Kristu ananena kwa atsogoleri achipembedzo Achiyuda mu zana loyamba kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iye anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi. . . . Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Yesu anatchanso otsutsa achipembedzo amenewo monga “akubadwa a njoka.”​—Mateyu 12:34; 23:33.

Chiyembekezo Chinakhalabe Chamoyo

11. Kodi ndi chifukwa chowonjezereka chotani kaamba ka chiyembekezo chimene Genesis 3:15 anapereka?

11 Chiyembekezo cha umulungu cha kulalira mutu wa chinjoka chophiphiritsira m’chenicheni chinaika chiyembekezo chopumitsa mtima pamaso pa banja lonse la munthu lomwe linayenera kudzakhalapo. Tingawone chifukwa chake mwakusanthula mbali zina za Genesis 3:15. “Mbewu” ya mkazi yatchulidwa. Chizindikiritso cha “mbewu” imeneyo chinali chophimbidwa m’chinsinsi kwa nthaŵi yaitali. Koma chinali chowonekera kuti Yehova Mulungu akaika “mbewu” yomwe pa nthaŵiyo inali yosazindikiridwa pa udani ndi chinjoka chophiphiritsira ndi “mbewu” zake zokana Mulungu. Chipambano chinalonjezedwa, inde, kutsimikiziridwa, kaamba ka “mbewu” ya “mkazi”! Chipambano chake chinaikidwa monga chiyembekezo pamaso pa mtundu wa anthu. Chotero ziwalo za banja la munthu zikayembekezera kudza kwa “mbewu” ya “mkaziyo.”

12. Mkupita kwa nthaŵi, nchiyani chowonjezereka chomwe chinavumbulidwa ponena za “mbewu” ya “mkazi”?

12 Mkati mwa mazana, Mulungu anavumbulutsa kuti “mbewu” imeneyi inali mwana wake wobadwa yekha amene anatumizidwa ku dziko lapansi kudzakhala Mesiya ndi kupereka moyo wake monga nsembe ya dipo. (Genesis 22:17, 18; Agalatiya 3:16; 1 Yohane 2:2; Chivumbulutso 5:9, 10) Kaamba ka chifukwa chimenechi chiyembekezo cha Mboni za Yehova sichiyedzamira pa Mitundu Yogwirizana. Icho chiri pa Yesu Kristu wamoyo, Wolankhulira Wamkulu wa Yehova Mulungu. Tingakhale ndi chidaliro kuti Kristu ali wamoyo, popeza kuti anawuka kuchokera kwa akufa ndi kukhazikitsidwa ku dzanja lamanja la Yehova kumwamba. Monga mmene Paulo akunenera kuti: “Ngati tiyembekezera Kristu m’moyo uno wokha, [moyo umene ukuphatikizapo zaka zathu za zana la 20] tiri ife aumphaŵi oposa anthu onse. Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula cha iwo akugona.” (1 Akorinto 15:19, 20) Monga momwe chakhazikitsidwira kaŵirikaŵiri mwa Malemba m’masamba a magazini ino, Yesu Kristu waikidwa lerolino monga Mfumu ya kumwamba.​—Chivumbulutso 11:15.

13, 14. Kodi ndi kuti kumene Mboni za Yehova zimaika chiyembekezo chawo, ndipo nchiyani chimene izo zimachita ponena za icho?

13 Ndi zowona kuti, Yesu Kristu sanalowe m’malo Yehova monga chiyembekezo cha mtundu wa anthu. Masalmo 37:34 amagwirabe ntchito: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.” Chiri choyenererabe kupitiriza kuyembekeza mwa Yehova ndi kulimbikitsa anthu onse kuleka kuyembekeza magulu opangidwa ndi anthu.

14 M’chigwirizano ndi nsonga imeneyi, Mboni za Yehova ziri zokangalika m’maiko 208, kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu. Iwo sangaletsedwe kuchita tero. Magulu a ndale zadziko, othandizidwa ndi kuchirikizidwa ndi magulu achipembedzo, alibe kuyenera kwa umulungu m’kuyesera kuwaletsa iwo. Tingapitirizebe kukhala mboni za Yehova ndi kuyembekeza mwa iye, monga mmene anachitira Davide wa ku Betelehemu, amene analemba kuti:

15. Kodi ndi mtundu wotani wa chiyembekezo umene Mfumu Davide anali nawo mwa Yehova?

15 “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa ku busa lamsipu; anditsogolera ku madzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga: Anditsogolera m’mabande a chilungamo chifukwa cha dzina lake. Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine. Mundiyalikira gome pamaso panga m’kuwona kwa adani anga: Mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka. Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga: Ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.”​—Masalmo 23, American Standard Version.

16. Kodi nchifukwa ninji chinganenedwe kuti Yesu anali ndi kawonedwe kofanana ndi kamene Davide anali nako?

16 Mfumu Davide anali mbusa wauzimu wa Yehova kaamba ka mafuko a Israyeli wakale, ndipo anatsegula njira kaamba ka Yerusalemu kukhala mzinda waukulu wa dziko, kumene mwana wake Solomo analamulira kwa zaka 40. Ndi chifukwa chabwino, Yesu Kristu ananenedwa kukhala “mwana wa Davide.” (Luka 1:31; 18:39; 20:41) Ngati Davide anayembekeza mwa Yehova Mulungu, mbadwa yake ya pa dziko lapansi Yesu Kristu akachita chofananacho. Ndipo anatero.

17. Kodi ndi umboni wotani umene ulipo wakuti Yesu anayembekeza mwa Yehova?

17 Monga umboni mbadwa yodziŵika kwambiri ya Davide ya pa dziko lapansi imeneyo, Yesu Kristu, anatsatira uphungu wa Masalmo 37:34 pamene ankatsirizika pa mtengo wozunzirapo, Yesu ananena kuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” (Luka 23:46) Iye ankagwira mawu ndi kukwaniritsa mawu a Davide pa Masalmo 31:5, operekedwa kwa Mulungu: “Ndipereka mzimu wanga m’dzanja lanu.” Chiyembekezo cha Yesu sichinagwiritsidwe mwala, ndi mmenenso chinaliri chija cha Mfumu Davide. Yesu anawukitsidwa kuchokera kwa akufa pa tsiku la chitatu. Masiku makumi anayi pambuyo pake iye anabwerera kwa atate wake wakumwamba. Pamapeto a nthaŵi za akunja mu 1914, Yehova anakweza Mwana wake kukhala Wolamulira wa dziko lapansi.

Nthaŵi ya Chiyembekezo Tsopano

18. Nchifukwa ninji lerolino iri nthaŵi yoyenera kaamba ka chiyembekezo?

18 Lerolino, pamene chaka cha 6,014 A.M. (m’Chaka cha Dziko) chikutenga banja la munthu kupita nalo mtsogolo, kodi ndi chiyembekezo chotani chomwe chingatengedwe kaamba ka banja la munthu? Funso limenelo tsopano liri loyenera kwenikweni popeza kuti tiri chifupifupi zaka 1,900 m’nyengo ya pambuyo pa Baibulo. Chakhala nthaŵi yaitali chiyambire pamene Davide analemba Masalmo 37:34.

19. Kodi Yehova anachitanji kaamba ka Yesu, kutipatsa ife chiyembekezo chotani?

19 Yehova Mulungu, Mulungu Wamphamvuyonse amene anawukitsa Yesu kuchokera kwa akufa, ali ndi thayo lokulira kaamba ka iye kuposa lija lomwe linali ndi anthu omwe anali ndi kawonekedwe kokhala ndi polekezera. Mwa kuukitsa ndi kukweza Mwana wake wobadwa yekha ku dzanja lake lamanja m’mwamba, Yehova Mulungu wawonjezera chifukwa kaamba ka ife cha kuyang’ana kwa iye ndi chiyembekezo chosakhoza kulephera, chiyembekezo chathu chotsirizira. Icho chingatanthauze moyo wosatha m’chimwemwe, monga mmene mlembi wouziridwa Paulo akunenera kuti: “Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo chimenecho.”​—Aroma 8:24.

20. Nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova adakali “Mulungu wa chiyembekezo”?

20 Mtumwiyo akupitiriza kunena kuti: “Koma chiyembekezo chimene chiwoneka sichiri chiyembekezo ayi; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichirindirira ndi chipiriro.” (Aroma 8:24, 25) Ndipo chotero chiyembekezo choyambirira chimenecho chidakalipobe, inde, chikuyandikira kukwaniritsidwa kwa ulemerero pa mtundu wa anthu. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:4, 5) Kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho chakuti chiri chiyembekezo kaamba ka mtundu wonse wa anthu, icho chiyenera kudziŵikitsidwa kwa onse. Iri liri lingaliro la “Mulungu wathu wa chiyembekezo.”

21, 22. Kodi nchiyani chimene tingayembekeze mitundu kuchita mtsogolo mofupikira?

21 Tsopano kwa nthaŵi zonse iri nthaŵi yake kaamba ka lingaliro limeneli kuti lichitidwe. Ngakhale m’nyengo yathu pamene mitundu ina ya UN yafikira kudziŵa kwa usayansi kwa maziko enieni a nkhani yonse, atsogoleri a maboma amenewa samakumva kufunika kwa kusiira kuthetsa kwa mavuto ku luntha lapamwamba kwambiri.​—Yerekezani ndi Genesis 11:6.

22 Mosiyana ndi kale lonse, chipembedzo chofala chiri ku mbali yochinjiriza, ndi msana wake woyedzamira ku khoma. Chisonkhezero chake chachinyengo chifunikira kuchotsedwa. Baibulo limasonyeza kuti mbali zolamulira zidzasonyeza ukulu wawo ndi kudzilekanitsa iwo eni kuchoka ku zipembedzo zodyera masuku pamutu zomwe kwa nthaŵi yaitali zakhala zikuyesa kuyamwa dongosolo la kachitidwe ka zinthu laudziko kaamba ka zonse zimene iwo angakhoze kupeza. Chotero, chiri chosadabwitsa, kuti mbali za ndale zadziko zidzatenga kaimidweka. Kuchoka kwawo kopanda kuvulazidwa ndi kumenyera kumeneku pa chipembedzo kudzasonyeza, kuchokera m’lingaliro la kapenyedwe kawo, kuti kulibe Mulungu amene ayenera kulambiridwa ndi kutumikiridwa. Kusonyeza kwa ulosi kuli kwakuti iwo kenaka adzatembenuka kulimbana ndi Mboni za Yehova, zomwe zidzakhalapo. Iwo adzayang’ana kaamba ka chipambano chosavuta pa Mboni za Yehova monga chotsirizira cha ndawala yawo ya kukana Mulungu.​—Chivumbulutso 17:12-17; Ezekieli 38:10-23.

23, 24. Kodi Yehova adzayankha motani ku kuukira kwa mitundu pa anthu ake?

23 Komabe, iwo potsirizira pake adzafika pa kudziwa kugonjetsa komvetsa manyazi komwe kuyenera kudza kwa omwe amafuna kulowa m’kulimbana ndi Yehova Wamakamu, yemwe sanagonjetsedwepo mu nkhondo. Chimenecho chidzachipangitsa kuwonekera mosavuta kuti akhala akutumikira zitsiriziro za mdani wamkulu wa Mulungu yekha wowona, wotchedwa “chinjoka” Satana, “mulungu wa dongosolo iri la zinthu.”​—2 Akorinto 4:4.

24 Ndi kunyazitsa chotani nanga kumene ichi chidzatanthauza kwa iwo! Chimene iwo anayembekezera kusonyeza chidzatsimikizira kukhala ukulu wa kudzimva, kuputa Mulungu weniweni wa kumwamba ndi dziko lapansi ku ukali wolungama. Kuti achepetse mtundu wa anthu iye anakhoza kunena kuti: “‘Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga,’ ati Yehova. ‘Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzyala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.’”​—Yesaya 55:8-11.

25. Nchifukwa ninji, pamenepo, ife tiriri ndi chifukwa chabwino tsopano cha kuyang’anira kwa Yehova monga “Mulungu wathu wa chiyembekezo”?

25 Mlengi ameneyu wa munthu waika mitima ya anthu kuzindikira kwa changu, konga ngati kumene iye ali nako. “Pakuti atero Yehova wa makamu: ‘Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso [langa. NW]’” (Zekariya 2:8) Chotero, pamenepo, Mboni za Yehova zidzafunikira kuyembekeza mwa Yehova. Iye adzakwaniritsa chiyembekezo chimenecho ku kukongoletsa kopambana pa kulamulira kwake kwa thambo lonse. Iye adzatsimikizira kuposa pa kutsutsana kulikonse kuti ali wamkulukulu, wamphamvuyonse, Mulungu wosatha, amene wakhalira ku ziyembekezo zapamwamba za zolengedwa zake m’miyamba monse ndi m’dziko lapansi. Aleluya!​—Masalmo 150:6.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Nchifukwa ninji chiyembekezo cha mitundu chiri chonyenga?

◻ Ndimotani mmene Mulungu anaperekera maziko kaamba ka chiyembekezo mu Genesis 3:15?

◻ Kodi ndi ati omwe anali malo a Yesu kulinga ku Masalmo 37:34?

◻ Nchifukwa ninji ife tsopano tiri ndi chifukwa kaamba ka chiyembekezo?

[Chithunzi patsamba 10]

Monga mmene nkhosa zimatsa-tirira mbusa wawo, chotero Davide anayang’ana ndi kuyembekeza mwa Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Pafupi ndi Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena