Yehova Amatidziŵa Bwino!
YEHOVA amatidziŵa mowonadi, makamaka ngati ndife atumiki ake okhulupirika. Mabwenzi a pondapo nane mpondepo, achibale, ngakhale makolo, samatidziŵa bwino monga mmene iye amachitira. Nkulekeranji, Mulungu amatidziŵa bwino kwenikweni kuposa ndi mmene timazidziŵira ife eni!
Chidziŵitso changwiro cha Yehova cha atumiki ake chinasonyezedwa bwino lomwe mu Salmo 139. Kodi nchiyani chimene Davide ananena mu salmo limenelo? Ndipo kodi ndimotani mmene kutidziŵa kwa Mulungu kuyenera kuyambukira mawu ndi kachitidwe kathu?
Unyinji wa Zimene Yehova Amadziŵa!
Popeza kuti Mulungu ndiye Mlengi wathu, tiyenera kumuyembekezera kukhala ndi chidziŵitso chokwanira cha ife. (Machitidwe 17:24-28) Chotero, Davide akakhoza kunena kuti: “Munandisanthula, Yehova, nimundidziŵa.” (Salmo 139:1) Kudziŵidwa ndi Mulungu kwa Davide kunali kofanana ndi kuja kopezedwa kupyolera m’kufufuza kosamalitsa. Atasangalala posanthulidwa ndi Yehova, wamasalmo anagonjera mokwanira ku ulamuliro ndi chitsogozo cha Mulungu. Mofananamo, Mboni za Yehova mwapemphero ‘zimapereka njira zawo pa Yehova, kudalira pa iye,’ otsimikizira kuti iye nthaŵi zonse adzachita chimene chiri cholondola. (Salmo 37:5) Muli kudzimva kwa chisungiko chauzimu m’mitima yathu chifukwa chakuti timafunafuna kutsogozedwa ndi nzeru yaumulungu, ndipo timagonjera mofunitsitsa ku chitsogozo chaumulungu. (Miyambo 3:19-26) Mofanana ndi Davide, tingapeze chitonthozo podziŵa kuti Mulungu amatiyang’anira, kumvetsetsa mavuto athu, ndipo nthawi zonse ndiwokonzekera kutithandiza.
“Inu mudziŵa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga,” anavomereza tero wamasalmo. (Salmo 139:2a) Mulungu anadziŵa zirizonse ponena za zochita za Davide, monga ngati kukhala kwake pamapeto pa kugwira ntchito kwa patsiku ndi kuuka pambuyo pa kugona kwausiku. Ngati ndife Mboni za Yehova, lolani kuti tikhale otsimikiziridwa kuti nafenso Mulungu amatidziŵa bwino tero.
Davide anavomereza kuti: “Muzindikira lingaliro langa muli kutali.” (Salmo 139:2b) Ngakhale kuti Mulungu amakhala kumwamba kutali ndi dziko lapansi, iye anadziŵa chimene Davide anali kuganiza. (1 Mafumu 8:43) Chidziŵitso choterocho sichiyenera kutidabwitsa, popeza kuti Yehova “ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7; Miyambo 21:2) Nsonga yakuti Mulungu amawona maganizo athu iyenera kutifulumiza kuganiza pa zinthu zimene ziri zoyera, zabwino, zoyenerera chitamando. Ndipo kuli koyenerera chotani nanga kuti tidzilongosola malingaliro athu mokhazikika m’pemphero lochokera kumtima kotero kuti tingakhale ndi chitsogozo chaumulungu ndi “mtendere wa Mulungu”!—Afilipi 4:6-9.
Wamasalmoyo anawonjezera kuti: “Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.” (Salmo 139:3) Kuyesa mopita Davide kuchokera pa malo awa kupita ku ena ndi pogona iye motsimikizirika kunatanthauza kuti Yehova anasanthula chirichonse chimene wamasalmo anachita. Wam’mwambamwambayo anali kuyesa zochita zonse za Davide kuti awone mkhalidwe weniweni wa kaimidwe kake. Mulungu anali ndi chidziŵitso chokwanira cha njira za Davide, njira zimene anatsatira m’moyo. Pamene Atate wathu wa kumwamba atisanthula ife mofananamo, lolani kuti atipeze tikumtumikira mokhulupirika ndi kukhala “panjira yachilungamo” imene imatsogolera ku moyo wosatha.—Miyambo 12:28.
Popeza kuti panalibe chirichonse chimene akanena chomwe chikakhala chobisika kwa Mulungu, Davide ananena kuti: “Pakuti asanafike mawu pa lilime langa, tawonani, Yehova, muwadziwa onse.” (Salmo 139:4) Titasautsidwa kwenikweni kotero kuti sitikudziwa chimene tinganene m’pemphero, mzimu wa Yehova “umatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka.” (Aroma 8:26) M’zokambitsirana zathu, Mulungu amadziŵa zinthu zimene tinangokhala pang’ono kunena koma n’kuleka, popeza kuti amadziwa malingaliro athu. Ndipo ngati tiri ndi chikondi chomachokera “m’chikhulupiriro chopanda chinyengo,” sitidzayesera kunyenga ena ndi “mawu osalaza.”—1 Timoteo 1:5; Aroma 16:17, 18.
Davide anawonjezera kuti: “Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine.” (Salmo 139:5) Mchenicheni, Yehova anabindikiritsa Davide mofanana ndi mzinda wolaliridwa pankhondo. Wamasalmo mwachiwonekere anadziŵa kuti anali ndi polekezera ku zimene akachita m’nthawi yaumoyo wake. Iye anadziwanso kuti chinali chosatheka kubisala ku diso latcheru ndi dzanja la Mulungu, kapena kulamulira kwake. Ndithudi, Davide sanayesere kufuna kuthawa koteroko, ndipo nafenso sitikutero. Koma lolani kuti tidziphunzitse ife eni kuzindikira kuti dzanja la Yehova liri pa ife monga Mboni zake.
Kudziŵidwa kwa Davide ndi Mulungu kunam’dzaza iye ndi mantha. Chotero, iye analengeza kuti: “Kudziŵa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: kundikhalira patali, sindifikirako.” (Salmo 139:6) Kutidziŵa kwake Mulungu aliyense payekha nkwakuya kwenikweni kotero kuti sitingakumvetsetse, mosasamala kanthu za kuzolowera ndi kuphunzitsidwa. Popeza kumaposa pa kumvetsetsa kwa munthu, tingakhale otsimikiza kuti Yehova amadziŵa zomwe ziri zabwino koposa kaamba ka ife. Chotero, titapemphera kaamba ka chinachake ndipo yankho lake litakhala ayi, tiyeni tigonjere ku chifuniro chaumulungu. Monga mmene mtumwi Yohane analemba kuti: “Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.”—1 Yohane 5:14.
Kulibe Kuthawa Mzimu wa Mulungu
Yehova samangoyankha mapemphero a atumiki ake okhulupirika koma mzimu wake umawagwiriranso ntchito ndi kuwathandiza kuchita chifuniro chake. Ndiiko nkomwe, Davide anafunsa kuti: “Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?” (Salmo 139:7) Wamasalmo anadziwa kuti iye sakathawa mzimu wa Yehova, kapena mphamvu yogwira ntchito, imene ingafikire ngakhala mbali zosafikirika za chilengedwe chaponseponse. Ndipo palibe amene angathawe pamaso pa Mulungu, uko ndiko kuti, kuzemba kuwonedwa ndi iye. Zowona, “Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova,” koma mneneri ameneyo sanakhoze kuzemba kaya chinsomba chimene Mulungu anaikiratu kuti chim’meze kapena kuwerengera kaamba ka ntchito yake yaumulungu. (Yona 1:3, 17; 2:10–3:4) Chotero tiyeni tidalire pa mzimu wa Yehova kutitheketsa kukwaniritsa ntchito yopatsidwa ndi Mulungu.—Zekariya 4:6.
Popeza kuti Davide anadziŵa kuti chikakhala chosatheka kuzemba Mulungu, iye ananena kuti: “Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku [Shelo, NW], tawonani, muli komweko.” (Salmo 139:8) M’tsiku la wamasalmo, ‘kukwera kumka kumwamba’ kunatanthauza kukwera m’mapiri aatali, omwe nsonga zake kaŵirikaŵiri zimakhala zophimbidwa ndi mitambo. Komabe, tidakakhala pansonga la phiri lalitali, sitikhala osafikirika ndi mzimu wa Mulungu. Kuwonjezerapo, sitikazemba kuwonedwa ndi iye tidakadziyalira mu Shelo, mophiphiritsira yotanthauza malo obisika a dziko lapansi.—Yerekezani ndi Deuteronomo 30:11-14; Amose 9:2, 3.
“Ndikadzitengera mapiko a mbanda kucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja,” anatero Davide, “kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.” (Salmo 139:9, 10) Kodi nchiyani chomwe chikutanthauzidwa ndi “mapiko a mbanda kucha”? Mawu amenewa akulongosola mwandakatulo mmene kuwala kwa mbanda kucha, monga ngati kokhala ndi mapiko, kumatambasuka mofulumira kuchokera kummawa kufika kumadzulo. Koma bwanji ngati Davide adakatenga mapiko a mbanda kucha ndi kufikira nyanja yakutali kapena zisumbu kumadzulo? Iye akadakhalabe wogonjera ku dzanja la Mulungu, kapena kulamulira ndi chitsogozo. Kupyolera mwa mzimu Wake, Yehova akakhala kumeneko kutsogoza wamasalmo mwachifundo.—Salmo 51:11.
Mdima Suli Vuto kwa Mulungu
Mtunda kapena mdima sizingaikedi munthu posafikirika ndi Mulungu. Chotero Davide akuwonjezera kuti: “Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku; ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana: Mdima ukunga kuunika.” (Salmo 139:11, 12) Munthu angabisidwe ndi mdima woti bii, monga ngati kuti waphimbidwa ndi uwo. Koma kwa Yehova iye angakhale wowonekera ngati kuti adaimirira m’kuwala kwa masana koti mbee. Palibe ndi mmodzi yense yemwe angabise Mulungu machimo alionse ochitidwira mumdima.—Yesaya 29:15, 16.
Kubindikiritsidwa sikumalepheretsa kuwonedwa ndi Mlengi wathu. Pa nkhaniyi Davide adanena kuti: “Pakuti inu munalenga imso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa; Ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. [Mafupa anga, NW] sanabisikira inu popangidwa ine mobisika, poumbidwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe [ziwalo zathupi], pakalibe chimodzi cha izo [chiwalo chimodzi chathupi].”—Salmo 139:13-16.
Yehova Mulungu, yemwe amadziŵa malingaliro athu obisika, anapanga imso za Davide. Pokhala mkatikati mwa thupi, imso ziri pakati pa ziwalo zobindikiritsidwa kwenikweni ndi zosafikirika, koma Mulungu akhoza kuziwona izo. Iye angakhozedi kuwona m’mimba ya mai, kapena m’chibaliro. Nkulekeranji, Yehova angawonedi kamwana kopangika m’katimo! Kungoganizira kokha ponena za njira zodabwitsa zimene iye anapangidwira m’chibaliro kunasonkhezera Davide kutamanda Mpangi wake. Wamasalmo mwachiwonekere analozera ku chibaliro cha mai kukhala “m’munsi mwake mwa dziko lapansi.” Kumeneko, zobindikiritsidwa ku maso a anthu koma zowonekera kwa Mulungu, mafupa a khanda, minyewa, minofu, misempha, ndi mopita mwazi, n’zolunzanitsidwa pamodzi.
Ziwalo zathupi la Davide zisanakhale zenizeni m’chibaliro cha amai wake, mawonekedwe ake anali odziwika kwa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kupangika kwa kamwana ka m’mimba kunatsatira njira yachindunji, monga ngati kulabadira malangizo olembedwa m’bukhu. Ichi chimasonyeza bwino chotani nanga nzeru ya Yehova ndi kuthekera kuwona zinthu zobindikiritsidwa! Chiyeneranso kutipangitsa kuyamikira kuti Mulungu analenga fuko la anthu ndipo ali ndi thayo la dongosolo lodabwitsa la kubala limene latulukapo kukhalapo kwathu monga anthu.
Zolinga za Mulungu Nzamtengo Wapatali Chotani Nanga!
Kuganizira za kupangika kwa khanda m’chibaliro kunapangitsa Davide kuyang’ana pa nzeru ya Mulungu. Chotero, wamasalmo anafuula kuti: “Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! (Salmo 139:17) Davide ananyadira zolinga za Yehova, ndipo ndi zambiridi kotero kuti anasangalatsidwa ndi “kuchurukira kwake.” Ngati zolinga za Mulungu nzamtengo wapatali kwa ife, tidzakhala ophunzira akhama a Malemba. (1 Timoteo 4:15, 16) Zolinga zake zolembedwa ziri “zopindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
Ponena za zolinga za Yehova, Davide ananena kuti: “Ndikaziŵerenga zichuruka koposa mchenga: ndikauka ndikhalanso nanu.” (Salmo 139:18) Popeza kuti zolinga za Mulungu nzambirimbiri kuposa ngakhale ndi mchenga, Davide atayamba kuzipenda pa kutuluka kwa dzuwa, iye sakazimaliza pofika nthawi ya kugona. Podzuka m’mawa, iye akakhalabe ndi Yehova. Uko ndiko kuti, iye akakhalabe akuŵerenga zolinga za Mulungu. M’chenicheni, popeza kuti timafunikira chitsogozo cha Yehova, kusinkhasinkha kwa pemphero pa zolinga zake ndi zifuno zingazikhala bwino lomwe m’maganizo athu panthawi yogona usiku ndi kukhala chinthu choyamba m’mawa.—Salmo 25:8-10.
Kubwezera Oipa
Popeza kuti Mulungu amapereka chitsogozo chanzeru, kodi Davide anadzimva motani ponena za okana chitsogozo chaumulungu? Iye anapemphera kuti: “Indedi, mudzawomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Popeza anena za inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.” (Salmo 139:19, 20) Davide sanayesere kupha oipa koma anapempherera kuti iwo angakumane ndi kubwezera pa dzanja la Yehova. Tiyenera kukhala ndi kawonedwe kofananako. Mwachitsanzo, tingapemperere kaamba ka kulimba mtima polankhula mawu a Mulungu pamene adani akutizunza. (Machitidwe 4:18-31) Koma sitimafuna kuchotsapo adani athu, popeza timadziŵa kuti Yehova anati: “Kubwezera chilango nkwanga, ine ndidzabwezera.”—Ahebri 10:30; Deuteronomo 32:35.
Ngati Mulungu akadati aphe oipa, amuna aliwongo la mwazi oterowo akadam’siya Davide. Iwo adali ndi cholembedwa cha liwongo la kukhetsa mwazi ndiponso adanena zinthu ponena za Yehova mogwirizana ndi malingaliro awo, osati mogwirizana ndi zolinga zake. Kuwonjezerapo, iwo anayenerera imfa kaamba ka kubweretsa chitonzo pa dzina la Mulungu mwa kulitenga ilo m’njira yopanda pake, mwinamwake mwa kuligwiritsira ntchito pamene ankapititsa patsogolo zolinga zawo zoipa. (Eksodo 20:7) Tisakhaledi aliwongo la machimo ofananawo!
Popeza kuti oipa anali ndi liwongo la kukhetsa mwazi ndi kubweretsa chitonzo pa dzina la Mulungu, Davide analengeza kuti: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: Ndiwayesa adani.” (Salmo 139:21, 22) Davide anadzimva woipidwa ndi amuna amenewa chifukwa chakuti anada Yehova mwakuya ndipo ankam’pandukira Iye. Iwo adali adani a wamasalmo chifukwa chakuti iye anada kuipa kwawo, kusapembedza, ndi kuwukira motsutsana ndi Wam’mwambamwamba.
Lolani Mulungu Akusanthuleni
Davide sanafune kufanana ndi anthu oipa, koma iye adadziwa kuti sakafunikira kukhala ndi udani pa iwo. Chotero iye anachonderera kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Mofanana ndi wamasalmo, tiyenera kufuna Mulungu kusanthula mitima yathu ndi kuwona ngati tiri ndi malingaliro osayenera. (1 Mbiri 28:9) Tiyenera kumpempha Yehova kutisanthula ife, kudziwa zolingalira zathu zamkati, ndi kuwona ngati pali njira iriyonse yowawitsa mwa ife. Ngati tavutitsidwa ndi nkhawa pa zolakwa zathu kapena ngati pali chinachake chopweteka mwa ife kapena cholakwika ndi zolinga zathu, tiyeni tipemphere modzichepetsa ndi kugonjera mokwanira ku chitsogozo cha mzimu wa Mulundu ndi uphungu wa Mawu ake. (Salmo 40:11-13) Kupyolera m’zimenezo, Bwenzi lathu labwino koposa, Yehova, angatitsogolere m’njira ya kunthaŵi yosadziŵika, kutithandiza kulondola njira yolungama yotsogolera ku moyo wosatha.
Chotero Salmo 139 imapereka chilimbikitso chenicheni. Iyo imasonyeza kuti, popeza kuti palibe chirichonse chimene chimazemba kuwonedwa ndi Atate wathu wa kumwamba, iye angatithandize m’nthaŵi iriyonse ya kusowa. (Ahebri 4:16) Kuwonjezerapo, popeza kuti Yehova amatidziŵa bwino kuposadi ndi mmene timazidziŵira ife eni, ndife achisungiko m’chisamaliro chake chachikondi. (Deuteronomo 33:27) Ngati tim’pempha iye modzichepetsa kutisanthula ndi kutidziŵitsa zifooko zaumwini, tingawongolere zinthu ndi thandizo lake. Chotero, motsimikizirika, kutidziŵa kwa Mulungu monga aliyense payekha kuyenera kuyambukira miyoyo yathu m’njira yabwino. Kuyenera kutifulumiza kukhala achilikizi okhulupirika a kulambira kowona ndi kuyenda modzichepetsa pamaso pa Yehova, amene amatidziŵa bwino.