Kodi Ndani Analemba Baibulo?
“BAIBULO liri lodzaza ndi kutsutsana,” amanena tero osuliza. “Pambali pa icho, ilo liri ndi nthanthi za anthu. Chotero, ndimotani mmene wina aliyense angalandirire Baibulo monga chitsogozo chodalirika kaamba ka moyo?”
Kodi mumagawana ndi kawonedwe ka osuliza kakuti Baibulo siriri china chirichonse koposa bukhu lolongosola kulingalira kolakwa kwa anthu? Atsogoleri ena achipembedzo amatero. Malemu Karl Barth katswiri wa za maphunziro achipembedzo wa chiSwiss Protestant analemba m’bukhu lake Kirchliche Dogmatik (Ziphunzitso za Tchalitchi): “Aneneri ndi atumwi anali okhoza kupanga zolakwa m’kulankhula ndi kulemba.” Zowona, kusiyana m’katchulidwe ka mawu kungapezeke m’nkhani za chochitika chokwaniritsidwa ndi olemba Baibulo oposa mmodzi. Ndipo malingaliro angapezeke, amene pamwamba, amawonekera kukhala osiyana kotheratu ndi awo opezeka kwinakwake m’Baibulo. Koma kodi izi ziri kwenikwenidi kutsutsana? Kodi Baibulo liri kokha chotulukapo cha munthu? Ndithudi, kodi ndani analemba Baibulo?
Yankho liri lapafupi: “Anthu analankhula kuchokera kwa Mulungu.” Koma kodi ndimotani mmene iwo anadziŵira zimene iwo akayenera kulankhula ndi kulemba? Munthu wongogwidwa mawu kumeneyo, mtumwi Simoni Petro, akupitiriza kulongosola kuti iwo analankhula “monga mmene anauziridwa ndi mzimu woyera.”—2 Petro 1:21.
M’chenicheni, nthaŵi ndi nthaŵi Baibulo limagogomezera kuti liri “mawu a Mulungu.” Mu maversi 176 a Masalmo 119 okha nsongayi imatchulidwa nthaŵi 176! Chimene chimachipanga icho kukhala chowonekera chiri chakuti kaŵirikaŵiri olemba amasangalatsidwa kudziŵikitsa kuti iwo alemba ntchito yakuti yakuti. Koma amuna amene analemba Baibulo sanatero. Ulemerero wonse unayenera kupita kwa Mulungu. Ilo linali bukhu lake, osati lawo.—1 Atesalonika 2:13 2 Samueli; 23:2.
“Anauziridwa ndi Mzimu Woyera”—Motani?
Ndimotani mmene amuna amenewa “anauziridwa ndi mzimu woyera”? Kalata ya kwa Mkristu wa m’zana loyamba Timoteo ikupereka yankho: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu.” Mawu akuti “Adaliuzira Mulungu” amatembenuza liwu loyambirira la Baibulo la Chigriki lakuti the·oʹpneu·stos, lomwe m’lingaliro lenileni, limatanthauza kuti “anapumidwa ndi Mulungu.” Mulungu anagwiritsira ntchito mphamvu yake yogwira ntchito yosawoneka—mzimu wake woyera—“kupumira” malingaliro ake m’malingaliro a olembawo. Chotero, Yehova Mulungu ali magwero ndi wotulutsa wa Baibulo. Malingaliro ake anatsogoza kulembedwako mofanana kwambiri ndi mmene mwamuna wa bizinesi amagwiritsira ntchito mlembi kulemba kalata kaamba ka iye.—2 Timoteo 3:16.
Ndiponso, mbali iyi ya “kupumiridwa ndi Mulungu” imapeza kufanana nako mu kalongosoledwe ka Baibulo kakuti “kuuziridwa ndi mzimu woyera.” Motani? “Kuuziridwa” kumagwiritsiridwa ntchito mu Chigriki kulozera ku sitima za pa madzi zomwe zimakokedwera ku njira ina ndi mphepo. (Yerekezani ndi Machitidwe 27:15, 17.) Chotero, monga mmene mphepo imawomba ndi kuyendetsa sitima ya pa madzi yomayenda, momwemonso olemba Baibulo analingalira, kulankhula, ndi kulemba pansi pa chisonkhezero cha Mulungu, pouziridwa ndi mzimu woyera pamene iye “anapumira” pa iwo.
Amuna Ogwiritsiridwa Ntchito ndi Mulungu Kulemba
Tiri kokha ndi tsatanetsatane wochepa wa mbiri yaumwini yonena za alembi a Baibulo. M’malo modzilingalira iwo eni kukhala ofunika kwambiri, iwo nthaŵi zonse anakalamira kulemekeza Mulungu mwakudzisunga iwo eni kumbuyo kwa zochitika. Tikudziŵa, ngakhale kuli tero, kuti iwo anaphatikizapo nduna za boma, oŵeruza, aneneri, mafumu, abusa, alimi, ndi asodzi—amuna 40 a iwo. Chotero, Baibulo, ngakhale kuti ndi uthenga wochokera kwa Mulungu, liri ndi kusiyanasiyana, kwabwino, ndi chisonkhezero cha kukhudza kwa munthu.
Ambiri a alembi a Baibulo sanadziwane wina ndi mnzake. Iwo anakhala ndi moyo ngakhale mazana ambiri pakati pa wina ndi mnzake ndipo anali osiyana kotheratu m’zokonda ndi zokumana nazo, limodzinso ndi chiyambi cha mayanjano ndi maphunziro. Komabe, kaya iwo anali achikulire kapena achichepere, kulemba kwawo kumasonyeza kugwirizana kotheratu. Ku utali wa nyengo yoposa chifupifupi zaka 1,600, iwo analemba kufikira Baibulo pomalizira linatsirizidwa. Pambuyo pa kusanthula kosamalitsa, mudzapeza kuti ndemanga za Baibulo zimawunikira chigwirizano chodziŵikiratu. Baibulo chotero limafuula malingaliro a mkonzi mmodzi, ngakhale kuli kwakuti alembi ambiri anagwiritsidwa ntchito.
Kodi ichi sichiyenera kutisonkhezera ife “kumvetsera koposa kwa masiku onse” ku bukhu lachilendo limeneli, Baibulo? Kodi sitiyenera kukhala okhoza kufikira mapeto amodzimodziwo amene Petro anachita, amene analemba kuti: “Zonse za izi zimangotsimikizira kwa ife uthenga wa aneneri, ku umene inu mudzachita bwino kupezekako, chifukwa uli monga nyali yoyaka m’malo a mdima”?—Ahebri 2:1; 2 Petro 1:19, The New English Bible.
Koma tsopano, bwanji ponena za kunena kwakuti Baibulo limadzitsutsa lokha? Kodi limatero? Kodi mumayankha motani?
[Bokosi patsamba 4]
“Liri bukhu lalikulu lotani nanga! Chachilendo kuposa za mkati mwake kwa ine chiri mtundu wake wa kalongosoledwe, kumene mawu amakhala m’chenicheni chotulukapo cha chilengedwe chonga mtengo, chonga maluŵa, chonga nyanja, chonga nyenyezi, chonga munthu iyemwini. Limaphuka, kuyenda, kuwala, kuseka, wina sadziŵa ndimotani, wina sadziŵa nchifukwa ninji, wina amapeza chirichonse kukhala chachilengedwe kotheratu. Ilo ndithudi liri Mawu a Mulungu, mosiyana ndi mabukhu ena omwe amangochitira umboni kokha nzeru za anthu.”—Ndemanga yonena za Baibulo ya wolemba ndakatulo ndi nyuzipepala wa mu zana la 19 wa ku German Heinrich Heine.
[Chithunzi patsamba 4]
Monga mmene mphepo imayendetsera sitima za pamadzi zomayenda, olemba Baibulo ‘anauziridwa ndi mzimu woyera wa Mulungu’