Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 21-23
  • Kodi Mulungu Adzachitapodi Kanthu Ponena za Chisalungamo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Adzachitapodi Kanthu Ponena za Chisalungamo?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chisalungamo​—Kodi Nchifukwa Ninji Chinaloledwa?
  • Kodi Ndiliti Pamene Chisalungamo Chidzatha?
  • “Ndipo Chotero Kodi Mulungu Ali Wosalungama?”
  • Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
    Nkhani Zina
  • Yehova Amakonda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Tingatani Ngati Pachitika Zopanda Chilungamo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • “Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 21-23

Kodi Mulungu Adzachitapodi Kanthu Ponena za Chisalungamo?

“SICHIRI konse chabwino.” Wophunzira wachichepere anawonekera kukhala wokhumudwa, wodzazidwa ndi mkwiyo pambuyo pokumana mwaumwini ndi kukhotetsa chilungamo kowonekeratu. “Ngati palidi Mulungu,” iye anapitiriza tero, “ndimotani mmene iye angalolere chisalungamo chotero?” Kodi mukanamvera chifundo mkazi wachichepereyu? Mwinamwake inde. Koma kodi mukanayankhanso chitsutso chake?

Pamene munali mwana, nthaŵi zina mungakhale munawona kuti makolo anu anakulolani kuchitiridwa mosalungama. Koma chisalungamo chowonekeratu choterocho sichinatsimikizire konse kuti iwo kunalibeko, kodi chinatero? Mofananamo, kulola chisalungamo kwa Mulungu sikumatsimikizira kusakhalapo kwake m’njira iriyonse.

Komabe, wophunzira wachichepereyo anayankha kuti iyi inali nkhani yosiyana. Iye anadziŵa kuti tate waumunthu wopanda ungwiro angakhale wosalungama iyemwini. Kapena chifukwa cha kusadziŵa nsonga zonse, iye sangazindikire chisalungamo pamene achiwona. Kuwonjezerapo, chifukwa cha kukhala ndi polekezera kwa anthu, iye angakhale wopanda mphamvu kuchita chirichonse ponena za chisalungamo chomwe anawona. Palibe chirichonse cha izi, iye anatsutsa tero, chomwe chingagwire ntchito kwa Mulungu wolungama yemwe ali wamphamvu zonse ndi wodziŵa zonse.

Nanunso mungaganize kuti kulola kwa chisalungamo sikuli kogwirizana konse ndi mikhalidwe ya Mulungu. Komabe, kodi zingachitike kuti m’nzeru zake zotheratu, Mulungu ali ndi chifukwa chotsimikizirika cha kulolera chisalungamo kwa nthaŵi yaitali?

Olemba Baibulo analingalira Mulungu kukhala “wokonda chilungamo ndi chiweruzo.” “Njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo,” analemba tero Mose.​—Salmo 33:5; Deuteronomo 32:4; Yobu 37:23.

Pambali pa kuwona Yehova monga Mulungu wolungama yemwe sakondwera ndi chisalungamo, olemba Baibulo anavomereza kuti iye tsiku lina akachotsa icho. Mwachitsanzo, Yesaya ananeneratu mkhalidwe uwu: “Tawonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo. Pamenepo chiweruzo chidzakhala m’chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m’munda wobalitsa.” (Yesaya 32:1, 16) Koma kodi ndi liti? Ndipo ngati Mulungu amalakalaka kuchotsa chisalungamo pa dziko, kodi nchifukwa ninji iye anachilola icho poyambapo?

Chisalungamo​—Kodi Nchifukwa Ninji Chinaloledwa?

Panali nthaŵi imene panalibepo chisalungamo m’chilengedwe. Icho chinakhalapo kokha pambuyo pa kupanduka kwa Adamu ndi Hava pansi pa chitsenderezo cha Satana Mdyerekezi ndi pamene chisalungamo chinadziŵika ku mtundu wa anthu. Satana sanawonongedwe pa nthaŵi yomweyo pa nthaŵi ya kupandukako. Chifukwa cha chifuno chake chabwino, Mulungu analola nyengo ya nthaŵi imene munthu akachita chisalungamo, ndipo ichi chikakhala kaamba ka chifuno cha kuyesa awo odzipereka kwa Iye, kaya ngati iwo akatsimikizira kukhala okhulupirika kwa Iye. Kusankha kwawo kukhala osunga umphumphu kukakhala kukana kuthekera kwa Satana kwa kupatutsa chilengedwe chonse cha anthu motsutsana ndi Mulungu. Ndi kuyeretsedwa kwa ulamuliro wa Mulungu, ntchito za Satana zikawonongedwa, ndipo chisalungamo chonse chikachotsedwa.

Pa nthaŵi ino, ngati Mulungu akanaletsa anthu mokakamiza kuchita chisalungamo, iye akanakhala akuwalanda iwo ufulu wa kusankha. Pambali pa icho, mwa kuwalola anthu kuziŵona zotulukapo za chisalungamo za zolakwa za ena, Mulungu akusonyeza mmene chinaliri choipa kwa Adamu ndi Hava kupanduka mosalungama motsutsana ndi malamulo aumulungu, kuwaloŵa m’malo ndi miyezo yawo yolakwika. Mwa kulola mtundu wa anthu kututa zomwe wafesa, Mulungu akuthandiza anthu owona mtima kuzindikira ukulu wa kuchitira zinthu m’njira yake.​—Yeremiya 10:23; Agalatiya 6:7.

M’kuwonjezerapo, machitidwe a chilungamo kapena chisalungamo chomwe anthu aliyense payekha amachita amapereka umboni wotsimikizirika. Machitidwe amenewa amampatsa Mulungu maziko olongosoka pamene iye akadziŵira yemwe ali woyenerera kukhala ndi moyo pa dziko lapansi m’dziko latsopano pamene chilungamo chokwanira chidzabwezeretsedwa. Polingalira chimenecho, timaŵerenga kuti: “Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.”​—Ezekieli 18:21.

Kodi Ndiliti Pamene Chisalungamo Chidzatha?

Zochita za Yehova Mulungu ndi mtundu wa anthu nthaŵi zonse zakhala zolungama ndi zozindikiritsidwa ndi chikondi chokoma mtima. Akumasonyeza chimenecho, pamene Abrahamu mtumiki wokhulupirika wa Mulungu sanamvetsetse chifukwa chimene chinachake chinali kuchitika, iye ananena za Mulungu kuti: “Musamatero ayi, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuti olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” (Genesis 18:25) Ndi kudza kwa Kristu, mikhalidwe ya Mulungu ya chilungamo ndi chikondi chokoma mtima inakulitsidwa. Makonzedwe a nsembe ya dipo mwa Kristu Yesu anatsegula njira kwa aliyense, Myuda ndi wosakhala Myuda, kupeza moyo wosatha. Ichi chinatsogolera mtumwi Petro kunena kuti: “Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Mboni za Yehova ziri zokangalika m’kulengeza kuti Mfumu Yaumesiya ya Mulungu yayamba kulamulira ndikuti nthaŵi iri pafupi pamene chilungamo chidzabwezeretsedwa ku dziko lathu lapansi ku mlingo wangwiro.a Izi zidzakwaniritsidwa pamene Mfumuyo idzawononga dziko lopanda chilungamo liripoli ndi kuphwanya mphamvu ya mulungu wake wosawoneka, Satana Mdyerekezi. Baibulo limasonyeza kuti izi zidzachitika posachedwapa pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” yomwe kaŵirikaŵiri imatchedwa Armagedo.​—Chibvumbulutso 16:14, 16.

‘Mulungu sali wosalungama pamene afikitsa mkwiyo wake,’ chotero Armagedo idzakhala nkhondo yachilungamo. (Aroma 3:5) Pambuyo pake, Kristu Yesu ndi olamulira anzake, onga ngati atumwi, adzalamulira kumwamba kwa zaka chikwi. (Chibvumbulutso 20:4) Mamiliyoni a anthu omwe avutika ndi chisalungamo cha m’zaka zapitazi adzaukitsidwa ku dongosolo lolungama pa dziko lapansi, mudzi woyambirira wa mtundu wa anthu, kudzakumana ndi chilungamo changwiro kwa nthaŵi yoyamba m’miyoyo yawo.

“Ndipo Chotero Kodi Mulungu Ali Wosalungama?”

Mtumwi Paulo anafunsa choncho ponena za chimodzi cha zochita za Mulungu. Kodi yankho ndilotani? “Ndithudi ayi,” analemba choncho Paulo. Akumayerekeza anthu kukhala dothi lomwe lawumbidwa ndi wowumba mbiya kukhala zotengera zoyenerera kaya mkwiyo kapena chifundo, Paulo analongosola kuti: “Ngakhale kuti Mulungu ali wokonzekera kusonyeza mkwiyo wake ndi kusonyeza mphamvu yake, chikhalirechobe iye moleza mtima amapirira ndi anthu omwe amamkwiyitsa, mosasamala kanthu za ukulu womwe amayenerera kuwonongedwa. Iye amawalezera mtima chifukwa cha anthu ena, kwa amene iye akufuna kukhala wachifundo, kwa amene iye akufuna kuvumbula chuma cha ulemerero wake.”​—Aroma 9:14, 20-24, The Jerusalem Bible.

Mofanana ndi wophunzira wachichepere wotchulidwa poyambirirayo, inu nthaŵi zina mungachipeze kukhala chovuta kumvetsetsa chifukwa chimene kaŵirikaŵiri Mulungu amalolera chisalungamo kapena cholakwa chinachake chachindunji. Koma kodi ndife ndani​—zowumba za manja ake​—kuti tikaikire kuleza mtima kwake ndi nzeru m’kuchita choncho? Yehova Mulungu anamuwuza Yobu kuti: “Ngakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndiri woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?”​—Yobu 40:8.

Sitidzafuna konse kukhala waliwongo lakuchita chimenecho. M’malomwake, tidzafuna kusangalala m’kudziŵa kuti ngakhale kuti chisalungamo chidakalipo, Mulungu wachilungamo posachedwapa adzachichotsa pa dziko lonse lapansi.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka umboni wakuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kwake dziko lapansi kosawoneka mu 1914, onani masamba 134-41 m’bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Bukhuli lirinso ndi chaputala pa mutu wakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?”

[Chithunzi patsamba 23]

Kuloledwa kwa chisalungamo sikungagwiritsidwe ntchito m’njira iriyonse kutsimikizira kusakhalapo kwa Mulungu

Kodi Mulungu ngwolakwa pamene woyendetsa galimoto woledzera akana kugwiritsira ntchito mikhalidwe ya luntha lachibadwa, kudziletsa, ndi kulingalira?

Nthaŵi yayandikira pamene chilungamo chokwanira chidzabwezeretsedwa ku dziko lathu lapansi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena