Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 3-4
  • Kodi Akufa Ali ndi Chiyembekezo Chotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akufa Ali ndi Chiyembekezo Chotani?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kodi Akufa Ali Amoyo?’
  • Kodi Akufa Adzakhalanso Ndi Moyo?
  • Kodi Mzimu wa Munthu Sufa?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Baibulo Limanenapo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu cha Chiukiriro Ncholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Imfa
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 3-4

Kodi Akufa Ali ndi Chiyembekezo Chotani?

BANJA lina la achichepere linali pa ulendo womka ku gombe la nyanja lakum’mawa kwa South Africa pa tchuthi. Makolo a mkaziyo anali m’galimoto lina chapatsogolo pang’ono. Mwadzidzidzi, tayala linaphulika. Pamene anali kukonzekera kulisintha cha pambali pa msewu, dilaiva woledzera anagunda magalimoto aŵiriwo. Mwamuna wachikulireyo ndi mkazi wake anafa. Mwamuna wocheperapoyo anafa masiku ochepekera pambuyo pake. Mkazi wake anathyoka nthiti ndi zivulazo zina. Mwana wake wakhanda anavulala ubongo umene unamchititsa kuuma ziŵalo.

Ndi tsoka lalikulu chotani nanga m’banja lokanthidwa limeneli! Pamene Carolann, mlongo wa mkazi wachichepereyo, anamva za chochitikachi, anakomoka. Masoka otere amachitika m’maiko onse. Kaŵirikaŵiri achibale ndi mabwenzi okanthidwa ndi chisoniwo amadabwa kuti, ‘Kodi akufa alidi akufa,’ kapena . . .

‘Kodi Akufa Ali Amoyo?’

Pafupifupi zipembedzo zonse zimaphunzitsa kuti moyo uli wosakhoza kufa. Chifukwa chake, otsatira awo amakhulupirira kuti omafawo salidi akufa koma kuti akali chikhalirebe amoyo kumwamba, m’purigatoriyo, kapena m’helo. Monga momwe kumaphunzitsidwira m’matchalitchi ambiri, a m’malo otsirizirawa amazunzika kwadzawoneni ku umuyaya wonse. Koma kodi Mulungu wachikondi akachititsadi kuvutika kotero pa zolengedwa zake?​—1 Yohane 4:8.

Kukawonekera kuti sangatero, koma tingatsimikize motani? Talingalirani mosamalitsa umboni wa Baibulo wotsatirawu. “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Kodi mawu owuziridwa amenewa amanena kuti munthu woyamba, Adamu, anapatsidwa moyo? Ayi, anakhala wamoyo, munthu wamoyo. Zimenezi zikutsimikiziridwa ndi mtumwi Paulo, amene adalemba kuti: “Monga momwe lemba linena, munthu woyamba, Adamu, anakhala moyo wamoyo.” Paulo anali kugwira mawu kuchokera ku Genesis.​—1 Akorinto 15:45, The Jerusalem Bible.

Kodi moyo wa munthu ungafe? Mneneri Ezekieli adalemba kuti: “Miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4, 20; Mlaliki 9:5, 10) Mwachiwonekere, ngati moyo uli wakufa, pamenepo munthuyo sadziŵa chirichonse, chifukwa chake sangathe kuzunzika. Mu nkhani yake yapoyera yoyamba pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro analengeza kuti: “Kudzali kuti wamoyo aliyense wosamvera mneneri ameneyu [Yesu], adzasakazidwa konse mwa anthu.” Chotero moyo ngwokhoza kufa.​—Machitidwe 3:23.

Kodi Akufa Adzakhalanso Ndi Moyo?

Onse amene amakhulupirira kuti Baibulo liri lowona amadziŵa kuti Yesu anafa ndipo anaukitsidwa pa tsiku lachitatu. (Machitidwe 10:39, 40) Kodi zimenezi zikanachitika motani? Mwamphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu.

Kodi chiukiriro cha Yesu sichikuphatikizidwa? Chikutero. Monga momwe Paulo analembera ku mpingo wa Korinto kuti: “Kristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula cha iwo akugona. Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu . . . Kristu.” (1 Akorinto 15:20-22) Chifukwa chake, ambiri adzaukitsidwa kwa akufa. Yesu anatinso: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, ku kuuka kwa moyo.” (Yohane 5:28, 29) Zimenezi zikutsimikizira chiukiriro cha mamiliyoni ambiri.

Ngati malongosoledwe apamwambapawa adzutsa chikondwerero chanu m’chiukiriro, inu mungafunse kuti, ‘Kodi chiukirirocho ncha ayani, ndipo liti?’ Tiyeni tipende mafunso ofunika amenewa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena