Pangani Yehova Kukhala Chikhulupiriro Chanu
“Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; . . . Udzikondweretsenso mwa Yehova.”—MASALMO 37:3, 4.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa awo omwe sanaike chikhulupiriro mwa Yehova m’zana loyamba, ndi kwa awo amene anatero? (b) Ndi mafunso otani amene angafunsidwe ponena za chipembedzo m’nthaŵi yathu?
M’ZANA loyamba la Nyengo yathu Yachisawawa, atsogoleri achipembedzo Achiyuda anadzinenera kukhala akulambira Mulungu. Koma iwo sanakhulupirire mwa iye. Anaphwanya malamulo ake ndi kuzunza oimira ake. (Mateyu 15:3; Yohane 15:20) Monga chotulukapo chake, ‘nyumba yawo inasiidwa’ ndi Yehova. (Mateyu 23:38) Mu 70 C.E., gulu lankhondo la Roma linasakaza Yerusalemu ndi kachisi wake, ndi kutaika kokulira kwa moyo wa atsogoleri achipembedzo ndi atsatiri awo. Koma awo amene anakhulupirira mwa Yehova anachinjirizidwa, popeza kuti iwo analabadira machenjezo a olankhulira ake ndipo anathaŵira ku malo opulumukirako.—Mateyu 24:15-22; Luka 21:20-24.
2 M’masiku ano otsiriza a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, kodi zipembedzo zadziko iri zikukhulupirira mwa Mulungu wowona, Yehova? Kodi iwo akumvera malamulo ake ndi kuchita chifuniro chake, kapena kodi iwo akutsanzira atsogoleri achipembedzo a m’zana loyamba amene Mulungu anawasiya? Ndi chiti cha zipembedzo zamakono chimene chingayembekezere kutetezeredwa ndi Yehova chifukwa iwo “amakhulupirira mwa Yehova ndi kuchita chokoma”?—Masalmo 37:3.
Kodi Chikondi Chaubale Chiri Kuti?
3. Nchifukwa ninji zoyesayesa za chipembedzo za kubweretsa mtendere zalephera?
3 Osati kale kwambiri, Papa John Paul II anachenjeza kuti “mtundu wonse wa anthu ukuyang’anizana ndi ziwopsyezo za kupulumuka kwake.” Iye anagogomezera kuti “ziwopsyezo zimenezo zingakhoze kuchinjirizidwa bwino koposa ndi zoyesayesa zogwirizana pakati pa magulu akulu azipembedzo.” Chiri chifuno cha Mulungu, iye anatero, kuti atsogoleri azipembedzo “agwire ntchito pamodzi” kaamba ka “mtendere ndi kugwirizana.” Komabe, ngati chimenecho chiri chifuniro cha Mulungu, chotero nchifukwa ninji Mulungu sanadalitse zaka mazana a zoyesayesa m’chitsogozochi? Iye sanachite tero chifukwa zipembedzo zimenezo sizinakhulupirire m’njira ya Mulungu ya kubweretsa mtendere mwa njira ya Ufumu wake wakumwamba. (Mateyu 6:9, 10) M’malomwake, iwo achirikiza ndale zadziko ndi nkhondo za mitundu. Monga chotulukapo chake, m’nthaŵi ya nkhondo, anthu achipembedzo a mtundu umodzi apha anthu achipembedzo a mtundu wina, ngakhale kupha anthu achipembedzo chawo chenicheni. Akatolika apha akatolika, aProtestanti apha aProtestanti, ndipo zipembedzo zina zachita zofananazo. Koma kodi abale owona auzimu amaphana wina ndi mnzake pamene akudzinenera kuti akutumikira Mulungu?
4. Kodi nchiyani chimene Yesu ananena kuti chinali muyezo wa chipembedzo chowona, ndipo nchifukwa ninji chinali “lamulo latsopano”?
4 Yesu anakhazikitsa muyezo kaamba ka chipembedzo chowona pamene ananena kwa otsatira ake kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Chotero awo amene amachita chipembedzo chowona ayenera kukondana wina ndi mnzake. Iri linali “lamulo latsopano” m’chakuti Yesu ananena kuti: “Monga ndakonda inu, . . . inunso mukondane wina ndi mnzake.” Iye anafunitsitsa kuika moyo wake pansi kaamba ka atsatiri ake. Iwo ayenera kukhala ofunitsitsa kuchita chofananacho—ayi, osati kutenga moyo wa mkhulupiriri mnzawo, koma kuika pansi moyo wawo ngati kuli koyenera. Chimenecho chinali chatsopano, popeza kuti choterocho sichinafunike ndi Lamulo la Mose.
5. Ndimotani mmene mawu a Mulungu mwamphamvu amagogomezera chifuno kaamba ka chikondi ndi umodzi pakati pa alambiri ake owona?
5 Mawu a Mulungu amanena kuti: “Munthu akati kuti: ‘Ndikonda Mulungu,’ nadana naye mbale wake, ali wabodza; pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuwona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuwona. Ndipo lamulo iri tiri nalo lochokera kwa iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.” (1 Yohane 4:20, 21) Mwachikondi chimenechi, awo amene amakhulupirira mwa Yehova amasunga umodzi wowona wa dziko lonse. Mtumwi Paulo, pa 1 Akorinto 1:10, akunena kuti: “Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.”—Onaninso 1 Yohane 3:10-12.
6. Nchifukwa ninji Mboni za Yehova zinganene kuti ziri “zopanda kanthu ndi mwazi wa anthu onse”?
6 The World Book Encyclopedia imanena kuti anthu mamiliyoni 55 anaphedwa mu Nkhondo ya Dziko II. Iwo anaphedwa ndi anthu a chipembedzo chirichonse chachikulu kupatulako Mboni za Yehova. Palibe ndi imodzi yonse ya imfa zimenezo imene inapangitsidwa ndi mboni ya Yehova popeza izo zinamvera lamulo la kukondana wina ndi mnzake ndi kukana kudziloŵetsa mu nkhondo za mitundu. Pamene kuli kwakuti mboni zambiri zinaphedwa kaamba ka kaimidwe kawo ka uchete, izo zikanena monga mmene ananenera mtumwi Paulo kuti “Ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.”—Machitidwe 20:26.
7, 8. Ndimotani mmene anthu ena a tchalitchi amavomerezera liwongo lawo la mwazi?
7 Phungu wa zaumulungu wa Chikatolika wa amuna a mlengalenga omwe anagwetsa mabomba a atomu pa Japan mu 1945 ananena posachedwapa kuti: “Kwa zaka 1,700 zapitazo tchalitchi chakhala chikupanga nkhondo kukhala yolemekezeka. Chakhala chikusonkhezera anthu kukhulupirira kuti iri ntchito yolemekezeka ya Chikristu. Ichi sichiri chowona. Tangopatsidwa chinyengo. . . . Uthenga wabwino wa nkhondo ya chilungamo uli uthenga umene Yesu sanauphunzitsepo. . . . Palibe china chirichonse m’moyo kapena chiphunzitso cha Yesu chimene chimalingalira kuti pamene kuli kopanda lamulo kupsyereza anthu ndi nkhondo ya nyukliya, chiri chalamulo kupsyereza anthu ndi mabomba a moto kapena choponya malaŵi a moto.”
8 Catholic Herald ya ku London inanena kuti: “Akristu oyambirira . . . analandira Yesu ndi Mawu ake ndi kukana kuloŵetsedwa m’gulu lankhondo la Roma ngakhale ngati chilango chinali imfa. Kodi mbiri yonse ikanakhala yosiyana ngati tchalitchi chikanamamatira ku kaimidwe kake koyambirira? . . . Ngati matchalitchi a lerolino angabwere ndi chitsutso chogwirizana cha nkhondo . . . , chomwe chikatanthauza kuti chiwalo chirichonse chikakhala chomangika ndi chikumbumtima kukhala, monga Akristu, otsutsa motsimikizirika, mtendere ungakhaledi wotsimikizika. Koma tikudziŵa kuti ichi sichidzachitika nkomwe.”
9. Nchifukwa ninji tikumaliza kuti Yehova wasiya zipembedzo za dziko iri?
9 Chotero, zipembedzo zadziko iri zanyalanyaza mowopsya malamulo a Mulungu. Izo sizikhulupirira mwa iye monga momwe anachitira Afarisi. “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.” (Tito 1:16) Monga chotulukapo chake, Mulungu wasiya zipembedzo zadziko iri monga mmene motsimikizirika iye anasiira chipembedzo chonyenga cha chiyuda m’zana loyamba.—Mateyu 15:9, 14.
Kupulumuka mwa Kukhulupirira Yehova
10, 11. Nchiyani chimene Mfumu Hezekiya anachita pamene Asuri analamulira kugonjera kwa Yerusalemu, ndipo kodi ndi ndani amene mlankhuli wa Sanakeribu anali kutonza?
10 Musaike chikhulupiriro chanu m’mayankho a anthu, ku mavuto a dziko iri. M’malomwake, khulupirirani mmodzi amene angakwaniritse malonjezo ake. (Yoswa 23:14) Monga chitsanzo, dziŵani chimene chinachitika m’zana lachisanu ndi chitatu asanabwere Kristu, m’masiku a Mfumu Hezekiya ya Yuda. Baibulo limanena za iye kuti: “Nachita iye zowongoka pamaso pa Yehova.” (2 Mafumu 18:3) Mkati mwa ulamuliro wake, mphamvu ya dziko yamphamvu Asuri inabwera molimbana ndi Yerusalemu. Mlankhuli wa Sanakeribu mfumu ya Asuri analamula kugonjera kwa Yerusalemu mwa kumanena kuti: “Itero mfumu, ‘Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m’dzanja lake. Kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova.’”—2 Mafumu 18:29, 30.
11 Nchiyani chimene Hezekiya anachita? Baibulo likunena kuti: “Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati: ‘Yehova Mulungu wa Israyeli wakukhala pakati pa akerubi, inu ndinu Mulungu [wowona NW], inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Tcherani khutu lanu, Yehova, nimumve. Tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mawu a Sanakeribu, amene anatumiza kutonza nawo Mulungu wamoyo. . . . Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m’dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti inu ndinu Yehova Mulungu, inu nokha.’”—2 Mafumu 19:15-19.
12. Ndimotani mmene Yehova anayankhira pemphero la Hezekiya?
12 Yehova anamva pemphero limeneli ndi kutumiza mneneri Yesaya kukauza Hezekiya: “Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asuri, ‘Iye sadzalowa m’mudzi muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.’” Kodi Hezekiya anayenera kutsutsa Asuri ndi gulu la nkhondo? Ayi, iye anayenera kukhulupirira mwa Yehova, chimene anachita. Chotulukapo chake? “Mngelo wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Asuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu.” Sanakeribu iyemwini analipira kaamba ka kutonza Yehova ndi atumiki a Yehova, popeza ana ake enieni pambuyo pake anamupha iye. Zowona ku mawu a Yehova, palibe chida ndi chimodzi chomwe chinabwera pa Yerusalemu.—2 Mafumu 19:32-37.
13, 14. Ndi pamaziko otani pamene anthu ochokera ku mitundu ya anthu onse adzapulumuka mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu?
13 M’tsiku lathu chinthu chofananacho chidzachitika. Awo amene amakhulupirira mwa Yehova adzapulumuka kutonza kwa dziko iri ndi mapeto a dziko iri. “Ndipo iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira inu, pakuti inu Yehova simumawasiya iwo akufuna inu.” (Masalmo 9:10) Koma Yehova asanaweruze dziko la liwongo la mwazi iri, iye akuitana owona mtima kubwera kwa iye kaamba ka chisungiko. Awa amapanga “khamu lalikulu” kuchokera ku mitundu yonse, omwe “abwera kutuluka m’chisautso chachikulu.” Iwo apulumuka mapeto a dongosolo iri la zinthu chifukwa iwo amakhulupirira mwa Yehova ndi kumtumikira iye “usana ndi usiku.”—Chivumbulutso 7:9-15.
14 Awa akuyankha ku chiitano chimene tsopano chikupangidwa ndi chiwonjezeko chokulira dziko lonse, monga kunanenedweratu pa Yesaya 2:2, 3: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova [kulambira kwake kowona] lidzakhazikika . . . Ndipo anthu ambiri adzanka, nati: ‘Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.’” Versi 4 limanena kuti: “Ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape. Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”
15. Ndani amene akukwaniritsa ulosi wa Yesaya 2:2-4, ndipo motani?
15 Ndi ndani, m’nthaŵi yathu, ‘asula malupanga awo kukhala zolimira’? Ndi ndani ‘amene saphunziranso nkhondo’? Kodi ndani amene ali ndi chikondi chosaphwanyika kaamba ka abale ndi alongo awo auzimu pa dziko lonse lapansi ndi chigwirizano ndi iwo? Ndi ndani m’chenicheni amene amakhulupirira mwa Yehova ndi kuitana ena kuchita chofananacho? Nsonga za m’nthaŵi yathu zimasonyeza kuti yankho lingakhale kokha: Mboni za Yehova. Iwo, mofanana ndi Hezekiya, amakhulupirira mwa Yehova ndi mtima wawo wonse ndi kuchitira chitsanzo mwa kusunga malamulo ake.
Mtsogolo Mowala
16, 17. Ndi mtsogolo mowala chotani mmene Yehova akupereka kwa awo amene amakhulupirira mwa iye?
16 Kwa awo amene amakhulupirira mwa iye, Yehova amapereka mtsogolo mowala koposa molingalirika pamene ataloŵetsa m’malo chitaganya cha dziko lakale ichi ndi lake latsopano. M’dziko latsopano pano padziko lapansi, sipadzakhala mantha kapena kusakhulupirika, sipadzakhala umphawi, kupanda chilungamo, kapena upandu. Anthu sadzaphananso mu nkhondo kapena mwa kuchotsa mimba. Chivumbulutso 21:4 chimalonjeza kuti “sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira kapena chowawitsa.”
17 M’kupita kwa nthaŵi, dziko lapansi lidzakhala paradaiso monga mmene Yesu analonjezera. (Luka 23:43) Ndipo popeza ngakhale imfa idzachotsedwa, awo amene amakhulupirira mwa Yehova adzakhala okhoza kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso. Kukwaniritsidwa kotheratu kudzakhala Mika 4:4: “Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsya.” Tangolingalirani kukhala mu chitaganya mmene aliyense mudzakumana naye adzakhala winawake amene mungakhulupirire! Nchifukwa ninji chidzakhala tero? Chifukwa, monga mmene Yesaya 54:13 akunenera “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.”
18. Ndi mapindu otani amene awo okhulupirira mwa Yehova angatute ngakhale tsopano?
18 Komabe, ngakhale tsopano mamiliyoni a Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse akututa mapindu mwa kukhulupirira mwa Yehova. Mwachitsanzo, chifukwa cha kumvera malamulo a Yehova ndi maprinsipulo, atumiki a Yehova ali omasuka ku kansa ya m’mapapo yopangitsidwa ndi kusuta fodya. Chifukwa cha kukhala m’malo owazinga oyera mwa makhalidwe, iwo kaŵirikaŵiri sali m’ngozi ya matenda a dziko lonse opatsiridwa mwa kugonana, kuphatikizapo AIDS. Kusagwiritsira ntchito kwawo molakwa kwa anamgoneka kumawachinjiriza mokulira molimbana ndi zowononga malingaliro ndi ziyambukiro zodzetsa imfa, zimene ambiri ogwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ali nazo. Ndipo popeza kuti iwo samalandira kuthiridwa mwazi, iwo amapewa matenda akupha amene amaperekedwa kupyolera m’mwazi, kuphatikizapo kutupa kwa chiwindi (hepatitis), kumene kumapha kapena kuvulaza kotheratu anthu olandira mwazi zikwi khumi chaka chirichonse mu United States mokha.
19. Ndimotani mmene Yehova adzapulumutsira awo amene amamtumikira ngakhale ngati afa tsopano?
19 Ngakhale ngati ena a awo amene tsopano amakhulupirira mwa Yehova afa chifukwa cha ukalamba, matenda, kapena ngozi, Yehova adzawapulumutsa iwo. Iye adzawapulumutsa iwo kupyolera mu chiwukiriro. Chotero, mtumwi Paulo amatilimbikitsa ife “kukhala ndi chikhulupiriro chathu, osati mwa ife tokha, koma mwa Mulungu amene amawukitsa akufa.”—2 Akorinto 1:9, NW.
Yehova Amachirikiza Atumiki Ake
20, 21. (a) Ndi chitsutso chotani chimene tingayembekezere, monga mmene chachitiridwa chithunzi ndi zimene zinachitika kwa Yesu? (b) Ndimotani mmene Yehova analemekezera anthu ake, monga mmene anachitira Yesu?
20 Sungani m’maganizo kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Chotero ngati mukhulupirira Mulungu, mudzatsutsidwa ndi Satana ndi dziko lake. Iwo adzayesera kuwononga chikhulupiriro chanu mwa kuseka kapena chizunzo, monga mmene zinaliri ndi Yesu. Pambuyo pa kupachikidwa pa mtengo wozunzirapo, “anthu akupitirirapo anamchitira mwano iye ndi kupukusa mitu yawo nati . . . ‘Ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika [pamtengo wozunzirapowo! NW]’ Chomwechonso ansembe akulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe nati: ‘Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha! . . . Amakhulupirira Mulungu; iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna.’”—Mateyu 27:39-43.
21 Masiku atatu pambuyo pake, Mulungu m’chenicheni anampulumutsadi Yesu mwa kumuukitsa iye kuchokera kwa akufa. Mbadwo umenewo wa kuseka, ngakhale kuli tero, unaphedwa kapena kuikidwa mu ukapolo ndi magulu ankhondo a Roma. Popeza Kristu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu adzayang’anira chiwukiriro, ngati oseka amenewa adzawukitsidwa kwa akufa, iwo adzayenera kugonjera kwa mmodzi amene anaseka zaka zikwi ziŵiri zapitazo! Inde, Yehova amalemekeza atumiki ake, pamene amanena kuti: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa. Munthu adzandichitanji?”—Masalmo 56:11.
22. Kodi nchiyani chimene Yehova akulengeza ponena za awo amene amakhulupirira iye, ndi awo amene samatero?
22 Ponena za atumiki ake, Yehova akulengeza kuti: “Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosawopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi ndipo suvutika chaka cha chirala, suleka kubala zipatso.” Koma Yehova akulengezanso kuti: “Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wa nyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake. Ndipo adzakhala ngati tsanya la m’chipululu, ndipo sawona pamene chifika chabwino.”—Yeremiya 17:5-8.
23. Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita ngati tikufuna moyo wosatha?
23 Chotero, m’nthaŵi zino zovuta, “khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata chowonadi. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.” (Masalmo 37:3, 4) Lolani kuti zopempha zanu zofikiritsidwa ziphatikizepo mphatso ya moyo wosatha m’dziko lolungama latsopano, lolonjezedwa ndi Mulungu mwa amene timakhulupirira.
Mafunso a Kubwereramo
◻ Kodi ndi muyezo wotani umene uyenera kusungidwa ndi awo amene amakhulupirira mwa Yehova?
◻ Kodi zipembedzo zadziko lino zimaphunzitsa kukhulupirira mwa Yehova?
◻ Ndimotani mmene kukhulupirira kwa Mfumu Hezekiya mwa Yehova kunalemekezedwera?
◻ M’tsiku lathu, ndimotani mmene ulosi wa Yesaya 2:2-4 ukukwaniritsidwira?
◻ Kodi ndi mtsogolo motani mmene mudzazindikiridwa ndi awo amene amakhulupirira mwa Yehova?
[Chithunzi patsamba 17]
Mlankhuli wa mfumu ya Asuri anatonza Yehova ndi kulamulira kugonjera kwa Yerusalemu
[Chithunzi patsamba 18]
M’dziko latsopano awo amene amakhulupirira mwa Yehova adzasangalala ndi mtendere ndi chisungiko chotheratu