Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/1 tsamba 20
  • Thandizo Labwino Koposa Lodziŵira Mtsogolo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizo Labwino Koposa Lodziŵira Mtsogolo
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mmene Ndinaphera Ludzu la Mawu a Mulungu
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/1 tsamba 20

Thandizo Labwino Koposa Lodziŵira Mtsogolo

Yosimbidwa Ndi Wina Amene Anapeza Njira ya ku Moyo

CHIPEMBEDZO chinachita mbali yaikulu m’moyo wa banja langa. Atate wanga anali Myuda, ndipo ngakhale kuti iwo anatembenukira ku Chikatolika ndi cholinga chofuna kukwatira amayi wanga, iwo anali adakali ndi ulemu waukulu kaamba ka Baibulo. Amayi anachokera ku banja lozama kwenikweni m’miyambo Yachikatolika​—aŵiri achemwali awo anali avirigo, msuwani wawo anali monsignor, ana aamuna aŵiri a alongo awo anali afriar.

Mkati mwa nkhondo yadziko yachiŵiri, kudera nkhaŵa, mantha, ndi chiwopsyezo cha nthaŵizonse cha kutengeredwa ku msasa wachibalo chifukwa chokhala Myuda zinachititsa imfa yamwamsanga kwa atate wanga. Pokhulupirira mozama m’chiphunzitso cha kusafa kwa moyo, amayi wanga anatengamo mbali m’kukumana kwa madzoma okhulupirira mizimu, moyesera kukambitsirana ndi atate wanga.

Pamene ndinakula, chipembedzo chamwambo chinapitirizabe kukhala mbali ya moyo wanga. Ndinakhalabe “Mkatolika wabwino.” Chikhalirechobe, chiphunzitso Chachikatolika sichinakhoze kulongosola zomwe zinali mtsogolo mwanga. Kodi nkwayani kumene ndikapita kaamba ka thandizo kuti ndidziŵe?

Monga mmene amayi wanga anachitira nthaŵi ina, nanenso ndinafunsira olankhula ndi mizimu. Popeza kuti iwo ankayamba kukumana kwawo kwa madzomako ndi chizindikiro cha mtanda ndi mapemphero, ine ndinakhutiritsidwa kuti zochitika zachilendo zimene ndinawona ndi maso zinachokera kwa Mulungu. Panali pa nthaŵi imeneyi pamene ineyo, pofuna kuchita chinachake kutonthoza kuvutika kwa enawo, ndinagwirizana ndi bungwe Lachikatolika limene linakonza maulendo opita ku malo oyera a Mariya ku Lourdes, kumene odwala anayembekezera kuchiritsa kozizwitsa.

Sindinamvepo za Mboni za Yehova kufikira tsiku limene mwamuna wanga analandira magazine aŵiri omwe ndinasangalala nawo kwambiri. Chimene chinandikondweretsa koposa chinali chakuti Baibulo linagwidwa mawu mochirikiza ndemanga za m’magazinewo. Pa nthaŵi yomweyo ndinazindikira kuti zofalitsidwa zimenezo zikakhala zothandiza kwenikweni m’kupeza chidziŵitso cha Mawu a Mulungu. Ndinalemba kufunsira sabusikripishoni ya magazine onse aŵiri. Mboni za Yehova zinandichezera, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo.

Ndinali wotenthedwa maganizo kwambiri ponena za zowonadi za Baibulo zimene ndinkaphunzira ndi kuyamba kuzilankhula izo kwa anzanga. Ndinadabwa kotheratu ndi kuyankha kwa mnzanga, amene anakonza maulendo achipembedzo, pamene ndinamuuza kuti ndinali kusanthula Baibulo ndi Mbonizo. Iye anakwiya kwambiri ndi kunena zinthu zoipa ponena za iwo kotero kuti ndinachokapo. Kenaka ndinayang’anizana ndi chitsutso kuchokera kwa mwamuna wanga. (Mateyu 10:36) Poyamba kunali kovuta, koma pamene ndinagwiritsira ntchito mowonjezereka zinthu zimene ndinaphunzira, moyo wa banja langa unasintha kukhala wabwinopo. Ndinabatizidwa mu 1977.

Tsopano ndinazindikira kuti sindikanapeza konse njira ya ku moyo ngati Mboni za Yehova sizinasonyeze chikondwerero mwa kuyesera kundithandiza kudziŵa zowonadi zodabwitsa za Baibulo. Ndinadziŵanso kuti nanenso ndinali ndi thayo kuchita zonse zimene ndikakhoza kuthandiza ena kudziŵa ponena za Yehova ndi chifuno chake chozizwitsa kaamba ka mtsogolo. Kodi ndimotani mmene ndikachitira chimenechi? Njira yabwino koposa inali kuyamba uminisitala wa nthaŵi zonse. Popeza ndinali kukhala m’nyumba yogawikana mwachipembedzo, chimenechi sichinali chopepuka kwa ine. Koma ndinadalira m’chirikizo la Yehova ndi chitsogozo ndi kuthaŵira mwa iye. Tsopano, ndikukhala m’zaka zachimwemwe koposa m’moyo wanga monga mpainiya wokhazikika. Ndiri wokhutiritsidwa kuposa ndi kalelonse kuti “Yehova ndiye wabwino” ndi kuti aliyense “wakukhulupirira iye” ali wachimwemwe.​—Salmo 34:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena