Chitokoso cha Kutsatira m’Mapazi Ake
“Popeza kuti Kristu anavutika kaamba ka inu ndipo anakusiirani chitsanzo chaumwini, kotero kuti inu mukatsatire m’mapazi ake.”—1 PETRO 2:21, Phillips.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chingakhale chitokoso chenicheni, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri cha chikondwerero kwa Akristu? (b) Kodi ndi mafunso otani amene akudzutsidwa pano?
KODI munayendapo kudutsa gombe la mchenga wokhawokha kapena kudutsa munda wokhala ndi chipale chofewa ndi kudzipeza inu eni wosangalatsidwa ndi mtundu wa mapazi osiidwa ndi winawake yemwe anapitamo inu musanatero? Kodi inu mwinamwake munayesera kuyenda mapazi angapo ndi kuyesa kuwatsatira iwo, mukumagwirizanitsa kayendedwe kanu ndendende ndi iwo monga mmene kungathekere? Ngati ndi tero, inu munapeza kuti sichinali chopepuka. M’chenicheni, kutsatira mosamalitsa m’mapazi a winawake—kaya m’chenicheni kapena mophiphiritsira—chiri chitokoso chenicheni. Ndipo komabe, mwakudziitana ife eni Akristu, tasonyeza chikhumbo chathu cha kuchita kokha chimenecho, kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Kristu.
2 Kodi muli wofunitsitsa kuikapo kuyesayesa komwe kuli koyenerera kukumaniza chitokoso chimenechi mokhutiritsa? Kuposa pamenepo, kodi muli wogamulapo kuchita tero, mosasamala kanthu ndi chonse chomwe chingadze? Ngati ndi tero, kumvetsetsa mokwanira mavuto akutsatira m’mapazi enieni kudzakupangitsani kukhala wokhutiritsa kwenikweni m’kutsatira mapazi ophiphiritsira a Kristu.
Phunzirani Kumamatira
3. Kodi nchifukwa ninji kutsatira mapazi a winawake kumawoneka panthaŵi yoyamba kukhala kosakhala kwa chibadwa?
3 Aliyense ali ndi njira yapadera yoyendera. Utali wa kanyamulidwe ka miyendo, mwachitsanzo, umasiyana kuchokera ku munthu ndi munthu, monga mmene umachitira mkhalidwe mu umene munthu amaikira phazi lake. Zala zake zingaloze kutsogolo mowongoka, kapena zingakhotere mkati kapena kunja mokhotako, kukhota kumene mothekera kwambiri kuli kogwirizana ndi phazi limodzi kuposa ndi linzake. Kodi mukuzindikira chitokosocho? Kuti mutsatire mosamalitsa mapazi a winawake, muyenera kugwirizanitsa utali wanu kanyamulidwe ka miyendo ndi mkhalidwe wa phazi wa iye. Poyamba ichi chidzawoneka kukhala chosakhala chachibadwa, koma chiyenera kuchitidwa. Palibe njira ina iriyonse.
4. Nchifukwa ninji kutsatira mapazi a Yesu kuli chitokoso chapadera?
4 Njira ya kayendedwe ka Kristu, kulankhula mophiphiritsira, inali yapadera, popeza kuti pakati pa anzake iye yekhayo anali munthu wangwiro, “amene sanadziŵa uchimo.” (2 Akorinto 5:21) Popeza kuti anthu mwachibadwa ali ochimwa opanda ungwiro, kuyenda m’mapazi a Yesu sikuli kayendedwe kawo kachibadwa. Paulo anakumbutsa Akristu mu Akorinto ponena za ichi, akumati: “Pakuti pali nkhwidzi ndi ndewu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?” Chikhoterero kulinga ku nsanje ndi ndewu, “ntchito zathupi,” chiri chanthaŵi zonse kaamba ka anthu opanda ungwiro, koma Yesu anayenda m’njira ya chikondi, ndipo “chikondi sichichita nsanje, . . . sichikalipitsidwa.” Chotero kuyenda m’mapazi a Kristu kumapereka chitokoso chokulira kuposa ngati tinafunsidwa kokha kutsatira mapazi a munthu wopanda ungwiro.—1 Akorinto 3:3; 13:4, 5; Agalatiya 5:19, 20; onaninso Aefeso 5:2, 8.
5, 6. (a) Nchifukwa ninji anthu ambiri alephera kutsatira mapazi a Kristu, kukumatsogolera Paulo kupereka uphungu wotani? (b) Kodi ndimotani mmene anthu akulimbikitsidwira kuyenda m’mapazi a Kristu lerolino, ndi chotulukapo chotani kaamba ka iwo?
5 Pambali pa kupanda ungwiro, kusadziŵa chifuniro cha Mulungu kungaletsenso munthu kuyenda m’mapazi a Kristu. Paulo chotero analangiza Akristu a ku Aefeso “kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, mu uchitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo.”—Aefeso 4:17, 18.
6 Mwanjira ya ntchito ya kulalikira Ufumu, anthu lerolino akulimbikitsidwa kuleka kuyenda m’njira yawo ya nthaŵi zonse, m’kusadziŵa zifuniro za Mulungu, mu mdima wa malingaliro, otsogozedwa ndi kupanda malingaliro kwa mtima kufunafuna zonulirapo zopanda phindu. Iwo akulimbikitsidwa kugwirizana ndi chitsanzo changwiro cha Kristu, “kuyenda mogwirizana ndi iye,” mwakutero “kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.” (Akolose 2:6, 7; 2 Akorinto 10:5) Anthu omwe ali ofunitsitsa kukumana ndi chitokoso chimenechi ali okhazikika m’chikhulupiriro chawo. Pamene azoloŵera kuyenda m’njira imene Kristu anayenda, chimakhala chopepuka mopita patsogolo kaamba ka iwo.
7. Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene tiri nacho chakuti, ngakhale kuti kaŵirikaŵiri chiri chitokoso, kutsatira m’mapazi a Yesu kuli kothekera?
7 Kaŵirikaŵiri, ngakhale kuli tero, chiri chitokoso. Kusiyana pakati pa cholengedwa changwiro ndi chopanda ungwiro kuli kokulira. Chotero zolengedwa zopanda ungwiro ziyenera kupanga kusintha kokulira m’malo mofuna kuyesera kutsatira chitsanzo changwiro. Anthu ena, mwinamwake chifukwa cha chibadwa kapena malo ozungulira, ali ndi mavuto okulira akugonjera ku njira ya moyo ya Chikristu kuposa mmene amachitira ena. Koma Yehova amatitsimikizira ife kuti aliyense yemwe mowonadi ali wofunitsitsa kuyesetsa iyemwini angachichite. “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo,” anatero mtumwi Paulo. (Afilipi 4:13; onaninso 2 Akorinto 4:7; 12:9.) Chofananacho chiri chowona kwa Akristu onse.
Perekani Chisamaliro
8, 9. (a) Nchifukwa ninji chisamaliro chosagawanika ndi kusumika maganizo kotheratu kuli kofunika pamene titsatira mapazi a winawake? (b) Kodi ndi kutsatira uphungu wa m’Baibulo wotani kumene kudzatichinjiriza ife kusazengereza kuchoka m’mapazi a Yesu?
8 Sitingatsatire mapazi enieni popanda kuyang’ana mosamalitsa pamene tikuponda. Ngati maso athu akhotera kwinakwake—kuyang’ana pa zinthu zomwe zikupita motizungulira kapena pa zinthu zina—tingakhale okhoza kuponda pena mwamsanga kapena pambuyo pake. Kusiyapo kokha ngati tipereka chisamaliro chosagawanika ndi kusumika mokulira, tingakhoze kusowa mapazi omwe tiyenera kutsatira. Chotero, nthaŵi zonse pali chifuno cha kukhala ogalamuka, makamaka pamene phokoso la mwadzidzidzi kapena zochewutsa zosayembekezeredwa zingachewutse malingaliro athu kuchoka pa ntchito yomwe tiri nayo.—Yerekezani ndi Yobu 18:10, 11.
9 M’njira yophiphiritsira, ichi chirinso chowona kwa aja omwe akutsatira m’mapazi a Yesu. Yesu anachenjeza atsatiri ake kupereka chisamaliro chathithithi kwa iwo eni, kuwopera kuti mitima yawo “ingalemetsedwe ndi maidyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno.” (Luka 21:34) Satana amagwiritsira ntchito zochewutsa za tsiku ndi tsiku zimenezi kutipangitsa ife kuchotsa maso athu pa mapazi a Yesu. Iye ali wofulumira kutichewutsa ife mwakutenga mwaŵi wa mkhalidwe wosayembekezereka, wonga ngati chitsutso, matenda, kapena kubwerera m’mbuyo kwa zachuma. Kutsimikizira kuti “sitinachewutsidwe,” tiyenera “kupereka chisamaliro chosakhala cha nthaŵi zonse ku zinthu zomvedwa,” m’mawu ena, kusumika maso athu mosachewutsidwa kuyang’ana pa mapazi a Kristu kuposa ndi kale lonse.—Ahebri 2:1; onaninso 1 Yohane 2:15-17.
Musapatuke
10. (a) Kodi ndi ngozi yotani yomwe iripo pamene unyinji wa mapazi umadutsana lina ndi linzake? (b) M’lingaliro lauzimu, kodi nchifukwa ninji zotulukapo za kutsatira mapazi olakwika ziri zowopsya?
10 Pa gombe lokhala ndi anthu ambiri, pangakhale unyinji wosiyanasiyana wa mapazi mu mchenga wokhala ndi madzi, ndipo unyinji wa mapazi odutsa ungapingase amene tikutsatira. Unyinji wa mapazi ungakhoze, chifupifupi m’kawonekedwe, kuwoneka wolingana. Chiri chofunika chotani nanga kukhala otsimikiza kuti tikutsatira olondola! Ngati sitero tingakhoze kunyengedwa kupita m’njira yolakwika. M’lingaliro lauzimu, ichi chingakhale ndi chotulukapo choipa. Ngozi ya kutsatira mapazi omwe angawonekere kukhala olondola koma amene m’chenicheni siali yasonyezedwa mu miyambo yomwe imachenjeza kuti: “Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yowongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”—Miyambo 16:25.
11. Kodi ndi chenjezo lotani limene Paulo anapatsa Akristu oyambirira, likumakhazikitsa chitsanzo kaamba ka ndani lerolino?
11 Chifukwa cha ngozi yowopsya kwambiri imeneyi, Paulo anadzimva wosonkhezeredwa kuchenjeza abale ake mu mpingo Wachikristu woyambirira: “Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kwa iye amene anakuitanani m’chisomo cha Kristu, kutsata uthenga wabwino wina . . . Ngati wina akulalikirani uthenga wabwino osati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.” (Agalatiya 1:6-9) M’kugwirizana ndi chitsanzo cha Paulo, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lerolino limatichenjeza ife za ampatuko ndi abale onyenga omwe amaika pansi, monga mmene zinaliri, mapazi a chinyengo. Akristu owona samafuna kupatuka kuchoka panjira imene Kristu wakhazikitsa pamaso pawo pa chitsogozo cha Mulungu.—Masalmo 44:18.
12. (a) Kodi ndimotani mmene 2 Timoteo 1:13 angatithandizire ife kupewa kusokeretsedwa m’kutsatira mapazi onyenga? (b) Kodi nchiyani chimene chimazindikiritsa mitundu ina ya mbiri yabwino?
12 Mwa kupereka chisamaliro chathithithi ku zizindikiro zodziŵitsa mapazi a Kristu, tidzapewa kupeyutsidwa. Chidziŵitso cholongosoka chonena za Yesu, chonena za ziphunzitso zake, ndi chonena za njira mu imene mpingo Wachikristu umagwirira ntchito chimatithandiza ife kuzindikira “chitsanzo cha mawu a moyo” chomwe chimatichinjiriza ife kwa awo omwe “amaipitsa mbiri yabwino yonena za Kristu.” (2 Timoteo 1:13) Mitundu ina ya iyo yotchedwa mbiri yabwino—m’chenicheni, iri mapazi onyenga—imalephera kulinga m’chitsanzo chimenecho cha chowonadi. Iyo imaipitsa imeneyo, kuphimba chithunzithunzi kukhala chosawoneka bwino. M’malo mwakumveketsa chowonadi cha Baibulo chenicheni ndi malamulo, iyo imawatsutsa iwo. M’malo mwa kutilimbikitsa ife ku ntchito yokulira mu utumiki wa Yehova, iyo imatsutsa mokomera kulefuka. Uthenga wawo suli weniweni ndipo sumalemekeza dzina la Yehova ndi gulu; uli wachabe, wofunafuna zophophonya, ndi woipa. Motsimikizirika kwenikweni, awa si mapazi omwe tifunikira kutsatira.
Sungani Liŵiro Loyenera
13. Kodi ndimotani mmene liŵiro likuphatikizidwira pamene tikutsatira mapazi a winawake?
13 Pamene tiyenda, utali wa kanyamulidwe ka miyendo yathu umatsimikiziridwa mwapang’ono ndi liŵiro pa limene tikuyenderapo. Mwachisaŵawa, kufulumira kumene tidzayenda, kudzakhalanso kutalika kwa kanyamulidwe ka miyendo yathu; kuchedwa kumene tidzayenda, kudzakhalanso kufupika kwake. Chotero, chidzakhala chopepuka kwa ife kutsatira mapazi enieni a wina ngati tisintha liŵiro lathu kuti ligwirizane ndi lake. Mofananamo, kuti tiyende mokhutiritsa m’mapazi ophiphiritsira a Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, tiyenera kusunga liŵiro lake.
14. (a) Kodi ndi m’njira zotani m’zimene ife sitingasungire liŵiro ndi Yesu? (b) Kodi nchifukwa ninji kungakhale kupusa kuyesera kuyenda mofulumira kuposa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
14 Kusasunga liŵiro ndi Kristu kukatanthauza chimodzi cha zinthu ziŵiri. Kaya tikuyesera kuyenda mofulumira kwambiri, kuthamangira kutsogolo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene Yesu akugwiritsira ntchito kukwaniritsa chifuno cha Yehova, kapena kusinkhasinkha m’mbuyo m’kutsatira chitsogozo cha ‘kapoloyo.’ (Mateyu 24:45-47) Monga chitsanzo choyambirira, Akristu ena akhala okhoza ku nthaŵi za kumbuyoku kukhala osaleza mtima ponena za kusintha kwa ziphunzitso kapena za gulu kapena kuyengeka kumene iwo adzimva kuti kunali koyenerera ndi koyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali. Atakwiitsidwa chifukwa chakuti anadzimva kuti zinthu sizinali kuyenda mofulumira kwambiri, iwo anachoka kwa anthu a Yehova. Kuli kupusa kotani nanga ndipo kuli khungu lotani nanga! Kaŵirikaŵiri chinthu chenicheni chomwe chinawakwiitsa iwo chinasinthidwa pambuyo pake—m’nthaŵi yoyenera ya Yehova.—Miyambo 19:2; Mlaliki 7:8, 9.
15. Ndimotani mmene Mfumu Davide ndi Yesu analiri zitsanzo zabwino za kusungilira liŵiro lolondola?
15 Njira yanzeru iri kuyembekeza kaamba ka Yehova kuti achitepo kanthu kuposa kuyesa kupanga liŵiro pa limene zinthu ziyenera kuchitikira. Mfumu yakale Davide anakhazikitsa chitsanzo chabwino. Iye anakana kuchita chiwembu molimbana ndi Mfumu Sauli m’kuyesera kufuna ufumu isanafike nthaŵi yoyenera ya Yehova ya kuwupatsa iwo kwa iye. (1 Samueli 24:1-15) Mofananamo, “Mwana wa Davide,” Yesu, anazindikira kuti iye akafunikira kuyembekeza kulowa kotheratu mu ufumu wake wakumwamba. Iye anadziŵa mawu a ulosi omwe anagwira ntchito kwa iye: “Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.” Chotero pamene gulu la Ayuda linafuna “kumgwira iye kuti amulonge mfumu,” Yesu mwamsanga anathaŵa. (Mateyu 21:9; Masalmo 110:1; Yohane 6:15) Zaka zina 30 pambuyo pake, molingana ndi Ahebri 10:12, 13, Yesu ankayembekezerabe ufumu wake. M’chenicheni, iye anayembekezera chifupifupi mazana 19 asanakhazikitsidwe monga Mfumu yolondola ya Ufumu wa Mulungu pa kukhazikitsidwa kwake mu 1914.
16. (a) Chitirani chitsanzo mmene tingayendere mochedwa kwambiri kuposa mmene tifunikira. (b) Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha kuleza mtima kwa Yehova, ndipo nchifukwa ninji tifunikira kupewa kugwiritsira ntchito molakwa kuleza mtimako?
16 Kulephera kusunga liŵiro lolondola, ngakhale ndi tero, kungatanthauzenso kulefuka, kusinkhasinkha m’mbuyo. Chotero, pamene Mawu a Mulungu amasonyeza kuti masinthidwe ayenera kupangidwa m’miyoyo yathu, kodi timachita popanda kuchedwa? Kapena kodi timatsutsa kuti popeza kuti Mulungu ali woleza mtima, tingasinkhesinke kupanga masinthidwe oterewo kufikira nthaŵi ina pambuyo pake, tikumayembekezera kuti chikakhala chopepuka panthaŵiyo? Ndi zowona, Yehova ali woleza mtima. Koma ichi sichiri tero kotero kuti ife tidzisinkhasinkha kupanga masinthidwe oyenerera. M’malomwake, iye “aleza mtima kwa inu osafuna kuti aliyense awonongeke koma kuti onse afike ku kulapa.” (2 Petro 3:9, 15) Chotero, chiri chabwino koposa chotani nanga, kutsatira wamasalmo yemwe ananena kuti: “Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu.”—Masalmo 119:60.
17. Kodi nchiyani chimene kusunga liŵiro labwino kungakhale nako ndi kulalikira Ufumu, kukumatsogolera kudzifunsa ife eni funso lotani?
17 Kusinkhasinkha m’mbuyo kungaphatikizeponso kulalikira Ufumu. Mogwirizana ndi Mateyu 25, Yesu panthaŵi ino akuweruza mtundu wa anthu, kusiyanitsa “nkhosa” kuchoka ku “mbuzi.” Ichi chikukwaniritsidwa kwa mbali yaikulu ndi kulalikira kwa “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu.” (Mateyu 24:14; 25:31-33; Chivumbulutso 14:6, 7) Nthaŵi yoikidwa kutsiriza ntchito yolekanitsa imeneyi moyenerera iri ndi polekezera. (Mateyu 24:34) Pamene nthaŵi yomwe iripo ikuyandikira ku mapeto ake tingayembekezere Yesu kufulumiza ntchitoyo. M’kuchita tero, iye akuchita monga chiŵiya cha Mulungu, amene pa kulankhula za ntchito ya kusonkhanitsa, amalonjeza kuti: “Ine, Yehova, ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Monga antchito anzake a Mulungu, kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Mwana wake, kodi tikufulumiza liŵiro lathu la kulalikira Ufumu kumlingo umene mkhalidwe wathu wa kuthupi ndi mathayo athu a kuuzimu amalola? Maripoti autumiki wa m’munda amasonyeza kuti mamiliyoni a Mboni za Yehova akutero!
Pewani Kudzidalira Mopambanitsa, Gonjetsani Chokhumudwitsa
18. Nchifukwa ninji munthu angakhalire wodzidalira mopambanitsa, ndipo ndimotani mmene Baibulo limachenjezera ponena za ngoziyi?
18 Kutalika kumene tidzapirira m’kutsatira mapazi a winawake, kudzakhalanso kuzoloŵera kokulira kumene njira yake ya kayendedwe idzakhala kwa ife. Ngati, ngakhale kuli tero, tikhala otopa, mwamsanga kapena pambuyo pake tidzaphonya kayendedweko. Chotero, pamene titsatira mapazi ophiphiritsira a Yesu, tiyenera kuzindikira ngozi ya kukhala odzidalira mopambanitsa, mosasamala kanthu za kudalira pa mphamvu zathu ndi zoyesayesa, tikumadzimva kuti tazoloŵera njira yake yangwiro ya kayendedwe. Chokumana nacho cha Petro cholembedwa pa Luka 22:54-62 chimatumikira monga chenjezo la panthaŵi yake. Icho chimagogomezeranso kuwona kwa 1 Akorinto 10:12, yomwe imanena kuti: “Iye wolingalira kuti ali chiriri adziyang’anire kuti angagwe.”
19. (a) Kodi nchiyani chimene chimachitika kwa Mkristu aliyense kuchokera kunthaŵi ndi nthaŵi? (Yakobo 3:2) (b) Kodi ndimotani mmene tifunikira kuwonera mawu a Paulo pa Aroma 7:19, 24?
19 Chifukwa cha kupanda ungwiro, Mkristu aliyense adzaphonya mapazi kuchokera kunthaŵi ndi nthaŵi. Kuphonyako kungakhale kwakung’ono, nthaŵi zina kokhoza kuwonedwa ndi ena. Kapena iko kungakhale kuphonya kotheratu kwa chizindikirocho chakuti kungakhoze kuwonedwa ndi onse. Chirichonse chomwe icho chingakhale, chiri chotonthoza chotani nanga kukumbukira kulangiza kowona mtima kwa Paulo kwakuti: “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna chimenecho ndichichita!” (Aroma 7:19, 24) Ndithudi, mawu amenewa safunikira kuwonedwa monga chodzikhululukira kaamba ka kuchita choipa. M’malomwake, iwo ali chilimbikitso kwa Akristu odzipereka olimbana ndi kupanda ungwiro, kuwathandiza iwo kulimbikira m’kuyesayesa kwawo kwa kukumanizana ndi chitokoso cha kuyenda m’mapazi angwiro a Yesu.
20. (a) Kodi ndimotani mmene Miyambo 24:16 imatithandizira ife m’liŵiro lathu kaamba ka moyo? (b) Nchiyani chomwe tifunikira kugamula kuchita?
20 “Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kaŵiri, nanyamukanso,” imatero Miyambo 24:16. M’liŵiro lathu kaamba ka moyo, palibe aliyense yemwe afunikira kudzimva wokakamizidwa kuleka. Liŵiro limeneli liri monga mpikisano, liŵiro lofunikira chipiriro, osati lautali wa mayadi zana limodzi. Kuphonya kochepera kumbali ya wothamangayo kudzakhoza m’kuthekera konse kumpangitsa kulephera mpikisanowo. Koma wothamanga wa mumpikisano, ngakhale ngati wakhumudwitsidwa, amakhala ndi nthaŵi ya kuchira ndi kutsiriza mpikisanowo. Chotero pamene kuphonya kwina kwaumwini kwakupangitsani inu kulira kuti, “Munthu wopanda chochita ine!” kumbukirani kuti mukali ndi nthaŵi ya kuchira. Mukali ndi mwaŵi wa kubwereranso m’mapaziwo ndi Mtsogoleri wanu, Yesu Kristu. Palibe chifukwa chirichonse cha kudetsedwa nkhaŵa! Palibe chifukwa chirichonse cha kutopera! Khalani wogamulapo, ndi chithandizo chaumulungu, kukumanizana ndi chitokoso mokhutiritsa mwa ‘kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Yesu.’—1 Petro 2:21.
Nchifukwa ninji Akristu afunikira
◻ kuphunzira kumamatira?
◻ kupereka chisamaliro chosagawanika?
◻ kusunga m’malingaliro chitsanzo cha chowonadi?
◻ kusungilira liŵiro lolondola?
◻ kupewa kudzidalira kopambanitsa?
◻ kulimbana ndi zokhumudwitsa?
[Chithunzi patsamba 15]
Mwakuyang’anitsitsa pa chonulirapo chake, wolungama adzauka ndithudi