Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuchiritsa Munthu Wobadwa Wakhungu
PAMENE Ayuda anayesera kumponya miyala Yesu pamene ali m’kachisi, iye anabisala ndi kuthaŵa. Koma sanachokemo m’Yerusalemu. Pambuyo pake, pa Sabata, iye ndi ophunzira ake akuyenda mu mzindawo pamene akuwona munthu yemwe anakhala wakhungu chibadwire. “Rabbi, anachimwa ndani,” Ophunzirawo amfunsa Yesu, “ameneyu, kapena atate ake kapena amake, kuti anabadwa wosawona?”
Mwinamwake ophunzira akukhulupirira, monga mmene amachitira a rabbi ena, kuti munthu angachimwe m’mimba ya amayi ake. Koma Yesu akuyankha kuti: “Sanachimwe ameneyu, kapena atate wake; koma kuti ntchito za Mulungu zikawonetsedwe mwa iye.” Khungu la munthuyo siriri chotulukapo cha vuto lachindunji kapena chimo lochitidwa kaya ndi munthuyo kapena makolo ake. Chimo la munthu woyamba Adamu linatulukapo mu kukhalapo kwa anthu onse opanda ungwiro, ndipo chotero ogonjera ku kufooka konga ngati kubadwa wakhungu. Kufooka kumeneku mwa munthu tsopano kukupereka mwaŵi kaamba ka Yesu kuwonetsera ntchito za Mulungu.
Yesu akugogomezera kufulumira kwa kuchita ntchito zimenezi. “Tiyenera kugwira ntchito za iye wondituma ine koma pokhala pali masana,” iye akutero. “Ukudza usiku woti palibe munthu angakhoze kugwira ntchito. Pakukhala ine m’dziko lapansi, ndiri kuwunika kwa dziko lapansi.” Posachedwapo imfa ya Yesu idzamuponya iye mu mdima wa manda kumene iye sangakhoze kuchita chirichonse. Pa nthaŵi ino, iye ali magwero a kuwunika ku dziko.
Pambuyo pa kunena zinthu zimenezi, Yesu alavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Apaka limeneli m’maso mwa munthu wakhunguyo ndi kunena kuti: “Muka, kasambe mthamanda la Siloyamu.” Munthuyo alabadira. Ndipo pamene achita tero, iye akhoza kuwona! Iye asangalala chotani nanga pa kubwerera kwake, akumawona kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wake!
Anansi ndi ena omwe amadziŵa iye adabwitsidwa. “Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?” iwo akufunsa tero. “Ndi iyeyu,” ena akuyankha tero. Koma ena sakukhulupirira icho: “Koma afanana naye.” Komabe munthuyu akunena kuti: “Ndine amene.”
“Nanga maso ako anatseguka bwanji?” anthuwo akufuna kudziwa.
“Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati kwa ine, ‘Muka ku Siloyamu kasambe.’ Chifukwa chake ndinachoka ndipo mmene ndinasamba ndinapenya.”
“Ali kuti iyeyu?” iwo akufunsa tero.
“Sindidziŵa ine,” iye akuyankha tero.
Anthuwo tsopano atsogoza munthu yemwe anali wakhungu pa nthaŵi imodzi kwa atsogoleri awo achipembedzo, Afarisi. Awanso ayamba kumufunsa iye mmene iye anawonera. “Anapaka thope m’maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndinapenya,” mwamunayo akulongosola.
Ndithudi, Afarisi afunikira kusangalala ndi wopemphapempha wochiritsidwayo! Koma m’malomwake iwo akukana Yesu. “Munthuyu sachokera kwa Mulungu,” iwo akunena tero. Nchifukwa ninji iwo akunena chimenechi? “Chifukwa sasunga Sabata.” Ndipo komabe Afarisi ena adabwitsidwa: “Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere?” Chotero pali kugawanikana pakati pawo.
Chotero, afunsa munthuyo: “Iwe unenanji za iye, popeza anakutsegulira maso ako?”
“Ali mneneri,” iye akuyankha tero.
Afarisi akukana kukhulupirira chimenechi. Iwo ali okhutiritsidwa kuti pafunikira kukhala kuvomerezana kwa chinsinsi pakati pa Yesu ndi munthu ameneyu kuti apusitse anthu. Chotero kuti athetse nkhaniyo, iwo aitana makolo a wopemphapemphayo ndi cholinga chofuna kuwafunsa iwo. Yohane 8:59; 9:1-18.
◆ Kodi nchiyani chimene chinali cha thayo kaamba ka khungu la munthuyo ndipo nchiyani chimene sichinali?
◆ Kodi nchiyani chimene chiri usiku pamene munthu aliyense sangagwire ntchito?
◆ Pamene munthuyo wachiritsidwa, kodi nchiyani chimene chiri chotulukapo kwa omwe amamdziŵa iye?
◆ Ndimotani mmene Afarisi anagawanikirana pa kuchiritsidwa kwa munthuyo?