Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 9/1 tsamba 5-6
  • Kulamulira kwa Mulungu—Njira Yabwino Koposa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulamulira kwa Mulungu—Njira Yabwino Koposa
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusintha Kwakukulu Kuli Pafupi!
  • Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Ufumu Umene Udzasintha Dziko Lonse Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yehova Ndiye Woyeneradi Kulamulira
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 9/1 tsamba 5-6

Kulamulira kwa Mulungu​—Njira Yabwino Koposa

MBIRI ya maboma imachipangitsa icho kukhala chowonekeratu kuti anthu opanda ungwiro sangalamulire moyenerera anthu ena. Monga momwe Lord Acton wa ku England ananenera kuti: “Mphamvu imakhoterera pa kuipitsa ndipo mphamvu yotheratu imaipitsa koposapo.” Chotero, monga momwe Baibulo likunenera kuti: “Wina apweteka mnzake pomulamulira.”​—Mlaliki 8:9.

Poyambirira, Yehova Mulungu anapatsa munthu ulamuliro pa zinyama koma osati pa anthu ena. Mulungu anawuza Mwana wake woyamba kulengedwa m’mwamba kuti: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame zamlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:26) Mlengi wa munthu anali Wolamulira wake. Kodi ndimotani, kenaka, mmene chimenecho chinasinthira?

Pamene munthu anawukira m’munda wa Edene, iye anakana Mulungu monga Wolamulira wake ndipo wapitiriza kuchita tero chiyambire pa nthaŵiyo. (Genesis, mutu 3) Ichi chinali chowonekera mu Israyeli wakale, mtundu umene Mulungu anausankha monga wake wake. Pamene Aisrayeli anafuna mfumu yaumunthu, Yehova anawuza mneneri wake Samueli kuti: “Sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yawo.”​—1 Samueli 8:7.

Ulamuliro wa Mulungu pa Aisrayeli unali ndi cholinga chabwino. Kupyolera mwa woimira wake Mose, Yehova anawapatsa iwo ndandanda ya malamulo yomwe inasonyeza kulingalira kwachikondi kaamba ka ubwino wawo. Iyo inawatetezera iwo kuchokera ku matenda ambiri ndi kupititsa patsogolo kulingalira kaamba ka achikulire, akazi amasiye, ndi ana amasiye. Lamulolo linafuna ulemu kaamba ka katundu wa ena ndi kuwona mtima m’machitachita a bizinesi. Ilo linatsutsa tsankho, umboni wonama, ndi chiphuphu. Kulamulira kwa Mulungu kunalidi kolungama ndi kolunjika.

Yehova analonjeza kulamulira osati kokha Israyeli koma mtundu wonse wa anthu. Iye akachotsera anthu ochimwa mphamvu ya kulamulira anthu anzawo ndi kuipereka iyo kwa Mwana wake wobadwa yekha. Akumaneneratu chimenechi, Mulungu ananena mu ulosi wa Ezekieli kuti: “Sudzakhalanso kufikira akadza iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa iye.”​—Ezekieli 21:27.

Kunali kwa Yesu Kristu kumene Mulungu anapereka chiweruzo cha kulamulira mtundu wa anthu monga woimira wa ulamuliro wa Yehova. Chifukwa chakuti Ufumu wa Mulungu mwa Kristu uli njira yabwino koposa yolamulira mtundu wonse wa anthu, Yesu anaphunzitsa amvetseri ake kupemphera kaamba ka iwo. “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi,” anatero Kristu: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:9, 10.

Mwa njira imene Yesu anachitira ndi anthu, iye anasonyeza mtundu wa wolamulira amene iye adzakhala. Kristu motsimikizirika anali ndi chifundo, popeza kuti “powona makamuwo, anagwidwa mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Yesu anasonyeza kuzama kwa chikondi chake kaamba ka atsatiri ake pamene iye ananena kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Iye anakonda anthu mokwanira kupereka moyo wake monga dipo. Nsembe imeneyo imachipangitsa kukhala chothekera kaamba ka awo olandira iyo kuwomboledwa kuchokera ku uchimo, matenda, ndipo ngakhale imfa.​—1 Yohane 2:1, 2; Chibvumbulutso 21:1-4.

Akumaneneratu mmene kulamulira kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu kukakhalira kolungama, kolunjika, ndi kwa mtendere, mneneri Yesaya anawuziridwa kulemba kuti: “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”​—Yesaya 9:6, 7.

Oimira a pa dziko lapansi a kulamulira kwa Mulungu adzakhala monga amuna amene tsopano akuwunikira mikhalidwe yachikondi ya Yesu monga oyang’anira mu mpingo wowona Wachikristu. Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo ankhalwe, amuna amenewa amasonyeza kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka nkhosa, monga momwe anachitira Yesu Kristu. Ponena za amuna aumulungu amenewo, mneneri Yesaya analemba kuti: “Tawonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.” (Yesaya 32:1) Oimira a ulamuliro wa Mulungu oterowo adzatumikiranso zikondwerero zaumulungu m’dziko latsopano.​—Salmo 45:16.

Kusintha Kwakukulu Kuli Pafupi!

Ufumu wa Mulungu usanatenge kulamulira kosatsutsika kwa mtundu wa anthu, kusintha kwakukulu kuyenera kuchitika. Kusintha kumeneku kudzabweretsa kumapeto kugawanikana kwautundu. M’malo mwa maboma ambiri a anthu owombana, padzakhala boma limodzi lolungama la kumwamba logwirizanitsa mtundu wa anthu monga munthu mmodzi wokhala mu mtendere. Akumaneneratu za chimenechi, mneneri Danieli analemba kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [maboma aumunthu], nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44.

Kulamulira kwa Mulungu kuli yankho lokha ku mavuto a boma oyang’anizana ndi mtundu wa anthu lerolino. Mkhalidwe mu umene anthu tsopano akudzipeza iwo eni uli wowopsyeza kukhalapo kwawo kwenikweni! Ndipo palibe kuthetsa kwa munthu komwe kungagwire ntchito. Chotero, chikakhala chanzeru kupereka chisamaliro ku kuthetsera kwa Baibulo ndi kuyang’ana kutsogolo ndi chidaliro ku nthaŵi yomwe siiri kutali kwenikweni pamene anthu owongoka mtima adzasangalala pansi pa kulamulira kosatokosedwa ndi kodalitsidwa kwa Mulungu.

[Chithunzi patsamba 6]

“Mfumu idzalamulira m’chilungamo”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena