Ngati Tichita Chifuniro cha Mulungu, Iye Sadzatileka Ife Nkomwe
Monga momwe yalongosoledwa ndi Grete Schmidt
NDINABADWIRA mu Budapest, Hungary, mu 1915. Nkhondo yoyamba ya dziko inali mkati, ndipo atate wanga anali kutsogolo ndi gulu lankhondo la Austria-Hungary. Pamene iwo anafa chaka chimodzi pambuyo pake, Amayi anabwerera ndi ine ku Yugoslavia, kumene achibale awo anakakhala.
Popeza Amayi sanakwatiwenso, iwo anayenera kupeza ntchito, chotero anaikiza kuleredwa kwanga kwa akulu awo. Azakhali anga anali ndi munda chifupifupi makilomita asanu kuchokera ku mzinda wa Maribor kumpoto kwa Yugoslavia. Kumeneko ndinathera zaka zambiri zachimwemwe, nthaŵi zonse ndikumayang’ana kutsogolo ku Sande pamene Amayi akabwera kuchokera ku Maribor kudzacheza. Pa nthaŵi imodzimodziyo, ndinakulitsa chikhumbo chokulira kaamba ka atate.
Unansi ndi Atate
Achibale anga anali Akatolika, ndipo popeza kumwamba ndi helo zimachita mbali yokulira m’chipembedzo cha Chikatolika, kuwombana kunabuka m’maganizo mwanga. Sindinadzimve kukhala woyenerera mokwanira kaamba ka kumwamba, koma ndinadzimva kuti sindinali woipa kwenikweni kuperekedwa ku helo. Ndinalankhula ponena za vuto limeneli ndi aliyense, kuchokera kwa agogo anga akazi kufika kwa wansembe wa m’mudzimo.
Amayi anali amene ndinawavutitsa kwambiri. Chotero pambuyo pa miyezi ingapo, iwo anandipatsa ine kabukhu mu chiSlovenian, Kodi Akufa Ali Kuti?, komwe anakapeza mu mzinda. Amayi anali asanakaŵerenge iko iwo eni, koma analingalira kuti kangayankhe mafunso anga.
Palibe ndi kalelonse m’moyo wanga wonse pamene ndinaŵerengapo chofalitsidwa chirichonse mobwerezabwereza monga kabukhu kameneko! Iko sikanayankhe kokha mafunso anga ponena za moyo ndi imfa komanso kanandisonyeza ine mmene ndingakulitsire unansi wathithithi ndi Atate wanga wakumwamba. Ndinaitanitsa timabukhu tisanu ndi cholinga chofuna kutigawira ito pa tchalitchi.
M’mudzi mwathu akazi anapezeka ku mautumiki a tchalitchi pa Sande, koma amuna anakhala kunja akumakambitsirana nkhani zawo zokondeka, zoweta ndi ulimi. Chotero, pamene wansembe anali kulalikira kwa akazi m’tchalitchi, ndinalalikira kwa amunawo kunja. Ndinali kokha ndi zaka 15, ndipo iwo mwachiwonekere anasangalala ndi kutenthedwa maganizo kwanga kwa uchichepere, popeza kuti iwo analipira kaamba ka timabukhuto, ndipo ndinagwiritsira ntchito zoperekazo kupeza zogawira zina.
Wansembeyo mwamsanga anadziŵa za zochita zanga ndipo anabwera kudzalankhula ndi azakhali anga. Sande yotsatira, iye anachenjeza kuchokera pa guwa lansembe: “Ndithudi, palibe wina aliyense m’mudzi wathu amene angakhale wopusa kukhulupirira nkhani za wachichepere wa zaka za pakati pa 13 ndi 19.” Monga chotulukapo chake, aliyense m’mudzimo anandiwukira ine. Ngakhale azakhali anga anachita manyazi ndi kudziŵitsa amayi anga kuti sakandisunganso ine.
Ndinadzimvadi kukhala wotaidwa, koma m’pemphero kwa Yehova, ndinapeza chitonthozo ndi kupezanso mphamvu. Ndinasamukira kwa amayi anga mu Maribor, ndipo tinali ndi nthaŵi ya chimwemwe pamodzi. Ngakhale kuti iwo sanagawane ndi zikondwerero zanga zauzimu, iwo anandilola ine kupezeka pa misonkhano ya mpingo waung’ono kumeneko. Pa August 15, 1931, ndinachitira chizindikiro kudzipereka kwanga kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi.
Ku chisoni changa chachikulu, Amayi wanga anadwala mwadzidzidzi ndi kumwalira milungu yoŵerengeka pambuyo pake. Mawu awo omalizira anatsala ozikidwa m’chikumbukiro changa: “Gretel, wokondedwa wanga, mamatira ku chikhulupiriro chako. Ndiri wotsimikizira kuti chiri chowonadi.” Pambuyo pa imfa yawo, kachiŵirinso ndinadzimva kukhala wotaidwa kotheratu, komabe unansi wanga ndi Atate wathu wa kumwamba unandichirikiza ine.
Okwatirana aŵiri omwe analibe ana a iwo eni ananditenga ine, ndipo ndinatumikira monga wophunzira ntchito mu shopu yosoka zovala imene mkaziyo anali kuitsogoza. Mwakuthupi ndinali bwinopo, koma chikhumbo cha mtima wanga chinali kutumikira Mulungu nthaŵi yonse. Mu mpingo wathu waung’ono mu Maribor, onse anali okhutiritsidwa kuti nthaŵi yotsala kaamba ka dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu inali yaifupi. (1 Akorinto 7:29) Mwachinsinsi ndinafunsa Yehova m’mapemphero anga kuimitsa kuloŵereramo kwake kufikira nditamaliza kuphunzira ntchito kwanga. Ndinamaliza pa June 15, 1933, ndipo tsiku lotsatira lenilenilo, ndinachoka kunyumba ndi cholinga chofuna kuyamba upainiya! M’chiyang’aniro cha uchichepere wanga—ndinali kokha ndi zaka 17—ngakhale abale ena anayesera kundiletsa ine, koma ndinali wogamulapo.
Masiku Oyambirira a Upainiya
Gawo langa loyamba linali Zagreb, mzinda wa chifupifupi nzika 200,000 osati kutali ndi Maribor. Mpingowo unali kokha ndi ofalitsa asanu ndi mmodzi. Ndinaphunzira zochulukira mwa kugwira ntchito ndi Mbale Tuc̀ek, mpainiya woyambirira weniweni mu Yugoslavia. Pambuyo pake, ndinachita upainiya ndekha kwa chifupifupi chaka chimodzi. Mwa pang’onopang’ono, ngakhale kuli tero, apainiya owonjezereka anabwera kuchokera ku Germany, popeza kuti ntchito yolalikira posachedwapa inali italetsedwa kumeneko ndi boma la Nazi.
Ndinathandiza ochulukira a apainiyawo mwa kutumikira monga wotembenuza wawo. Kugwira ntchito ndi Akristu achikulire amenewa chinali chokumana nacho cha mtengo wapatali kwa ine. Ndinawonjezeka m’chidziŵitso ndi kumvetsetsa, ndipo chiyamikiro changa chinakula mokhazikika kaamba ka mwaŵi wa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu.
M’kupita kwa nthaŵi, tinakhala gulu losangalatsa la apainiya 20 kutumikira mu Balkan States. Kukalamira kwathu kofala kwa kudziŵikitsa Mawu a Mulungu kunatigwirizanitsa ife pamodzi, aliyense wokonzekera kuthandiza mnzake m’nthaŵi ya kusowa. Tonsefe tinasonkhezeredwa ndi kufunitsitsa kopezeka kokha pakati pa anthu a Mulungu. “Chomangira” chapadera chimenechi, chikondi, chimapitiriza pakati pa awo a m’gululo omwe adakali ndi moyo lerolino.—Akolose 3:14.
Moyo wa mpainiya uli wodzazidwa ndi zokumana nazo ndipo umapereka zosiyanasiyana monga mmene irili mitambo m’thambo. Tinadzimva olemeretsedwa kupyolera m’chokumana nacho cha mtengo wapatali cha kufikira pa kudziŵa maiko ndi anthu omwe kalelo anali osadziŵika kwa ife, kuphatikizapo miyambo yawo ndi njira zawo za moyo. Pambali pa icho, tinakumanizana ndi mmene Yehova amasamalira kaamba ka atumiki ake okhulupirika, monga mmene Paulo akutitsimikizirira ife pa Aefeso 3:20: ‘Kwa iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife.’
Chisamaliro chachikondi cha Yehova chinachitiridwa chitsanzo pamene Mbale Honegger anatichezera ife kuchokera ku Switzerland ndipo anawona kuti tinayenera kuyenda makilomita 40 kukafikira midzi ya kunja yozungulira Zagreb. Iye anawona kuti tinachotsa nsapato zathu ndi kuzikoloŵeka izo pa mapewa athu mwamsanga pamene tinachoka mu mzindawo ndi cholinga chofuna kutetezera nsapatozo. Chotero iye anatigulira ife njinga 12, ngakhale ndi tero, monga mmene iye pambuyo pake ananenera, chinatenga ndalama zonse zimene iye anali nazo! Yehova motsimikizirikadi amafulumiza mitima ya owongoka. Njingazo, monga mphatso yochokera kumwamba, zinatumikira monga mabwenzi athu okhulupirika mkati mwa zaka 25 za utumiki wa upainiya.
Kamodzi, Willi ndi Elisabeth Wilke ndi ine tinafika pa mudzi waung’ono wa Croatia, kumene aliyense wa ife anagwira ntchito payekha—kuchokera kunja kulinga pakati pa mudziwo. Tinali kugawira kabukhu kakuti Righteous Ruler, komwe kanasonyeza Yesu Kristu pa tsamba loyambirira. Kokha chaka chimodzi pasadakhale, mu 1934, mfumu ya ku Yugoslavia, Alexander, anaphedwa, ndipo mwana wake Peter anayenera kumulowa iye m’malo pa mpando wachifumu. Ngakhale kuli tero, anthu a m’mudzimo analakalaka boma lodzilamulira m’malo mwa kukhala ndi mfumu kuchokera ku Serbia (kum’mwera kwa Yugoslavia).
Patapita maora angapo a kulalikira, kufuula kozizwitsidwa kunamveka kuchokera ku mbali ya mudziwo. Kumeneko, Mbale Wilke ndi ine tinapeza Mlongo Wilke atazunguliridwa ndi gulu la chifupifupi amuna ndi akazi 20, ena ali okonzekeretsedwa ndi zikwakwa, ena ali otanganitsidwa kutentha timabukhu tathu. Mlongo Wilke sanali wokhoza kulankhula chinenerocho mokwanira bwino kuthetsa kusakhulupirira kwa anthu a m’mudziwo.
“Azimayi ndi azibambo,” ndinafuula tero, “kodi nchiyani chimene mukuchita?”
“Sitikufuna Mfumu Peter!” iwo anayankha chifupifupi m’liwu limodzi.
“Nafenso sitikufuna,” ndinayankha tero.
Atadabwitsidwa, anthuwo analoza ku chithunzithunzicho pa kabukhuko ndi kufunsa kuti, “Chotero nchifukwa ninji mukupanga kubukitsa kaamba ka iye?” Iwo anaganiza molakwika kuti Yesu Kristu anali Mfumu Peter!
Kusamvanako kunathetsedwa, ndipo umboni wokwanira ponena za Mfumu Yesu Kristu unaperekedwa. Ena omwe anatentha timabukhu tawo tsopano anafuna tatsopano. Tinasiya mudziwo mu mkhalidwe wachimwemwe, tikumadzimva kuti dzanja lotetezera la Yehova linali pa ife.
Pambuyo pake tinafutukula kulalikira kwathu kufika ku Bosnia, mbali yapakati ya Yugoslavia. Kumeneko, chifupifupi theka la chiŵerengero cha anthuwo anali Asilamu, ndipo kachiŵirinso tinakumanizana ndi miyambo yatsopano limodzinso ndi unyinji wa kukhulupirira malaulo. M’midzimo, anthu anali asanawonepo mkazi atakwera njinga, chotero kufika kwathu kunali kodabwitsa, kukumadzutsa chikhumbo cha kufuna kudziŵa. Atsogoleri a chipembedzo anafalitsa mphekesera yakuti mkazi wokwera pa njingayo anabweretsa tsoka pa mudzi. Pambuyo pa chimenecho tinasiya njinga zathu kunja kwa mudziwo ndi kulowa tikuyenda pansi.
Popeza kuti mabukhu athu tsopano anabwera pansi pa chiletso, apolisi kaŵirikaŵiri anatigwira ife. Kaŵirikaŵiri, tinalamulidwa kuchoka m’gawolo. Apolisi aŵiri ankatiperekeza ife kupita ku malire, mtunda wa makilomita 50 kufika ku 100. Iwo anadabwitsidwa kuti tinali odziŵa kupalasa njinga, okhoza kuyenda limodzi nawo mosasamala kanthu za chenicheni chakuti tinali titanyamula zovala zathu zonse ndi mabukhu ndi sitovu ya paraffin yaing’ono. Otiperekeza athu nthaŵi zonse anali achimwemwe kupeza malo odyera m’mphepete mwa njirayo, ndipo kaŵirikaŵiri anali kutiitana ife kaamba ka chakumwa kapena ngakhale chakudya. Tinasangalala ndi zochitikazi, popeza kuti ndalama zathu zochepera sizinatilole kaamba ka zowonjezereka zoterozo. Ndithudi, tinagwira mwaŵi wa kuwauza iwo ponena za chiyembekezo chathu, ndipo kaŵirikaŵiri ankalandira zina za zofalitsidwa “zoletsedwazo.” Kaŵirikaŵiri, tinalekana mu mkhalidwe wabwino.
Kenaka chinafika chaka cha 1936. Tinkalalikira mu Serbia pamene mbiri inatifikira kuti msonkhano wa mitundu yonse ukachitidwa mu Lucerne, Switzerland, mu September. Basi yapadera inayenera kuchoka ku Maribor, koma kumeneko kunali makilomita 700 kuchokera kumene tinali—ulendo wautali wa pa njinga! Mosasamala kanthu za icho, tinayamba kusunga ndalama zathu ndipo, pambuyo pake m’chakacho, tinapanga ulendowo.
Tinkafunsa chilolezo kuchokera kwa alimi kukhala usiku m’nyumba zawo zosungira zakudya za ng’ombe m’malo molipira kaamba ka chipinda panyumba ya alendo. M’mawa, tinkafunsa ngati tingaguleko wina wa mkaka wawo, koma kaŵirikaŵiri ankatipatsa ife kwaulere ndipo nthaŵi zina kuwonjezera chakudya cha m’mawa chokwanira. Tinasonyezedwa kukoma mtima kwa umunthu kochulukira, ndipo ichi chinakhala mbali yachimwemwe ya zikumbutso za upainiya wathu.
Tisanachoke ku Maribor kupita ku Lucerne, apainiya owonjezereka anafika kuchokera ku Germany. Pakati pawo panali Alfred Schmidt, yemwe anatumikira zaka zisanu ndi zitatu mu Beteli pa Magdeburg, Germany. Chaka chimodzi pambuyo pake ndinakhala mkazi wake.
Chifupifupi apainiya onse mu Yugoslavia anali okhoza kupezeka pa msonkhano mu Lucerne. Unali msonkhano wanga woyambirira, ndipo ndinali wosangalatsidwa ndi chikondi ndi chisamaliro chosonyezedwa ndi abale a chiSwiss, pambali pa kukhala osangalatsidwa ndi kukongola kwa mzinda wa Lucerne. Ndinadziŵa zochepera kuti zaka 20 pambuyo pake, ndidzachita upainiya kumeneko!
Kugwira Ntchito Pansi pa Ziletso
Kubwerera kuchokera ku Switzerland wokongola kupita ku Yugoslavia, mwamsanga tinayamba kukumana ndi chizunzo chenicheni. Tinagwidwa ndi kuikidwa m’ndende yaikulu mu Belgrade. Mbale yemwe anali ndi thayo la ntchito mu Yugoslavia anapempha chilolezo cha kutichezera ife, koma ichi chinakanizidwa. Ngakhale kuli tero, iye analankhula ndi wosunga ndendeyo m’liwu lokwezeka loterolo kotero kuti tinkamva iye, ndipo kumveka kwa liwu lake lenileni kunali chilimbikitso chokulira kwa ife.
Pambuyo pa masiku angapo, tinatengedwa omangidwa kupita ku malire a Hungary; mabukhu athu ndi ndalama zathu zinalandidwa. Chotero, tinafika mu Budapest opanda ndalama nkomwe, koma ndi nsabwe zambiri zikumamatira kwa ife monga chokumbutsa kuchokera ku ndende. Mwamsanga tinakumana ndi apainiya ena ndi kugawana nawo mu ntchito yolalikira kumeneko.
Lolemba lirilonse apainiyafe mu Budapest tinakumana pa malo osambira a chiTurkish, ndipo pamene tinali kusamalira matupi athu, alongo ndi abale mosiyana anasangalala ndi “kusinthana kwa chilimbikitso . . . aliyense kupyolera mwa chilimbikitso cha mnzake.” (Aroma 1:12, NW) Kukumana mokhazikika kunatumikiranso monga chofufuzira ngati winawake anadwala kapena anaikidwa m’ndende.
Tinali tisanazolowerane kwenikweni ndi malo otizinga atsopano amene, pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi, chilolezo chathu cha kukhala mu Hungary chinatha. Pa nthaŵiyo, Alfred ndi ine tinali titakwatirana. Tsopano tinalandira malangizo kupeza chilolezo chopitira ku Bulgaria. Okwatirana achipainiya kumeneko anali atathamangitsidwa, ndipo timabukhu zikwi khumi tomwe anaorda tinali titakonzeka pa fakitale yosindikiza yaing’ono mu Sofia. Mabukhu a okwatiranawo anali atatenthedwa mwapoyera, chotero tinadziŵa mtundu wa kulandiridwa womwe tikayembekezera.
Pomalizira pake tinapeza chilolezo cha miyezi itatu kupita ku Bulgaria. Tinali kudutsa Yugoslavia usiku, ndipo mbale wa thayo anakumana nafe pa malo okhazikitsidwa ndi ndalama zokagulira timabukhuto. Pomalizira pake, tinafika mwachisungiko mu Sofia ndi kupeza chipinda chabwino.
Sofia unali mzinda wamakono wokhala ndi chifupifupi nzika 300,000, koma kunalibe Mboni kumeneko. Tsiku limodzi pambuyo pa kufika kwathu, tinapita ku malo osindikizirawo. Mwiniwakeyo anali atamva za kuletsedwa kwa mabukhu athu ndi kuthamangitsidwa m’dziko kwa okwatiranawo omwe anaorda timabukhuto, chotero pamene iye anamva kuti tinabwera kudzagula iwo, iye anali pafupi kutikupatira ife. Tinalongedza timabukhuto m’matumba opanda kanthu ndi kuyenda kudutsa apolisi ambiri, amene, ndiri wachimwemwe kunena kuti, sanathe kumva kufulumira kwa kugunda kwa mtima wathu!
Vuto lathu lotsatira linali kumene tikasunga timabukhuto ndi mmene tikagawirira unyinji wokulira woterowo mu kokha miyezi itatu. Ndinali m’chenicheni wochititsidwa mantha ndi mulu wa timabukhuto! Ndinali ndisanawonepo ambiri chotero. Koma kachiŵirinso Yehova anali Mthandizi wathu. Tinali ndi chipambano chokulira, kugawira kufika ku 140 pa tsiku, ndipo m’milungu yoŵerengeka, Mbale ndi Mlongo Wilke anafika kudzatithandiza.
Tsiku lina, ngakhale kuli tero, zinthu zinali pafupi kuipa. Ndinali kuchitira umboni m’gawo la malonda kumene pa khomo paliponse panali chikwangwani cha mkuwa ndi mawu akuti Dr. Uje ndi Uje. Patapita chifupifupi maora aŵiri, ndinakumana ndi mwamuna wachikulire yemwe anandiyang’ana mosamalitsa ndi kusakhulupirira. Anandifunsa ngati ndinadziŵa kumene ndinali.
“Sindidziŵa kwenikweni chimene nyumbayi iri, koma ndawona kuti maloya onse abwino akuwoneka kukhala anaphatikiza maofesi awo pano,” ndinayankha tero.
“Uli mu Bungwe lowona za m’Dziko,” iye anayankha tero.
Ngakhale kuti mtima wanga unatsala pang’ono kuima, mwabata ndinayankha kuti: “Eya, chimenecho ndicho chifukwa chake amuna onsewa anali aubwenzi chotero kwa ine!” Ndemanga imeneyi inafewetsa mkhalidwe wake, ndipo iye anandibwezera pasiporti yanga pambuyo pa kuifufuza iyo mosamalitsa. Ndinachoka ndi kuusa moyo kwa mpumulo, woyamikira kwa Yehova kaamba ka chinjirizo lake.
Potsirizira pake, timabukhu tonse tinagawiridwa, ndipo tsiku linafika kaamba ka ife kuchoka mu “dziko la maluŵa a rose,” Bulgaria. Chinali chovuta kusiya anthu aubwenzi oterowo, koma chikumbukiro chawo chinakhaladi chozama m’mitima yathu.
Popeza tinali ndi mapasiporti a chiGerman, tinali okhoza kubwerera ku Yugoslavia, koma tinapatsidwa kokha kukhala kwa nthaŵi yaifupi. Pambuyo pake, ndi cholinga chofuna kupulumuka kumangidwa, tinayenera kugona m’malo osiyanasiyana usiku uliwonse. Tinakhala mwa njira imeneyi kwa chifupifupi miyezi isanu ndi umodzi. Kenaka, mkati mwa theka lomalizira la 1938, tinalandira kalata kuchokera ku ofesi ya Sosaite mu Bern, Switzerland, kutilangiza ife kuyesera kupita ku Switzerland. Gulu lankhondo la Nazi linali litatenga kale Austria, ndipo chitsenderezo cha ndale zadziko chinali kukula. M’chenicheni, boma la Yugoslavia linali litapereka kale ena a apainiya a chiGerman kwa a Nazi.
Chotero mwamuna wanga ndi ine tinayenda mosiyana kupita ku Switzerland, Alfred kudzera njira ya ku Italy ndipo ine kupyolera ku Austria. Tinagwirizananso mwachimwemwe ndipo tinagawiridwa ntchito ku munda wa Sosaite, Chanélaz, ndipo pambuyo pake pa Beteli mu Bern. Ichi chinali chokumana nacho chatsopano kotheratu kwa ine. Tsopano ndinayenera kuphunzira kusunga nyumba m’njira ya chiSwiss, ndipo ndinafikira pa kuyamikira gulu la Yehova kuposa ndi kale lonse.
Mphamvu Yochirikiza ya Yehova
Pambuyo pa kutumikira pa Beteli mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II ndi pambuyo pake, mu 1952 Alfred ndi ine tinalowanso ntchito ya upainiya, ntchito yomwe inawongolera miyoyo yathu. Sitinakhalepo ndi ana a ife eni, koma mkati mwa kupita kwa zaka, talandira zisonyezero zochulukira za chikondi kuchokera kwa ana athu auzimu. Mwachitsanzo, mu February 1975 tinalandira kalata yotsatirayi:
“Ndimakumbukira tsiku limene mwamuna wa tsitsi la imvi, wanzeru anachezera phungu wa Tchalitchi cha Evangelical wowuma khosi ndi kumugawira iye phunziro la Baibulo. Modzisunga ndi mosuliza, banja langa ndi ine tinalandira ndipo kenaka tinasanthula nsonga iriyonse monga mmene anachitira anthu a ku Bereya, kufikira tinayenera kuvomereza kuti munatibweretsera chowonadi. . . . Ndimotani nanga mmene Yehova Mulungu aliridi Atate wachifundo! Kwa iye kupite chitamando ndi ulemu ndi chiyamiko kaamba ka kukoma mtima kwake ndi chifundo. Koma tikuyamikani inunso, okondedwa Alfred ndi Gretel, kuchokera pansi pa mitima yathu, kaamba ka kuleza mtima kopambanitsa komwe munatisonyeza ife. Lolani kuti Yehova molemerera akudalitseni kaamba ka chimenecho. Ife mowona mtima tikuyembekezera kuti adzatipatsanso ife mphamvu ya kupirira.”
Mu November 1975 mwamuna wanga Alfred anamwalira mwadzidzidzi ndi nthenda ya mtima. Kwa zaka 38 tinatumikira Yehova limodzi, kupirira zosangalatsa ndi zokhumudwitsa za upainiya. Ichi chinapanga unansi wathu kukhala wathithithi. Ngakhale kuli tero, ndi imfa yake kudzimva kumene kuja kwa kupereŵera ndi kukhala wotayidwa kunalowereranso mwa ine. Koma mwa kutenga pothaŵirapo mwa Yehova, ndinatonthozedwanso.
Unansi wanga ndi Atate wathu wa kumwamba wandichirikiza ine kupyola zoposa zaka 53 mu utumiki wake wa nthaŵi zonse. Ndipo ziyamikiro zanga zimapitiriza kukhala zija za Yesu Kristu: “Sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi ine.”—Yohane 16:32.
[Chithunzi patsamba 23]
Alfred ndi Frieda Tuc̀ek akuchita upainiya mu Yugoslavia ndi ziwiya zokwanira, mu 1937
[Chithunzi patsamba 25]
Alfred ndi Grete Schmidt akuchita upainiya mu Mostar, gawo la Chisilamu la Yugoslavia, mu 1938
[Chithunzi patsamba 26]