Kodi “Chofunikira” Nchiyani?
BUKHU LAMAKEDZANA la W limeneli la Mauthenga Abwino lachita mbali yofunika m’kutembenuzidwa kwa ndemanga yopangidwa ndi Yesu kwa Marita, mlongo wa bwenzi lake lapamtima Lazaro. Pamene Yesu anachezera banjalo, Marita anachilingalira kukhala chofunika koposa kukonzera Yesu chakudya chabwino, koma mokoma mtima anamlangiza kuti atsatire chitsanzo cha mbale wake Mariya, yemwe anakhala pansi ku mapazi ake akumvetsera kwa iye. Iye anati: “Koma chisoŵeka chinthu chimodzi, pakuti Mariya anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.”—Luka 10:42.
Mawu ameneŵa akutembenuza lemba Lachigiriki la mu 1881 lokonzedwa ndi Westcott ndi Hort, maziko a New World Translation. Mawu amtsinde a 1984 Reference Edition ya Baibulo limeneli amasonyeza kuti kuŵerenga kumeneku kunachokera ku malembo apamanja a Sinai (א) ndi Vatican (B), onse aŵiri oimira mtundu umodzimodzi wa lemba. Koma malembo apamanja a Alexandria (A) amaŵerenga kuti: “Komabe, chinthu chimodzi, nchofunika. Kwa iye . . . ” Monga mmene mawu amtsinde akusonyezera, Bukhu Lamakedzana W, limodzi ndi gumbwa wa Chester Beatty (P45) ndi gumbwa wa Bodmer (P75), onse aŵiri a m’zaka za zana lachitatu C.E., amavomerezana ndi matembenuzidwe otchulidwa pomalizirawa. Koma malembo apamanja onsewa anavumbuluka patapita nthaŵi yaitali Westcott ndi Hort atafalitsa kale malemba awo m’chaka cha 1881, kotero kuti sanakhale ndi mpata wolingalira matembenuzidwe ena ameneŵa. Komabe, matembenuzidwe aliwonse a malemba amene tingasankhe kuwazindikira lerolino, Yesu akutiuza momvekera bwino kuika zinthu zauzimu m’malo oyamba m’miyoyo yathu—chilangizo chimene tingachite bwino kuchitsatira.