Chinsinsi cha bukhu Lamakedzana la Vatican
BUKHU Lamakedzana la Vaticanus 1209 likuwoneka m’bukhu lowonamo zinthu loyamba la Laibulale ya Vatican, lokonzedwa m’chaka cha 1475. Mmene linafikira kumeneko palibe wina aliyense amene amadziŵa. Ilo liri limodzi la mabukhu amakedzana Achigriki atatu aakulu kukhala atapulumuka kufika ku tsiku lino, likumakhala pamodzi ndi anzake, Sinaiticus ya zana lachinayi, ndi Alexandrinus ya kumayambiriro kwa zana lachisanu.
Ngakhale kuti kufunika kwa manusikripiti ya Vatican imeneyi kunali kodziŵika bwino lomwe kwa ophunzira kumayambiriro mu zana la 16, kokha oŵerengeka analoledwa kulisanthula ilo. Laibulale ya Vatican inakonzekera kusonkhanitsidwa kwa kuŵerenga kosiyanasiyana kwa manusikripitiyo mu 1669, koma ichi chinataika ndipo sichinapezedwenso kufikira mu 1819.
Wolamulira Napoleon wa ku France analanda Roma mu 1809 ndi kutenga manusikripiti ya mtengo wakeyo ku Paris, kumene iyo inasanthulidwa ndi Leonhard Hug, wophunzira wotchuka, koma ndi kugwa kwa Napoleon bukhu lamakedzanalo linabwezeretsedwa ku Vatican mu 1815. Kwa zaka 75 zotsatira ilo linalinso chinthu cha chinsinsi, chobisidwa ndi Vatican.
Konstantin von Tischendorf, mmodzi wa ophunzira aakulu koposa a manusikripiti a m’dziko, analoledwa kusanthula manusikripitiyo mu 1843 kokha kwa maora asanu ndi limodzi, pambuyo pa kusungidwa akuyembekezera kwa miyezi ingapo. Zaka ziŵiri pambuyo pake, wophunzira wa Chingelezi Dr. S. P. Tregelles analoledwa kuwona bukhu lamakedzanalo koma osati kuliphunzira ilo. Iye analongosola kuti: “Nzowona kuti kaŵirikaŵiri ndinawona MS. imeneyo, koma iwo sanandilole kuigwiritsira ntchito iyo; ndipo iwo sanandilole kutsegula iyo popanda kufufuza matumba anga, ndi kundilanda cholembera, inki, ndi pepala; ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo ma prelati [ansembe] aŵiri anandiika ine m’kukambitsirana kokhazikika mu Chilatin, ndipo ngati ndinayang’ana pa ndime kwa nthaŵi yaitali, iwo anali kutsomphola bukhulo m’manja mwanga.”
Nchifukwa ninji Tchalitchi cha Roma Katolika chinali cha’khokera chotero kusonyeza dziko manusikripiti yake ya mtengo wapatali?
Nchifukwa Ninji Inabisidwa?
Kwa Tchalitchi cha Roma Katolika, kalembedwe ka Latin Vulgate ka Malemba Opatulika kadakali “ulamuliro wake wofunika koposa.” Mogwirizana ndi kalata yotumizidwa kwa ansembe Divino Afflante Spiritu ya Pius XII, yofalitsidwa m’chaka cha 1943, kutembenuzidwa kwa Chilatin kwa m’zana lachinayi kumeneku ndi Jerome kumawonedwanso kukhala “kotetezeredwa kotheratu kuchokera ku chophophonya chirichonse mu nkhani za chikhulupiriro ndi makhalidwe abwino.” Bwanji ponena za malemba a Chihebri ndi Chigriki kuchokera kumene Vulgate inatembenuzidwa? Izi, kalata yotumizidwa kwa ansembeyo ikunena kuti, ziri za mtengo ‘kutsimikizira’ ulamuliro wa Vulgate. Chotero manusikripiti iriyonse ya Chigriki, ngakhale Bukhu Lamakedzana la Vatican, sinalingaliridwe konse kukhala ya ulamuliro monga mmene iriri Latin Vulgate. Kaimidwe kameneka kotengedwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika mwachibadwa kapangitsa mavuto.
Mwachitsanzo, pamene wophunzira wa m’zana la 16 Erasmus anatembenuza “Chipangano Chatsopano” chake cha Chigriki, iye anachonderera kwa maulamuliro a Bukhu Lamakedzana la Vatican kusaphatikizapo mawu onama ochokera ku 1 Yohane mutu 5, mavesi 7 ndi 8. Erasmus anali wolondola, komabe mochedwa kwenikweni kufika mu 1897 Papa Leo XIII anasungirira lemba loipitsidwa la Chilatin la Vulgate. Kokha ndi chofalitsidwa cha matembenuzidwe amakono a Roma Katolika ndi pamene kulakwika kwa lemba kumeneku kwavomerezedwa.
Pamene Bukhu Lamakedzana la Sinaiticus linavumbulidwa ku dziko m’mbali yomalizira ya zana la 19, chinakhala chowonekeratu kwa maulamuliro a Roma Katolika kuti Bukhu Lamakedzana lawo la Vaticanus linali m’ngozi ya kuzimiririka. Podzafika kumapeto kwa zanalo, makope abwino ojambulidwa potsirizira pake anapangidwa kukhalako.
Manusikripitiyo iri ndi masamba 759. Iyo iribe mbali yokulira ya Genesis, masalmo ena, ndi mbali zomalizira za Malemba Achikristu a Chigriki. Iyo iri yolembedwa pa chikopa chopuntha chopyapyala, chabwino koposa, cholingaliridwa kukhala chochokera ku zikopa za nswala, mu mtundu wopepuka, wowongoka. Chizindikiritso chake chalamulo chiri Bukhu Lamakedzana B (Codex B), ndipo iyo ingawonedwe lerolino mu Laibulale ya Vatican. Iyo siri yobisidwanso, ndipo phindu lake potsirizira pake lamvetsetsedwa ndi kuyamikiridwa m’dziko lonse.
[Chithunzi patsamba 31]
Bukhu Lamakedzana la Vaticanus 1209 lofunika koposa linabisidwa ndi Vatican kwa mazana angapo
[Mawu a Chithunzi]
Kalembedwe kofananako kuchokera ku Codices E Vaticanis Selecti