Mungapeze Chimwemwe m’Dziko Lochititsa Tondovi!
MARIE ali ndi mkhalidwe wowala, wachimwemwe. Nzosakhulupirika kuti kokha zaka zingapo zapitazo, mkazi wazaka zakubadwa 32 ameneyu anadzilongosola mwiniwake kukhala wakufa mkati. Marie adali mkhole wa kuchita tondovi kwakukulu. Iye akulongosola kuti: “Kunali ngati mtambo wakuda waukulu umene unkachoka pang’onopang’ono.” Inde, mwachimwemwe anapezanso chimwemwe chake.
Chaka chirichonse anthu mamiliyoni zana limodzi pa dziko lonse amakanthidwa ndi kuchita tondovi kwakukulu! Vuto limeneli siliri kokha kusasangalala kumene ambirife timakhala nako kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Kuchita tondovi kwakukulu kumaloŵetsamo kusakondwa kosalekeza. Munthu wochita tondoviyo amataya chikondwerero m’moyo, samapeza ubwino m’chirichonse, ndipo amadzimva kukhala wopanda chiyembekezo ndiponso wopanda pake. Mu 1983 World Health Organization inalongosola kuti: “Pakalipano pali chikaikiro chochepa chakuti pali matenda a kuchita tondovi m’mbali zonse za dziko.”
Ophunzira Baibulo osamalitsa sakudabwa ndi lipoti limeneli. Baibulo limadziŵitsa nthaŵi zathu kukhala “masiku otsiriza,” ozindikiritsidwa ndi “nthaŵi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Makhalidwe amayanjano amene nthaŵi zakale ankapereka chilikizo m’nthaŵi za mavuto a maganizo anyonyotsoka. M’nkhani yakuti “The Age of Melancholy?”, Dr. Gerald Klerman akugwirizanitsa kuwonjezeka kwa kuchita tondovi ndi kusintha kumeneku. Iye akulongosola kuti: “Madongosolo atatu ochilikiza enieni a mayanjano anali banja, tchalitchi, ndi anansi apafupi. . . . Nchodziŵikiratu nthaŵi ino kuti madongosolo ochilikiza atatu onsewo ali m’mikhalidwe yosiyanasiyana ya kusokonezeka.”
Kudali kusokonezeka kwa banja la Marie kumene kunatsogolera ku kuda nkhaŵa kwake. “Pamene amayi anga opeza anachoka popanda kunena kalikonse, ndinadzimva kukhala wokanidwa ndiponso wosungulumwa. Ndidali ndi zaka 12 zakubadwa, ndipo mwadzidzidzi dziko langa linawoneka kukhala litazondoka,” akukumbukira motero Marie. Mwamsanga pambuyo pake anangochoka panyumba chifukwa chakuti abambo ake anayamba kumfikira ndi zolinga zachisembwere, ndipo akuvomereza kuti: “Ndinadzimva moipa, ndipo ndinataya chidaliro chirichonse mwa ine mwini.” Pamenepo kunayambika kuchita tondovi kwake kwakukulu.
Tsiku lina pamene Marie anali wochita tondovi mopambanitsa, Mboni za Yehova ziŵiri zinafikira panyumba pake. Panthaŵi yomweyo anasonyeza chikondwerero chachikulu mu uthenga wawo wosangalatsa wa Baibulo. “Kalelo, ndinkangowona kupanda pake kwa moyo ndi zinthu zina zambiri zoipa, koma tsopano ndinakhala wokhutiritsidwa kuti ndingakhale m’dziko latsopano kumene Mulungu akawongolera chisalungamo chonse. Ndi thandizo la Mulungu ndingathe kuyenerera kaamba ka dalitso loterolo; mwakutero, moyo wanga unakhaladi watanthauzo.” Pamene ankapezeka pa misonkhano ya Mboni, anapeza chikondi chenicheni ndi chilikizo lamaganizo. (Yohane 13:34, 35) Kupereka uphungu kwaluso kwa akulu a mu mpingo kunamthandizanso kusintha kulingalira kwake koipa. (Yakobo 5:14) Kuchita tondovi kwake kunayamba kutha. Unyinji wa anthu ena onga Marie, amene ali ochita tondovi ndi mikhalidwe ya dziko apeza “chimwemwe cha Yehova” mwakudziŵa chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo.—Nehemiya 8:10; 1 Timoteo 2:4.
Komabe, kodi kuchita tondovi kwa Marie kunatha panthaŵi yomweyo? Kodi tiyenera kulingalira kuti Akristu ali ochinjirizidwa ku kuchita tondovi? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyenera kuyang’anitsitsa pa vuto limeneli ndi zochititsa zake zocholoŵanacholoŵana. Kudziŵa maziko enieni a kuchita tondovi kungakupangitseni kukhala wachipambano m’kuchita ndi iko mwa inu eni kapena m’kuthandiza winawake wokanthidwa nako.
Maziko a Kuchita Tondovi Kwakukulu
M’zochitika zina kuchita tondovi kumakhala ndi zochititsa zakuthupi, monga ngati matenda, kudya mopereŵera, ndi mavuto a mahormone. Kungakhalenso kochititsidwa ndi zopatsa ululu, zoipitsa, mankhwala, ndi maallergen.a Komabe, Baibulo limavumbula kuti “zolingalira” zake za munthu zingakhale zochititsa.—Salmo 94:19.
Anthu ambiri amene amachita tondovi, mofanana ndi Marie, akumana ndi zochitika zambiri zoipa moŵaŵitsa kapena mikhalidwe yotsendereza. Ambiri amadzimva monga mmene anachitira wamasalmo kuti: “Mzimu wanga wadzala nawo mavuto . . . Zinandizinga pamodzi. Munandichotsera [Yehova] kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima.” (Salmo 88:3, 17, 18) Chotero mofanana ndi wamasalmo, amadzimva kukhala olakidwa ndi mavuto kapena zotaika ndi kuwona moyo wawo wonse kukhala wopanda chiyembekezo. Angadzimve ngati kuti ali okha mumdima ndipo kuti Mulungu weniweniyo wawataya.
Kodi nchifukwa ninji amafikira mapeto osalimbikitsa oterowo, kwenikwenidi kukhala ndi mtima wowawa? Sikuli kokha chifukwa cha mavuto awo akunja; kumakhalanso chifukwa cha malingaliro opweteka kapena kuipidwa ndi iwo eni. Amadzimva kukhala osakhoza kuchita ndi vutolo kapena kutaikiridwako. “Koma moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima,” ikulongosola tero Miyambo 15:13. Kusweka moyo koteroko kukaphatikizapo malingaliro akuti munthuyo ngwolephera kapena kuti ena amalingalira motero. Ngakhale Mkristu wa m’zaka za zana loyamba Epafrodito, pambuyo pochira ku matenda ake owopsya mkati mwa ntchito yokonzedwa ndi mpingo wakwawo, “anavutika mtima chifukwa [mpingo] udamva kuti anadwala.”—Afilipi 2:25-30.
Popeza kuti ‘mzimu wosweka uphwetsa mafupa,’ kapena kudodometsa mkhalidwe weniweni wa munthuyo, malingaliro a kusadzidalira kaŵirikaŵiri amakhala maziko a kuchita tondovi kwakukulu. (Miyambo 17:22) Kusweka moyo kungapangitsidwenso ndi kudera nkhaŵa kwakukulu ponena za mmene ena amatiwonera, kudziyesa wangwiro, mkwiyo wosathetsedwa, kusunga udani, mikangano yosathetsedwa, kapena liŵongo (lenileni kapena longoyerekeza).
Chotero zopangitsa kuchita tondovi kwakukulu nzambiri. Komabe, Marie anapeza chimwemwe chenicheni pambuyo pokhala Mkristu. “Pamenepo ndinakhala ndi chiyembekezo,” iye anatero. Koma anayenerabe kupirira kuchita tondovi kwa kanthaŵi ndithu. Kodi ndimotani mmene m’kupita kwa nthaŵi anthu oterowo angakulakire?
[Mawu a M’munsi]
a Wonani “Depression: All in One’s Head?” mu Awake! ya October 22, 1987.