Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 4/15 tsamba 20-23
  • Babulo Wamkulu Azengedwa Mlandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Babulo Wamkulu Azengedwa Mlandu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Babulo Wamakono Asuliza Dzinalo
  • Chifukwa Chimene Timadera Ziphunzitso Zachibabulo
  • Chifukwa Chimene Timakanira Nthanthi Zokana Mulungu
  • Chifukwa Chimene Timadera Zipatso za Babulo Wamkulu
  • Chifukwa Chimene Timatsutsira Mkhalidwe Woipa wa Babulo
  • Chifukwa Chimene Timadera Chigololo Chauzimu cha Babulo
  • Chifukwa Chimene Timanyansidwira Ndi Liwongo la Mwazi la Babulo
  • Babulo Wamkulu Wakugwa Ndipo Woweruzidwa
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuweruza Hule la Makhalidwe Oipa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Mkazi Wachigololo wa Mbiri Yoipa—Kugwa Kwake
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 4/15 tsamba 20-23

Babulo Wamkulu Azengedwa Mlandu

MU MPAMBO wa misonkhano kuzungulira dziko mu 1988-89, mamiliyoni a Mboni za Yehova anapanga chigamulo kulongosola kuda kwawo kwa mkhalidwe wa Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga​—makamaka monga waimiridwa ndi Chikristu cha Dziko. Anthu ena owona mtima angafunse kuti, Kodi kameneko sikaimidwe kolimba mopambanitsa? Ayi, kutalitali! Pamene tiwona mmene aneneri a Irayeli wakale molimba mtima anatsutsira kulambira mafano kwa tsiku lawo ndi mmene Yesu anavumbulira chinyengo cha chipembedzo cha m’nthaŵi yake ndi mawu olimba, ife monga Mboni za Yehova timakhulupirira kuti kaimidwe kameneka kali kolungamitsidwa mokwanira. Iko kali ngakhale kolamulidwa ndi Mulungu.​—Yesaya 24:1-6; Yeremiya 7:16-20; Mateyu 23:9-13, 27, 28, 37-39.

Chotero ndi pamaziko otani omwe timadera mkhalidwe wa Babulo Wamkulu? Kodi ndi umboni wa mbiri yakale wotani umene tiri nawo wa kulephera kwa chipembedzo kulemekeza Mfumu Ambuye wowona wa chilengedwe chaponseponse, Yehova?

Babulo Wamakono Asuliza Dzinalo

Mfumu Ambuye wa chilengedwe chaponseponse sali wopanda dzina. Iye wazidziŵikitsa iyemwini kwa nthaŵi 7,000 m’Baibulo monga Yehova. Iye akupereka kufunika kwakukulu ku dzina lake. Lachitatu la Malamulo Khumi limalongosola kuti: “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.” Ndipo Yesu anawunikira dzina la Atate wake mu Pemphero la Ambuye, akumati, “Dzina lanu liyeretsedwe.”​—Eksodo 20:7; Mateyu 6:9.

Cholembera cha Chikristu cha Dziko m’kulemekeza dzina la Mulungu chiri chosasangalatsa. Ngakhale King James Bible ya 1611 imagwiritsira ntchito dzina la Yehova, lokha ndipo m’kugwirizana, kokha nthaŵi zisanu ndi ziŵiri.a Matembenuzidwe ena achotsa kotheratu dzinalo. Zipembedzo zambiri koposa zimalephera kulilemekeza ilo. M’malomwake, izo zakweza Utatu wawo “woyera” ndipo, mu nkhani zina, Mariya iye wotchedwa Amayi wa Mulungu pamwamba pa Mulungu wa Baibulo. Dzina la mtengo wapatali la Yehova laloledwa kumira kuloŵa mu kusagwiritsidwa ntchito kofananako.b

Mwachiyamikiro, Chisilamu chimazindikira Mulungu mmodzi, amene amatcha Allah, m’chigwirizano ndi bukhu lawo loyera, Koran. Ngakhale kuli tero, iwo samagwiritsira ntchito dzina lake, Yehova, monga mmene linavumbulidwira choyamba m’Baibulo chifupifupi zaka zikwi ziŵiri Koran isanakhaleko. Ahindu amalambira mamiliyoni a milungu ndi milungu yachikazi, koma Yehova sali pakati pawo.

Chodziŵika bwino monga cha mlandu ponena za dzina la Mulungu chiri Chiyuda. Kwa zaka zikwi zingapo, Ayuda adzinenera kukhala anthu a dzina la Mulungu, ndipo komabe chifukwa cha mwambo wawo, iwo achititsa dzina la Mulungu wowona kugwera m’kusagwiritsiridwa ntchito kotheratu.

Chotero, monga mboni za Mfumu Mbuye Yehova, tiyenera kulongosola kunyansidwa kwathu kulinga ku kunyalanyaza kwa dzina loyera la Mulungu ku mbali ya Babulo Wamkulu.

Chifukwa Chimene Timadera Ziphunzitso Zachibabulo

Mamiliyoni angapo a anthu adyeredwa masuku pamutu ndi kusungidwa m’mantha pa maziko a chiphunzitso cha Chibabulo chakuti munthu ali ndi moyo wosafa. Kuchokera ku nthaŵi zakale, chipembedzo chonyenga chadyerera mantha a kuthekera kwa kuzunzidwa kosatha kwa m’moto wa helo pambuyo pa imfa. Kunyenga kwamachenjera kwa chiphunzitso chimenecho kuli kuzunzika kwa kanthaŵi m’moto wa purigatoriyo. Anthu owona mtima amalipira kuti akhale ndi Misa ikunenedwa kaamba ka akufa koma samadziŵa nkomwe pamene zolipirazo zimaleka kukhala zoyenera! Ziphunzitso zamwano zimenezi ziribe maziko m’Baibulo.​—Yerekezani ndi Yeremiya 7:31.

M’chenicheni, Baibulo limaphunzitsa kuti munthu ali moyo, wokhala ndi moyo wokhoza kufa. Kaamba ka kusamvera kwake Adamu sanaweruzidwe ku moto wa helo kapena purigatoriyo koma ku imfa. Chitangolongosoledwa mopepuka, “mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23; Genesis 2:7, 17; 3:19) Chiyembekezo cha Malemba kaamba ka akufa nchozikidwa, osati pa moyo wosafa, koma, m’malomwake, pa lonjezo la Mulungu la chiwukiriro ku moyo wangwiro pa dziko lapansi la paradaiso.​—Yohane 5:28, 29; Chibvumbulutso 21:1-4.

Komabe chiphunzitso china Chachibabulo chiri Utatu “woyera.” Chiphunzitso chimenechi cha anthu atatu mwa Mulungu mmodzi sichinali nkomwe mbali ya chikhulupiriro cha Ahebri akale. (Deuteronomo 5:6, 7; 6:4) Myuda iyemwini, Yesu motsimikizirika sanakhulupirire konse kapena kuphunzitsa kuti iye anali Mulungu wamphamvuyonse. Iye sanadzinenere kukhala ndi mbali m’mbali zitatu monga kunaphunzitsidwira m’chiphunzitso kapena chiphunzitso choikidwiratu cha Chibabulo.​—Marko 12:29; 13:32; Yohane 5:19, 30; 14:28; 20:17.

Chotero, tikukana ziphunzitso zamwano za Babulo monga zaphunzitsidwa m’zipembedzo zonyenga za dziko. Tikupereka kulambira kwa Mulungu wowona mmodzi, Yehova, kupyolera mwa Mwana wake, yemwe anadzakhala “chiwombolo” kaamba ka machimo osati kokha a Akristu odzozedwa koma a dziko lonse la mtundu wa anthu.​—1 Yohane 2:2.

Chifukwa Chimene Timakanira Nthanthi Zokana Mulungu

Apapa ndi atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko akusonyeza chisoni pa kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu, ndipo ambiri amachigwiritsira ntchito kulungamitsa kuchirikiza kwawo ndale zadziko. Komabe, funso liyenera kufunsidwa: Kodi ndani analola machitidwe a chisalungamo ndi kuchita mosalinganiza komwe kunayambitsa kubadwa kwa kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu, makamaka m’zana lapita? Chinachitika m’njira yowonekera m’mabwalo a Chikristu cha Dziko. Mwachitsanzo, Tchalitchi cha ku Russia cha Orthodox chinagwirizana ndi a czar, omwe mwankhalwe anatsendereza anthu. Kusoweka kwa mapindu owona Achikristu ku mbali ya aja omwe anadzipereka iwo eni monga oimira a Mulungu kunatsogolera ku mikhalidwe imene inapanga malo obadwirako kaamba ka kusakhulupirira kukhalako kwa Mulungu.

Zipembedzo za Chikristu cha Dziko nazonso zakupatira chiphunzitso chosalemekeza Mlengi cha chisinthiko. Iwo amapereka kucholowanacholowana ndi kusiyanasiyana kwa mitundu ya miyoyo yoposa pa miliyoni imodzi ku mphamvu zakhungu za chilengedwe. M’chenicheni, iwo amanena kuti kusiyanasiyana kumeneku kunafikira kukhalako mwa mpambo wa nyongolotsi za phindu. Nthanthi yotereyi imapanga Mulungu kukhala wosafunikira ndi munthu kukhala wopanda thayo kwa aliyense. Mikhalidwe yabwino kapena yoipa imakhala nkhani ya chosankha chaumwini. (Salmo 14:1) Chotulukapo chimodzi chiri chakuti kuchotsa mimba tsopano kukuthamangira ku makumi a mabiliyoni chaka chirichonse​—m’maiko odzinenera kukhala achipembedzo!

Timakana nthanthi ndi machitachita zokana Mulungu zimenezi. Timalambira Yehova, “Iye amene ali ndi moyo ku nthaŵi za nthaŵi, amene analenga m’mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo.”​—Chibvumbulutso 10:6; 19:6.

Chifukwa Chimene Timadera Zipatso za Babulo Wamkulu

Chikristu cha Dziko chalephera kulabadira mauthenga achenjezo ku mipingo isanu ndi iŵiri yosonyezedwa mu Chibvumbulutso mitu 2 ndi 3. Amenewa amalangiza motsutsana ndi kachitidwe ka chipatuko, kulambira mafano, ndi dama, ndi motsutsana ndi kufunda ndi kunyalanyaza.

Kuchezera ku chifupifupi iriyonse ya malo olambirira kudzabumbula ndi anthu achipembedzo ambiri motani amene akweza cholengedwa pamwamba pa Mlengi. Tero motani? Mwa kulemekeza kwawo mafano ndi zithunzithunzi zopaka utoto ndi kulambira kwawo koperekedwa kwa “oyera,” a Madonna, ndi mitanda.​—Yerekezani ndi Salmo 115:2-8; 2 Akorinto 5:7; 1 Yohane 5:21.

Mu nkhani yawo, mawu a Paulo ali ndi kukwaniritsidwa: “Chifukwa kuti, ngakhale anadziŵa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera, Mulungu . . . Anapusa; nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka ndi cha mbalame, cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.”​—Aroma 1:21-23.

Chifukwa Chimene Timatsutsira Mkhalidwe Woipa wa Babulo

Zaka 20 zapitazo zawona kugonana kwa ofanana ziwalo kukuvomerezedwa kapena kuloledwa monga njira ina ya moyo. Mamiliyoni a ogonana ofanana ziwalo “achoka m’chipinda chotsekeredwa” ndipo tsopano akuima pa makwalala, akufuula “Kunyada [kwawo] kwa Kugonana kwa Ofanana Ziwalo.” Kodi ndimotani mmene Mulungu amawonera kugonana kwawo kwa ofanana ziwalo?

Baibulo linasonyeza mowonekera bwino zaka 3,500 zapitazo kuti: “Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.” (Levitiko 18:22) Ndipo chifupifupi zaka 2,000 zapitazo Paulo anasonyeza kuti miyezo ya Mulungu sinasinthe pamene analemba kuti: “Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazdi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okha okha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho ya kuyenera kulakwa kwawo.”​—Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 6:9, 10; 1 Timoteo 1:10.

Komabe, ambiri a atsogoleri a Chikristu cha Dziko akuchita kugonana kwa ofanana ziwalo kotero kuti akhala okhoza kukhazikitsa gulu lamphamvu lochirikiza kugonana kwa ofanana ziwalo mu zambiri za zipembedzo zazikulu. Iwo akufuna kuti njira yawo ya moyo izindikiridwe ndi kuti apatsidwe malo a uminisitala. Nkhani yolozeredwako ndi ija ya mpingo wa Chiprotesitanti waukulu koposa mu Canada, United Church of Canada, umene atsogoleri ake anachita masankho a 205 kwa 160 pa August 24, 1988, moyanja kuvomereza kugonana kwa ofanana ziwalo ku uminisitalawo.

Chifukwa Chimene Timadera Chigololo Chauzimu cha Babulo

Chibvumbulutso chimatsutsa chigololo cha Babulo ndi “mafumu a dziko,” atsogoleri ake a ndale zadziko. Mkazi wachigololoyo akuchitiridwa chithunzi monga wokhala pa “madzi ambiri,” kutanthauza “anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.” (Chibvumbulutso 17:1, 2, 15) Mwa kukhala ndi unansi wopitirizabe ndi atsogoleri a ndale zadziko, chipembedzo chonyenga kwa zaka mazana chagwiritsira ntchito chisonkhezero chake poyera kapena mobisa m’kudidikiza ndi kudyera masuku pamutu anthu wamba.

Zitsanzo za kudidikiza kumeneku ziri zigwirizano, kapena mapangano, amene Vatican inasaina ndi Nazi ndi olamulira a Chifasizimu m’zana lino la 20. Monga chotulukapo, chisonkhezero cha tchalitchi pa nkhosa chinatsogolera ku chichirikizo chotheratu cha olamulira nakhalwe. Mu 1929 Vatican inapanga chigwirizano ndi wolamulira wotsendereza ufulu wa Chifasizimu Benito Mussolini. Kodi nchiyani chomwe chinatsatira mu Germany? Cardinal Faulhaber wa ku Germany, akulunjikitsa mawu otsatirawa kwa Pius XI, akupereka chidziwitso m’kulingalira kwa papa ponena za Hitler kuti: “Ndiri wokondweretsedwa; iye ali munthu woyamba wa ndale za boma kulankhula poyera motsutsana ndi Chibolshevizimu.” Faulhaber pambuyo pake ananena kuti: “Ulendo wanga ku Roma unatsimikizira chimene ndiyenera kukhala ndi kuchilingalira kwa nthawi yaitali. Mu Roma, Chisosholizimu cha Mtundu ndi Chifasizimu zikulingaliridwa kukhala chipulumutso chokha kuchokera ku Chikomyunizimu ndi Chibolshevizimu.”

Abishopu a Chikatolika a ku Germany anali atatsutsa nthanthi ya Nazi isanafike 1933. Koma monga mmene mkonzi wa ku Germany Klaus Scholder akulongosolera m’bukhu lake lakuti The Churches and the Third Reich, abishopu analamulidwa ndi kazembe wa Vatican ku Germany, Cardinal Pacelli, kukonzanso kaimidwe kawo kulinga ku Chisosholizimu cha Mtundu. Kodi nchiyani chomwe chinafulumizitsa kusinthaku? Chinali chiyembekezo cha chigwirizano pakati pa Ulamuliro Wachitatu ndi Vatican, chomalizidwa pa July 20, 1933.

Klaus Scholder akusimba kuti: “Pa masankho ndi voti la anthu wamba la pa 12 November [1933] Hitler anakolola zipatso za chigwirizano cha Ulamuliro ndi masankho okwezeka modabwitsa a ‘yes’ (ovomereza), pamwamba pa bungwe lonse loimira masankho la Chikatolika cholamulira.”

Ngakhale kuti atsogoleri a Chiprotesitanti owerengeka anasonyeza kutsutsa ku chipambano cha Nazi mu 1933, mawu awo mwamsanga anataika m’kufuula kwa unyinji wa anthu kwa utundu. Scholder akulongosola kuti: “Mowonekera panali kukonzekera kowonjezereka m’tchalitchi cha Chiprotesitanti kusiya chenjezo lochitidwa nthawi yapita ndipo tsopano potsirizira kugwidwanso m’kutenthedwa maganizo kwa mtundu. . . . Ndemanga za lamulo la tchalitchi zinawonekera kwa nthawi yoyamba zomwe zinachirikiza Ulamuliro watsopano popanda kusiyako.” M’chenicheni, Chiprotesitantizimu chinadzigulitsa icho chokha kwa utundu cha Nazi ndipo chinakhala wothandizira wake, monga mmene Tchalitchi cha Chikatolika chinali chitachitira.

Kubwerera kumbuyo kwa zaka mazana, cholembera cha m’mbiri chimasonyeza kuti, chipembedzo chonyenga chagwirizana ndi magulu a nduna zolamulira zamphamvu ndipo chasonkhezera kutchuka kwawo ku chivulazo cha anthu wamba. ‘Mkhalidwe wa maganizo wa Kristu’ sunawunikiridwe ndi atsogoleri a chipembedzo cha dziko, amene mwanjala afunafuna mphamvu, zinthu zakutupi, ndi chuma. Monga Mboni za Yehova, ife timada chigololo chauzimu choterocho.​—Yohane 17:16; Aroma 15:5; Chibvumbulutso 18:3.

Chifukwa Chimene Timanyansidwira Ndi Liwongo la Mwazi la Babulo

Mu bukhu la Chibvumbulutso, Babulo Wamkulu akupatsidwa mlandu waukulu wa liwongo la mwazi: “Ndipo ndinawona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu. Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa pa dziko.”​—Chibvumbulutso 17:6; 18:24.

Mbiri yakale ya chipembedzo chonyenga ndi imodzi ya udani ndi kukhetsa mwazi, ndi Chikristu cha Dziko chokhala ndi liwongo la mwazi koposa. Nkhondo zadziko ziŵiri zinayambika m’malo otchedwa mitundu ya Chikristu. Atsogoleri a ndale zadziko “Achikristu” anatembenukira ku zida zankhondo mu 1914 ndi 1939, ndipo atsogoleri achipembedzo m’mitundu yonse yomenya nkhondo anapereka dalitso lawo. The Columbia History of the World ponena za Nkhondo ya Dziko ya I imalongosola kuti: “Chowonadi chinachotseredwa mtengo limodzi ndi moyo, ndipo panalibe ngakhale mpang’ono ponse liwu lokwezedwa motsutsa. Osunga mawu a Mulungu anatsogoza nyimbo zankhondo. Nkhondo yotheratu inadzatanthauza udani wotheratu.” (Kanyenye ngwathu.) Atsogoleri achipembedzo a nkhondo anasonkhezera asilikali awo kupitirizabe ndi kunyada kwawo kwa ufuko pamene achichepere a mbali zonse ziŵiri anakhala chakudya cha mfuti. Bukhu la mbiri yakale limodzimodzilo likulongosola kuti: “Kuwononga maganizo a anthu kwa dongosolo kochititsidwa ndi zisonkhezero za utundu . . . mowonjezereka kunatsekereza kufunafuna kaamba ka mtendere.”

Chipembedzo dziko lonse chikupitirizabe kuyambitsa udani pamene mikangano ibuka pakati pa Myuda ndi m’Silamu, m’Hindu ndi m’Sikh, Mkatolika ndi m’Protesitanti, m’Silamu ndi m’Hindu, m’Buda ndi m’Hindu. Inde, chipembedzo chonyenga chikupitirizabe kuthandizira ku kukhetsa mwazi wa “onse amene anaphedwa pa dziko.”​—Chibvumbulutso 18:24.

M’chiyang’aniro cha umboni wonse woikidwa pamwambapo, Mboni za Yehova zimamva kuti chigamulo cha msonkhano wa 1988 chiri choyenera ndi cha pa nthaŵi. Moyenerera, timatsutsa chipembedzo chonyenga monga mkazi wachigololo wa liwongo la mwazi, Babulo Wamkulu. Tikulengeza ku dziko njira yowona yokha ku mtendere ndi kulambira kowona​—kutembenukira kwa Mfumu Ambuye wa chilengedwe chaponseponse, Yehova Mulungu, kupyolera mwa Mmodzi amene anamtumiza ku dziko lapansi, Kristuyo, kapena Mesiya, Yesu. Ichi chimatanthauza kulandira Ufumu wa Mulungu monga boma lolunjika losatha, limene ilo lokha lingakhutiritse zosowa za mtundu wa munthu. Ndipo chimatanthauzanso kuti tsopano iri nthaŵi ya kumvera lamulo lakuti: “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu], anthu anga, ngati simufuna kugawana naye machimo ake, ndipo ngati simufuna kulandira mbali ya miliri yake.”​—Chibvumbulutso 18:4, NW; Danieli 2:44; Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

a Genesis 22:14; Eksodo 6:3; 17:15; Oweruza 6:24; Salmo 83:18; Yesaya 12:2; 26:4.

b Kaamba ka kulingaliridwa kwa tsatanetsatane kwa kufunika ndi kukula kwa dzina la Mulungu, onani broshuwa ya masamba 32 ya Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena