Kodi Ntchito Yolimba Imabweretsa Chimwemwe?
“NDIKO nkomwe, ntchito iri chirichonse kaamba ka mwamuna, kodi sitero?” anafunsa tero Bunpei Otsuki, mwamuna wotchuka wopambana m’dziko la malonda la Japan. Iye anali kulongosola chifukwa chimene sanafune kutenga tchuthi cha m’chirimwe. Mawu ake ali ofanana ndi anthu a ku Japan omwe anamanganso dzikolo kuchokera ku mavuto ake a nthaŵi ya pambuyo pa nkhondo. Anthu a ku Japan alongosoledwa kukhala anthu achangu chiyambire pamene Wolamulira Gulu la Sitima ya Pamadzi Perry wa ku United States anatsegula Japan kuchokera ku nyengo yaitali ya kudzipatula. Ndipo iwo ali onyadira m’kukhala ogwira ntchito molimba.
Ngakhale kuli tero, Japan tsopano ikusulizidwa kaamba ka kugwira ntchito molimba kwambiri, pokhala ndi maora ogwira ntchito a pa chaka otalika koposa pakati pa mitundu yotchedwa ya maindasitale. Boma la Japan likuyesera kuchotsapo chithunzi cha kumwerekera m’kugwira ntchito. “Chigawo cha Boma Choyang’ana pa Ntchito Chikunena kuti ‘Lekani Kugwira Ntchito Molimba Chotero,’” ukuŵerengedwa tero mutu wa nyuzipepala ina. M’mawu ake a ndawala kaamba ka nyengo ya tchuthi ya m’chirimwe ya 1987, chigawocho chinafika pa kunena kuti, “Kutenga tchuthi kuli umboni wa kukhoza kwanu.” M’mawu ena, boma likufunsa mtunduwo kuti, “Nkugwiriranji ntchito molimba chotero?”
Ndithudi, sionse mu Japan omwe ali odzipereka, ogwira ntchito molimba. Kufufuza kwa posachedwapa kwa Productivity Center ya ku Japan kwa ogwira ntchito atsopano oposa pa 7,000 kunavumbula kuti kokha 7 peresenti ya iwo amapereka kufunika koyambirira pa ntchito pamwamba pa moyo waumwini. Chikhoterero chimenechi chingawonedwenso m’maiko ena. Mu Germany Allensbacher Institut für Demoskopie inaphunzira kuti kokha 19 peresenti ya anthu a ku Germany m’gulu la amsinkhu wa pakati pa 18 ndi 29 anadzinenera kuti iwo amapereka zabwino koposa zawo pa ntchito mosasamala kanthu za mapindu operekedwa.
Atayerekezedwa ndi wachichepere wotsogoza moyo wosavutikira, ogwira ntchito achilendo mu Japan amagwira ntchito molimba koposa. Wolemba ntchito wa mu Tokyo akulankhula monyadira wolembedwa ntchito wake wa ku Algeria yemwe amachita ntchito ya manja. Iye akunena kuti: “Anthu a ku Japan sangafunsire kaamba ka ntchito ya mtundu umenewu, ndipo ngakhale ngati anatero, iwo angaileke mwamsanga.” Ayi, osati ngakhale anthu a ku Japan ogwira ntchito molimba ali a khama mwachibadwa. Pamene anthu agwira ntchito molimba, payenera kukhala chisonkhezero champhamvu.
Zifukwa kaamba ka Kugwira Ntchito Molimba
“Chuma, kusatekeseka, zinthu, ndi kupambanabe m’dziko”—izi ndizo zinthu zomwe anthu a ku Germany ogwira ntchito molimba amazifuna, likusimba tero pepala lakuti Der Spiegel la mlungu ndi mlungu la ku Germany. Inde, ambiri amagwira ntchito molimba kuti apeze chuma chakuthupi kotero kuti angasangalale ndi mlingo wa kusatekeseka m’moyo. Ena amagwira ntchito molimba ndi cholinga cha “kupambanabe m’dziko” kapena kukwera makwerero a kutchuka ndi malo. Ambiri omwe ali osonkhezeredwa mwamphamvu ndi dongosolo lopikisana la maphunziro kuti alondole zonulirapo zimenezo mopanda mwaŵi amangothera m’kuchita zinthu zotopetsa zimodzimodzi mosalekeza za chitaganya cha indasitale—kumangodzitopetsa iwo eni ndipo popanda chipambano chirichonse.
Ndalama ndi malo, ngakhale kuli tero, sindizo zifukwa zokha zimene anthu amagwirira ntchito molimba. Ena amagwira ntchito chifukwa cha ntchito. Kwa iwo, ntchito iri chirichonse. Ena amasangalala ndi ntchito yawo. “Ndinakondweretsedwa kwenikweni ndi chomwe ndinali kuchita m’chipinda changa chosanganizira mankhwala,” akuvomereza tero Haruo, “kotero kuti zolondola zauzimu zinachotsedwa.”
Kenaka pali aja omwe ali odzipereka ku ntchito za phindu kaamba ka utumiki ndi ubwino wa ena. Iwo amagwira ntchito molimba kuti apulumutse miyoyo. Mwachitsanzo, wogwira ntchito yozima moto amagwira ntchito molimba tsiku lirilonse kusunga chiwiya chake m’dongosolo.
Koma kodi zonsezi ziri zifukwa zabwino kaamba ka kugwira ntchito molimba? Kodi izo zidzatsogolera ku chimwemwe? Ndithudi, ndi ntchito yotani yomwe kwenikweni ingakupangeni inu kukhala wachimwemwe?