Kodi Amalankhuladi Ndi Akufa?
MAGULU ampira mu Brazil nthaŵi zina amafuna thandizo kupyolera mwa olankhula ndi mizimu. Nchifukwa ninji? Ndi cholinga chofuna kupeza chilangizo chifukwa cha kuwopera kuti gulu lolimbana nalo lingapambane. Molingana ndi nyuzipepala imodzi, “mwaŵi wa kulankhula mwachindunji ndi mphamvu zoposa za munthu m’kufunafuna mayankho ku mitundu yonse ya mavuto umapereka chisonkhezero champhamvu pa mamiliyoni a anthu.” M’maiko ena, a ndale zadziko apamwamba, a zaluso, ndi anthu a bizinesi amalankhula mokhazikika ndi mizimu. M’kuyesayesa kufuna kuchiritsa kapena kuthetsa vuto la ndalama, ena amayesera kulankhula ndi akufa, omwe amakhulupiriridwa kuti amasangalatsidwa kwambiri.
Koma kodi chiri choyenera kuyesera kulankhula ndi akufa? Kodi chiridi chothekera kuchita tero? Ndipo kodi pali ngozi zina zirizonse zolowetsedwamo? Mungadabwitsidwe kuwona chimene Baibulo limanena.
Nchiyani Chinachitika mu Nkhani ya Sauli?
Lingalirani chokumana nacho cha moyo weniweni cholembedwa m’Baibulo: Akuwopa adani a Chifilisti, Mfumu Sauli wa Israyeli wakale anafuna wobwebweta mu Endori. Iye anafunsa iye kulankhula ndi mneneri Samueli wakufa. Pakumva kalongosoledwe kake ka mwamuna wachikulire wovala malaya odula manja, Sauli analingalira mzukwa umenewu kukhala Samueli. Ndipo nchiyani chimene chinali uthengawo? Aisrayeli adzaperekedwa m’dzanja la Afilisti, ndipo tsiku lotsatira Sauli ndi ana ake akakhala ndi “Samueli,” kusonyeza kuti iwonso akafa pamene akumenyana ndi Afilisti. (1 Samueli 28:4-19) Kodi chimenecho ndi chimene chinachitika?
Osati kwenikweni. Sauli anavulazidwa koposa m’nkhondo ndi Afilisti, koma anachita kudzipha. (1 Samueli 31:1-4) Ndipo mosiyana ndi kulosera kwakuti ana onse a Sauli akafa limodzi naye, mwana wake wamwamuna Isiboseti anapulumuka.
Koma kodi chinali choyenera kufunsa akufa poyambirira paja? Ayi, icho sichinali. Malemba amatiuza ife kuti: “Sauli anafa chifukwa cha kulakwa kwake . . . ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta.” (1 Mbiri 10:13) Kodi tingaphunzire chinachake kuchokera ku ichi? Inde. Sauli anafa chifukwa cha kufunsira wobwebweta kufunsira akufa. Nchifukwa ninji? Chifukwa mwakuchita ichi, iye sanamvere lamulo lomvekera la Mulungu: “Asapezeke mwa inu . . . wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Nchifukwa ninji kufunsira akufa chiri chinthu chonyansa kwa Mulungu? Tisanayankhe funso limenelo, tingafunse kuti:
Kodi Chiridi Chotheka?
Ngati wina aliyense akafunikira kulankhula ndi akufa, womwalirayo m’chenicheni ayenera kukhala wamoyo. Iwo ayenera kukhala ndi moyo wosafa. Komabe Baibulo limanena kuti: “Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake, munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Chotero, munthu iyemwini ali moyo. Iye alibe moyo wosakhoza kufa womwe umakhalabe ndi moyo pambuyo pa imfa yathupi. M’chenicheni, Malemba amanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4) M’kuwonjezerapo, Mawu a Mulungu amanena kuti: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . Pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingalira ngakhale kudziŵa ngakhale nzeru [ku Sheol, NW] ulikupitako,” manda wamba a mtundu wa anthu.—Mlaliki 9:5, 10.
Kutalitali ndi kusangalatsidwa, chotero, akufa sadziŵa kanthu. Chotero sichiri chotheka kulankhula ndi iwo. Kuchita m’chigwirizano ndi lamulo la Mulungu lotsutsa kufunsira akufa chotero kumatichinjiriza ife ku kunyengedwa. Komabe, mauthenga ochokera ku mabwalo a mizimu ali othekera, monga mmene chokumana nacho cha Mfumu Sauli chikusonyezera.
Koma Nchiyani Chimene Chiri Magwero?
Popeza chinthu chimodzi, kunyenga kuli kofala pakati pa awo amene amadzinenera kukhala akulankhulana ndi akufa. The World Book Encyclopedia imatidziŵitsa ife kuti: “Chasonyezedwa kuti obwebweta amanamiza anthu pa misonkhano ya mizimu kuwapangitsa iwo kukhulupirira kuti mizimu ingalankhule ndi amoyo. Asayansi akupereka kalongosoledwe kaamba ka zimene zimachitika pa misonkhano ya mizimu yoteroyo. Mwachitsanzo, obwebweta ena ali olankhulira mwa ena. Ena amagwiritsira ntchito owathandiza ndi mitundu yosiyanasiyana ya ziwiya zonamizira. Ena amagwiritsira ntchito matsenga. Anthu ambiri amene amapezekapo pa misonkhano ya mizimu ali ndi chikhumbo champhamvu cha kulankhula ndi wakufa wokondedwa. Chikhumbo chimenechi chingawapangitse iwo kukhulupirira kuti uthenga uliwonse woperekedwa ndi obwebweta umachokera ku dziko la mizimu.”
Koma kodi tiyenera kulingalira kokha m’nkhani zoterozo? Ayi, popeza kumamatira ku lamulo la Mulungu lotsutsa kufunsira akufa kumatichinjirizanso ife m’njira yowonekera koposa. Mauthenga amachokeradi ku mabwalo a mizimu, koma magwero awo ali zolengedwa zamphamvu zofunafuna kusokeretsa mtundu wa anthu. Baibulo limawazindikiritsa iwo monga “mphamvu zoipa za mizimu”—Satana Mdyerekezi ndi angelo osamvera odziŵika monga ziwanda. (Aefeso 6:12) Pamene Mfumu Sauli anachezera wobwebweta mu Endori, chinali chiwanda chimene chinawoneka monga mneneri wakufa Samueli.
Monga mmene chachitiridwira chitsanzo m’nkhani ya Sauli, ziwanda ziribe china chirichonse chopindulitsa chopereka, ndipo thandizo lawo loyerekezedwalo liri la kanthaŵi kochepa. Monga wolamulira wawo, Mdyerekezi, izo ziri zabodza. (Marko 3:22; Yohane 8:44) M’chigwirizano ndi ichi, wofufuza mphamvu ya malingaliro wa ku Britain malemu Sir Arthur Conan Doyle analemba kuti: “Ife, mosasangalala, tiyenera kuchita ndi kunyenga kotheratu kumbali ya zoipa kapena mphamvu zosalamulirika. Aliyense yemwe wafufuza m’nkhaniyi, ndikhulupirira kuti, wakumana ndi zitsanzo za kunyenga kwadala kumene mwakamodzikamodzi kumasakanizidwa ndi zabwino ndi kukambitsirana kwenikweni.” (The New Revelation, tsamba 72) Ndithudi, simukufuna kuti munyengedwe, kodi sitero?
Tsopano, lingalirani ichi: Mbiri yakale imatiuza ife ponena za malonda a ukapolo ndi kuvutitsa kogwirizana nako. Kodi winawake mofunitsitsa angavomereze zovuta zoterozo ndi kunyozedwa? Ndithudi ayi. Chotero nchifukwa ninji tiyenera kudzilola ife eni kuikidwa mu ukapolo ndi mizimu yoipa? Iyo simanama kokha komanso imabera anthu ufulu wawo ndipo ingawatsogolere ku chiwawa ndi kupha. Mwachitsanzo, José wa zaka zakubadwa 29 wa ku Pernambuco, Brazil, ananena kuti ‘mzimu unalowa mwa iye, kumukakamiza iye kupha mwana wake wamkazi wa chaka chimodzi.’ Inde, kulowetsedwa m’mizimu yoipa kungatsogolere ku ukapolo woterowo. Chabwino, chotero, mofanana ndi mmene akapolo ovutitsidwa maganizo a nthaŵi yakale anafunafuna ufulu, choteronso awo amene ali mu ukapolo ku ziwanda lerolino ayenera kufuna kumasulidwa. Njira imodzi ya kupezera ufulu umenewu iri kuleka kufunsa obwebweta ndi kuyesera kulankhula ndi akufa. Kaamba ka chimenecho, kodi pali . . .
Chifuno Chirichonse cha Kulankhula ndi Akufa?
Ayi, popeza ife sitiri opanda thandizo. Mofanana ndi ana amene amakhulupirira atate wawo, ife mwaufulu tingafunse kaamba ka thandizo lochokera kwa Atate wathu wa kumwamba, yemwe ali wosangalatsidwa kuthandiza owona mtima. (Luka 11:9-13) Mneneri wa Mulungu Yesaya analemba kuti: “Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe: ‘Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza,’ kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa? Kuchilamulo ndi ku umboni!”—Yesaya 8:19, 20.
Inde, tiri ndi maziko olimba kaamba ka chidaliro mwa Yehova Mulungu ngati tichita chifuniro chake ndi kukana kukhala ndi kugwirizana kulikonse ndi mizimu yoipa. Wophunzira Wachikristu Yakobo analemba kuti: “Dzigonjetsereni inu eni kwa Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.” (Yakobo 4:7, NW) Pambuyo pa kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, munthu amene anakhulupirira mizimu kwa zaka 28 ananena kuti: “Osawopa chimene Mdyerekezi angachite kwa awo amene amasiya machitachita a mizimu, koma, m’malomwake, khulupirirani Yehova Mulungu.”
Kudzaza malingaliro ndi chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu ndi kugwirira ntchito pa icho kudzatitheketsa ife “kuvala zida zonse [zauzimu] za Mulungu” kuti tikhoze “kuchirimika pokana machenjero a Mdyerekezi” ndipo kuti tisaikidwe ukapolo ndi mphamvu zoipa za mizimu. (Aefeso 6:11) Kuwonjezerapo, kupemphera kwa Yehova mokhazikika kudzapereka chinjirizo lamphamvu motsutsana ndi kuvutitsidwa ndi ziwanda.—Miyambo 18:10.
Chiri chotonthoza chotani nanga kudziŵa ponena za chowonadi cha mkhalidwe wa akufa! Kufa kuli monga tulo. (Yohane 11:11) Ndipo Yesu Kristu anatsimikizira kuti padzakhala chiukiriro cha akufa.—Yohane 5:28, 29.
Limodzi ndi mkazi wake ndi ana, mwamuna mmodzi amene anali wokhulupirira mizimu anaphunzira kuchokera m’Malemba kuti palibe wina aliyense afunikira kuyesera kulankhula ndi akufa kapena winawake wodzinenera kukhala iwo. Mofanana ndi banja iri ndi ena ambiri kuzungulira padziko, inu nanunso mungasangalale ndi ufulu wauzimu. (Yohane 8:32) Phunzirani chowonadi chonena za akufa ndi chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu. Kenaka mungayang’ane kutsogolo ku dongosolo latsopano la Yehova, kumene mungalankhule ndi oukitsidwa okondedwa ndi kusangalala ndi moyo wosatha pansi pa mikhalidwe ya mtendere.—Yesaya 25:8.
[Chithunzi patsamba 4]
Kodi ndani kwenikweni amene analankhula pamene Mfumu Sauli anafunsira kaamba ka uthenga wochokera kwa mneneri wakufa Samueli?