Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/15 tsamba 3-4
  • Kodi Chisudzulo Chiyenera Kuloledwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chisudzulo Chiyenera Kuloledwa?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kawonedwe Kosiyana ndipo Kowombana
  • Udakali Mkhalidwe Wothetsa Nzeru
  • Chisudzulo Chiridi ndi Minkhole
    Galamukani!—1991
  • Kuwonjezereka Kwakukulu kwa Zisudzulo
    Galamukani!—1992
  • Chisudzulo—Zotulukapo Zake Zoŵaŵa
    Galamukani!—1992
  • Msampha wa Chisudzulo
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/15 tsamba 3-4

Kodi Chisudzulo Chiyenera Kuloledwa?

MU JUNE 1986 ochita voti mu Ripabuliki ya Irish anachita voti ndi malire a 3 mpaka 2 kusungilira kuletsa kwawo kusudzulana. Ichi chinapanga Ripabulikiyo kukhala dziko lokha Kumadzulo kwa Europe mu limene kusudzulana sikuli kwa lamulobe.

Mwachiwonekere, mosasamala kanthu za funde lakawonekedwe ka ufulu ndi kalingaliridwe, kawonedwe ka anthu ambiri pa nkhani yosinthidwa mwa malingaliro ya kusudzulana kadakali kosonkhezeredwabe mwamphamvu ndi chiyambi chawo. Fuko, maphunziro, ndi nsonga za mayanjano zonse zimachitako mbali. Koma pa zinthu zonse, chipembedzo, kapena popanda icho, chimakhalabe chisonkhezero chimodzi champhamvu koposa.

Nchiyani chimene chiri kawonedwe kanu ka kusudzulana? Ngati okwatirana adzimva kukhala opanda chimwemwe akumakhala pamodzi ndipo ali mwachiwonekere osagwirizana, kodi iwo ayenera kuloledwa kuthetsa kupanda chimwemwe kwawo mwakupeza chisudzulo? Kodi ndimotani mmene mungayankhire funso limeneli? Mofunika koposa, ndi pa chiyani pamene mungazike yankho lanu?

Kawonedwe Kosiyana ndipo Kowombana

Kwa mamiliyoni omwe amasungilira miyezo ya Roma Katolika, palibe chisudzulo. “Mu ukwati Wachikristu,” ikulongosola The Catholic Encyclopedia, “sipangakhale chisudzulo chotheratu [ndi kuyenera kwa kukwatiranso], chifupifupi pambuyo pa kukhazikitsidwa kotheratu kwa ukwatiwo.” Komabe, Tchalitchi cha Roma Katolika chimapereka chilekaniro pa mikhalidwe ina, ndipo kachitidwe kameneka kali kugwiritsiridwa ntchito mofala. Mwachitsanzo, mu April 1986 The Denver Post inasimba kuti: “Akatolika a kumaloko akufunsira kaamba ka kuthetsa maukwati kokulira kotero kuti Archdiocese ya ku Denver ikuwononga $250,000 pa ogwira ntchito owonjezeredwa ndi kompyuta yowathandiza iwo kugwira ntchito yokulirayo.” Ripotilo mowonjezera linanena kuti “mu Archdiocese ya Denver, pali ndandanda ya utali wa zaka zitatu ya nkhani 700 za kuthetsa ukwati.”

Aprotesitanti mu zipembedzo mazana ochuluka kuzungulira dziko akuyang’anizana ndi unyinji wokulira wa malamulo a tchalitchi ndi ziwongolero pa chisudzulo. Mwachisawawa, ngakhale kuli tero, malamulo a chiProtesitanti amavomereza chisudzulo kokha pa maziko owopsya kwambiri. Koma chimene chikulingaliridwa kukhala chowopsya chingasiyane mokulira kuchokera ku tchalitchi chimodzi ndi chinzake. Milandu yonga ngati chigololo, nkhalwe, ndi kuthaŵa mkazi mwachisawawa imalandiridwa, koma iyo ndithudi siiri yokhayo. Matchalitchi ena tsopano ali ndi mapwando ndi mautumiki a chisudzulo okhala ndi nyimbo ndi mapemphero mofanana ndi m’maukwati. Pa phwando limodzi loterolo, “malumbiro aukwati amathetsedwa. Okwatiranawo amabweza mphete zawo za paukwati kwa mtumiki. Utumikiwo umatha ndi chilengezo chochokera kwa mtumikiyo kuti ukwatiwo wathetsedwa, ndipo okwatiranawo amapatsana chanza,” ikusimba tero The New York Times.

Ayuda ali ndi mwambo wolimbikitsidwa ndi mabwalo a milandu a chipembedzo. Malamulo a chiRabi amavomereza chisudzulo kaya mwa kugwirizana kwachibale kwa okwatiranawo kapena pa maziko a zolakwika za kuthupi kapena mkhalidwe wosapiririka. Chisudzulo chimalingaliridwa kukhala chalamulo, ngakhale kuli tero, kokha pamene mwamuna apereka “chikalata,” kapena chiphaso cha chisudzulo, ndipo ichi chingakhale magwero a m’kangano. Chifukwa cha kukalipitsidwa amuna ena amakana kupereka chikalatacho kapena iwo amachigwiritsira ntchito monga chinthu chotsatsira malonda. “Vuto limeneli lasiya zikwi za akazi Achiyuda odzipereka m’mkhalidwe wopweteka wa kubindikiritsidwa kwa mayanjano a mu ukwati,” anatero prezidenti wa New York City Council Andrew Stein m’nkhani yake ku msonkhano wa arabi, maloya, ndi ena. Popanda chikalata cha chilekaniro, kukwatiwanso kwa mkaziyo kungalingaliridwe kukhala kopanda lamulo, ndipo mbadwa iriyonse imadziŵikitsidwa monga mwana wobadwa mu ukwati wosayeretsedwa, kapena mwana wamthengo, mu Boma lamakono la Israyeli.

Ponena za opanda chipembedzo ndi osakhulupirira mwa Mulungu, amene mosamvetsetsa amayendera limodzi ndi lamulo la dziko, nkhaniyo siiri yopepuka. Ichi chiri chifukwa chakuti lamulo la chisudzulo limasiyana kuchokera ku dziko ndi dziko ndipo ngakhale ku gawo ndi gawo mkati mwa dziko limodzimodzilo. Ulamuliro umodzi umandandalitsa maziko 50 pa amene chisudzulo chalamulo chingapezedwe m’mbali zosiyanasiyana za United States. Izi zimaphazikizapo “mkhalidwe woipa kwambiri ndi kuipa,” “palibe chifukwa chomvekera cha kusungidwa kwa ukwati,” ndi “kukana kwa mkazi kuchoka ndi mwamuna ku boma limenelo.” M’nthaŵi zaposachedwapa, ngakhale chitsimikiziro chomalizira cha lingaliro la chabwino ndi choipa lachotsedwa ndi chimene chikutchedwa mofala kuti chisudzulo cha palibe cholakwika.

Udakali Mkhalidwe Wothetsa Nzeru

Ngakhale kuti ambiri amalamulo ndi zitsogozo zosiyana ndi zowombana zimenezi pa chisudzulo zikunenedwa kukhala zozikidwa pa Baibulo, kodi izo zakhala zachipambano m’kulimbikitsa kukhazikitsidwa kwa ukwati kapena kupititsa patsogolo chimwemwe cha anthu? Liŵiro la kukula kwa chisudzulo​—chisudzulo chimodzi pa maukwati aŵiri onse m’maiko ena​—limapereka yankho lomvekera. Si kokha kuti malamulo amenewa akhala opanda chipambano m’kulimbikitsa chomangira cha ukwati koma iwo awonjezeranso ku kusoweka kwa chimwemwe ndi kuvutika kwa miyoyo ya mamiliyoni.

M’chiyang’aniro cha ichi, chiri chofunika koposa kwa awo omwe ali odera nkhaŵa mowona mtima ndi kuchita chimene chiri chabwino kupeza chimene Baibulo kwenikweni limanena pa nkhaniyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena