Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/1 tsamba 4-7
  • Mbali Yodabwitsa ya Ubwino wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali Yodabwitsa ya Ubwino wa Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchuluka kwa Ubwino wa Mulungu
  • Ubwino wa Mulungu kwa Akhulupiriri
  • Kodi Mudzapindula Mokulira Chotani Ndi Ubwino wa Mulungu?
  • Kusangalala Ndi Ubwino wa Mulungu
  • Yehova Ndiye Chitsanzo Chachikulu Pankhani Yosonyeza Ubwino
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Ubwino Waukulu wa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”
    Yandikirani Yehova
  • Pitirizani Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/1 tsamba 4-7

Mbali Yodabwitsa ya Ubwino wa Mulungu

MULUNGU ngwabwino! Kodi kanenedwe koteroko mwakamva kapena kukagwiritsiradi ntchito inumwini nthaŵi zingati? Koma kodi munalingalirapo za mbali yonse ya ubwino wa Mulungu kaamba ka inu? Kusinkhasinkha koteroko kumazamitsa chiyamikiro chathu cha mtundu wa Mulungu amene timalambira.

Ngakhale kuli tero, choyamba, tiyenera kumvetsetsa chimene ubwino uli. Ndithudi, ubwino uli mkhalidwe wa kukhala wabwino mosiyana ndi kukhala woipa. Koma ubwino umaposa zimenezo. Uwo uli mkhalidwe wogwira ntchito. Munthu wabwino amachita zabwino. Ndipo Mulungu, mu ubwino wake, amatichitira zinthu zabwino zambiri kotero kuti mitima yathu imakondwera naye.

Kuchuluka kwa ubwino wa Mulungu kukuwonekera m’mawu ake kwa Mose m’chipululu cha Sinai. Kumeneko, iye analonjeza mtumiki wake wokhulupirika kuti: ‘Ndidzapititsa ubwino wanga wonse pamaso pako.’ Akumakwaniritsa lonjezo limenelo ndi kugwiritsira ntchito dzina lake, Mulungu akupitirizabe kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.”​—Eksodo 33:19; 34:6, 7.

Chotero, ubwino wa Mulungu umaphatikizapo chifundo limodzinso ndi chisomo chake, kukoma mtima kwake, ndi chowonadi chake. Kuwonjezerapo, ubwino wake umawoneka mwa iye pokhala “wolekereza,” ndi woleza mtima. Ngakhale nditero, izi sizitanthauza kuti iye ali ngati kholo lolekerera mopambanitsa, akumalola uchimo kupitirizabe kwamuyaya mosaletsedwa. Iye adzakhalabe “wosamasula wopalamula” kwa ochimwa osalapa. Mulungu wabwino sangalole kuipa kupitirizabe osaletsedwa.

Kuchuluka kwa Ubwino wa Mulungu

Tsopano, talingalirani njira zina zimene Mulungu wasonyezera ubwino wake. Choyamba, iye anali wabwino kwa anthu mwa kulenga dziko lapansi pachiyambi. Iye sanangopereka zofunikira zazikulu zokha kaamba ka moyo wa munthu. M’malomwake, iye anakometsa pulaneti yathu molemera kupangitsa kukhalamo kukhala kosangalatsa kwenikweni. Iye anapereka zakudya ndi zakumwa zosiyanasiyana mochulukira. Iye anapanga mitundu yosiyanasiyana ya nyama zochititsa chidwi ndi mbalame, ndipo analenganso maluŵa omawonjezera mtundu ndi kukongola ku malo otizinga. Kuwonjezerapo, iye anapanga malo amitundu yosiyanasiyana osangalatsa kuwawona. Kulekeranji, nthaŵi iriyonse titawona kuloŵa kwa dzuŵa kwaulemerero kapena kupangika kwa mitambo kodabwitsa, timawona umboni wa ubwino wa Mulungu!

Pamene iye analenga mwamuna ndi mkazi, ubwino wa Mulungu unawonedwanso. Iye anapatsa Adamu ndi Hava matupi angwiro athanzi labwino, ndi kuwaika m’munda wa Edene. Kenaka iye anawapatsa ntchito yosangalatsa ndi yodzetsa chitokoso: “Mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” Chotero, iye anawaikira chiyembekezo chakusangalala ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la paradaiso pakati pa mbadwa zawo zambirimbiri. (Genesis 1:26-28; 2:7-9) Inali mphatso ya ukwati yabwino chotani nanga kwa okwatirana oyamba aŵiriwo!

Ngakhale pamene Adamu ndi Hava anapanduka, Mulungu sanawasiye iwo kotheratu. Panthaŵi imeneyo, ngati iye akanawalanga ndi imfa ya panthaŵi yomweyo, iye akanachitabe chimene chinali cholungama. Komabe, iye anali wabwino kwa amene tsopano anali okwatirana ochimwa. Anawalola kukhalabe kwa kanthaŵi ndi kukhala ndi ana.​—Genesis 5:1-5.

Ndiponso, ubwino wa Mulungu wapitirizabe kulinga kwa mtundu wa anthu ochimwa chiyambire pa nthaŵiyo. Monga mmene Mfumu Davide ananenera kuti: “Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.” (Salmo 145:9) Iye amapereka mochuluka kotero kuti moyo wa munthu ungapitirizebe pa chuma chake, dziko lapansi. Yesu ananena kwa Ayuda a m’tsiku lake kuti: “Atate wanu wakumwamba . . . amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi osalungama.” (Mateyu 5:45) Njala iriyonse kapena kusoŵa kumene kulipo sikuli chifukwa chakuti Mulungu walephera kupereka kwa mtundu wa anthu. Kuli chifukwa cha chinyengo, nkhanza, ndi kulephera kwa anthu.

Mulungu amalolanso mtundu wa anthu kugwiritsira ntchito miyala ya mtengo wapatali ya dziko lapansi, ndipo iye sanawabisire mlingo winawake wa chidziŵitso cha miyamba ya nyenyezi ndi kapangidwe ka zinthu. Mowonadi, Yehova ngwabwino kwa mtundu wa anthu, ngakhale kuti modzitukumula ambiri amati kulibe Mulungu, ndipo ena amagwiritsira ntchito molakwa ubwino wake kukwaniritsa zolinga zadyera, ku mlingo wa kuponderezadi anthu anzawo.​—Salmo 14:1.

Ubwino wa Mulungu kwa Akhulupiriri

Motero, ngati Mulungu wakhaladi wabwino kwa mtundu wa anthu mwachisawawa, zochita zake ndi akhulupiriri zimakondweretsadi mtima. Choyamba, pamene Adamu ndi Hava anapanduka poyambapo, Mulungu analosera kuti “mbewu” ikawonekera imene m’kupita kwa nthaŵi ikathetsa ziyambukiro zoipa za uchimo wawo. (Genesis 3:15) Pamene nthaŵi inapita, mbadwa zambiri za Adamu zinalambira Mulungu mokhulupirika mosasamala kanthu za kupanda ugwiro kwawo, ndipo ulosi woyambirira umenewu unawapatsa chiyembekezo cha mtsogolo mwabwinopo. Mmodzi wa alambiri okhulupirika ameneŵa, Abrahamu, anafika pa kutchedwadi “bwenzi la Mulungu.”​—Yakobo 2:23.

Mulungu analonjeza Abrahamu kuti mbadwa zake zikachuluka kukhala mitundu yambiri ndikuti mzera woyambirira wa ana ake ukatenga dziko la Kanani. M’kukwaniritsa zimenezi, Aisrayeli, mbadwa za Abrahamu, pambuyo pake anadzalinganizidwa kukhala mtundu. (Genesis 17:3-8; Eksodo 19:6) Kachiŵirinso, Mulungu anali wabwino kwa mtundu watsopano umenewu, kuwalanditsa iwo ku ukapolo mu Igupto, kuwatetezera m’chipululu, kuwapatsa mpambo wa malamulo ndi ansembe, ndipo pomalizira pake kuwapatsa dziko lachonde la Kanani monga choloŵa.

M’kupita kwa nthaŵi, Israyeli anakhala ufumu, ndipo Yehova anapatsa ntchito kwa mfumu yaumunthu yachitatu ya mtunduwo, Solomo, kumanga kachisi m’Yerusalemu monga malo apakati a dziko lonse a kulambiridwa Kwake. Pamene kachisiyo anamalizidwa, panali madyerero aakulu a kupereka kachisi ndi phwando lachisangalalo. Pambuyo pake, cholembedwacho chikunena kuti, Aisrayeli “anadalitsa mfumu, napita ku mahema awo osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova [anachita].” (1 Mafumu 8:66) Kunali zochitika zinanso pamene mitima ya Aisrayeli inasefukira ndi chisangalalo chifukwa cha ubwino wa Mulungu kwa iwo.

Ngakhale kuli tero, choipapo nchakuti iwo nthaŵi zonse sanayamikire mwaŵi wawo wakukhala alambiri a Mulungu wowona yekha. M’kupita kwa nthaŵi, Aisrayeli onse anakhala osakhulupirika, ndipo mu 607 B.C.E., Yehova anawalekerera kutengeredwa ku Babulo monga akapolo. Monga mmene Mulungu ananenera kwa Mose, chifukwa cha ubwino Wake weniweniwo adzakhalabe “wosamasula wopalamula.”​—Eksodo 34:7.

Komabe, pambuyo pa zaka 70 Mulungu mokoma mtima anabwezera otsalira okhulupirika a Aisrayeli ku dziko lakwawo. Kodi nchiyani chidamsonkhezera kutero? Ubwino wake. Yeremiya analemba mwaulosi kubwerera kwa Aisrayeli kuchoka ku Babulo akumati: “Ndipo adzadza nadzayimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova.” Mneneriyo anapitirizabe kuti: “Anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.”​—Yeremiya 31:12, 14.

M’kupita kwa nthaŵi, Yesu anadza ku dziko lapansi natsimikizira kukhala “mbewu” yonenedweratuyo mu ulosi uja woperekedwa kumbuyoko mu Edene. (Genesis 3:15) Baibulo limanena kuti: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Imfa ya Yesu inapereka dipo kuwombola anthu mu uchimo ndi kuwabwezeretsa ku ungwiro. Chotero, ziyambukiro zoipa za chimo la Adamu pomalizira pake zikalakidwa. Monga mmene Paulo analembera kwa Aroma kuti: “Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.” (Aroma 5:19) Tiyamikira ubwino wa Mulungu, anthu a mitima yolungama tsopano anakhala ndi chiyembekezo cha kupeza moyo wosatha. Iwo angakhaledi mabwenzi a Mulungu, monga mmene Abrahamu anachitira.

Mulungu akupitirizabe kusonyeza ubwino lerolino kwa awo omulambira. Iye amapereka uphungu kupyolera m’Baibulo kuwathandiza kusamalira mavuto awo. (Salmo 119:105) Iye amapereka mphatso yaulere ya mzimu wake kuwathandiza kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake yolungama. Ndipo iye amavumbula zifuno zake, kotero kuti Akristu owona ayang’ane kutsogolo ku dziko latsopano lachilungamo lomwe lidzaperekedwa pambuyo pa kupita kwa dziko lino lakale. (Miyambo 4:18; 2 Petro 3:13) Akristu ali ndi chidaliro ponena za zinthu zoterozo chifukwa chakuti Mulungu, mu ubwino wake, wazivumbula izo m’Mawu ake osalakwa.​—2 Timoteo 3:16.

Inde, kulingalira ubwino wa Mulungu kumakondweretsadi mitima yathu kulinga kwa iye. Koma kumadzutsanso funso:

Kodi Mudzapindula Mokulira Chotani Ndi Ubwino wa Mulungu?

Kwenikweni, kaya ndinu yani, inu mukupindulabe ndi ubwino wa Mulungu. Mumapuma, mumadya, mumamwa, mumasangalala ndi moyo​—zonsezo ziri mphatso zochokera kwa Mulungu. Koma kodi mumapindula nazo mokwanira monga kungathekere? Kumbukirani, ubwino wa Mulungu kwa Adamu ndi Hava unachepetsedwa pamene iwo anachimwa. Mofananamo, iye adzachepetsa zopereka zake kwa ife pokhapo ngati tichita m’njira yolondola kulinga ku ubwino wake. Kodi tingatero motani?

Wamasalmo anapemphera kuti: “Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.” (Salmo 119:66) Limenelo liyenera kukhalanso pemphero lathu. Popeza kuti Mulungu ngwabwino, tifunikira kuphunzira kukhala abwino mofanana naye. Paulo analimbikitsa kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.”​—Aefeso 5:1.

Timatero, choyamba mwa kuphunzira Baibulo kuti tidziŵe chimene ubwinowo uli. Kenaka, timapempha thandizo la Mulungu kuti tikulitse mkhalidwe umenewu. Ubwino uli chipatso cha mzimu, limodzi ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, . . . chikhulupiriro, chifatso [ndi] chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Tingakulitse mikhalidwe yonseyi mwa kudalira pa mzimu wa Mulungu, kuphunzira Baibulo lomwe linawuziridwa ndi Mulungu, kupemphera kwa iye kaamba ka thandizo, ndi kuyanjana ndi Akristu a maganizo ofananawo.​—Salmo 1:1-3; 1 Atesalonika 5:17; Ahebri 10:24, 25.

Baibulo limanenanso kuti: “Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzayimbira chilungamo chanu.” (Salmo 145:7) Inde, Mulungu amatiyembekezera kuwuza ena za ubwino wake. Tiyenera kulankhula momasuka ponena za Atate wathu wakumwamba.

Chomalizira, sitiyenera kutenga mosasamala ubwino wa Mulungu. Zowona, Yehova amakhululukira ochimwa. Mfumu Davide anali wachidaliro za yankho lachiyanjo pamene anapemphera kuti: “Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu: Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.” (Salmo 25:7) Kodi zimenezo zimatanthauza kuti tingadzilole kuchita machimo ndi kuyembekezera mwachidaliro kuti Mulungu adzatikhululukira? Kutalitali. Kumbukirani, ubwino wa Mulungu umatanthauza kuti iye ali “wosamasula wopalamula” kwa ochimwa osalapa.

Kusangalala Ndi Ubwino wa Mulungu

Pamene tikusangalala ndi ubwino wa Mulungu mokwanira, mitima yathu imakondwa chotani nanga kulinga kwa iye! Timalimbikitsidwa kutsatira chilangizo chabwino cha mtumwi Paulo chakuti: “Yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi chowonadi.”​—Aefeso 5:8, 9.

Tsiku lirilonse, timazindikira nkhaŵa ya chikondi cha Mulungu kwa ife. Ngakhale pansi pa mikhalidwe yovutitsitsa, timadziŵa kuti iye samasiya omukonda. Inde, tikusangalala ndi mtendere wamaganizo koposa wa wamasalmo: “Inde, ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga: Ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.”​—Salmo 23:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena