Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 9/15 tsamba 28-30
  • Akristu—Olimba Komabe Osinthika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu—Olimba Komabe Osinthika
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Mungakhale Olimba
  • Pamene Mungakhale Osinthika
  • Akulu​—Olimba komabe Osinthika
  • Kulitsani Mkhalidwe wa Kulolera
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yololera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Mverani Atsogoleri
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Pitirizani Kusunga Amuna Oterowo Okondedwa”
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 9/15 tsamba 28-30

Akristu​—Olimba Komabe Osinthika

MTENGO wa oak wa ulemerero uli chithunzi chenicheni cha mphamvu. Pamene mphepo yamphamvu iwomba, iwo kaŵirikaŵiri umakhala ndi vuto lochepera pochirimika ku iyo. Pamene kuli kwakuti tsinde la mtengo wa oak limapulumuka mikuntho yambiri chifukwa cha mphamvu yake ndi kusasinthika koyerekezera kapena kulimba, udzu waung’ono nawonso umapulumuka koma kaamba ka chifukwa chosiyana. Chinsinsi chake? Kusinthika. Iwo umakhota koma sumathyoka pansi pa mphamvu ya mphepo.

Kusinthika kapena kusasinthika​—nchiti, chotero, chimene chiri chofunika koposa? M’chenicheni, Mkristu amafunikira m’sakanizo wa zonse ziŵirizo. Komabe, kulinganizika kwa kulimba ndi kusinthika ntahŵi zina kungakhale kukusoweka ngakhale pakati pa anthu ena a Mulungu. Iwo ali ndi maprinsipulo apamwamba, koma ochepa amayedzamira ku kusakhoterera. Ena ali onga ngati ‘bango lokankhidwa ndi mphepo.’ (Mateyu 11:7) Iwo amagonjera ku zitsenderezo ndi zisonkhezero za dziko iri loipa. Kapena iwo angakhale olekerera ku nsonga ya kukhala ovomera zirizonse.

Monga mmene Solomo ananenera: “Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake.” (Mlaliki 3:1) Ndiliti, chotero, imene iri nthaŵi ya kukhala wolimba ndipo ndi iti imene iri nthaŵi ya kukhala wosinthika?

Pamene Mungakhale Olimba

Kamodzi, Mfumu Sauli wa Israyeli analamulidwa kotheratu kuti: “Muka tsopano, nukanthe Amaleki [mtundu wa udani] nuwononge konse konse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe, mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng’ombe ndi nkhosa, ngamila ndi buru.” (1 Samueli 15:3) Amaleki anali ndi mbiri ya kutsutsa ponse paŵiri Mulungu ndi anthu ake ndipo chotero anayenera kuwonongedwa kotheratu. (Deuteronomo 25:17-19) Ngakhale kuli tero, “Sauli ndi athu anasunga wamoyo Agagi [mfumu ya Amaleki] ndi nkhosa zokometsetsa ndi ng’ombe . . . , ndipo sanafune kuziwononga.” Kukhotetsa malamulo kwa Sauli sikunali kolandirika kwa Yehova. “Tawonani!” analengeza mneneri Samueli, “Kumvera ndiko kokoma kuposa nsembe.”​—1 Samueli 15:9-22.

Phunziro mu ichi liri lomvekera: Sipangakhale kusinthika pamene chibwera ku kumvera Mulungu. “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu,” anatero mtumwi Yohane, “kuti tisunge malamulo ake [a Mulungu]; ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Chokumana nacho cha Sadreki, Miseki, ndi Abedinego chimachitira chitsanzo kuti ndi ku utali wotani umene atumiki a Mulungu ayenera kukhala ofunitsitsa kufika m’kusonyeza chimvero chimenechi. Iwo anakana kulambira fano limene mfumu ya Chibabulo Nebukadinezara analiimika. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti lamulo la Mulungu momvekera lintsutsa kulambira mafano. (Eksodo 20:4-6) Iwo sanalingalire kuti mikhalidweyo inayeneretsa kukhotetsa lamulo laumulungu limeneli. M’malomwake, iwo mosagonjera anasankha imfa kuposa kusamvera.​—Danieli 3:16-18.

Akristu ambiri ali ndi mavuto ochepera m’kugonjera ku malamulo olongosoledwa bwino a Baibulo. Koma Akritsu akuuzidwa kuti: “Mverani atsogoleri anu.” (Ahebri 13:17) Akulu mu mpingo angapereke nthaŵi zokhazikika kaamba ka mpingo kukumana kaamba ka utimiki wa m’munda. Kapena iwo angalunjikitse kuti zipangizo za Nyumba ya Ufumu ziyenera kugwiritsiridwa ntchito m’njira ina yake. Zowona, palibe lemba la Baibulo lomwe limanena mmene thermostat iyenera kusinthidwira kapena ndani amene ayenera kuchita masinthidwe oterowo. Komba, pamene akulu apanga zosankha zoterozo, kodi sichikakhala chabwino kugwirizana nawo?

Mofananamo, mwamuna angapange zosankha zosiyanasiyana kaamba ka banja lake. Mkazi Wachikristu moyenerera sangavomerezane ndi chiŵruzo chake m’njira ina yake, koma iye amafuna kumvera “lamulo la mwamuna wake.” (Aroma 7:2) Chimvero kwa akulu, amuna, makolo, ndi olemba ntchito sichiyenera kuikidwa pambali m’dzina la kusinthika.​—Akolose 3:18-24.

Pamene Mungakhale Osinthika

Mosasamala kanthu za chimenecho, palinso ntahŵ ya kukhala osinthika. Mtumwi Paulo anasonyeza ichi pamene iye ananena kuti: “Kufatsa kanu kuzindikirike ndi anthu onse.” (Afilipi 4:5) Liwu la Chigriki limene Paulo anagwiritsira ntchito pano limathantauza “osati kuwumirira pa lemba la lamulo; limalongosola kulingalira kumene kumayang’ana ‘mwa umunthu ndipo molingalirika pa nsonga za nkhaniyo.’” (W. E. Vine, An Expository Dictionary of New Testament Words) Kufatsa nthaŵi zonse kuli nkhani ya kukhala wofunitsitsa kusinthira ku mikhalidwe yomwe iripo.

Mwachitsanzo, m’mishonale wotumikira m’dziko lachilendo mwamsanga angazindikire kuti malamulo a kumaloko a makhalidwe ali osiyana ndi aja a kudziko mu limene iye analeredwa. Koma ngati iye anayalanyaza njira za anthu a kumaloko ndi kukana kupanga masinthidwe ena ake, kodi utumiki wake ukakhala wokhutiritsa motani? Chotero iye mwanzeru amasinthira ku njira zopindulitsa za mwambo watsopano.​—1 Akorinto 9:19-23.

Mosangalatsa, mwamsanga pambuyo potchula akazi aŵiri mu mpingo omwe anali ndi zovuta zaumwini, Paulo analimbikitsa Akristu a ku Filipi kukhala ofatsa. (Afilipi 4:2-5) Ngakhale kuti Paulo sakutiuza ife mtundu wa mkangano wawo, kusoweka kwa kufatsa kaŵirikaŵiri kuli pa maziko a unansi wokwinjika. Palibe wina aliyense amene amadzimva womasuka pakati pa winawake wosuliza kapena wolamulira mopambanitsa. “Usapambanitse kukhala wolungama,” akuchenjeza tero Solomo, “usakhale wanzeru koposa. Bwanji ufuna kudziwononga wekha?”​—Mlaliki 7:16.

Akristu ayenera kupanga mpata kaamba ka kupanda ungwiro kwa ena. Chiri chabwino chotani nanga pamene tiyesera kuyang’ana pa nkhanizo kuchokera ku lingaliro la munthu wina! Momvetsa chisoni, ngakhale ndi tero, Akristu ena mu Korinto wakale anali odera nkhaŵa mopambanitsa ponena za “kuyenera” kwawo kwaumwini kotero kuti iwo anakhoterera ku kutenga akhulupiriri anzawo ku bwalo la milandu. Mwa kutulutsa mavuto awo pakati pa osakhulupirira, iwo sanali kubweretsa kokha chitonzo pa mpingo komanso kukulitsa udani pakati pa iwo eni.​—1 Akorinto 6:1-6.

Paulo chotero analimbikitsa Akristu olakwiridwa a mu Korinto kukhala ndi mkhalidwe wogonjera. Iye anafulumiza kuti: “Koma, pamenepo, pali chosowa konse konse mwa inu kuti muli nayo mirandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsyidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?” (1 Akorinto 6:7) Mkristu amalingalira icho kukhala chopindulitsa kusungirira maunansi abwino ndi abale ndi alongo ake auzimu.

Kukhala wodzichepetsa kuli mwapadera koyenerera kaamba ka awo okhala ndi ulamuliro. Mwachitsanzo, makolo angaike nthaŵi kaamba ka imene ana awo amuna ndi akazi ayenera kukhala kunyumba madzulo. Koma tangolingalirani kuti mwana wapempha kupatulidwa ku lamulolo ku chochitika chimodzi? Kodi icho sichikakhala choyenerera kulingalirapo mikhalidwe yachindunji yokhudzidwayo? Ndipo bwanji ponena za akulu Achikristu? Kodi kufatsa sikuli umodzi wa ziyeneretso zawo? (1 Timoteo 3:3) Inde. Koma ndi liti ndipo ndimotani mmene ayenera kusonyezera mkhalidwe umenewu?

Akulu​—Olimba komabe Osinthika

Mtumwi Petro kamodzi anasiyanitsa amuna “ofatsa” ndi “ovuta kusangalatsa.” (1 Petro 2:18, NW) Mkulu angapereke malingaliro kuthandiza mbale kuwongolera kuthekera kwake kwa kulankhula. Koma ngati mkuluyo agwiritsira ntchito muyezo wolimba kwambiri ndipo alephera kuika m’kulingalira maphunziro, kuthekera, ndi mikhalidwe ya mbaleyo, nchiyani chomwe chingachitike? Mbaleyo angakane uphunguwo kapena kukhala wokhumudwitsidwa kwambiri, akumamaliza kuti akulu ali “ovuta kusangalatsa.”

Akulu ayeneranso kukhala osinthika ponena za kugwiritsira ntchito malamulo osiyanasiyana mu mpingo. Iwo sayenera nkomwe kulola malamulo ‘kupangitsa mawu a Mulungu kukhala achabe’ kwa kupatsa malamulo oterowo mphamvu yokulira kuposa malamulo angwiro a Mawu a Yehova.​—Mateyu 15:6; 23:23.

Chiri choyenerera kwa akulu kukhala osinthika pamene maprinsipulo a Malemba sakuvulazidwa ndi kusinthidwa koteroko. Mwachitsanzo, iwo angadziŵe kuti pa misonkhano yaikulu, yokhala ndi anthu ambiri, kusungidwa kwa mipando sikumalimbikitsidwa mokulira. Koma kodi lamulo loterolo liyenera kukakamizidwa mu mpingo waung’ono kumene mipando iri yambiri? Kapena akulu angadzimve kuti mwachisawawa mtundu winawake wa zovala​—monga ngati jaketi ndi tayi kaamba ka amuna​—uli woyenerera kaamba ka kulalikira kwa ku khomo ndi khomo. Mmenemo ndi mmene zinaliri mu mpingo wina wa m’dziko la Kum’mwera kwa America. Mosasamala kanthu za chimenecho, mkulu kumeneko anazindikira kuti mwamuna wachichepere sanali kupita m’kugawana mbiri yabwino ndi ena. Chifukwa chake? Iye sakanatha kugula jaketi ndi tayi. Mkuluyo anamaliza kuti kusinthika kunali koyenerera ndipo chotero analimbikitsa mwamuna wachichepereyo kuyamba kugawana chikhulupiriro chake ndi ena.

Kusintha kuyeneranso kusonyezedwa m’kusamalira nkhani za chiŵeruzo mu mpingo. Ngakhale kuti kuchita cholakwa kungayeneretse kuchotsedwa kwa wochita cholakwayo, bwanji ngati kulapa kwasonyezedwa? Yehova anakhazikitsa dongosolo loyenerera m’kuchita kwake ndi anthu a ku Nineve. Mulungu anauza Yona kuti: “Atsala masiku makumi anayi, ndipo Nineve adzapasuka.” Komabe, pamene anthuwo anasonyeza kulapa, Yehova sanawumirire pa kutsatira chiwonongeko cholengezedwacho. Iye anazindikira kuti mikhalidwe inasintha. (Yona 3:4, 10) Mofananamo, akulu ayenera kukondwera ‘m’kukhululukira m’njira yokulira’ kumene kuli umboni wowonekera wa kulapa kowona.​—Yesaya 55:7.

Kusungirira kulinganizika pakati pa kulimba ndi kusinthika sikuli kopepuka. Anthu opanda ungwiro mwachibadwa amawoneka kukhala okhoterera kupita ku kupambanitsa. Koma Akrsitu omwe amakalamira kukhala olimba komabe osinthika adzafupidwa molemelera. Chifukwa iwo amayesera kukhala osinthika, iwo adzasangalala ndi maunansi abwino ndi ena ndipo adzapewa tsoka lokulira la malingaliro. Ndiponso, chifukwa chakuti akulu oikidwa ali olimba, osasinthika m’ntchito zabwino monga osunga umphumphu, iwo amaika chitsanzo chabwino chomwe chimapindulitsa chidaliro ndi chigwirizano cha mpingo wonse, pamene onse apitirizabe pamodzi ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.​—Isaiah 32:2; 1 Corinthians 15:58.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena