Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/15 tsamba 3-6
  • Kodi Imfa ya Yesu Imatanthauzanji kwa Inu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Imfa ya Yesu Imatanthauzanji kwa Inu?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ilo Nchiyani?
  • Kodi Nlofunikiranji?
  • Zimene Ilo Limatheketsa
  • Kodi Ndani Amene Akuwomboledwa?
  • Zifukwa za Chiyamikiro
  • Kodi Mudzachitanji?
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”
    Yandikirani Yehova
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/15 tsamba 3-6

Kodi Imfa ya Yesu Imatanthauzanji kwa Inu?

“PA MAGULU ankhondo onse amene anagubapo, zoombo zankhondo zonse zimene zinamangidwapo, maupo onse a nyumba zamalamulo amene anachitidwapo, ndi mafumu onse amene analamulirapo, zonse kuika pamodzi, sizinayambukire moyo wa munthu pano pa dziko lapansi mwamphamvu monga mmene munthu mmodziyu anachitira.” Analemba tero mlembi James A. Francis ponena za Yesu Kristu.

Anthu amawona Yesu m’njira zosiyanasiyana, koma Baibulo limamzindikiritsa monga Mwana wa Mulungu ndi mwamuna wa chikondi chodzikana. Yesu anasonyeza njira yaikulu imene anasonyezera chikondi chimenecho pamene ananena za iyemwini kuti: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.”​—Mateyu 20:28.

Kodi dipo limeneli nlofunika motani? Kodi nchifukwa ninji linali lofunikira? Kodi ndani amene akuwomboledwa? Ndithudi, kodi imfa ya Yesu imatanthauzanji kwa inu?

Kodi Ilo Nchiyani?

Dipo ndi chinachake chimene chimamasula. Kuperekera wina dipo kumatanthauza kumtulutsa ku ukapolo kapena chilango mwa kupereka malipiro. M’lingaliro lauzimu, “kupereka dipo” kumatanthauza kupulumutsidwa ku chimo ndi chilango chake. Ndicho chifukwa chake Yesu anafa. Monga mmene mtumwi Wachikristu Paulo analembera kuti: “Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 6:23.

Malipiro owombola Mwamalemba amagwirizanitsidwa ndi kupereka dipo. Salmo 49:6-9 limati: “Iwo akutama kulemera kwawo; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chawo; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu: (Popeza chiombolo cha moyo wawo ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthaŵi zonse:) Kuti akhale ndi moyo osafa, osawona chibvundi.” Dipo ndi chiombolo chokwaniritsidwa ndi Mulungu, osati ndi munthu wina aliyense wopanda ungwiro.

Kodi Nlofunikiranji?

Dipo nlofunika chifukwa chakuti atate wathu woyamba waumunthu, Adamu, anachimwa. Iye motero anataya moyo wosatha wangwiro, anaweruzidwa mwachilungamo ku imfa, namwalira pomalizira pake. (Genesis 2:15-17; 3:1-7, 17-19; 5:5) Monga mbadwa zake, takhala ndi choloŵa cha uchimo ndi imfa. Paulo analemba kuti: “Monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Inde, “mwa Adamu onse amwalira.” (1 Akorinto 15:22) Chotero wamasalmo Davide molondola ananena kuti: “Ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo mai wanga anandilandira m’zoipa.”​—Salmo 51:5.

Kumasulidwa ku uchimo ndi imfa nkofunika ngati mbadwa yochimwa iriyonse ya Adamu iti ilandire moyo wamuyaya. Pamene kuli kwakuti anthu opanda ungwiro sangapereke dipo limeneli, Yehova mwachikondi anatero kupyolera mwa Yesu Kristu. Komabe, kodi nchiyani chikugulidwa ndi dipolo? Chabwino, pamene Adamu anachimwa, iye anataya moyo waumunthu wangwiro wosatha, ndi zouyenerera zake zonse ndi ziyembekezo. Chotero, chinthu chimodzimodzicho chinawomboledwa ndi nsembe ya dipo la Yesu.

Zimene Ilo Limatheketsa

Chilungamo chinakhutiritsidwa pamene mtundu wa anthu unayamba kufa, mphotho ya uchimo. Chotero dipo liri kachitidwe ka chifundo cha Mulungu ndi kukoma mtima kwachikondi. Moyo waumunthu wangwiro wa Yesu, ndi zouyenerera zake zonse ndi ziyembekezo, zinataika mu imfa ndikusatengedwanso konse, popeza kuti iye sanaukitsidwe monga munthu wa nyama ndi mwazi koma monga cholengedwa chauzimu chosafa. (1 Akorinto 15:50; 1 Petro 3:18) Chotero moyo waumunthu woperekedwa nsembe wa Yesu Kristu unapitirizabe kukhala ndi mphamvu yowombola, kapena yopereka dipo.

Monga munthu wopanda chimo, Yesu anaima m’malo ofanana ndi aja okhalidwa ndi Adamu wangwiro poyambapo. Chifukwa chokhala womvera kwa Mulungu mpaka imfa, Yesu anaikidwa kukhala Mkulu Wansembe wamkulu, ndipo anapereka mtengo wa nsembe yake yangwiro yaumunthu kumwamba. (Ahebri 9:24-26) Chifukwa chakuti Mulungu analandira mtengo wowombola umenewu, Yesu anakhoza kuombola mbadwa zokhulupirira za Adamu ku uchimo ndi imfa mwa kugwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yake chifukwa cha iwo. (1 Akorinto 6:20; 7:23; 1 Yohane 2:1, 2) Motero Yesu “anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.” (Ahebri 5:8, 9) Ichi chimawatheketsa kukhala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu mwa Mwana wake.

Kodi Ndani Amene Akuwomboledwa?

Pamenepa, kodi ndani akupindula ndi dipo limeneli? Anthu amene akusonyeza chikhulupiriro m’kakonzedwe kameneka ndipo mwakutero amabwera m’chiyanjo ndi Mulungu. Mwakumtumikira mokhulupirika, iwo angamasulidwe ku uchimo ndi mphotho yake imfa ndi kulandira moyo wamuyaya.​—Yohane 17:3.

Munthu woyambayo akanakhoza kusankha kumvera Mulungu kapena ayi. Iye anasankha kusamvera. “Adamu sananyengedwa,” koma anafa monga wochimwa wodzifunira. (1 Timoteo 2:14) Komabe, bwanji ponena za mbadwa za Adamu? Iwo angasankhe kaya kutumikira Mulungu malinga ndi kukhoza kwawo kopanda ungwiro kapena kusamvera Mlengi wawo.​—Yoswa 24:15.

Yesu ‘anadza . . . kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.’ (Marko 10:45) Koma kodi “ambiri” amenewo ndani? Mwachiwonekere Adamu sakuphatikizidwamo chifukwa chakuti anali munthu wangwiro amene mwadala anasankha kusamvera Mulungu ndi kufa monga wochimwa wodzifunira, wosalapa. Koma bwanji ponena za banja lake lalikulu, lachiŵerengero chofika mamiliyoni zikwizikwi? Ndi malipiro olingana nawo, Yesu Kristu akuchotsapo choloŵa cha kukanidwa chokhala pa banja la Adamu. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 2:5, 6.) Yesu akugwiritsira ntchito mtengo wa malipiro ake owombola mmalo mwa akhulupiriri “ambiri.”

Akhulupiriri owomboledwa akuphatikizapo ponse paŵiri Ayuda ndi Akunja, kapena anthu amitundu. Paulo akuti: “Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.” (Aroma 5:18) Mwakufera pa mtengo, “Kristu [anaombola Ayuda] ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo [mwawo]; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense wopachikidwa pamtengo.” (Agalatiya 3:13; Deuteronomo 21:23) Aroma 4:11 amasonya kwa Akunja pamene amanena kuti pamene Abrahamu, kholo la Ayuda, anali wosadulidwa, anakhala “la kholo onse akukhulupira, angakhale iwo sanadulidwa.” Chotero, pamenepa, nsembe ya dipo la Yesu imapindulira Ayuda ndi Akunja okhulupirira.

Njira yotengedwa ndi munthu aliyense imadziŵitsa kaya iye adzapindula kuchokera ku nsembe ya Yesu. Mofanana ndi Adamu, oipa mwadala samakhala ndi phindu la dipo ndi moyo wamuyaya kukakamizidwa pa iwo. Monga mmene Kristu ananenera kuti: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.” (Yohane 3:36) Dipo limatheketsanso chiukiriro kwa akufa okhala m’chikumbukiro cha Mulungu. (Yohane 5:28, 29) Ngati atsimikizira kukhala omvera ndi oyamikira, kugwira ntchito kwa mapindu a dipo kwa iwo kudzatanthauza kukhala ndi moyo kosatha. Koma kwa awo okhala ndi moyo mu “masiku otsiriza” ano, pali kuthekera kwa moyo wamuyaya osafunikira kufa mpang’ono pomwe.​—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-14, 21, 34; Yohane 11:25, 26.

Zifukwa za Chiyamikiro

Aliyense wokhumba kupindula ndi dipolo ayenera kukhala ndi chiyamikiro chozama kaamba ka ilo. Ndipo chiyamikiro choterocho nchoyenerera motani nanga! Ndiiko nkomwe, dipolo linafuna chikondi chochuluka ku mbali ya Mulungu ndi Kristu.

Yehova Mulungu anasonyeza chikondi chachikulu m’kupereka dipo kupyolera mwa imfa ya Mwana wake. Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.” (Yohane 3:16, 17) Kodi simuyenera kuyamikira kusonyeza chikondi kwa Mulungu kumeneku?

Lingalirani mowonjezereka ponena za kuya kwa chikondi cha Yehova m’kupereka dipolo. Mwana wa Mulungu asanatumizidwe ku dziko lapansi kudzakhala ndi moyo ndi kufa monga munthu wangwiro, iye analiko asanakhale munthu. Iye anali “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse,” mwa amene “zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo.” (Akolose 1:13-16) Yehova anakonda Mwana wake motani nanga! Ngakhale nditero, Mulungu sanangotumiza aliyense wa mamiliyoni a angelo olungamawo ku dziko lapansi. Chikondi chake kaamba ka mtundu wa anthu chinali chachikulukulu kotero kuti anatumiza Mwana wake woyamba kubadwa.

Lingaliraninso, chikondi chakuya chimene Yesu anasonyeza m’chigwirizano ndi dipolo. Monga cholengedwa chauzimu kumwamba, iye anali “mmisiri” wa Mulungu. Zowonadi, “[Mwana wa Mulungu ana] sekerera ndi ana a anthu.” (Miyambo 8:22-31) Komabe, sizinali zosavuta kwa iye kuchoka kumwamba, kusiya mikhalidwe yake yabwino m’chiyanjo ndi Atate wake ndi angelo zikwi makumimakumi. Ali ku malo ake akumwamba okwezedwa, Mwana wa Mulungu anakhoza kuwona mikhalidwe yoipa pa dziko lapansi ndi ngozi za uchimo ndi imfa pa mtundu wa anthu. Iye anadziŵanso kuti kupereka dipo kukafuna imfa yake. Komabe, iye ‘anatenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; . . . anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa.’ Chifukwa cha kukhulupirika koteroko, Yesu anakwezedwera ku moyo waulemerero wakumwamba. (Afilipi 2:5-11) Nchikondi chotani nanga chimene anachisonyeza kulinga ku dipolo! Kodi mukuyamikira zimene Yesu anachita?

Kodi Mudzachitanji?

Richard, mtsogoleri wachipembedzo Wachingelezi waku Chichester (c. 1198-1253) nthaŵi ina anapemphera kuti amuna ndi akazi “amdziŵe Yesu Kristu bwinopo, kumkonda iye moposerapo, ndi kumtsatira mosamalitsa koposerapo.” Nsembe ya dipo la Yesu mowonadi imapereka chifukwa chabwino cha kumdziŵa, kumkonda, ndi kumtsatira.

Ngati sipadakakhala dipo, monga ochimwa tikanafa popanda chiyembekezo, popeza kuti “mbola ya imfa ndiyo uchimo.” (1 Akorinto 15:56) Pamenepa, kodi mungachitenji kuti mupulumutsidwe ku imfa yotulukapo chifukwa cholumidwa ndi uchimo? Mufunikira kuphunzira ponena za kakonzedwe ka Mulungu kaamba ka chipulumutso kupyolera mwa Yesu Kristu. Ndiyeno muyenera kuwonetsa kuti mukusonyeza chikhulupiriro m’dipolo. Motani? Mwakusonyeza chiyamikiro cha kumtima kaamba ka ilo, kudzipereka kwa Mulungu, ndi kumawuza ena za kakonzedwe kameneka ka chipulumutso.

Njira imeneyi ingakuikeni pakati pa “khamu lalikulu” omwe “akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,” Yesu Kristu. (Chibvumbulutso 7:9, 14) Chawo chiri chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’paradaiso wa padziko lapansi. (Luka 23:43) Inde, ndipo inu mungakhale mbali ya gulu lachimwemwe limenelo, ngati imfa ya Yesu iridi chinachake chamtengo wapatali kwa inu.

[Chithunzi patsamba 4]

Yesu wopanda chimo anaima m’malo ofanana ndi aja okhalidwa ndi Adamu wangwiro poyambapo

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi mumayamikira tanthauzo lenileni la imfa ya Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena