Ripoti la Olengeza Ufumu
“Chowonadi Chidzakumasulani”—Ndi Kubweretsa Chimwemwe
MU BRITAIN, chowonadi cha Baibulo chamasula anthu oposa 113,000, ndipo ambiri akukupatira chowonadi tsiku lirilonse. Zowonadi mawu a Yesu akukwaniritsidwa: “Ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Ufulu umenewu umatulukapo m’chimwemwe, monga mmene zokumana nazo zotsatirazi kuchokera ku Britain zikusonyezera.
◻ Pamene Penny anali mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, ikusimba tero ofesi ya nthambi, mkazi wachikulire anamuuza iye modudukira kwenikweni, “Ndiri wotanganitsidwa.” Penny anayankha kuti akafikiranso. Masiku ochepa pambuyo pake, pa nthaŵi yomwe sakafikira nthaŵi zonse, anali kuchezera osapezeka panyumba ndipo mosalingalira anafikira pa nyumba imodzimodziyo. Mkazi wachikulireyo anatsegula chitseko ndi kuitanira Penny mkati. “Ndinadziŵa kuti udzabweranso,” anatero mkaziyo, “ndipo ndinali kukuyembekezera.” Iwo anakambitsirana chiyembekezo cha Ufumu, ndipo mkaziyo ananena kuti anayembekeza kuti chikatsimikizira kukhala chowona. Iye anali wa zaka 79, ndipo mwamuna wake anali atamwalira zaka zitatu kumayambiriro. Iye sanalandire chitonthozo chirichonse kuchokera ku tchalitchi chake ndipo sanawone chifukwa chirichonse chokhalira ndi moyo. Iye anafuna kufa. Pambuyo pake, Penny atayamba kale phunziro la Baibulo ndi iye, mkaziyo anawuza Penny kuti anali kukonzekera kudzipha koma anadziŵa kuti chinali cholakwika. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti akampatsa chitonthozo ndi kumthandiza kupezanso chiyembekezo. Mwapang’onopang’ono, pamene iye ankaphunzira, kuthedwa nzeru kwake kunatembenukira ku chiyembekezo, ndi kukhutiritsidwa kozama ndi chiyamikiro kwa Yehova. Iye anathetsa chigwirizano chake cha nthaŵi yaitali ndi tchalitchicho, anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 80, ndipo tsopano ali wofalitsa wokhazikika wokhala ndi changu chachikulu. Zowonadi, chowonadi cha Mawu a Mulungu chamumasula iye ndikumubweretsera chimwemwe chachikulu.
◻ Chowonadi chonena za Ufumu wa Mulungu chimabweretsa ufulu kuchokera ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga. Icho chingasinthenso umunthu wa munthu, ndipo kusintha kumeneku kaŵirikaŵiri kumakondweretsa ena ndi kuwathandiza iwo kuwona chowonadi, monga mmene chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.
Mkazi wachichepere anagogoda pa khomo pa nyumba ya Mboni ndi kupempha phunziro la Baibulo. Kodi nchiyani chinabweretsa chimenechi? Makolo a mkaziyo anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo chiyambukiro chomwe chinakhala nacho pa makolo ake—makamaka atate wake—chinali chozizwitsa kwenikweni ndi chokondweretsa kotero kuti mwana wamkazi ameneyu anadabwitsidwa mowonadi. Atate wake, omwe anali kusuta ndudu 80 pa tsiku, analeka kotheratu kusuta pamene chinalongosoledwa kwa iwo kuti Yehova samavomereza. Chifupifupi mwamsanga pambuyo pake iwo anabweza kwa owalemba ntchito awo mtokoma wonse wa katundu amene anali ataba kuchokera kwa iwo pa nyengo ya nthaŵi. Mwana wamkaziyo anadzimva kuti chirichonse chomwe chikayambukira makolo ake m’njira yoteroyo motsimikizirika chinafunikira kufufuzidwa. Tsopano makolowo ali obatizidwa, ndipo mwana wamkaziyo akupezeka pa misonkhano yonse.
Chowonadi chimene Yesu analengeza chinabweretsa chimwemwe kwa awo otchulidwa pamwambapo ndi ena osaŵerengeka. Icho chingachitenso chimodzimodzi kwa aliyense yemwe amalandira chowonadi cha Baibulo ndi kuchigwiritsira ntchito m’miyoyo yawo.—Salmo 19:7, 8.