Chidziŵitso pa Nyuzi
Mfungulo ku Chimwemwe?
“Zaka ziŵiri za kuvutika, chimwemwe kosatha.” Kumeneku, mogwirizana ndi nyuzipepala ya ku Japan Yomiuri Shimbun, kuli kulankhula kofala kwa lerolino pakati pa ophunzira a ku China mu Japan. Ndi ziyembekezo za kukhala olemera, ophunzira amenewa amabwereka ndalama kuti abwere ku Japan, kumene amakhulupirira kuti kumagwa mvula ya ndalama kuchokera kumwamba. Iwo amayembekezera kuti mwa kugwira ntchito yapambali zaka ziŵiri pamene akali kupita ku sukulu, iwo angasunge mamiliyoni aŵiri a yen (chifupifupi $15,400, U.S.) ndipo kenaka kubwerera kwawo kukakhala moyo wachimwemwe kosatha pambuyo pake.
Kudalira koteroko pa ndalama monga mfungulo ku chimwemwe kuli kofalikira pa dziko lonse. Kufufuza kwa posachedwapa pakati pa achichepere m’maiko 9 a 11 kunavumbula kuti “‘ndalama’ zinali zoyambirira pa ndandanda” ya zodandaulitsa ndi nkhaŵa zawo, ikutero Asahi Evening News.
Kodi kukhulupirira m’chuma ndithudi kudzatsegula chitseko ku chimwemwe? Mfumu yanzeru Solomo anachenjeza kuti “okonda siliva sadzakhuta siliva.” (Mlaliki 5:10; 7:12) Kuika ndalama m’malo oyamba sikumatulukapo m’chikhutiritso chowona, osatinso kutsimikizira chisungiko cha mtsogolo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Ngakhale siliva wawo, ngakhale golidi wawo sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zefaniya 1:18) Mosiyanako, ngakhale kuli tero, wamasalmo Davide analemba kuti: “Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika.” Kukhulupirira mwa Yehova, osati m’ndalama, kuli mfungulo ku kusangalala ndi chimwemwe kosatha.—Salmo 40:4; Yesaya 30:18.
Chothetsa Nzeru cha Ubatizo
Mavuto aŵiri a ubatizo wa mwana wakhanda adzuka mu nthaŵi za posachedwapa mkati mwa Church of England. Loyambirira limakhudza ubatizo “wosasankha,” umene mtsogoleri wina anaulongosola kukhala mtundu wina wa “kuloŵetsa kwauzimu.” Lachiŵiri liri kukana kwa chiŵerengero chomawonjezeka cha atsogoleri achipembedzo kubatiza makanda amene makolo awo samachirikiza mokangalika Church of England.
Atsogoleri achipembedzo ambiri azindikira kuti makolo kaŵirikaŵiri samakhala ndi chikhumbo cha kupezeka ku tchalitchi ndipo sakafuna ngakhale ana awo kuchita tero. Nchifukwa ninji kenaka kubatiza ana akhanda? “Iwo amafuna mwambo wobatiza ndi kupatsa dzina kaamba ka makanda awo,” ikuchitira ndemanga tero The Times, “kokha monga momwe amafunira kupereka kapena kulandira mphatso za tsiku lakubadwa, kukometsa nyumba zawo pa Krisimasi . . . Chiri mbali ya mwambo wawo: icho sichimafunikira kukhala ndi chifukwa.”
Mtsogoleri wachipembedzo wina analeka ntchitoyo chifukwa chakuti anafikira kumaliza kwakuti maubatizo a mwana wakhanda sayenera kuchitidwa. Iye ananena kuti: “Munthu yekha amene angapange kudzipereka koteroko kwa Kristu ali munthu iyemwiniyo.” Iye akanawonjezera kuti Yesu Kristu anali ndi zaka 30 zakubadwa pamene anabatizidwa ndikuti liwu la Chigriki kaamba ka ubatizo, ba·ptiʹzo, limatanthauza kuviika kapena kumiza. Pambuyo pobatizidwa mu Mtsinje wa Yordano, Yesu anabwera “kutuluka m’madzi.” (Marko 1:10; Mateyu 3:13, 16) Palibe pamene Baibulo limalozera ku kuwaza madzi pa ana akhanda. Popeza kuti ubatizo uli chizindikiro cha kudzipereka kwa wina kwa Mulungu monga wotsatira mapazi a Kristu, sichiri chosankha chomwe mwana wakhanda angapange.
Njira Zoletsa Kubala ndi Akatolika
Kutsutsa kwa Tchalitchi cha Chikatolika ku kuletsa kubala kunatsimikiziridwa ndi John Paul II pa Msonkhano wa Mitundu Yonse Wachiŵiri pa Nthanthi ya Zaumulungu ya Mkhalidwe wochitidwa mu Roma November yatha. Mogwirizana ndi nyuzipepala ya Vatican City, L’Osservatore Romano, iye ananena kuti: “Ichi sichiri chiphunzitso choyambitsidwa ndi munthu. Icho chalembedwa ndi dzanja lolenga la Mulungu mu mkhalidwe weniweni wa umunthu wa munthu. Kuchikaikira icho kumafikira ku kukaniza Mulungu chimvero cha luntha lathu,” ndipo chotero, iye akuwonjezera kuti, “sichingakaikiridwe ndi wanthanthi ya zaumulungu wa Chikatolika.”
Koma kalata yolembedwera abishopu onse atchalitchi yotchedwa Humanae Vitae imene inalozeredwako ndi Papa John Paul ndipo yolembedwa zaka 20 zapitazo ndi Paul VI “mwamsanga inakaikiridwa ndi chiŵerengero chachikulu cha anthanthi ya zaumulungu,” inawona tero nyuzipepala ya ku Italy La Stampa, ndipo inanyalanyazidwa ndi “unyinji waukulu wa Akatolika.”
Mowonekera bwino, kusasintha kwa tchalitchi pa funso la kulamulira kubala kwalekanitsa anthanthi ya zaumulungu ndipo mokulira kwasokoneza Akatolika owona mtima. Kukana komapitirizabe pa kugwiritsira ntchito mtundu uliwonse wa njira zoletsa kubala kunachititsa ngakhale John Paul kusonkhezera anthanthi ya zaumulungu onse kulankhula “chinenero chofananacho.” Komabe, mosiyana ndi kudzinenera kwa papa kuti kaimidwe ka tchalitchi pa nkhani ya kuletsa kubala “kanalembedwa ndi dzanja lolenga la Mulungu,” nyuzipepala ya ku Italy La Repubblica inawona kuti “palibe vesi kuchokera mu Mauthenga Abwino kapena Chipangano Chakale lomwe lasonyezedwa kutsimikizira chiphunzitsocho.”
Palibe kulikonse kumene Baibulo limakambitsirana kugwiritsira ntchito kwa njira zoletsa kubala kapena kulamulira kubala mu ukwati, silimanenanso kuti Akristu akulamulidwa kubala ana. Mawu a Mulungu amasiya funso la kulinganiza banja ku chikumbumtima cha Akristu okwatirana aŵiri aliwonse. Mwa kupereka lamulo lake ponena za kulamulira kubala, Tchalitchi cha Chikatolika “chapitirira zimene zilembedwa.”—1 Akorinto 4:6.