Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 12/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Atumiki Olalikira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Phunzitsani Ana Anu Kutamanda Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 12
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 12/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ M’chigwirizano ndi chidziŵitso chatsopano ponena za osabatizidwa oyamba kutulukira mu utumiki wapoyera, kodi wophunzira Baibulo angaitanidwe kwa kanthaŵi kochepa kuti awone mmene ntchito imachitidwira?

Kwakukulukulu, osabatizidwa amene amapita ndi Mboni za Yehova mu utumiki wakumunda ali anthu amene ayenerera monga ofalitsa a mbiri yabwino.

Anthu ambiri amalemekeza Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo yabwino ndi yapadera ya ‘kupanga ophunzira, kuwaphunzitsa’ kuchokera ku khomo ndi khomo ndi kupyolera m’maphunziro a Baibulo apanyumba. (Mateyu 28:19, 20) Pamenepa, kodi nchiyani chimene anthu aunyinji angalingalire ponena za munthu wopita ndi Mboniyo mu utumiki? Iwo mosapita m’mbali angalingalire kuti mnzakeyo ndi mtumikinso kapena ali pafupi kukhala tero.

Chitalingaliridwa, zochepera zokha zingaganiziridwe.

M’nthaŵi za kamodzi kamodzi akulu ena alola mtola nkhani, profesa wa pa koleji, kapena onga ameneŵa kupita ndi Mboni ku utumiki wa kunyumba ndi nyumba kuti awone mmene umachitidwira. Ndithudi, mawonekedwe a munthuyo ndi kachitidwe pa zochitika zoterozo sayenera kuwombana ndi miyezo yathu. Ndipo Mboniyo ingafune kutchula kwa eninyumba kuti mnzakeyo ndi mtola nkhani kapena profesa amene ali wokondweretsedwa m’kuwona mmene timachitira ntchito yathu yofunika ya Baibulo.

Ndiponso, makolo Achikristu amapita ndi ana awo mu utumiki ngati ameneŵa ali achichepere kwenikweni kapena mwinamwake osafika pa kukhala ofalitsa osabatizidwa. Chotero makolo ameneŵa samasiya ana awo osasamaliridwa. Kukhala nawo mu utumiki wakumunda kumalola makolowo kulankhula kwa ana awo ponena za Mawu ndi njira za Mulungu “poyenda [iwo] panjira.” (Deuteronomo 6:4-7) Koma iyi ndi mbali ya moyo wa banja Lachikristu, osati nkhani ya kubweretsa kwa Mboniyo munthu wina monga kokha wopenyerera. Ndithudi, kuphunzitsa koteroko kochitidwa ndi makolo kumakonzekeretsa ana kaamba ka nthaŵi pamene adzatamanda Yehova monga ofalitsa.​—Mateyu 21:15, 16; yerekezerani ndi Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 99, 100.

Ngakhale ndi tero, bwanji ponena za munthu kwa amene Mboni ikutsogoza phunziro la Baibulo, munthu amene ali panjira ya kukhala wophunzira? Iye ali ndi chifukwa chabwino chakuuzira achibale, ogwira nawo ntchito, anansi, ndi ena ponena za “zinthu zazikulu za Mulungu” zimene iye waziphunzira kuchokera m’Malemba. (Machitidwe 2:11) Mwamwaŵi, padzakhala nthaŵi pamene iye adzawona kufunika kwa kugawana ndi Mboni za Yehova m’makonzedwe a gulu a “kulengeza mawu a Mulungu.”​—Machitidwe 13:5.

Posachedwapa Nsanja ya Olonda inandandalitsa masitepe oyenera wophunzira woteroyo asanapite ndi Mboni zakumaloko mu utumiki, kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Chiridi chanzeru kuti akhale ndi chidziŵitso chenicheni cha Baibulo, ayenera kumvetsetsa ndi kukhala mogwirizana ndi miyezo ya makhalidwe abwino a Mulungu, ndipo ayenera kukhumba mwini yekha kugawana mu utumiki wapoyera ndi Mboni za Yehova. Chotero akulu aŵiri apampingo angakhale ndi kukambitsirana kothandiza ndi kolimbikitsa kwa nsonga zoterozo ndi iye limodzi ndi Mboni imene ikuphunzira naye Baibulo.a Ichi chiyenera kuchitidwa wophunzira Baibuloyo asanaitanidwe kupita ndi wofalitsa mu utumiki wakumunda kuti akalandire kuphunzitsidwa kopita patsogolo.

Momvetsetseka, pamene wophunzira wayenerera kupita mu utumiki wakumunda ndipo atero kwa nthaŵi yoyamba, iye angafune kwa nthaŵi zoŵerengeka kupita ndi wofalitsa kukaphunzira mmene ntchito yolalikira m’chenicheni imachitidwira. Mtumiki wopita naye angapereke kuphunzitsa kwa kaŵirikaŵi, monga ngati kumupempha iye kuthandiza mwa kuŵerenga malemba kwa kanthaŵi, ndipo m’kupita kwa nthaŵi kumulola iye kutsogolera m’kuchitira umboni kwa mwininyumba. Chotero, iye angapereke ripoti lake loyamba la utumiki wakumunda pamene iye m’chenicheni agawana m’kuchitira umboni wakumunda. Kugawana kwake kopita patsogolo mowonjezereka m’ntchito kumagwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m’mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.”​—Luka 6:40.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka tsatanetsatane, onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, tsamba 17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena