Nchifukwa Ninji Pali Upandu Wochulukira Chotero?
“WOCHULUKIRA wa upandu uli wolimbana ndi katundu,” ikudzinenera tero broshuwa ya boma ya ku Britain. Komabe, m’dziko limenelo upandu ndi chiwawa molimbana ndi anthu ukusimbidwa kukhala “mtundu womawonjezereka mofulumira wa upandu,” ngakhale kuti umapanga kokha 5 peresenti ya milandu yonse.
Mkhalidwe umenewu umawunikira kuwonjezereka kwa dziko lonse kwa upandu. Upandu wa kupambutsa zoyendera, mbala zokhala ndi zida, kugwirira chigololo, ndi machitidwe ena a chiwawa amawonetsedwa mokhazikika m’madanga a manyuzipepala a dziko, kaŵirikaŵiri akumakoka chisamaliro kuposa maripoti a upandu wopanda chiwawa. Mwachiwonekere, kenaka, ponse paŵiri inu ndi katundu wanu mungakhale chandamale cha upandu. Koma nchifukwa ninji? Nchiyani chomwe chimapangitsa anthu kukhala apandu?
Apandu ambiri ali anthu a mwaŵi. Monga chotulukapo chake, maulamuliro amakalamira kulimbana ndi kukwera kwa upandu mwa kulimbikitsa anthu kukhala ozindikira mokulira za chomwe chikuchitika m’mudzi mwawo. Pamene kuli kwakuti miyezo yoteroyo imagwiritsiridwa ntchito kuyesera kuchinjiriza machitidwe a upandu, kodi iyo imaletsa anthu kukhala apandu? Ayi.
Umunthu wa upandu uli nkhani ya kuphunzira kokulira. Mosangalatsa, Mawu a Mulungu, Baibulo, amapereka kawonedwe m’kulingalira kwa mpandu pamene likuchenjeza anthu achichepere za awo omwe monyenga amanena kuti: “Bwera kuno; tiye tipeze winawake woti timuphe! Tiye tiwukire anthu ena opanda liwongo kaamba ka chisangalatso cha iko! Iwo angakhale a moyo ndipo abwino pamene tiwapeza iwo, koma adzakhala akufa pamene tithana nawo! Tidzapeza mitundu yonse ya chuma ndi kudzaza nyumba zathu ndi zofunkha! Bwera gwirizana nafe, ndipo tidzagawana chomwe tidzaba.” (Miyambo 1:11-14, Today’s English Version) Inde, umbombo, kusirira, ndi kawonedwe kokondetsa zinthu zakuthupi kamapititsa patsogolo upandu.
Kugwiritsira ntchito molakwa anam’goneka ndi chikhulupiriro chakuti chisangalatso kapena chimwemwe chiri chabwino m’moyo zimalamuliranso kulingalira kwa ambiri m’zana lino la 20. Ndalama zimafunikira kulipirira zotaika, ngakhale ngati zimafunikira kuvulaza wina kapena kutenga moyo wake kuti apeze ndalama. ‘Nthaŵi zino zovuta kuchita nazo,’ chiri ndithudi chowona kwa chiŵerengero chomakulakula cha anthu kuti “iwo amafulumira kuloŵa mu upandu, osaleza mtima kuti akhetse mwazi.”—2 Timoteo 3:1, 3, 4; Miyambo 1:16, The New English Bible.
Upandu uli “chimo lalikulu koposa maka[maka] molimbana ndi makhalidwe abwino,” ikutero Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary. Tikukhala mu mbadwo wosweka m’makhalidwe abwino. Mtumwi Paulo anachenjeza Akristu a ku Efeso za anthu omwe “angoyenda m’chitsiru cha mtima wawo, odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuwumitsa kwa mitima yawo. [Amenewa] sazindikiranso kanthu konse.” Mofananamo, tifunikira kupereka chilabadiro lerolino.—Aefeso 4:17-19.
Kodi kuwonetsedwa kwa zojambulidwa za matepi a video za nkhalwe, kulemekeza nkhondo, ndi kulondola kwadyera kwa zosangulutsa zoipa zonsezo sizimathandizira ku kupanga ena kukhala apandu pamene kukupanga anthu opanda liwongo kukhala chandamale cha upandu? Komabe pali mbali ina m’choloŵanecholoŵane wa chinyengo cha upandu. Kodi icho nchiyani?
Ali Satana Mdyerekezi. Mkwiyo wake umayambitsa chiwawa ndi upandu wopanda pake womwe umazindikiritsa dziko lomwe liripoli. (1 Yohane 5:19; Chibvumbulutso 12:12) Cholinga chake chiri kupatutsa anthu onse kuchoka kwa Mulungu wowona, Yehova. Ngakhale kuti iye angapambane ndi ambiri, Baibulo mwaulosi limavumbula kuti iye adzalephera kuswa umphumphu wa atumiki owona a Mulungu. Pomalizira pake, Satana adzachotsedwa. Komabe, ngakhale Satana atachotsedwa, kodi chimenecho chidzatanthauza kutha kwa upandu? Ndipo kodi mapeto a upandu ali pafupi tsopano?